Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Pamaso pa Bwalo la Akulu, Kenaka kwa Pilato
USIKU watsala pang’ono kutha. Petro wamkana Yesu kachitatu, ndipo ziŵalo za Bwalo la Akulu zamaliza kuzenga mlandu kwawo konyoza ndipo abalalika. Komabe, iwo akukumananso Lachisanu mmawa mbandakucha, panthaŵiyi pa Holo yawo ya Bwalo la Akulu. Mwachidziŵikire cholinga chawo nchofuna kupangitsa kuzenga mlandu kwa usikuko kuwoneka kwalamulo. Pamene Yesu wabweretsedwa kwa iwo, iwo akunena monga mmene ananenera usiku uja kuti: “Ngati uli Kristu, utiuze.”
‘Ndikakuuzani, simudzavomereza,’ wayankha motero Yesu. “Ndipo ndikakufunsani kanthu, simudzayankha.” Komabe, molimba mtima Yesu akusonya chizindikiritso chake, akumati: “Kuyambira tsopano Mwana wa munthu adzakhala pa dzanja lamanja la mphamvu ya Mulungu.”
“Umo mtero, muli Mwana wa Mulungu kodi?” onsewo akufuna kudziŵa.
“Munena kuti ndine,” Yesu akuyankha motero.
Kwa anthu ofunitsitsa kuphawa, yankho limeneli lakwanira. Akulilingalira kukhala kuchitira mwano. “Tifuniranjinso mboni?” iwo akufunsa motero. “Pakuti ife tokha tinamva m’kamwa mwa Iye mwini.” Choncho akumanga Yesu, nachoka naye, nampereka kwa kazembe Wachiroma, Pontiyo Pilato.
Yudase, wopereka wa Yesu, wakhala akuwona zochitikazo. Pamene awona kuti Yesu watsutsidwa, akulapa. Chotero akunka kwa ansembe aakulu ndi akulu kukabweza ndalama zasiliva 30, akumalongosola kuti: ‘Ndinachita koipa ine, pakupereka mwazi wosalakwa.’
‘Tiri nacho chiyani ife? Udziwonere wekha,’ iwo akuyankha motero mopanda chifundo. Chotero Yudase akuponya ndalama zasilivazo m’kachisi napita nayesera kudzipachika yekha. Komabe, nthambi imene Yudase wamangirirako chingwe yaduka, ndipo thupi lake ligwera pamatanthwe pansipo, niliphulika.
Ansembe aakuluwo sali otsimikiza ndi zimene angachite ndi ndalama zasilivazo. ‘Sikuloledwa kuziika m’chosonkhera ndalama za Mulungu,’ iwo akutsimikiza motero, ‘chifukwa ndizo mtengo wa mwazi.’ Choncho, pambuyo pofunsana, iwo akugula munda wa woumba mbiya ndi ndalamazo kuti adziikamo alendo. Chotero mundawo ukutchedwa ‘Munda wa Mwazi.’
Udakali mmawa pamene Yesu wabweretsedwa kubwalo la kazembeyo. Koma Ayuda amene atsagana naye akukana kuloŵa chifukwa akukhulupirira kuti kuyanjana koteroko ndi Akunja kudzawadetsa. Chotero kuti awathandize, Pilato akutulukira kunja. ‘Chifukwa chanji mwadza nacho cha munthu uyu?’ iye akuwafunsa motero.
‘Akadakhala wosachita zoipa uyu sitikadampereka iye kwa inu,’ iwo akuyankha motero.
Akumafuna kupeŵa kudziloŵetsamo, Pilato akuyankha kuti: ‘Mumtenge iye inu, ndi kumweruza iye monga mwa chilamulo chanu.’
Akumaulula cholinga chawo chambanda, Ayudawo akufuula kuti: ‘Tiribe ulamuliro wakupha munthu aliyense.’ Ndithudi, ngati apha Yesu mkati mwa Phwando la Paskha, ichi chikapangitsa msokonezo wa unyinji, popeza kuti ambiri amamulingalira Yesu kukhala wapamwamba. Koma ngati angathe kuwapangitsa Aroma kumupha pa mlandu wa ndale, ichi chikawachotsera liŵongo pamaso pa anthu.
Chotero atsogoleri achipembedzowo, osatchula kuzenga mlandu kwawo koyambirira kumene anatsutsa Yesu chifukwa cha kuchitira mwano, tsopano akupanga zinenezo zosiyana. Iwo akupanga chinenezo cha mbali zitatu ichi: “Tinapeza munthu uyu [1] alikupandutsa anthu a mtundu wathu, ndi [2] kuwaletsa kupereka msonkho kwa Kaisara, [3] nadzinenera kuti Iye yekha ndiye Kristu mfumu.”
Ndimlandu wakuti Yesu amanena kuti ndiye mfumu umene ukudetsa nkhaŵa Pilato. Chotero, iye akuloŵanso m’nyumba yachifumu, namuitana Yesu, namfunsa kuti: “Kodi ndiwe mfumu ya Ayuda?” Kunena m’mawu ŵena, kodi waswa lamulo mwakudzilengeza wekha kukhala mfumu motsutsana ndi Kaisara?
Yesu akufuna kudziŵa zimene Pilato wamva kale ponena za iye, chotero akumfunsa kuti: ‘Kodi munena ichi mwa inu nokha, kapena ena anakuuzani za ine?’
Pilato akunena kuti sakudziŵa kalikonse ponena za iye ndipo akufuna kudziŵa nsonga zenizeni. “Ndiri ine Myuda kodi?” iye akuyankha. ‘Mtundu wako ndi ansembe aakulu anakupereka kwa ine; wachita chiyani?’
Yesu sakuyesa konse kuthaŵa nkhaniyo, ya ufumu. Yankho limene Yesu akupereka tsopano mosakaikira lamdabwitsa Pilato. Luka 22:66–23:3; Mateyu 27: 1-11; Marko 15:1; Yohane 18:28-35; Machitidwe 1:16-20.
◆ Kodi Bwalo la Akulu likukumaniranjinso m’mamawa?
◆ Kodi Yudase wafa motani, ndipo kodi nchiyani chomwe chikuchitidwa ndi ndalama zasiliva 30 zija?
◆ Kodi nchifukwa ninji Ayuda akufuna kuti Aroma amuphe Yesu, mmalo momupha okha monga mmene anayesera pa zochitika zoyambirira?
◆ Kodi ndizinenezo zotani zimene Ayuda akupanga motsutsana ndi Yesu?