Mutu 11
Opulumuka Sayenera Kukhala “Mbali ya Dziko”
1, 2. (a) Kodi Yesu ananenanji ponena za unansi wa ophunzira ake kudziko? (b) Kodi zimenezo sizimatanthauzanji, ndipo chifukwa ninji?
KODI Yesu anatanthauzanji m’kunena kuti otsatira ake ali “m’dziko,” ndipo komabe iwo sanayenera kukhala “mbali ya dziko”? (Yohane 17:11, 14) Kuti tikhale pakati pa awo opulumuka kudzakhala m’Dongosolo Latsopano la Mulungu, tifunikira kuzindikira chimenechi.
2 Choyamba lingalirani chimene kusakhala “mbali ya dziko” sikumatanthauza. Iko sikumatanthauza kuti tiyenera kudzilekanitsa mofanana ndi anthu okonda kukhala okha m’phanga kapena kudzipatula kukadzibindikiritsa m’malo okhala ansembe kapena malo ena akutali. Mosiyana ndi zimenezo, usikuwo asanafe Yesu anapempherera ophunzira ake kwa Atate wake, akumati: “Ndikupemphani, osati kuti muwachotse m’dziko, koma kuti muwayang’anire chifukwa cha woipayo. Iwo sali mbali ya dziko, monganso ine sindiri mbali ya dziko.”—Yohane 17:15, 16, NW.
3, 4. (a) Kodi ndim’ntchito zotani m’zimene kuli kofunika kwa Akristu kukhala pamodzi ndi anthu adziko? (b) Koma kodi iwo ayenera kupewa chiyani?
3 Mmalo mwakudzibisa kwa anthu, ophunzira a Yesu ‘anatumizidwa m’dziko,’ kukadziŵikitsa chowonadi. (Yohane 17:18, NW) Mwakutero, iwo anatumikira monga “kuunika kwa dziko,” akumalola kuunika kwa chowonadi kuwala kotero kuti anthu awone mmene chowonadi cha Mulungu chimayambukirira mopindulitsa miyoyo ya anthu.—Mateyu 5:14-16, NW.
4 Akristu amawonana ndi anthu ambiri pamene akugwira ntchito kuti adzichirikize ndi mabanja awo ndi pamene iwo akumka ndi mbiri ya Ufumu wa Mulungu kwa anthu. Chotero, monga momwe mtumwi Paulo akusonyezera, iwo sakuyembekezeredwa “kuturuka m’dziko” m’njira yeniyeni. Iwo sangathe kuleka kotheratu ‘kukhalira pamodzi’ ndi anthu adziko. Koma iwo angathe ndipo ayenera kupewa njira zolakwa zimene unyinji wa anthu umachita.—1 Akorinto 5:9-11, NW.
5. Kodi ndimotani mmene kulekana ndi dziko kofunikako kukusonyezedwera mwafanizo m’chochitika cha Nowa ndi banja lake?
5 Mkhalidwewo uli wofanana ndi uja wa m’tsiku la Nowa pamene Yehova anawona kuti “anthu onse anavunditsa njira yawo padziko lapansi.” (Genesis 6:12) Koma Nowa ndi banja lake anali osiyana. Mwakukana kugwirizana ndi chivundi chowazinga ndipo mwakulalikira chilungamo, Nowa ‘anatsutsa dziko.’ Iye analisonyeza kukhala losagwirizana mwadala ndi chifuniro cha Mulungu. (Ahebri 11:7; 2 Petro 2:5) Ndicho chifukwa chake, pamene Chigumula chadziko lonse chinawononga anthu opanda umulungu, iye ndi banja lake anapulumuka. Iwo anali “m’dziko” koma panthawi imodzimodziyo sanali “mbali ya dziko.”—Genesis 6:9-13; 7:1; Mateyu 24:38, 39.
Kodi Nchiyani Chimene Chiri Chikondi Choyenera kwa Anthu Adziko?
