Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Kuchokera kwa Pilato Kunka kwa Herode Nkubwereranso
PAMENE Ayuda akuneneza Yesu kuti ankati ndiye mfumu, Pilato akuloŵanso m’nyumba ya kazembe kuti amfunse. Ngakhale kuti Yesu sakuyesa nkomwe kudzibisa kuti ndi mfumu, iye akulongosola kuti Ufumu wake suli chiwopsezo ku Roma.
Yesu akumuuza Pilato kuti: ‘Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi; ufumu wanga ukadakhala wa dziko lino lapansi, anyamata anga akadalimbika nkhondo, kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda; koma tsopano ufumu wanga suli wochokera konkuno.’ Chotero Yesu akuvomereza katatu kuti ali ndi Ufumu, ngakhale kuti suli wochokera ku dziko lapansi.
Komabe, Pilato akumfunsabe nati: “Nanga kodi ndiwe Mfumu?” Ndiko kuti, kodi ndiwe mfumu ngakhale kuti Ufumu wako suli wa dziko lino.
Yesu akumulola Pilato kudziŵa kuti watsimikizira bwino, akumayankha kuti: ‘Munena kuti ndine Mfumu. Ndinabadwira ichi ine, ndipo ndinadzera ichi kudza ku dziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi chowonadi. Yense wakukhala mwa chowonadi amva mawu anga.’
Inde, kukhalapo kwenikweniko kwa Yesu padziko lapansi nkuti achitire umboni ku ‘chowonadi,’ makamaka chowonadi cha Ufumu wake. Yesu ngokonzekera kukhala wokhulupirika ku chowonadi chimenecho ngakhale ngati chikamtengera moyo wake. Ngakhale kuti Pilato akufunsa kuti: ‘Chowonadi nchiyani?’ iye sakudikirira kaamba ka kulongosola kowonjezereka. Iye wamva zokwanira kuti apereke chiweruzo.
Pilato abwerera ku khamu lomwe likudikirira kunja kwa nyumba yachifumuyo. Mwachiwonekere Yesu ali kumbali kwake, iye akuwawuza ansembe aakuluwo ndi omwe ali nawo kuti: ‘Ndiribe kupeza chifukwa cha milandu ndi munthu uyu.’
Pokwiya ndi chosankhacho, makamuwo ayamba kuumirira kuti: “Amautsa anthuwo, naphunzitsa m’Yudeya lonse, kuyambira ku Galileya ndi kufikira kuno komwe.”
Kusalingalira kopanda maziko kwa Ayudawo kuyenera kukhala kukumdabwitsa Pilato. Chotero, pamene ansembe aakulu ndi akulu akupitiriza kufuula, Pilato atembenukira kwa Yesu namfunsa kuti: “Sukumva kodi zinthu zambiri zotere akunenera Iwe?” Komabe, Yesu sakuyankha. Kudekha kwa nkhope yake pamaso pa zinenezo zoipazo kukumdabwitsa Pilato.
Pamene wamva kuti Yesu ndi m’Galileya, Pilato akupeza njira yotulukira m’mlandu wake. Wolamulira wa Galileya, Herode Antipas (mwana wa Herode Wamkulu), ali m’Yerusalemu kaamba ka Paskha, chotero Pilato akutumiza Yesu kwa iye. Koyambirirako, Herode Antipas analamula kuti Yohane Mbatizi adulidwe mutu, kenaka Herode anachita mantha pamene anamva za ntchito zozizwitsa zimene Yesu ankazichita, akumawopa kuti mwina Yesu anali Yohane amene anauka kwa akufa.
Tsopano, Herode akusangalala ndi chiyembekezo chowona Yesu. Ichi sichifukwa chakuti iye akudera nkhaŵa ubwino wa Yesu kapena kuti akufuna kupanga kuyesayesa kwenikweni kulikonse kuwona ngati zinenezo zotsutsana naye nzowona kapena ayi. Mmalomwake, iye akungofuna kudziŵa ndikuyembekezera kuwona Yesu akuchita chozizwitsa china.
Komabe, Yesu akana kukhutiritsa chikhumbo cha Herode. Kwenikweni, pamene Herode akumfunsa, iye sakuyankha kanthu. Atagwiritsidwa mwala, Herode ndi alonda ake amnyoza Yesu. Anamveka chofunda chonyezimira namseka. Kenaka ambweza kwa Pilato. Monga chotulukapo, Herode ndi Pilato, omwe kalelo anali adani, akhala mabwenzi.
Pamene Yesu wabwerera, Pilato akuitana ansembe aakulu, ndi akulu Achiyuda, ndi anthu onse nanena: ‘Munadza kwa ine ndi munthu uyu ngati munthu wakupandutsa anthu: ndipo tawonani, ine ndinamfunsa za mlanduwu pamaso panu, ndipo sindinapeza pa munthuyu chifukwa cha zinthu zimene mumnenera; inde, ngakhale Herode yemwe; pakuti iye anambwezera iye kwa ife; ndipo tawonani, sanachita iye kanthu kakuyenera kufa. Chifukwa chake ndidzamkwapula ndi kummasula iye.’
Chotero, Pilato wamulengeza kaŵiri Yesu kukhala wopanda liŵongo. Iye ngwofunitsitsa kummasula, popeza wazindikira kuti ansembewo ampereka kwa iye chifukwa chakaduka. Koma pamene Pilato akupitiriza kuyesera kumasula Yesu, iye akulandira chifukwa chowonjezereka chochitira tero. Pamene iye ali pampando wake wachiweruzo, mkazi wake akutumiza uthenga, kumfulumiza kuti: ‘Musachite kanthu ndi munthu wolungamayo; pakuti lero m’kulota [mwachiwonekere kokhala ndi chiyambi chaumulungu] ndasauka kwambiri chifukwa cha iye.’
Komabe, kodi Pilato angammasule motani munthu wopanda liŵongoyu, monga momwe akudziŵira kuti ayenera kutero? Yohane 18:36-38; Luka 23:4-16; Mateyu 27:12-14, 18, 19; 14:1, 2; Marko 15:2-5.
◆ Kodi Yesu akuliyankha motani funso lokhudza ufumu wake?
◆ Kodi nchiyani chomwe chiri ‘chowonadi’ chimene Yesu akuchitira umboni mkati mwa moyo wake wapadziko lapansi?
◆ Kodi chiweruzo cha Pilato nchotani, kodi anthuwo akuvomereza motani, ndipo kodi Pilato akuchitanji ndi Yesu?
◆ Kodi Herode Antipas ndiye yani, kodi nchifukwa ninji wakondwa kwakukulu kuwona Yesu, ndipo kodi akuchita nayenji?
◆ Kodi nchifukwa ninji Pilato ali wofunitsitsa kumasula Yesu?