Opani Yehova, Wakumva Pemphero
“Wakumva pempero inu, zamoyo zidzadza kwa inu.”—SALMO 65:2.
1. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuyembekezera Yehova kukhala ndi ziyeneretso kaamba ka ofuna kumfikira m’pemphero?
YEHOVA MULUNGU ndiye “Mfumu ya nthaŵi zosatha.” Iye ‘Ngwakumvanso pemphero,’ amene “zamoyo zonse zidza kwa iye.” (Chivumbulutso 15:3; Salmo 65:2) Koma kodi izo ziyenera kudza motani kwa iye? Mafumu a padziko lapansi amalamulira zinthu zonga kavalidwe ndi mkhalidwe zofunika kwa ololedwa pamaso pawo. Pamenepa, ndithudi, tiyenera kuyembekezera Mfumu Yosathayo kukhala ndi ziyeneretso zimene ziyenera kufikiridwa ndi aliyense wofuna kufika pamaso pake ndi pembedzero ndi chiyamiko.—Afilipi 4:6, 7.
2. Kodi ndi mafunso otani omwe amabuka pankhani ya pemphero?
2 Kodi Mfumu Yosathayo imafunanji kwa omfikira m’pemphero? Kodi ndani angapemphere ndi kumvedwa? Ndipo kodi ayenera kupempherera chiyani?
Kufikira Mfumu Yosatha
3. Kodi ndi zitsanzo ziti zimene mungapereke za mapemphero operekedwa ndi atumiki oyambirira a Mulungu, ndipo kodi iwo anamfikira iye kupyolera mwa nkhoswe?
3 Asanachimwe, Adamu, “mwana wa Mulungu,” mwachiwonekere ankakambitsirana ndi Mfumu yosathayo. (Luka 3:38; Genesis 1:26-28) Pamene mwana wamwamuna wa Adamu Abele anapereka “mwana woyamba wankhosa zake” kwa Mulungu, mosakaikira choperekachi chinatsagana ndi mawu a pembedzero ndi chiyamiko. (Genesis 4:2-4) Nowa, Abrahamu, Isake, ndi Yakobo anamanga maguwa ansembe ndi kufikira Yehova m’pemphero ndi zopereka zawo. (Genesisi 8:18-22; 12:7, 8; 13:3, 4, 18; 22:9-14; 26:23-25; 33:18-20; 35:1, 3, 7) Ndipo mapemphero a Solomo, Ezara, ndi wamasalmo wouziridwa mwaumulungu amasonyeza kuti Aisrayeli anafikira Mulungu popanda nkhoswe iriyonse.—1 Mafumu 8:22-24; Ezara 9:5, 6; Salmo 6:1, 2; 43:1; 55:1; 61:1; 72:1; 80:1; 143:1.
4. (a) Kodi ndi njira yatsopano yotani yofikira Mulungu m’pemphero imene inakhazikitsidwa m’zaka za zana loyamba? (b) Kodi nchifukwa ninji kuli koyenerera mwapadera kuti pemphero liperekedwe m’dzina la Yesu?
4 Njira yatsopano yofikira Mulungu m’mpemphero inakhazikitsidwa m’zaka za zana loyamba za Nyengo Yathu ya Onse. Inali kupyolera mwa Mwana wake, Yesu Kristu, amene anali ndi chikondi chapadera kaamba ka anthu. M’kukhalako kwake asanakhale munthu, Yesu anatumikira mwachisangalalo monga “mmisiri,” wokonda zinthu zogwirizanitsidwa ndi anthu. (Miyambo 8:30, 31) Monga munthu padziko lapansi, Yesu mwachikondi anathandiza mwauzimu anthu opanda ungwiro, anachiritsa odwala, ndipo ngakhale kuukitsa akufa. (Mateyu 9:35-38; Luka 8:1-3, 49-56) Kuposa zonse, Yesu ‘anapereka moyo wake monga dipo kaamba ka ambiri.’ (Mateyu 20:28) Pamenepa, nkoyenerera chotani nanga, kuti awo opindula ndi dipoli amfikire Mulungu kupyolera mwa ameneyu amene amakonda anthu kwambiri! Iyi tsopano ndiyo njira yokha yofikira Mfumu Yosatha, pakuti Yesu iye mwiniyo anati: “Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa ine” ndipo, “Ngati mudzapempha Atate kanthu, adzakupatsani inu m’dzina langa.” (Yohane 14:6; 16:23) Kupempha zinthu m’dzina la Yesu kumatanthauza kumzindikira kukhala njira yofikira Wakumva pempheroyo.