6. Kodi nkoyenera kusonyeza chikondi chirichonse kwa anthu adziko?
6 Kodi kusakhala ‘mbali ya dziko’ kukatanthauzanso kuti mukukhala ‘wodana ndi anthu’? Kuchita motero kukanachititsa munthuyo kusagwirizana ndi Yehova Mulungu, amene, Mwana wake Yesu anati “anakonda dziko lapansi [la mtundu wa anthu] kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti wakukhulupirira iye asataike, koma akhale nawo moyo wosatha.” Chotero kukoma mtima ndi chifundo cha Mulungu kwa anthu amitundu yonse chimapereka chitsanzo kwa tonsefe choti titsatire.—Yohane 3:16; Mateyu 5:44-48.
7, 8. (a) Kodi Baibulo limanenanji ponena za kukonda dziko? (b) Kodi nchiyani chimene chiri dziko limene tiyenera kulekana nalo? (c) Kodi nchifukwa ninji tiyenera kupewa dziko ndi zikhumbo zake?
7 Koma kodi mtumwi Yohane sakutiuza kuti, “musakonde za dziko, kapena za m’dziko. Ngati wina akonda dziko, chikondi cha Atate sichiri mwa iye”? Ngati Mulungu mwiniyo anakonda dziko, kodi nchifukwa ninji mtumwiyo ananena zimenezi?—1 Yohane 2:15, NW.
8 Baibulo limasonyeza kuti Mulungu amakonda dziko lamtundu wa anthu kokha monga anthu amene ali mu mkhalidwe wopanda ungwiro, wakufa ndi wofunikira chithandizo kwambiri. Kumbali ina, Satana walinganiza unyinji wa anthu kutsutsana ndi Mulungu. Liri “dziko” limenelo—chitaganya cha anthu odana ndi Mulungu ndi chokhala pansi pa ulamuliro wa Satana—limene Akristu owona ayenera kudzilekanitsa nalo. (Yakobo 1:27) Mawu a Mulungu amachenjeza motsutsana ndi kukonda zikhumbo zolakwa ndi ntchito zadziko limenelo kuti: “Chirichonse—m’dziko chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso ndi kusonyezera monyadira chuma cha munthuyo sizichokera kwa Atate, koma kudziko. Ndipo dziko lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala kunthawi yonse.—1 Yohane 2:15-17, NW.
9, 10. (a) Kodi kunganenedwe motani kuti zikhumbo zimenezi ‘zichokera kudziko’? (b) Kodi zikhumbo zimenezi zakhala ndi chiyambukiro chotani pa anthu?
9 Inde, chilakolako chathupi chimenecho ndi chilakolako chamaso ndi kudzikweza kwamunthu ‘zichokera kudziko.’ Zinali zimenezo zimene zinabuka mwamakolo oyamba a anthu ndi kuwatsogolera kukufunafuna kusadalira Mulungu kotero kuti alondole zikhumbo zadyera. Kulondola zikhumbo zaudziko zadyera zimenezi kunatsogolera kukuswa malamulo a Mulungu.—Genesis 3:1-6, 17.
10 Lingalirani zimene mumawona mokuzingani. Kodi anthu ochuluka samaika miyoyo yawo pa zilakolako zathupi ndi zamaso ndi “kusonyezera monyadira chuma cha munthuyo”? Kodi sindizo zinthu zimenezi zimene zimaumba ziyembekezo ndi zikondwerero, zikumalamulira mmene amachitira kwa wina ndi mnzake? Chifukwa cha ichi, mbiri ya anthu iri ndi cholembedwa chanthawi yaitali cha kupanda chigwirizano ndi nkhondo, cha chisembwere ndi upandu, ndi cha umbombo wa zamalonda ndi chitsenderezo, cha kukhumbira upamwamba konyada, ndi kufunafuna kutchuka ndi ulamuliro.
11. Chotero, pamenepa, kodi nchifukwa ninji chikondi cha Mulungu kaamba ka dziko sichiri chosagwirizana ndi zimene Mawu ake amatsutsa?
11 Pamenepa, tingathe kuwona, kuti kukonda dziko monga momwe amachitira Mulungu kuli kosiyana kwambiri ndi kukonda zilakolako zake zoipa ndi machitachita, zimene iye amatsutsa. Kukonda anthu kwa Mulungu kwatsegula njira yomasukira ku zilakolako zauchimo zimenezo ndi zotulukapo zake zoipa, kuphatikizapo imfa yeniyeniyo. Anasonyeza chikondi chimenecho mwakupereka Mwana wa iyemwini kuwombolera anthu. Koma ngati wina akana nsembe imeneyo napitirizabe m’kusamvera, Baibulo limati “mkwiyo wa Mulungu ukhala pa iye.”—Yohane 3:16, 36; Aroma 5:6-8.
