Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
◼ Kodi Ayuda anali ndi ulamuliro walamulo wa kupha Yesu, monga mmene chikulingaliridwira ndi mawu a Pilato pa Yohane 19:6?
Sitingakhale otsimikizira kuti kaya panthaŵi imeneyo Aroma anali atapereka ulamuliro kwa Ayuda wa kupha.
Atsogoleri a Chiyuda atayambitsa kugwidwa kwa Yesu, iwo anachita mtundu wa mlandu. Mkati mwa mlanduwo iwo “anafuna umboni wonama wa kutsutsa Yesu, kuti amuphe iye.” Pomalizira iwo anamutcha Yesu waliwongo la kuchitira mwano ndipo ananena kuti iye motero anali “woyenera kumupha.” (Mateyu 26:59, 60, 65, 66) Koma pambuyo pa “kukhala upo wa kumchitira Yesu kuti amuphe,” iwo anamtenga iye kwa wolamulira wa Chiroma, Pilato.—Mateyu 27:1, 2.
Mikhalidwe imeneyi yatsogoza ambiri kukumaliza kuti Ayuda analibe chivomerezo cha Chiroma kupha Yesu Kristu pa mlandu wa chipembedzo umenewo. Machiwonekere lotsimikizira kawonedwe kameneka liri yankho la Ayuda pamene Pilato anawawuza iwo kuweruza wopatsidwa mlanduyo pansi pa lamulo la Chiyuda. Iwo anayankha kuti: “Tiribe ulamuliro wakupha munthu aliyense.” (Yohane 18:31) M’chenicheni, mwambo wokambidwa mu Jerusalem Talmud unanena kuti chifupifupi zaka 40 Yerusalemu asanawonongedwe mu 70 C.E., Ayuda anataya ulamuliro wawo wa kuweruza ochimwa.
Chiri chachilendo chotani nanga, chotero, kuŵerenga mawu a Pilato pa Yohane 19:6. Akumayankha ku kufuula kochokera kwa atsogoleri achipembedzo kaamba ka kupachikidwa kwa Yesu, Pilato anauza iwo kuti: “Mtengeni iye inu nimumpachike, pakuti ine sindipeza chifukwa mwa iye.” Ganizo limene likuwoneka kukhala lowombana ndi chimene Ayuda ananena pa Yohane 18:31.
Wodziŵa mbiri yakale wa Chiyuda Flavius Josephus anapereka mbiri ya umboni wowona ndi maso imene ingawunikire pa kuwombana kumeneku. Iye akusimba kuti mkati mwa kuwukira kwa Aroma pa Yerusalemu mu 70 C.E., owukirawo anabwerera m’malo opatulika a kachisi. Ena a omenya a mwazi amenewa anali m’malo omwe anali a kunja kwa malire chifukwa cha kupatulika kwawo. Woipidwa ndi kupangitsa kukhala chosapatulika kumeneku kwa chimene ngakhale Aroma anali kuwona monga malo opatulika, Kazembe Tito anaitana kuti:
“Anthu onyansa inu! Kodi simunaike chochinga [kapena khoma lalifupi logawanitsa mbali ya malo opatulika] kuchinjiriza Nyumba yanu Yoyera? Kodi inu pa malo ena osiyanasiyana simunaike miyala yolembedwa m’zilembo za Chigriki ndi zathu, kuletsa aliyense kupita kupyola guwa la nsembe? Ndipo kodi ife sitinakupatseni inu kuyenera kwa kupha aliyense yemwe akapita kupyola iwo, ngakhale ngati iye anali m’Roma? Nchifukwa ninji nanga, inu anthu a liwongo, mukuponda matupi akufa mkati mwake?”—The Jewish War, lotembenuzidwa ndi G. A. Williamson, tsamba 312. Kanyenye ngwathu.
Chotero, ngakhale ngati Aroma sanavomereze Ayuda kupereka chilango cha imfa kaamba ka kulakwira boma, chikuwoneka kuti iwo anapereka ulamuliro wa kupha kaamba ka milandu ina yaikulu ya chipembedzo. Ayuda omwe anapereka Yesu kwa Pilato angakhale analingalira icho kukhala chokhumbika kulola Aroma kuchita kuphako, mwinamwake kuti apangitse imfa yake kukhala yonyansa koposa, ndipo chotero kulira konse kwapoyera kukanatsogozedwa motsutsana ndi alendo. (Agalatiya 3:13; Deuteronomo 21:23) Pilato, ngakhale ndi tero, mwinamwake akumafuna kupewa vuto limenelo, anawauza iwo: “Mtengeni iye inu nimumpachike.” Iye angakhale anali kusonyeza, kachiŵirinso, kuti iye anadzimva kuti ngati nkhaniyo inali ya chipembedzo inali kulakwa kokwanira, atsogoleri a Chiyuda ayenera kukhala ndi thayo la kupha Yesu.
[Zithunzi patsamba 31]
Mawu ozokotedwa awa ochokera pa malo opatulika a kachisi (onani mkati) anachenjeza Akunja molimbana ndi kupita kudutsa khoma lotsika la kachisi
[Mawu a Chithunzi]
Kutulutsidwanso kwa mzinda wa Yerusalemu panthaŵi ya kachisi wachiŵiri—wokhala pa mabwalo a Holyland Hotel, Yerusalemu
[Mawu a Chithunzi]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.