5. Kodi ndi uti umene uli mkhalidwe wa Mulungu kulinga ku dziko la anthu, ndipo kodi umenewu uli nchiyani ndi pemphero?
5 Makamaka ife tiyenera kuzindikira chikondi chimene Yehova anasonyeza mwa kupereka dipolo. Yesu anati: “Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi [la anthu] kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asataike, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Kuya kwa chikondi cha Mulungu kwafotokozedwa bwino lomwe m’mawu aŵa a wamasalmo: “Pakuti monga mmwamba mutalikira ndi dziko lapansi, motero chifundo chake chikulira iwo akumuwopa iye. Monga kummaŵa kutanimpha ndi kumadzulo, momwemo anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu. Monga atate achitira ana ake chifundo, Yehova achitira chifundo iwo akumuwopa iye. Popeza adziŵa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi.” (Salmo 103:11-14) Nkotsitsimula maganizo chotani nanga kudziŵa kuti mapemphero a Mboni za Yehova zodzipereka amapita kwa Atate wachikondi woteroyo kupyolera mwa Mwana wake.
Mwaŵi Wokhala ndi Malire
6. Kodi Yehova ayenera kufikiridwa mumkhalidwe wotani m’pemphero?
6 Mafumu aumunthu samangovomereza aliyense kuloŵa m’nyumba yachifumu. Kukakambirana ndi mfumu uli mwaŵi wokhala ndi malire. Choteronso pemphero kwa Mfumu yosatha. Ndithudi, omfikira kupyolera mwa Yesu Kristu ndi kuzindikira koyenerera ukulu wa ulemerero wa Mulungu angayembekezere kumvedwa. Mfumu Yosatha iyenera kufikiridwa mumkhalidwe waulemu, wopembedza. Ndipo okhumba kumvedwawo ayenera kusonyeza “kuwopa Yehova.”—Miyambo 1:7.
7. Kodi nchiyani chimene chiri “kuwopa Yehova”?
7 Kodi “kuwopa Yehova” nchiyani? Ndiko ulemu wa kwa Mulungu wochokera mumtima, wokhala ndi mantha abwino a kusamkondweretsa. Mantha ameneŵa amachokera m’kuyamikira kwenikweni chifundo chake chachikondi ndi ubwino. (Salmo 106:1) Kumaphatikizapo kumvomereza kukhala Mfumu yosatha, imene iri ndi kuyenera ndi mphamvu zopereka chilango, kuphatikizapo imfa, kwa aliyense wosamumvera. Anthu osonyeza kuwopa Yehova angapemphere kwa iye ndi kuyembekezera kumvedwa.
8. Kodi nchifukwa ninji Mulungu amamva mapemphero a omuwopa?
8 Mwachibadwa, Mulungu samayankha mapemphero a anthu oipa, osakhulupirira, ndi odzilungamitsa. (Miyambo 15:29; Yesaya 1:15; Luka 18:9-14) Koma amene amawopa Yehova amamvedwa chifukwa chakuti achita mogwirizana ndi miyezo yake yolungama. Komabe, iwo achita zambiri. Owopa Yehova adzipereka kwa Mulungu m’pemphero ndi kusonyeza kumeneku mwa kuloŵa muubatizo wammadzi. Chotero iwo amakhala ndi mwaŵi wopanda malire wa pemphero.
9, 10. Kodi anthu osabatizidwa angapemphere ndi kuyembekezera kumvedwa?