Khalani Osalamulidwa ndi “Wolamulira wa Dziko Lino”
12. Kodi tingadziŵe motani kuti chikondi chimene tingakhale nacho kwa anthu adziko chiri chokondweretsa kwa Mulungu kapena ayi?
12 Pamenepa, bwanji za ife? Kodi ife ‘timakonda’ anthu m’dzikoli m’lingaliro lakufuna kuwathandiza mowona mtima kupeza njira ya kumoyo m’chiyanjo cha Mulungu? Kapena kodi timakonda zinthu zenizenizo zimene zimawalepheretsa kukhala atumiki a Mulungu—mzimu wawo wakudzigangira, kuwonetsera kwawo chuma chawo, kudalira m’kufunika kwawo ndi ulemelero wawo? Ngati tikonda kukhala ndi anthu amikhalidwe yotero, ndiko kuti ‘tikukonda dziko’ m’njira imene mtumwiyo anaitsutsa.
13. Kodi ndimotani mmene kukonda dziko kungalepheretsere munthu kutumikira Mulungu?
13 Anthu ochuluka m’tsiku la Yesu anakonda njira zadziko. Chotero iwo anapewa kuchitapo kanthu molimba mtima monga ophunzira a Yesu. Iwo sanafune kutaya kutchuka kwawo ndi malo awo atchito pakati pa anthu m’magulu awo achitaganya ndi achipembedzo. Iwo anakonda thamo la anthu kuposa chivomerezo cha Mulungu. (Yohane 12:42, 43) Nzowona, ena anachita ntchito zachifundo nachita ntchito zina zachipembedzo. Koma iwo anatero kwakukulukulu chifukwa chakuti anafuna kuwonedwa ndi ena. (Mateyu 6:1-6; 23:5-7; Marko 12:38-40) Kodi inu simumawona anthu akusonyeza kukonda njira yolakwa yadziko kofananako lerolino? Komabe Baibulo limasonyeza kuti “chikondi” chamtundu uwu chingatsogolere kokha kuchiwonongeko.
14. Kodi ndani amene anaika Yesu pachiyeso pamene anali padziko lapansi, ndipo limodzi ndi chotulukapo chotani?
14 Mwana wa Mulungu anaikidwa pachiyeso m’nkhani zomwezi. Kuyesayesa kunapangidwa kwakusonkhezera mwa iye chikhumbo chadyera chakupanga chiwonetsero cha kuchititsa chidwi anthu—kukhala wofanana ndi dziko. Iye anasonyezedwa ngakhale ufumu pamitundu yonse yadziko limodzi ndi ulemelero wawo. Koma anakana kwamtu wagalu zosonkhezera zilakolako zadyera zimenezo. Zinachokera kwa uyo amene poyambapo anakaikira ulamuliro wa Yehova Mulungu, Satana Mdyerekezi.—Luka 4:5-12.
15. Sonyezani kuchokera m’Baibulo lanu amene ali “wolamulira wa dziko lino.”
15 Kudziŵa chopereka cha Satana cha ulamuliro woperekedwa kwa Yesu nkofunika kuti tizindikire chifukwa chake sitiyenera kukhala “mbali ya dziko.” Kumasonyeza kuti dziko lonse lamtundu wa anthu, kuphatikizapo maulamuliro ake, wolamulira wake wosawoneka ndiye Mdani wa Mulungu. Yesu mwiniyo analankhula za Satana kukhala “wolamulira wa dziko lino.” (Yohane 12:31, NW; 14:30; 2 Akorinto 4:4) Mtumwi Paulo nayenso anasonya ku “makamu amizimu yoipa,” aziwanda okhala pansi pa ulamuliro wa Satana, kukhala monga ‘maboma, olamulira ndi maulamuliro ‘adziko amdima uno’ osawoneka. Paulo anachenjeza Akristu za kufunika kwa zida zankhondo zauzimu zotetezerera “olamulira” amenewa.—Aefeso 6:10-13, NW.
