Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Funso la Cholowa
ANTHU mwachiwonekere akudziŵa kuti Yesu wakhala akudya m’nyumba ya Mfarisi. Chotero iwo akusonkhana kunja mwa zikwi ndipo akudikira pamene Yesu atuluka. Mosiyana ndi Afarisi omwe amatsutsa Yesu ndi kuyesera kumgwira iye m’kukamba chinachake cholakwika, anthuwo mofunitsitsa akumvetsera kwa iye ndi chiyamikiro.
Akutembenukira choyamba kwa ophunzira ake, Yesu akunena kuti: “Tachenjerani nokha ndi chotupitsa mikate cha Afarisi, chimene chiri chinyengo.” Monga mmene chachitiridwa chitsanzo mkati mwa chakudyacho dongosolo lonse la chipembedzo la Afarisi liri lodzazidwa ndi chinyengo. Koma ngakhale kuti kuipa kwa Afarisi kungakhale kobisika mwa kusonyeza kudzipereka, m’kupita kwa nthaŵi icho chidzavumbulidwa. “Kulibe kanthu kovundikiridwa,” Yesu akutero “kamene sikadzaululidwa, ndi kobisika kamene sikadzadziŵika.”
Yesu akupitiriza kubwereza chilimbikitso chomwe iye anapereka kwa 12 aja pamene anawatumiza pa ulendo wolalikira ku Galileya. Iye akunena kuti: “Musawope iwo akupha thupi ndipo akatha ichi alibe kanthu kena angakhoze kuchita.” Popeza Mulungu samaiwala ngakhale mpheta imodzi, Yesu akutsimikizira otsatira ake kuti Mulungu sadzawaiwala iwo. Iye akunena kuti: “Ndipo pamene paliponse adzamuka nanu ku mlandu wa sunagoge ndi kwa akulu, . . . mzimu woyera udzaphunzitsa inu nthaŵi yomweyo zimene muyenera kuzinena.”
Munthu kuchokera m’khamu akulankhula, “Mphunzitsi,” iye akuchonderera, “uzani mbale wanga agawane ndi ine chuma chamasiye.” Lamulo la Mose linakhazikitsa kuti mwana woyamba kubadwa ayenera kulandira mbali ziŵiri za cholowa, chotero sipayenera kukhala chifukwa cha kukanganirana. Koma munthuyo mwachidziŵikire akufuna koposa gawo lake la lamulo la cholowacho.
Yesu moyenerera akukana kudziloŵetsamo. “Munthu iwe, ndani anandiika ine ndikhale woweruza kapena wa kugawira inu?” Iye akufunsa tero. Iye kenaka akupereka chenjezo lofunika koposa iri kwa khamulo: “Yang’anirani, mudzisungire kupewa m’siriro uliwonse, chifukwa moyo wake wa muthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.” Inde, mosasamala kanthu kuti ndi zochuluka zotani zimene munthu angakhale nazo, mwachibadwa iye adzafa ndi kusiya zonse kumbuyo. Kuti agogomezere nsonga imeneyi, limodzinso ndi kusonyeza kupusa kwa kulephera kumangirira dzina labwino ndi Mulungu, Yesu akugwiritsira ntchito fanizo. Iye akulongosola:
“Munda wake wa munthu mwini chuma unapatsa bwino. Ndipo anaganizaganiza mwa yekha, nanena, ‘Ndidzatani ine, popeza ndiribe mosungiramo zipatso zanga?’ Ndipo anati, ‘Ndidzatere: Ndidzapasula nkhokwe zanga ndi kumanganso zazikulu, ndipo ndidzasungiramo zinthu zanga zonse ndi chuma changa; ndipo ndidzati kwa moyo wanga: “Moyo iwe, uli nacho chuma chambiri chosungika kufikira zaka zambiri; tapumulatu, nudye, numwe, nukondwere.”’ Koma Mulungu anati kwa iye, ‘Wopusa iwe, usiku womwe uno udzafunidwa moyo wako. Ndipo, zinthu zimene unazikonsa, zidzakhala za yani?’”
M’kumaliza, Yesu akuwona: “Atero iye wodzikundikira chuma mwiniyekha wosakhala nacho chuma cha kwa Mulungu.” Pamene kuli kwakuti ophunzirawo sangakodwe mu msampha ndi kupusa kwa kukundika chuma, iwo mopepuka angacheutsidwe kuchoka ku kutumikira Yehova ndi moyo wonse ndi zisamaliro za tsiku ndi tsiku za moyo. Chotero Yesu akugwiritsira ntchito chochitikacho kubwereza uphungu wabwino umene iye anaupereka chifupifupi chaka chimodzi ndi theka chapitacho mu Ulaliki wa pa Phiri. Akutembenukira kwa ophunzira ake, iye akunena kuti:
“Chifukwa chake ndinena ndi inu, Musade nkhaŵa ndi moyo wanu chimene mudzadya kapena ndi thupi lanu chimene mudzavala. . . . Lingalirani makungubwi kuti safesa ayi kapena kutema ayi, koma alibe nyumba yosungiramo kapena nkhokwe, koma Mulungu azidyetsa. . . . Lingalirani maluwa makulidwe awo; sagwiritsira ntchito ndi kusatuta; koma ndinena kwa inu, Ngakhale Solomo mu ulemerero wake wonse sanakhale ngati limodzi la awa. . . .
“Ndipo inu musafunefune chimene mudzadya ndi chimene mudzamwa, ndipo musakaike mtima; pakuti izi zonse mitundu ya anthu pa dziko lapansi amazifuna, koma Atate wanu adziŵa kuti musowa zimenezi. Komatu, tafunafunani ufumu wake, ndipo izi adzakuwonjezerani.”
Makamaka m’nthaŵi za mavuto a zachuma ndi pamene mawu a Yesu amafunikira kulingaliridwa mosamalitsa. Munthu yemwe amakhala wodera nkhaŵa mopanbanitsa ponena za zosowa zake zakuthupi ndi kuyamba kutengeka kuchoka ku kulondola zinthu zauzimu m’chenicheni akuchitira chitsanzo kusoweka kwa chikhulupiriro mu kuthekera kwa Mulungu kupereka kaamba ka atumiki Ake. Luka 12:1-31; Deuteronomo 21:17.
◆ Nchifukwa ninji, mwinamwake, munthuyo akufunsa ponena za cholowa, ndipo ndi chenjezo lotani limene Yesu akupereka?
◆ Ndi fanizo lotani limene Yesu akugwiritsira ntchito, ndipo nchiyani chomwe chiri nsonga yake?
◆ Ndi uphungu wotani umene Yesu akuwubwereza, ndipo nchifukwa ninji uli woyenerera kaamba ka chochitikachi?