MUTU 79
Ayuda Ankayembekezera Kuwonongedwa
YESU ANAWAPHUNZITSA POGWIRITSA NTCHITO NGOZI ZIWIRI ZIMENE ZINACHITIKA
MAYI WINA WOLUMALA ANACHIRITSIDWA PA TSIKU LA SABATA
Yesu anayesetsa kugwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana pophunzitsa anthu pofuna kuwathandiza kuti aziganizira kwambiri za ubwenzi wawo ndi Mulungu. Anapezanso mwayi wochita zimenezi atangomaliza kukambirana ndi anthu aja panja pa nyumba ya Mfarisi.
Anthu ena pagululo anayamba kunena za ngozi ina imene inachitika. Anayamba kufotokoza za “Agalileya amene magazi awo, [wolamulira wachiroma Pontiyo] Pilato anawasakaniza ndi nsembe zawo.” (Luka 13:1) Kodi anthuwa ankatanthauza chiyani?
Mwina Agalileya amenewa ndi amene anaphedwa pamene Ayuda ambiri ankachita ziwonetsero pokwiya ndi zimene Pilato anachita. Iye anagwiritsa ntchito ndalama zimene anthu ankapereka kukachisi kumangira ngalande yobweretsera madzi mumzinda wa Yerusalemu. Pilato ayenera kuti anatenga ndalama zimenezi mogwirizana ndi akuluakulu a pakachisipo. N’kutheka kuti anthu amene ankafotokoza nkhaniyi ankaganiza kuti Agalileyawo anakumana ndi tsoka limeneli chifukwa cha zinthu zoipa zimene ankachita. Koma Yesu sanagwirizane ndi zimenezi.
Iye anafunsa kuti: “Kodi mukuganiza kuti Agalileya amenewo anali ochimwa kwambiri kuposa Agalileya ena onse chifukwa chakuti zimenezo zinawachitikira?” Yankho la funsoli ndi lakuti ayi. Koma Yesu anagwiritsa ntchito nkhani imeneyi pochenjeza Ayuda kuti: “Choncho ndikukuuzani kuti ngati simulapa, nonsenu mudzawonongeka mofanana ndi iwowo.” (Luka 13:2, 3) Kenako Yesu anafotokozanso za ngozi ina imene mwina inali itangochitika kumene komanso mwina inali yokhudzana ndi ntchito yomanga ngalande ya madzi ija. Iye anafunsa kuti:
“Nanga bwanji za anthu 18 aja, amene nsanja inawagwera ku Siloamu n’kuwapha? Kodi mukuganiza kuti iwo anali ochimwa kwambiri kuposa anthu onse okhala mu Yerusalemu?” (Luka 13:4) Gulu la anthulo linkaganiza kuti anthu amenewa anafa chifukwa chakuti anali ndi makhalidwe enaake oipa. Koma Yesu sankaganiza choncho. Iye ankadziwa kuti: “Nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezereka” zimachitika ndipo n’zimene zinachititsa kuti anthuwo afe. (Mlaliki 9:11) Koma anthuwo ankafunika kuphunzirapo kenakake pangozi imene inachitikayo chifukwa Yesu anawauza kuti: “Ngati simulapa, nonsenu mudzawonongeka ngati mmene iwo anawonongekera.” (Luka 13:5) Koma n’chifukwa chiyani Yesu anabwereza mfundo imeneyi pa nthawiyi?
Iye anachita zimenezi chifukwa cha mmene zinthu zinkayendera pa ntchito yake yolalikira ndipo anagwirizanitsa zimene zinkachitika pa utumiki wakewo ndi fanizo. Pofotokoza fanizolo iye ananena kuti: “Munthu wina anali ndi mkuyu m’munda wake wa mpesa, ndipo anapita kukafuna chipatso mumtengowo, koma sanapezemo chilichonse. Ndiyeno anauza munthu wosamalira munda wa mpesawo kuti, ‘Kwa zaka zitatu tsopano ndakhala ndikubwera kudzafuna nkhuyu mumtengo uwu, koma sindinapezemo ngakhale imodzi. Dula mtengo umenewu! N’chifukwa chiyani ukungowononga nthaka?’ Wosamalira mundayo anayankha kuti, ‘Mbuyanga, bwanji muusiye chaka chino chokha. Ine ndikumba mouzungulira n’kuthirapo manyowa. Ukadzabala zipatso m’tsogolo, zidzakhala bwino, koma ngati sudzabala mudzaudule.’”—Luka 13:6-9.
Kwa zaka zoposa zitatu Yesu anayesetsa kuthandiza Ayuda kuti azikhulupirira Mulungu.Ngakhale kuti Yesu anachita zimenezi, ndi anthu ochepa okha amene anakhala ophunzira ake kapena kuti zipatso za ntchito imene anagwira. Koma pa nthawiyi anali m’chaka cha 4 cha utumiki wake ndipo anayamba kugwira ntchitoyi mwakhama kwambiri kuposa kale. Pamene ankagwira ntchito yolalikira komanso yophunzitsa ku Yudeya ndi ku Pereya zinali ngati akukumba komanso kuthira manyowa mozungulira mtengo wa mkuyu, womwe unkaimira Ayuda. Kodi ntchitoyi inayenda bwanji? Ayuda ochepa okha ndi amene anakhala okhulupirira. Koma mtundu wonse wa Ayuda unakana kulapa machimo awo moti unkayembekezera kuwonongedwa.
Umboni winanso wosonyeza kuti anthuwa sankafuna kukhulupirira Mulungu unaonekera pa tsiku lina la Sabata. Pa tsikuli Yesu ankaphunzitsa m’sunagoge ndipo anaona mzimayi wina amene anali wopindika msana chifukwa chakuti mzimu woipa unamudwalitsa kwa zaka 18. Yesu anachitira chifundo mayiyo ndipo anamuuza kuti: “Mayi, mwamasuka ku matenda anu.” (Luka 13:12) Yesu ataika manja ake pa mayiyo nthawi yomweyo msana wake unawongoka moti anayamba kulemekeza Mulungu.
Koma zimenezi zinakwiyitsa kwambiri mtsogoleri wa sunagogeyo ndipo anayamba kuuza anthu amene anali pa sunagogepo kuti: “Pali masiku 6 oyenera kugwira ntchito. Muzibwera masiku amenewo kudzachiritsidwa, osati tsiku la sabata.” (Luka 13:14) Mtsogoleriyo sankakana kuti Yesu anali ndi mphamvu zochiritsa koma iye ankadzudzula anthuwo chifukwa chobwera kusunagogeko pa tsiku la Sabata kuti adzachiritsidwe. Poyankha Yesu anatchula zimene anthuwo ankachita ngakhale pa tsiku la Sabata. Iye ananena kuti: “Onyenga inu, kodi aliyense wa inu samasula ng’ombe yake kapena bulu wake m’khola pa sabata ndi kupita naye kukam’mwetsa madzi? Kodi sikunali koyenera kuti mayi uyu, amenenso ndi mwana wa Abulahamu, amene Satana anamumanga zaka 18, amasulidwe m’maunyolo amenewa tsiku la sabata?”—Luka 13:15, 16.
Anthu amene ankadana ndi Yesu anachita manyazi koma anthu ambiri ankasangalala chifukwa choona zinthu zamphamvu zimene Yesu ankachita. Kenako Yesu anabwerezanso kufotokoza mafanizo awiri onena za Ufumu amene anawafotokoza pa nthawi imene ankaphunzitsa anthu atakwera boti ku nyanja ya Galileya.—Mateyu 13:31-33; Luka 13:18-21.