16. Kodi ndimbali yaikulu yotani yadziko imene yasokeretsedwa ndi Satana ndi imene iri muulamuliro wake?
16 Apang’ono okha akhalabe omasuka ku ulamuliro wa wolamulira wosawoneka ameneyu ndi makamu ake. Motero “dziko,” ndiko kuti unyinji wonse wa anthu odana ndi Mulungu, “ligona m’mphamvu ya woipayo.” Mwachisonkhezero chaziwanda iye ‘amasokeretsa dziko lonse lokhalidwa ndi anthu,’ kuphatikizapo olamulira ake adziko lapansi, akumaŵaloŵetsa m’njira yowombana ndi Mulungu ndi Ufumu wake.—1 Yohane 5:19; Chivumbulutso 12:9; 16:13, 14; 19:11-18.
17. (a) Kodi khalidwe losonyezedwa ndi dziko limatsimikizira chiyani ponena za amene ali kutsogolera anthu? (b) Kodi kukanakhala kokondweretsa kwa Mlengi ngati tinasonyeza mzimu woterowo?
17 Zimenezi zingamvekere kukhala zovuta kuzikhulupilira. Komabe, kodi anthu ambiri adziko lino samasonyeza mowonekera bwino mkhalidwe ndi ntchito za Mdani wa Mulungu? M’dziko lonse lapansi timawona kunama, chinyengo, chiwawa ndi mbanda zimene zimadziŵikitsa awo amene ali ‘ochokera kwa Mdyerekezi,’ amene iye ali “atate” wawo wauzimu. (1 Yohane 3:8-12; Yohane 8:44; Aefeso 2:2, 3) Ndithudi mzimu uwu sumachokera kwa Mlengi Wachikondi.
18. Kodi ndimotani mmene khalidwe lathu ponena za ulamuliro limasonyezera kuti kaya ngati tiri omasuka ku ulamuliro wa “wolamulira wa dziko lino”?
18 Ndiponso, kodi unyinji waukulu wa anthu sumadalira pa malinganizidwe a anthu kudzetsa mtendere ndi chisungiko? Kodi mumadziŵa anthu angati amene amayang’anadi kwa Mulungu ndi Ufumu wake kaamba ka chothetsera mavuto a anthu? Komabe chidaliro chawo m’madongosolo andale zadziko a anthu nchoikidwa pamalo olakwika, monga momwe Yesu ananenera kuti: “Ufumu wanga suli mbali yadziko lino.” “Magwero” a Ufumu wake saali adziko lino, chifukwa chakuti anthu sanaukhazikitsa kapena kuuchititsa kulamulirabe. Ndiwo makonzedwe a Mulungu mwini. (Yohane 18:36, NW; Yesaya 9:6, 7) Chotero, kuti tikhale pakati pa awo oyembekezera kupulumuka pamene Ufumu umenewo uwukira adani ake onse, tifunikira kuzindikira chenicheni chotsimikizirika chakuti Satana akulamulira dziko lino ndi madongosolo ake. Zimenezo zimaphatikizapo makonzedwe ake andale zadziko monga Mitundu Yogwirizana. Tifunikira kumasuka kwa onseŵa mwakuima kwathu nji kumbali ya boma lolungama la Yehova mwa Kristu Yesu.—Mateyu 6:10, 24, 31-33.
19. Monga momwe kwachitiridwa umboni ndi mbiri, kodi ndim’njira zotani zimene Akristu oyambilira anasonyezera kuti iwo sanali “mbali ya dziko”?