9 Kuti amvedwe ndi Mulungu, munthu ayenera kufotokoza zinthu m’pemphero zimene ziri zogwirizana ndi chifuniro chaumulungu. Inde, iye ayenera kukhala wowona mtima, komatu zambiri zimafunika. “Wopanda chikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa [Mulungu],” analemba motero mtumwi Paulo, “pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti aliko, ndi kuti ali wobwezera mphoto iwo akumfuna iye.” (Ahebri 11:6) Eya, pamenepa, kodi anthu osabatizidwa angalimbikitsidwe kupemphera ndi kuyembekezera kumvedwa?
10 Pozindikira kuti pemphero ndimwaŵi wokhala ndi malire, Mfumu Solomo anapempha Yehova kuti amve kokha alendo omwe anapempherera molunjika kachisi wa Mulungu mu Yerusalemu. (1 Mafumu 8:41-43) Zaka mazana ambiri pambuyo pake, mlendo Wakunja Korneliyo “anapembedzera Mulungu kosaleka” monga munthu wopembedza. Atapeza chidziŵitso cholongosoka, Korneliyo anadzipereka yekha kwa Mulungu, yemwe pambuyo pake anampatsa mzimu woyera. Pambuyo pa izi, Korneliyo ndi Akunja ena anabatizidwa. (Machitidwe 10:1-44) Mofanana ndi Korneliyo, aliyense lerolino wopita patsogolo kulinga kukudzipereka angalimbikitsidwe kupemphera. Koma munthu aliyense payekha yemwe ali wosawona mtima m’kuphunzira Malemba, wosadziŵa zofunika zaumulungu kaamba ka pemphero, ndi amene sanasonyezebe mkhalidwe wokondweretsa Mulungu sanganenedwe kuti ngwowopa Yehova, kuti ali ndi chikhulupiriro, kapena kuti akumfunafuna iye mowona mtima. Munthu woteroyo sangathe kupereka mapemphero ovomerezedwa ndi Mulungu.
11. Kodi chiyani chimene chachitika kwa ena omwe ankapita patsogolo kulinga kukudzipereka, ndipo kodi iwo ayenera kudzifunsa chiyani?
11 Anthu ena amene poyambapo ankapita patsogolo kulinga kukudzipereka pambuyo pake angawonekere kukhala akuzengereza. Ngati iwo alibe chikondi chokwanira cha pa Mulungu m’mitima yawo cha kupanga kudzipereka kotheratu kwa iye, ayenera kudzifunsa iwo eni kaya ngati adakali ndi mwaŵi wabwino koposawu wa pemphero. Mwachiwonekere iwo alibe, popeza kuti omfikira Mulungu ayenera kumfunafuna mowona mtima ndi chilungamo ndi chifatso. (Zefaniya 2:3) Munthu aliyense wowopadi Yehova ndiye wokhulupirira amene amapanga kudzipereka kwa Mulungu ndi kukusonyeza mwa kubatizidwa. (Machitidwe 8:13; 18:8) Ndipo ndi okhulupirira obatizidwa okha omwe ali ndi mwaŵi wopanda malire wofikira Mfumu Yosatha m’mpemphero.
“Kupemphera mu Mzimu Woyera”
12. Kodi ndiliti pamene kukunganenedwe kuti munthu ‘akupemphera mumzimu woyera’?
12 Pamene munthu adzipereka kwa Mulungu ndi kukusonyeza mwa kubatizidwa, amakhala woyenerera ‘kupemphera mu mzimu woyera.’ Pamfundoyi, Yuda analemba kuti: “Koma inu, okondedwa, podzimangira nokha pachikhulupiriro chanu choyeretsetsa, ndi kupemphera mumzimu woyera, mudzisunge nokha m’chikondi cha Mulungu, ndi kulindira chifundo cha Ambuye wathu Yesu Kristu, kufikira moyo wosatha.” (Yuda 20, 21) Munthu amapemphera mu mzimu woyera pamene apemphera mosonkhezeredwa ndi mzimu wa Mulungu, kapena mphamvu yogwira ntchito, ndi mogwirizana ndi zinthu zolembedwa m’Mawu Ake. Malemba, olembedwa mouziridwa ndi mzimu wa Yehova, amatisonyeza mmene tingapempherere ndi zimene tiyenera kupempha m’pemphero. Mwachitsanzo, tingapemphere mwachidaliro kuti Mulungu atipatse mzimu wake woyera. (Luka 11:13) Pamene tipemphera ndi mzimu woyera, mapemphero athu amavumbula mkhalidwe wa mtima umene Yehova amakonda.
