Kodi Baibulo Limadzitsutsa?
WOLEMBA Henry Van Dyke panthaŵi ina analemba kuti: “Lobadwira Kum’maŵa ndi kulankhula chinenero ndi mawu okuluŵika a Kum’maŵa, Baibulo limayenda m’njira za dziko lonse ndi mapadzi ozoloŵereka ndipo limaloŵa m’dziko lirilonse kukafunafuna ake kulikonse. Laphunzira kulankhula zinenero mazana ambiri mokhoza kufikira mtima wa munthu. Ana amamvetsera nkhani zake mozizwa ndi kusangalala, ndipo amuna anzeru amazisanthula monga mafanizo a moyo. Oipa ndi onyada amanthunthumira ndi machenjezo ake, koma kwa opwetekedwa ndi achisoni liri ndi liwu la nakubala. . . . Palibe munthu amene ali wosauka kapena wopanda kanthu akakhala nacho chumachi monga chakechake.”
Ndithudi, Baibulo “laphunzira kulankhula m’zinenero mazana ambiri.” Oposa limodzi la mabuku ake okwanira 66 atembenuzidwa m’zilankhulo zokwanira 1,970. Mamiliyoni amawona Baibulo monga mphatso yochokera kwa Mulungu ndipo amaliŵerenga mosangalala ndi kupindula. Komabe, ena amanena kuti liri ndi mfundo zotsutsana ndipo motero nlosadalirika. Kodi kufufuza kosamalitsa kumasonyezanji?
Monga momwe kwasonyezedwera ndi chithunzithunzi chathu chapachikuto, Mulungu anagwiritsira ntchito amuna okhulupirika kulemba Baibulo. Ndithudi, kupenda mosamalitsa Baibulo kumavumbula kuti linalembedwa ndi amuna pafupifupi 40 m’nyengo ya zaka mazana 16. Kodi iwo anali akatswiri antchito yakulemba? Ayi. Pakati pawo munthu akhoza kupeza mbusa, msodzi, wamsonkho, sing’anga, wosoka mahema, wansembe, mneneri, ndi mfumu. Zolemba zawo kaŵirikaŵiri zimatchula anthu ndi miyambo yosazoloŵereka kwa ife a m’zaka za zana la 20. Kunena zowona, olemba Baibulo enieniwo sinthaŵi zonse kuti anamvetsetsa tanthauzo la zimene analemba. (Danieli 12:8-10) Chotero sitiyenera kudabwa ngati tikumana ndi nkhani zovuta kumvetsetsa pamene tiŵerenga Baibulo.
Kodi zovuta zoterozo zingamveketsedwe? Kodi Baibulo limadzitsutsa? Kuti tidziŵe, tiyeni tipende zitsanzo zina.
Kodi Izi Nzovuta Zenizeni?
▪ Kodi Kaini Anapeza kuti mkazi wake? (Genesis 4:17)
Wina akhoza kulingalira kuti pambuyo pakuphedwa kwa Abele, padziko lapansi panangotsala Kaini mbale wake waliŵongoyo, ndi makolo ake, Adamu ndi Hava. Komabe, Adamu ndi Hava anali ndi banja lalikulu. Malinga ndi Genesis 5:3, 4, Adamu anali ndi mwana wamwamuna wotchedwa Seti. Cholembedwacho chimawonjezera kuti: “Masiku ake Adamu atabala Seti, anali zaka mazana asanu ndi atatu; ndipo anabala ana amuna ndi akazi.” Chotero Kaini anakwatira mlongo wake kapena mmodzi wa adzukulu ake. Popeza kuti mtundu wa anthu panthaŵiyo unali pafupi kwambiri ndi ungwiro waumunthu, mwachiwonekere ukwati woterowo sunapereka maupandu athanzi amene lerolino akanavulaza mwana wobadwa muukwati woterowo.
▪ Kodi ndani amene anagulitsa Yosefe ku Igupto?
Genesis 37:27 amanena kuti abale a Yosefe anasankha kumgulitsa kwa Aismayeli. Koma vesi lotsatira limati: “Ndipo anapita pamenepo Amidyani a malonda: ndipo [abale a Yosefe] anamtulutsa namkweza Yosefe m’dzenjemo, namgulitsa kwa Aismayeli ndi ndalama za siliva makumi aŵiri; ndipo anamka naye ku Igupto.” Kodi Yosefe anagulitsidwa kwa Aismayeli kapena kwa Amidyani? Eya, Amidyani angakhale anatchedwanso Aismayeli, amene anali abale awo kudzera mwa kholo lawo Abrahamu. Kapena amalonda Achimidyani anali kuyenda pamodzi ndi Aismayeli apaulendo. Mulimonse mmene zingakhalire, abale a Yosefe ndiwo anamgulitsa, ndipo pambuyo pake anakhoza kuwauza kuti: “Ine ndine Yosefe mbale wanu, ine ndemwe munandigulitsa ndiloŵe m’Aigupto.”—Genesis 45:4.