19 Mbiri imasonyeza kuti Akristu oyambirira anali nzika zaulemu, ndi zomvera lamulo. Koma iwo anali otsimikiza kusakhala ‘ambali ya dziko,’ ngakhale ngati izi zinadzetsa chizunzo pa iwo. Tikuŵerenga mawu onga ngati awa:
“Chikristu choyambirira chinazindikiridwa mwapang’ono ndipo chinali kuwonedwa ndi chiyanjo chapang’ono ndi awo amene analamulira dziko lachikunja. . . . Akristu anakana kugwira ntchito zina za nzika Zachiroma. . . . Iwo sanakhale ndi malo antchito aukumu andale zadziko.”—On the Road to Civilization, A World History.57
“Iwo anakana kukhala ndi mbali iriyonse yokangalika m’ntchito yaboma kapena gulu lankhondo lochinjiriza ufumuwo. . . . Kunali kosatheka kuti Akristu, popanda kukana ntchito yopatulika kwambiri, akatenge ntchito yausilikali wankhondo, ya oweruza m’makhoti ang’ono, kapena ya ukalonga.”—History of Christianity.58
“Origen [amene anakhala ndi moyo m’zaka zazana lachiŵiri ndi lachitatu la Nyengo Ino] . . . akunena kuti ‘Tchalitchi Chachikristu sichingaloŵe m’nkhondo yomenyana ndi mtundu uliwonse. Iwo aphunzira kuchokera kwa Mtsogoleri wawo kuti iwo ali ana amtendere.’ M’nyengo imeneyo Akristu ambiri anaphedwera chikhulupiliro chifukwa chakukana ntchito yankhondo.”—Treasury of the Christian World.59
20. Kuti akhale omasuka kuulamuliro wochitidwa ndi “wolamulira wa dziko lino,” kodi ndimachitachita ogawanitsa otani adziko amene atumiki a Yehova amapewa?
20 Mwakupitirizabe kusaphatikizidwa m’nkhani zadziko, atumiki a Yehova samathandizira utundu wake wogawanitsawo, kusankhana mafuko kwake, kapena mikangano yake yapakati pa anthu. Mkhalidwe wawo wotsogozedwa ndi Mulunguwo umathandizira mtendere ndi chisungiko pakati pa anthu amitundu yonse. (Machitidwe 10:34, 35) Kunena zowona, opulumuka “chisautso chachikulu” chikudzacho, adzachokera “m’mitundu yonse ndi mafuko ndi anthu ndi malilime.”—Chivumbulutso 7:9, 14, NW.
Mabwenzi a Dziko Kapena Mabwenzi a Mulungu?
21. Kodi nchifukwa ninji munthu amene amatsatira Baibulo sangayembekezerenso kukondedwa ndi dziko?
21 Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Mukadakhala a dziko, dziko likadakonda zake zalokha. Koma popeza simuli adziko, koma ine ndakusankhani inu mwadziko, chifukwa cha ichi dziko likudani inu. . . . Ngati anandizunza ine, adzakuzunzani inunso.” (Yohane 15:19, 20, NW) Chowonadi chosavuta ndicho chakuti njira yokha yokhalira ndi ubwenzi wadziko ndiyo kukhala wofanana nalo—kukhala ndi zilakolako zake, zikhumbo, ndi tsankho, kukhumbira kuganiza ndi nthanthi zake, ndi kutengera zizolowezi ndi njira zake. Koma ochilikiza dzikoli amaipidwa ndi kuvumbulidwa kwa zolakwa zawo kapena kuchenjezedwa za maupandu a kumene njira yawo ikutsogolera. Ndicho chifukwa chake, ngati munthu atsatira ziphunzitso Zabaibulo mu mkhalidwe ndi njira ya moyo nalankhula moziyanja, iye sangapewe konse udani wadziko.—Yohane 17:14; 2 Timoteo 3:12.
22. Kodi ndichosankha chotani ponena za ubwenzi chimene chikuyang’anizana ndi aliyense wa ife?
22 Chotero, Baibulo limasonyeza kuti tiri ndi chosankha chowonekera bwino. Pa Yakobo 4:4, NW timaŵerenga kuti: “Kodi simudziŵa kuti ubwenzi wadziko uli udani ndi Mulungu? Kotero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko akudzichititsa mdani wa Mulungu.” Mulungu alinso ndi miyezo yake yaubwenzi, ndipo siiri yogwirizana ndi yadziko lamtundu wa anthu ochimwa.—Salmo 15:1-5.
23. (a) Kodi nchiyani chimene chikasonyeza kuti munthu ali bwenzi ladziko? (b) Kodi tingasonyeze motani kuti tiri mabwenzi a Mulungu?
