Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Magwero a Chimwemwe
MKATI mwa utumiki wake mu Galileya, Yesu anapanga zozizwitsa, ndipo iye tsopano akubwereza izi mu Yudeya. Mwachitsanzo, iye akutulutsa mwa munthu chiwanda chomwe chinamuletsa iye kulankhula. Makamu akuzizwitsidwa, koma osuliza akudzutsa chitsutso chofanana ndi chomwe chinadzutsidwa mu Galileya. “Ndi Beelzebule mkulu wa ziwanda amatulutsa ziwanda,” iwo akudzinenera tero. Ena akufuna umboni wokulira kuchokera kwa Yesu ponena za chizindikiritso chake, ndipo akuyesera kumuyesa iye mwa kufunsa kaamba ka chizindikiro chochokera kumwamba.
Akumadziŵa chimene iwo akulingalira, Yesu akupereka yankho lofananalo kwa osuliza ake mu Yudeya monga limene anapereka kwa awo a mu Galileya. Iye akuwona kuti ufumu uliwonse wogawanika mkati mwake upasuka. “Chotero,” iye akufunsa, “ngati Satana agawanika kudzitsutsa mwini, udzaima bwanji ufumu wakwe?” Iye akusonyeza malo owopsya a asulizi ake mwa kunena kuti: “Ngati ine nditulutsa ziwanda ndi chala cha Mulungu, pamenepo ufumu wa Mulungu wafikira inu.”
Awo owona zozizwitsa za Yesu ayenera kuvomereza ku izo m’njira yofanana monga mmene anachitira awo amene mazana ambiri kumbuyoko anawona Mose akuchita chozizwitsa. Iwo anafuula: “Chiri chala cha Mulungu!” Chinalinso “Chala cha Mulungu” chomwe chinasema Malamulo Khumi pa magome a miyala. Ndipo “chala cha Mulungu”—mzimu wake woyera, kapena mphamvu yogwira ntchito—chiri chimene chikutheketsa Yesu kutulutsa ziwanda ndi kuchiritsa odwala. Chotero Ufumu wa Mulungu ndithudi wafikira osuliza amenewa, popeza Yesu, Mfumu yoikidwa ya Ufumuwo, ali pamenepo pakati pawo.
Yesu kenaka akuchitira chitsanzo kuti kuthekera kwake kwa kutulutsa ziwanda uli umboni wa mphamvu yake pa Satana, mongadi mmene munthu wamphamvu amabwera ndi kulaka munthu wokonzekeretsedwa ndi zida wochinjiriza nyumba yake yachifumu. Iye akubwerezanso fanizo limene analikamba mu Galileya ponena za mzimu wonyansa umene utuluka mwa munthu, koma pamene munthuyo sadzaza nyumbayo ndi zinthu zabwino, mzimuwo ubwerera ndi ina isanu ndi iŵiri, ndipo mkhalidwe wa munthuyo ukhala woipirapo kuposa poyamba.
Pamene akumvetsera pa ziphunzitso zimenezi, mkazi kuchokera m’khamulo wasonkhezeredwa kufuula mokwezeka: “Yodala mimba imene idakubalani ndi mawere amene mudayamwa!” Popezakuti chikhumbo cha mkazi aliyense Wachiyuda chiri kukhala mayi wa mneneri ndipo makamaka Mesiya, chiri chomvekera kuti mkazi ameneyu anganene chimenechi. Mwachidziŵikire iye analingalira kuti Mariya akakhala wachimwemwe mwapadera chifukwa chokhala mayi wa Yesu.
Ngakhale kuli tero, Yesu mwamsanga akuwongolera mkaziyo ponena za magwero owona a chimwemwe. “Ayi”, iye akuyankha, “m’malomwake, Odala iwo akumva mawu a Mulungu nawasunga!” Yesu sanasonyeze mpang’ono pomwe kuti mayi wakwe, Mariya, ayenera kupatsidwa ulemu wapadera. M’malomwake, iye anasonyeza kuti chimwemwe chowona chimapezeka mkukhala mtumiki wokhulupirika wa Mulungu, osati m’kugwirizana kapena zokwaniritsa zirizonse za kuthupi.
Monga mmene iye anachitira mu Galileya, Yesu akupitirizanso kudzudzula anthuwo kaamba ka kufunsa chizindikiro chochokera kumwamba. Iye akuwawuza iwo kuti chizindikiro sichidzapatsidwa koma chizindikiro cha Yona. Yona anakhala chizindikiro ponse paŵiri mwakukhala kwake masiku atatu mu nsomba ndi mwa kulalikira kwake molimba mtima, komwe kunatulukapo m’kusonkhezeredwa kwa anthu a ku Nineve kupala. “Ndipo, onani!” Yesu akutero, “wakuposa Yona ali pano.” Mofananamo, mfumu yaikazi ya ku Seba inazizwa pa nzeru ya Solomo. “Ndipo, onani!” Yesu akunenanso tero, “woposa Solomo ali pano.”
Yesu akulongosola kuti pamene munthu ayatsa nyali, iye samaiyika iyo m’chipinda chapansi kapena pansi pa muyezo koma pa choikapo nyali chake kotero kuti anthu awone kuwunika. Mwinamwake iye akusonyeza kuti kuphunzitsa ndi kupanga zozizwitsa pamaso pa anthu osamverawo m’khamu lake kuli kofanana ndi kubisa kuwala kwa nyali. Maso a owona oterowo sali opepuka, kapena olunjikitsa chidwi, chotero chifuno cholinganizidwacho cha zozizwitsa zake sichikukwaniritsidwa.
Yesu wangotulutsa kumene chiwanda ndipo wapangitsa wosalankhula kulankhula. Ichi chiyenera kusonkhezera anthu okhala ndi maso opepuka, kapena olunjikitsa chidwi, kutamanda chochitika cha ulemerero chimenechi ndi kulengeza mbiri yabwinoyo! Komabe, ndi osuliza amenewa, chimenechi sindicho chimene chikuwoneka. Chotero Yesu akumaliza kuti: “Potero, yang’anira. Kuwunika kuli mwa iwe kungakhale mdima. Pamenepo, ngati thupi lako lonse liwunikidwa losakhala nalo dera lake la mdima, lidzakhala lowunikidwa monsemo ngati pamene nyali ndi kuwala kwake ikuwunikira iwe.” Luka 11:14-36; Eksodo 8:18, 19; 31:18; Mateyu 12:22, 28.
◆ Nchiyani chomwe chiri chivomerezo ku kuchiritsa kwa Yesu kwa munthuyo?
◆ Nchiyani chomwe chiri chala cha Mulungu, ndipo ndimotani mmene Ufumu wa Mulungu wafikirira amvetseri a Yesu?
◆ Nchiyani chomwe chiri magwero a chimwemwe chowona?
◆ Ndimotani mmene munthu angakhalire ndi diso lopepuka?