13. Ngati tipemphera mu mzimu woyera, kodi nchiyani chimene tidzapeŵa, ndipo ndi uphungu wotani wa Yesu umene tidzagwiritsira ntchito?
13 Pamene tipemphera ndi mzimu woyera, mapemphero athu samakhala odzala ndi mawu ocholowana kwenikweni. Iwo samaphatikizamo mawu otchulidwa mobwerezabwereza. Ayi, iwo samakhala ndi zithokozo zopanda pake kotheratu, zitamando zosawona mtima. Mapemphero a mtundu umenewo ngochuluka m’Chikristu Chadziko ndi mbali yotsala ya Babulo Wamkulu, ulamuliro wa dziko wa chipembedzo chonyenga. Koma Akristu owona amalabadira uphungu wa Yesu: “Pamene mukupemphera simuyenera kukhala ngati achinyengo; popeza kuti amakonda kupemphera ataimirira m’masunagoge ndi m’ngondya za makwalala aakulu, kotero kuti awonedwe ndi anthu . . . ndipo pamene mukupemphera musamabwerezabwereza mawu monga mmene amachitira akunja; popeza kuti iwo [molakwa] amaganiza kuti adzamvedwa chifukwa cha kuchuluka kwa zimene anena. Chotero musafanane nawo.”—Mateyu 6:5-8, Byington.
14. Kodi ndindemanga zabwino zotani zimene zapangidwa ndi ena ponena za pemphero?
14 M’kuwonjezera pa Yesu ndi alembi a Baibulo, ena anena mawu omveka onena za pemphero. Mwachitsanzo, mlembi Wachingelezi John Bunyan (1628-88) anati: “Pemphero ndilo kutsanuliridwa kowona mtima, ndi kwanzeru, kwa moyo kwa Mulungu, kupyolera mwa Kristu, m’mphamvu ndi mothandizidwa ndi Mzimu, kupempha zinthu zimene Mulungu walonjeza.” Minisitala Wachiprotestante Thomas Brooks (1608-80) anati: “Mulungu samamvetsera katchulidwe ka mawu a mapemphero anu, kuti ngaluntha motani; kapena kutalika kwa mapemphero anu, kuti ngautali wotani; kapena kuchuluka kwa mapemphero anu, kuti ndi angati; osatinso dongosolo la mapemphero anu, kuti ngolongosoka motani; koma iye amayang’ana pakuwona mtima kwawo.” Pandemanga zimenezi pangawonjezeredwe mawu awa a Bunyan: “Popemphera nkwabwino kukhala ndi mtima wopanda mawu, kuposa kukhala ndi mawu opanda mtima.” Koma ngati tiri owona mtima ndi kufikitsa ziyeneretso zofunika zaumulungu, kodi tingatsimikizire motani kuti Mfumu yosatha idzamva mapemphero athu?
Samapita Osamvedwa
15. Monga mfundo yaikulu, kodi nchiyani chimene Yesu ananena pa Luka 11:5-8?
15 Yehova Mulungu samatseka makutu kumapemphero a atumiki ake odzipereka. Izi zinamveketsedwa m’mawu othutsa mtima a Yesu pamene ophunzira ake anafunsa malangizo onena za pemphero. Mwapang’ono iye anati: “Ndani wa inu adzakhala ndi bwenzi lake, nadzapita kwa iye pakati pa usiku, nadzati kwa iye, bwenzi, ndibwereke mikate itatu; popeza wandidzera bwenzi lochokera paulendo, ndipo ndiribe chompatsa; ndipo iyeyu wamkatimo poyankha akati, usandivuta; pakhomo mpotseka tsopano, ndipo ana anga ali nane pamodzi pogona; sindikhoza kuuka ndi kukupatsa? Ndinena ndi inu, ngakhale sadzauka ndi kumpatsa, chifukwa ali bwenzi lake, koma chifukwa cha liwuma lake adzauka nadzampatsa iye zirizonse azisoŵa.” (Luka 11:1, 5-8) Kodi ndiiti imene inali mfundo ya fanizoli?