23 Kukhala kwathu ndi ubwenzi wa Mulungu kumadalira kwakukulukulu pakukhala kapena kusakhala kwathu wa lirilonse lamagulu adzikoli. Ngati tisonyeza mzimu wadziko, kukhala ndi lingaliro lake la moyo, pamenepo tikudzisonyeza kukhala mabwenzi adziko, osati a Mulungu. Mzimu wadziko umavala “ntchito za thupi” zonga ngati “dama, chodetsa, kukhumba zonyansa, kupembedza mafano, nyanga, madano, ndewu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magawano, mipatuko, njiru, kuledzera, mchezo, ndi zina zotere.” Baibulo limanena momvekera bwino kuti “iwo akuchitachita zotere sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu.” Kumbali ina, ngati tiri mabwenzi a Mulungu, tidzakhala ndi mzimu wake limodzi ndi zipatso zake za “chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiliro, chifatso, chiletso.”—Agalatiya 5:19-23.
24. (a) Kodi nchifukwa ninji kuli kupanda nzeru kukhala otsanzira anthu amene dziko limawapatsa ulemu? (b) Kodi ndimotani mmene lingaliro lathu kulinga kuchuma chakuthupi limasonyezera amene ife tikufunafuna kukhala bwenzi lathu lenileni?
24 Pamenepa, kodi ndimzimu wayani, umene ife timasonyeza? Limenelo lidzatithandiza kudziŵa kuti ife kwenikweni tiri mabwenzi ayani. Kukhala monga momwe tikukhaliramu, ogonjera kuchisonkhezero cha dziko loipa liripoli, sitiyenera kudabwa ngati tiwona kufunika kwa kupanga masinthidwe m’miyoyo yathu mmalo mwakuti tikondweretse Mulungu. Mwachitsanzo, anthu audziko, amaunjika ulemu ndi ulemerero pa anthu amene chisonkhezero chawo chokhumbira ukumu chimatsogolera ku chuma chochuluka, ulamuliro, kapena kutchuka. Anthu amadzifanizitsa ndi ngwazi zaudziko ndi anthu olambiridwa monga mafano oterowo, akumawatsanzira m’mawu, khalidwe, kawonekedwe, ndi kavalidwe. Kodi inu mufuna kuwoneka kukhala wokhumbira anthu oterowo? Zochita zawo ziri zosemphana kotheratu ndi zimene Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kupanga zonulirapo zathu m’moyo. Baibulo limatitsogoza ku chuma chauzimu ndi nyonga ndi ulemu wakutumikira monga oimira a Mulungu ndi aneneri padziko lapansi. (1 Timoteo 6:17-19; 2 Timoteo 1:7, 8; Yeremiya 9:23, 24) Mawu onyengelera azamalonda adziko amatembenuzira anthu kukukondetsa zinthu zakuthupi, kuwachititsa kukhulupilira kuti chimwemwe chimadalira pachuma. Chotero amapereka chisamaliro chokulira kwambiri pa zimenezi kuposa zinthu zopindulitsa mwauzimu. Inde, kulondola njira yadziko kudzakuchititsani kupeza ubwenzi wadziko. Koma kudzakudulani ku ubwenzi wa Mulungu. Kodi ndiuti umene umatanthauza zochuluka kwambiri kwa inu? Kodi ndiuti umene udzatsogolera kuchimwemwe chachikulu kwambiri ndi chosatha kwambiri?
25. (a) kodi tiyenera kuyembekezera chiyani kudziko pamene tisiya njira zake? (b) Kodi nchiyani chimene kwenikweni chidzatikhozetsa ‘kusanduliza maganizo athu’ kuwona zinthu monga momwe Mulungu amachitira?
