-
Yehova Amapereka “Mzimu Woyera kwa Amene Akum’pempha”Nsanja ya Olonda—2006 | December 15
-
-
11. Kodi Yesu anafotokoza motani mmene fanizo la atate ndi mwana wake likugwirizanira ndi pemphero?
11 Fanizo la Yesu la wolandira mlendo wolimbikira likusonyeza khalidwe la munthu wokhulupirira amene amapempherayo. Fanizo lotsatira likusonyeza khalidwe la Yehova Mulungu amene amamva mapempherowo. Yesu anafunsa kuti: “Kodi alipo tate pakati panu kapena, amene mwana wake atam’pempha nsomba angam’patse njoka m’malo mwa nsomba? Kapena atam’pempha dzira iye n’kum’patsa chinkhanira?” Yesu anapitiriza kufotokoza fanizolo kuti: “Choncho ngati inu, ngakhale muli oipa, mumadziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kuli bwanji Atate wakumwamba! Iye adzapereka mowolowa manja mzimu woyera kwa amene akum’pempha.”—Luka 11:11-13.
12. Ndi motani mmene fanizo la atate amene akumva pempho la mwana wake limasonyezera kuti Yehova amafuna kutiyankha mapemphero athu?
12 Pogwiritsa ntchito chitsanzo cha atate amene anapereka kwa mwana wake chimene anali kufuna, Yesu anafotokoza bwino mmene Yehova amamvera ndi anthu amene amapemphera kwa iye. (Luka 10:22) Choyamba, taonani kusiyana pakati pa mafanizo awiriwa. Mosiyana ndi mwamuna wa mu fanizo loyamba lija amene ankanyinyirika kuthandiza mnzake, Yehova ali monga kholo laumunthu, limene lili tcheru kufuna kuyankha pempho la mwana wake. (Salmo 50:15) Yesu anasonyezanso kuti Yehova ali ndi mtima wofuna kutithandiza mwa kufotokoza za atate waumunthu n’kumuyerekezera ndi atate wakumwamba. Iye anati, ngati atate waumunthu, ngakhale ‘ali woipa’ chifukwa cha uchimo wobadwa nawo, amapatsa mwana wake mphatso yabwino, kuli bwanji Atate wathu wakumwamba, pokhala wokoma mtima, adzapereka mzimu woyera kwa banja lake la anthu omulambira.—Yakobe 1:17.
-
-
Yehova Amapereka “Mzimu Woyera kwa Amene Akum’pempha”Nsanja ya Olonda—2006 | December 15
-
-
14. (a) Kodi ndi maganizo olakwika ati amene amavutitsa anthu ena akakumana ndi ziyeso? (b) Tikamakumana ndi ziyeso, n’chifukwa chiyani tingapemphere kwa Yehova ndi chidaliro?
14 Fanizo la Yesu la atate wachikondi likutsindikanso kuti, ubwino wa Yehova umaposa ubwino umene kholo lililonse laumunthu lingasonyeze. Choncho, sitiyenera kuganiza kuti ziyeso zimene timakumana nazo zikutanthauza kuti Mulungu sakukondwera nafe. Satana, yemwe ndi mdani wathu wamkulu, ndi amene amafuna kuti tiziganiza choncho. (Yobu 4:1, 7, 8; Yohane 8:44) Maganizo odziimba mlandu oterowo, sachokera m’Malemba. Yehova satiyesa “ndi zinthu zoipa.” (Yakobe 1:13) Satipatsa chiyeso chonga njoka kapena mayesero onga chinkhanira. Atate wathu wakumwamba amapereka “zinthu zabwino kwa onse om’pempha.” (Mateyo 7:11; Luka 11:13) Indedi, tikazindikira kwambiri za ubwino wa Yehova ndiponso kuti amafuna kutithandiza, tidzalimbikitsidwa kwambiri kuti tizipemphera ndi chidaliro. Tikamatero, ifenso tidzatha kulankhula mawu ofanana ndi a wamasalmo amene analemba akuti: “Koma Mulungu anamvadi; anamvera mawu a pemphero langa.”—Salmo 10:17; 66:19.
-