▪ Kodi ndi Aisrayeli angati amene anafa kaamba kochita chisembwere ndi akazi Achimoabu ndi kudziloŵetsa m’kulambira Bala wa Peori?
Numeri 25:9 amanena kuti: “Ndipo akufa nawo mliri [wochokera kwa Mulungu kaamba ka makhalidwe awo oipa] ndiwo zikwi makumi aŵiri ndi zinayi.” Komabe, mtumwi Paulo anati: “Kapena tisachite dama monga ena a iwo [Aisrayeli m’chipululu] anachita dama, nagwa tsiku limodzi zikwi makumi aŵiri ndi zitatu.” (1 Akorinto 10:8) Mwinamwake chiŵerengero cha ophedwawo chinali pakati pa 23,000 ndi 24,000, kotero kuti chirichonse cha ziŵerengerozo chikakhala chokhutiritsa. Komabe, lemba la Numeri makamaka limasonyeza kuti “akulu onse a anthu” odziloŵetsa m’tchimo limeneli anaphedwa ndi oweruza. (Numeri 25:4, 5) Mwina panali okwanira 1,000 a “akulu a anthu” aliŵongo ameneŵa, akupanga chiwonkhetso cha 24,000 atawonkhetsedwa ndi 23,000 otchulidwa ndi Paulo. Pamene kuli kwakuti mwachiwonekere 23,000 anaphedwa mwachindunji ndi mliri wochokera kwa Mulungu, onse 24,000 anakumana ndi mliri wa Yehova chifukwa chakuti aliyense wa iwo anafa pansi pa lamulo lake la chiweruzo cha imfa.—Deuteronomo 4:3.
▪ Popeza kuti Agagi anakhalako m’nthaŵi ya Sauli mfumu ya Israyeli, kodi sikulakwa pamene Balamu anatchula pasadakhale wolamulira wa Ameleki wokhala ndi dzina limenelo?
Pafupifupi mu 1473 B.C.E., Balamu analosera kuti mfumu ya Israyeli “idzamveka koposa Agagi.” (Numeri 24:7) Sipanakhale kutchulidwa kulikonse kwa Agagi kufikira m’nthaŵi yakulamulira kwa Mfumu Sauli (1117-1078 B.C.E.). (1 Samueli 15:8) Komabe, kumeneku sikunali kulakwa chifukwa chakuti “Agagi” lingakhale linali dzina lachifumu lofanana ndi Farao mu Igupto. Nkothekeranso kuti Agagi linali dzina laumwini logwiritsiridwa ntchito mobwerezabwereza ndi olamulira Achimeleki.
▪ Kodi ndani amene anapangitsa Davide kutenga chiŵerengero cha Aisrayeli?
Samueli Wachiŵiri 24:1 amanena kuti: “Ndipo mkwiyo wa Yehova unayakanso pa Israyeli, nafulumiza Davide [kapena, “pamene Davide anafulumizidwa,” mawu amtsinde] pa iwo, nati, Muka, nuŵerenge Israyeli ndi Yuda.” Koma sanali Yehova amene anachititsa Mfumu Davide kuchimwa, popeza kuti 1 Mbiri 21:1 imati: “Satana [kapena, “wotsutsa,” mawu amtsinde] anaukira Israyeli, nasonkhezera Davide aŵerenge Israyeli.” Mulungu sanakondwere ndi Aisrayeli nchifukwa chake analola Satana Mdyerekezi kudzetsa tchimoli pa iwo. Chotero, 2 Samueli 24:1 amanena monga ngati kuti Mulungu ndiye anachita zimenezo. Mokondweretsa, matembenuzidwe a Joseph B. Rotherham amanena kuti: “Mkwiyo wa Yahweh unayaka pa Israyeli, kotero kuti anapereka Davide kuti asonkhezeredwe motsutsana nawo akumati, Pita nuŵerenge Israyeli ndi Yuda.”
