MUTU 77
Yesu Anapereka Malangizo pa Nkhani ya Chuma
FANIZO LA MUNTHU WACHUMA
YESU ANATCHULA ZA MBALAME NDI MALUWA POPHUNZITSA
“KAGULU KA NKHOSA” KAMENE KADZALAMULIRE MU UFUMU
Pamene Yesu ankadya kunyumba ya Mfarisi uja, anthu ambiri anasonkhana panja pa nyumbayo. Pa nthawi inanso ali ku Galileya anthu ambiri anasonkhana kuti amuone. (Maliko 1:33; 2:2; 3:9) Anthu ambiri a ku Yudeya ankafuna kuona Yesu komanso kumumva akuphunzitsa. Zimenezi zinali zosiyana kwambiri ndi zimene Afarisi anachita pa nthawi imene Yesu ankadya kunyumba ya Mfarisi uja.
Zimene Yesu anayamba kunena pa nthawiyi zinali zofunika kwambiri kwa ophunzira ake. Iye ananena kuti: “Samalani ndi chofufumitsa cha Afarisi, chimene chili chinyengo.” Yesu anaperekapo chenjezo limeneli nthawi ina m’mbuyomo koma zimene anaona kunyumba ya Mfarisi uja zinamuchititsa kuti abwerezenso mfundo imeneyi kuti ophunzirawo aone kufunikira kwa zimene anawachenjezazo. (Luka 12:1; Maliko 8:15) Afarisi ankadzionetsa ngati anthu opemphera n’cholinga choti asamaoneke kuti anali anthu oipa. Komabe ankafunika kuwaulula chifukwa anali anthu oopsa kwambiri. Moti Yesu ananena kuti: “Komatu palibe chobisika chimene sichidzaululika, ndi chinsinsi chimene sichidzadziwika.”—Luka 12:2.
N’kutheka kuti anthu ambiri amene anafika pamalowa anali Ayuda amene anali asanamvepo zimene Yesu anaphunzitsa ali ku Galileya. Choncho Yesu anayamba kubwereza mfundo zikuluzikulu zimene anaphunzitsa ali ku Galileya. Ndiyeno anauza anthu onse amene ankamumvetsera kuti: “Musamaope amene amapha thupi lokha, amene sangathe kuchita zoposa pamenepa.” (Luka 12:4) Yesu analimbikitsanso ophunzira ake kuti azikhulupirira kuti Mulungu adzawasamalira ngati mmene analimbikitsiranso ophunzira ake ena m’mbuyomo. Anthuwo ankafunikanso kuvomereza kuti Yesu ndi Mwana wa munthu komanso kudziwa kuti Mulungu akhoza kuwathandiza.—Mateyu 10:19, 20, 26-33; 12:31, 32.
Ndiyeno munthu wina amene anali pagulupo anayambitsa nkhani ina imene inkamudetsa nkhawa. Iye anati: “Mphunzitsi, mundiuzireko m’bale wanga kuti andigawireko cholowa.” (Luka 12:13) Chilamulo chinkanena kuti mwana woyamba kubadwa ankayenera kulandira magawo awiri achuma chochokera kwa makolo ake. Kutsatira mfundo imeneyi kunkathandiza kuti anthu apachibale asamakangane pogawana chumacho. (Deuteronomo 21:17) Koma zikuoneka kuti munthuyo ankafuna zinthu zambiri kuposa zimene ankayenera kulandira mogwirizana ndi malamulo. Yesu anakana kulowerera nkhaniyi. Iye anafunsa munthuyo kuti: “Munthu iwe, ndani anandiika ine kukhala woweruza kapena wogawa chuma chanu?”—Luka 12:14.