25 Nkosavuta kugonjera kunjira yadziko. Ndipo, chifukwa chamzimu wake woipa, ochilikiza dzikoli adzaipidwa nazo ngati mutenga njira yosiyana. (1 Petro 4:3, 4) Zipsinjo zidzaikidwa pa inu kuti mugonjere, kulola chitaganya cha anthu audziko kukuchititsani kukhala ofanana nacho. Nzeru zadziko, nthanthi zake zonena za chimene chimadzetsa chipambano m’moyo, zidzagwiritsiridwa ntchito kuyesa kulamulira kuganiza kwanu. Chotero, kumafunikira kuyesayesa kwenikweni ndi chikhulupiliro kuti ‘musinthe maganizo anu’ kuti muwone zinthu mwalingaliro la Mulungu, ndi kuzindikira chifukwa chake ‘nzeru yadziko lino iliri yopusa m’maso mwake.’ (Aroma 12:2; 1 Akorinto 1:18-20; 2:14-16; 3:18-20) Mwaphunziro lakhama la Mawu a Mulungu tingathe kuwona bwino nzeru yonyenga yadziko. Tingathe kuwona zoturuka zoipa zimene zikuturuka kale ku “nzeru” yotero, ndi chitsiriziro chowononga kumene imatsogolerako. Pamenepo tingathenso kufika pakuzindikira mokwanira nzeru yanjira ya Mulungu ndi madalitso otsimikizirika amene iyo imatsimikizira.
Nkosapindulitsa Kupereka Moyo ndi Nyonga ku Dziko Limene Likupita
26. Kodi kukakhala kwanzeru kuloŵa m’ntchito zamagulu adziko othandiza osowa ndi lingaliro lakuwongolera mikhalidwe?
26 Anthu ena angatsutse kuti: ‘Koma ambiri a magulu adziko amachita zabwino, amachititsa chinjirizo, thanzi, maphunziro ndi ufulu wa anthu.’ Zowona, magulu ena amaperekadi mpumulo wakanthawi pa oŵerengeka a mavuto a anthu. Komabe iwo onse ali mbali yadziko yodana ndi Mulungu. Ndipo amatembenuzira maganizo a anthu kukupitirizidwabe kwa dongosolo lazinthu liripoli. Palibe lirilonse la iwo limene limachilikiza boma la Mulungu la dziko lapansi, Ufumu wake wokhala m’manja mwa Mwana wake. Ndiiko komwe, ngakhale apandu ena angalere mabanja, kuwapezera zosowa, ndi kuchita ntchito zachifundo m’chitaganya. Koma kodi zinthu zimenezi zikalungamitsa kupereka kwathu chichilikizo m’njira iriyonse kumagulu aupandu?—Yerekezerani ndi 2 Akorinto 6:14-16.
27. Kodi ndinjira yokha iti imene ife tingathandizire nayo anthu m’dziko lino kukhala pakati pa opulumuka kuloŵa m’Dongosolo Latsopano la Mulungu?
27 Kodi tingasonyezedi anthu chikondi chopanda mpeni kumphasa mwakudzigwirizanitsa ndi lirilonse lamagulu adziko, tikumawonongerako nthawi ndi nyonga? Ngati inu mufuna kuthandiza munthu wina wodwala kapena wokanthidwa ndi nthenda, kodi mukanatero mwakuyandikana naye kwambiri kotero kuti muyambukiridwa ndi matenda kapena nthenda imodzimodziyo? Kapena kodi simukanakhala wothandiza kwambiri ngati inu mwininu mukanakhalabe wathanzi ndi kuyesa kuthandiza munthuyo kupeza njira yopezera thanzi labwino? Chitaganya cha anthu chamakono chiri chodwala ndi chamatenda mwauzimu. Palibe aliyense amene angachipulumutse, pakuti Mawu a Mulungu amasonyeza kuti matenda ake akutsogolera ku imfa yake. (Yerekezerani ndi Yesaya 1:4-9.) Koma ife tingathandize anthu alionse paokha m’dziko kupeza njira yopezera thanzi labwino lauzimu ndi kupulumuka kuloŵa m’Dongosolo Latsopano la Mulungu—malinga ngati ife enife tisungabe kukhala kwathu osiyana ndi dziko. (2 Akorinto 6:17) Pamenepa, mwanzeru, peŵani kuloŵetsedwa m’njira zadziko. Yesetsani kupeŵa kukhala woyambukiridwa ndi mzimu wadziko ndi kutsanzira njira zake zosalungama. Musaiŵale konse kuti: “Dziko lipita, ndi chilakolako chake, koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala kunthawi zonse.”—1 Yohane 2:17, NW.