16. Ponena za pemphero, kodi Yesu anafuna kuti tichitenji?
16 Ndithudi Yesu sanatanthauze kuti Yehova ngwosafunitsitsa kutithandiza. Mmalo mwake, Kristu akufuna kuti tikhulupirire Mulungu kotheratu ndi kumkonda mokwanira kupemphera mosaleka. Motero, Yesu anapitiriza kuti: ‘Ndinena ndi inu, pitirizani kupempha, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; pitirizani kufunafuna, ndipo mudzapeza; pitirizani kugogoda, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu. Pakuti yense wakupempha alandira; ndi wofunayo apeza; ndi iye amene agogoda adzamtsegulira.’ (Luka 11:9, 10) Pamenepa, motsimikizirika, tiyenera kupitirizabe kupemphera pamene tikumana ndi chizunzo, kuvutika ndi chofooka china chaumwini chokhalitsa, kapena chiyeso china chirichonse. Yehova nthaŵi zonse ngwokonzekera kuthandiza atumiki ake okhulupirika. Iye samatiuza konse kuti: “Osandivuta.”
17, 18. (a) Kodi Yesu anatilimbikitsa motani kupempha mzimu woyera? (b) Kodi ndimotani mmene Yesu anayerekezera zochita za kholo la padziko lapansi ndi za Mulungu?
17 Ngati titi tisangalale ndi unansi wathithithi ndi Atate wathu wakumwamba, tifunikira mzimu wake woyera, kapena mphamvu yogwira ntchito. Motero, Yesu anapitiriza kuti: “Ndipo ndani wa inu ali atate, mwana wake akadzampempha mkate, adzampatsa mwala? Kapena nsomba, nadzamninkha njoka mmalo mwa nsomba? Kapena akadzampempha dzira kodi adzampatsa chinkhanira? Potero, ngati inu okhala oipa, mudziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wakumwamba adzapatsa mzimu woyera kwa iwo akumpempha iye? (Luka 11:11-13) Mateyu 7:9-11 amanena za kupatsa mwala mmalo mwa mkate. Tanthauzo la mawu a Yesu limamveketsedwa mowonjezereka ngati titazindikira kuti mkate wa maiko amakedzana a m’Baibulo unali wampangidwe ndi ukulu wofanana ndi mwala wobulungira, waphanthiphanthi. Mitundu ina ya njoka imafanana ndi mitundu yakutiyakuti ya nsomba, ndipo pali chinkhanira chaching’ono choyera chimene chimafanana pang’ono ndi dzira. Koma atapemphedwa mkate, nsomba, kapena dzira, kodi ndi atate wotani amene angapatse mwana wake mwala, njoka, kapena chinkhanira?
18 Kenako Yesu anayerekeza ntchito za kholo lapadziko lapansi ndi za Mulungu kuziŵalo za banja Lake la olambira. Ngati ife, ngakhale kuti ndife oipa chifukwa cha uchimo wobadwa nawo, timapatsa ana athu mphatso zabwino, tiyenera kuyembekezera koposa chotani nanga Atate wathu wakumwamba kupatsa mphatso yabwino kwambiri ya mzimu wake woyera kwa atumiki ake okhulupirika omwe amaipempha modzichepetsa!
19. (a) Kodi nchiyani chomwe chikutanthauzidwa ndi mawu a Yesu olembedwa pa Luka 11:11-13 ndi Mateyu 7:9-11? (b) Ngati titsogozedwa ndi mzimu woyera, kodi tidzaziwona motani ziyeso zathu?