Kenako Yesu anauza anthuwo kuti: “Khalani maso ndipo chenjerani ndi kusirira kwa nsanje kwamtundu uliwonse, chifukwa ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera m’zinthu zimene ali nazo.” (Luka 12:15) Ngakhale munthu atakhala ndi chuma chambiri bwanji, pa nthawi ina adzamwalirabe ndipo adzasiya zinthu zonse zomwe ali nazo. Pofuna kuthandiza anthuwo kumvetsa mfundo imeneyi Yesu anafotokoza fanizo losaiwalika lomwe linawathandiza kuzindikira kufunika kokhala ndi mbiri yabwino pamaso pa Mulungu.
Iye ananena kuti: “Munda wa munthu wina wachuma unabereka bwino. Choncho anayamba kudzifunsa kuti, ‘Ndichite chiyani tsopano, popeza ndilibe mosungira zokolola zangazi?’ Ndiyeno anati, ‘Ndichita izi: Ndipasula nkhokwe zanga ndi kumanga zikuluzikulu, ndipo tirigu wanga yense ndi zinthu zanga zonse zabwino ndidzazitutira mmenemo. Ndipo ndidzauza moyo wanga kuti: “Moyo wangawe, uli ndi zinthu zambiri zabwino mwakuti zisungika kwa zaka zambiri. Ungoti phee tsopano, ndipo udye, umwe ndi kusangalala.”’ Koma Mulungu anamuuza kuti, ‘Wopanda nzeru iwe, usiku womwe uno moyo wako adzaufuna. Nanga chuma chimene waunjikachi chidzakhala cha ndani?’ Umu ndi mmene zimakhalira kwa munthu amene wadziunjikira yekha chuma, koma amene sali wolemera kwa Mulungu.”—Luka 12:16-21.
Pamenepatu mfundo ya Yesu inali yakuti ophunzira ake komanso anthu ena akanatha kukopeka n’kuyamba kufunafuna kapena kudziunjikira chuma. Kapena sakanatha kutumikira Yehova ndi mtima wonse chifukwa chodera nkhawa kwambiri za moyo wawo. Choncho Yesu anabwerezanso malangizo amene anapereka pa ulaliki wake wa paphiri umene unachitika pafupifupi chaka ndi hafu m’mbuyomo.
Ananena kuti: “Lekani kudera nkhawa moyo wanu kuti mudzadya chiyani kapena kudera nkhawa matupi anu kuti mudzavala chiyani. . . . Onetsetsani makwangwala, iwo safesa mbewu kapena kukolola. Alibe nyumba yosungiramo zinthu kapena nkhokwe, komatu Mulungu amawadyetsa. Kodi inu si ofunika kwambiri kuposa mbalame? . . . Onetsetsani mmene maluwa amakulira. Iwo sagwira ntchito kapena kuwomba nsalu. Koma ndikukuuzani, Ngakhale Solomo mu ulemerero wake wonse sanavalepo zokongola ngati duwa lililonse mwa maluwa amenewa. . . . Choncho lekani kudera nkhawa za chimene mudzadya ndi chimene mudzamwa, ndipo siyani kuvutika mumtima. . . Atate wanu amadziwa kuti zinthu zonsezi n’zofunika kwa inu. . . . Pitirizani kufunafuna ufumu wake, ndipo zinthu zimenezi zidzawonjezedwa kwa inu.”—Luka 12:22-31; Mateyu 6:25-33.
Kodi ndi ndani amene ankafunika kufunafuna Ufumu wa Mulungu? Yesu ananena kuti amene azidzachita zimenezi ndi anthu ochepa okhulupirika a “kagulu ka nkhosa.” Ndipo patapita nthawi zinadzadziwika kuti chiwerengero cha anthuwo chinali 144,000. Kodi kagulu kameneka kankayembekezera chiyani? Yesu ananena kuti: “Atate wanu wavomereza kukupatsani ufumu.” Anthu a mu kaguluka saganizira kwambiri zopeza chuma cha m’dzikoli, chomwe anthu akhoza kuba, koma amaganizira za “chuma chosatha kumwamba,” komwe akalamulire ndi Khristu.—Luka 12:32-34.