19 Mawu a Yesu akumveketsa kuti tiyenera kumpempha Mulungu mzimu wake woyera wochuluka. Titatsogozedwa nawo, ‘sitidzadandaula ndi zofunika zathu m’moyo’ ndi kuwona ziyeso ndi zokhumudwitsa kukhala zotivulazadi. (Yuda 16) Zowona, “munthu wobadwa ndi mkazi ngwamasiku oŵerengeka, nakhuta mavuto,” ndipo ambiri sanakhale ndi moyo kuwona kutha kwa mavuto awo kapena kuŵaŵidwa mtima. (Yobu 14:1) Koma tiyeni tisalole kuwona ziyeso zathu kukhala miyala, njoka, ndi zinkhanira zimene Wakumva pemphero watipatsa mwanjira ina yake. Ndiye phata lenileni la chikondi ndipo samayesa aliyense ndi zinthu zoipa. Mmalo mwake, amatipatsa ‘mphatso iriyonse yabwino ndi yangwiro.’ Pomalizira, iye adzalungamitsa chirichonse mokomera onse omkonda ndi kumuwopa. (Yakobo 1:12-17; 1 Yohane 4:8) Awo amene akhala akuyenda m’chowonadi kwa zaka zambiri amadziŵa kuchokera m’zokumana nazo zawo kuti zina za ziyeso zawo zovutitsa koposa, kupyolera mwa pemphero ndi chikhulupiriro, zakhoza kuwapindulitsa ndipo zawonjezera zipatso za mzimu wa Mulungu m’miyoyo yawo. (3 Yohane 4) Kwenikweni, kodi tingaphunzire kudalira pa Atate wathu wakumwamba mwanjira yabwino kwambiri yotani ndi kuthandizidwa kukulitsa zipatso zamzimu za chikondi, chisangalalo, mtendere, kuleza mtima, chifundo, ubwino, chikhulupiriro, chifatso, ndi kudziletsa kuposa iyi?—Agalatiya 5:22, 23.
20. Kodi mawu a Yesu olembedwa pa Luka 11:5-13 ayenera kukhala ndi chiyambukiro chotani pa ife?
20 Motero mawu a Yesu olembedwa pa Luka 11:5-13 amatipatsa chitsimikiziro chodalitsika cha chikondi cha Yehova ndi chisamaliro chachikondi. Zimenezi ziyenera kudzaza mitima yathu ndi chiyamikiro chakuya koposa ndi chikondi. Ziyenera kulimbikitsa chikhulupiriro chathu ndi kuwonjezera chikhumbo chathu cha kupita kaŵirikaŵiri ku chopondapo mapazi cha Mfumu Yosatha ndi kukhala pamaso pake mwachikondi. Ndiponso, mawu a Yesu amatitsimikizira kuti sadzatibweza tiri opanda kanthu. Atate wathu wakumwamba amakondwera kwenikweni kutiwona tikutulira nkhaŵa zathu pa iye. (Salmo 55:22; 121:1-3) Ndipo pamene ife, monga atumiki ake odzipereka okhulupirika, tipempha mzimu wake woyera, iye amatipatsa mosatonza. Ameneyu ndiye Mulungu wathu wachikondi, ndipo tingakhale ndi chikhulupiriro chokwanira chakuti Ngwakumva mapemphero athu.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi tiyenera kufikira Mulungu m’pemphero kupyolera mwa yani, ndipo chifukwa ninji?
◻ Kodi ndi m’njira yotani mmene pemphero liriri mwaŵi wokhala ndi malire?
◻ Kodi kumatanthauzanji “kupemphera mumzimu woyera”?
◻ Kodi mungatsimikizire motani Mwamalemba kuti mapemphero a Mboni zobatizidwa za Yehova amamvedwa?
[Zithunzi patsamba 14]
Monga mmene Atate aumunthu amapatsira mphatso zabwino kwa ana awo, Yehova amapatsa mzimu woyera kwa ompempha