▪ Kodi ndimotani mmene munthu angagwirizanitsire kusiyana kwa ziŵerengero zoperekedwa za Aisrayeli ndi Ayuda m’kuŵerenga kwa Davide?
Pa 2 Samueli 24:9 pali ziŵerengero za Aisrayeli 800,000 ndi Ayuda 500,000, pamene 1 Mbiri 21:5 imapereka chiŵerengero cha amuna ankhondo a Israyeli okwanira 1,100,000 ndi a Yuda kukhala 470,000. Olembedwa nthaŵi zonse kutumikira mtunduwo anali asirikali 288,000, ogaŵidwa m’magulu 12 lirilonse lokhala ndi asirikali 24,000, ndipo gulu lirilonse likumatumikira mwezi umodzi m’chaka. Panalinso akalinde 12,000 pa akalonga 12 a mafukowo, akupanga chiwonkhetso cha 300,000. Mwachiwonekere, 1,100,000 otchulidwa pa 1 Mbiri 21:5 amaphatikizapo 300,000 amenewo olembedwa kale, pamene 2 Samueli 24:9 samatero. (Numeri 1:16; Deuteronomo 1:15; 1 Mbiri 27:1-22) Ponena za Yuda, 2 Samueli 24:9 mwachiwonekere anaphatikizapo amuna 30,000 osolola lupanga oyang’anira okhazikitsidwa kumalire ndi Filisti koma amene sanaphatikizidwe m’chiŵerengero choperekedwa pa 1 Mbiri 21:5. (2 Samueli 6:1) Ngati tikukumbukira kuti 2 Samueli ndi 1 Mbiri analembedwa ndi amuna aŵiri osiyana okhala ndi kawonedwe kazinthu ndi zolinga zosiyana, tikhoza kugwirizanitsa ziŵerengerozi mosavuta.
▪ Kodi ndani anali atate wa Sealitiyeli?
Malemba ena amasonyeza kuti Yekoniya (Mfumu Yehoyakimu) anali atate wakuthupi wa Sealitiyeli. (1 Mbiri 3:16-18; Mateyu 1:12) Koma wolemba Uthenga Wabwino Luka anatcha Sealitiyeli “mwana wa Neri.” (Luka 3:27) Mwachiwonekere Neri anapatsa mwana wake wamkazi kwa Sealitiyeli kukhala mkazi wake. Popeza kuti mwachizoloŵezi Ahebri anatcha mkamwini mwana, makamaka polemba mizera yobadwira, Luka moyenerera anatcha Sealitiyeli mwana wa Neri. Mofananamo, Luka anatcha Yosefe mwana wa Heli, amene kwenikweni anali atate wa mkazi wa Yosefe, Maria.—Luka 3:23.
Kugwirizanitsa Malemba Onena za Yesu
▪ Kodi Yesu Kristu anatulutsa ziŵanda mwa amuna angati zimene zinakaloŵa m’gulu la nkhumba?
Wolemba Uthenga Wabwino Mateyu akutchula amuna aŵiri, koma Marko ndi Luka amatchula mmodzi yekha. (Mateyu 8:28; Marko 5:2; Luka 8:27) Mwachiwonekere, Marko ndi Luka ananena za mwamuna mmodzi wogwidwa ndi ziŵanda chifukwa chakuti Yesu analankhula kwa iye ndipo nkhani yake inamveka yapadera kwambiri. Mwinamwake, mwamunayo anali wachiwawa kwambiri kapena anavutitsidwa ndi ziŵanda kwanthaŵi yaitali kwambiri. Pambuyo pake, mwinamwake mwamunayo anafuna kutsagana ndi Yesu. (Marko 5:18-20) Mwanjira yochita ngati yofanana, Mateyu analankhula za amuna akhungu aŵiri amene anachiritsidwa ndi Yesu, pamene Marko ndi Luka anatchula mmodzi yekha. (Mateyu 20:29-34; Marko 10:46; Luka 18:35) Kumeneku sikunali kudzitsutsa, popeza kuti panali mwamuna mmodzi yekha woteroyo.
▪ Kodi malaya amene Yesu anavala patsiku la imfa yake anali amawonekedwe otani?
Malinga ndi Marko (15:17) ndi Yohane (19:2), asilikaliwo anaveka Yesu malaya achibakuwa. Koma Mateyu (27:28) anawatcha “malaya ofiira achifumu,” kugogomezera kufiira kwake. Popeza kuti mawonekedwe achibakuwa ndialionse okhala ndi msanganizo wa kufiira ndi kubiriŵira (blu), Marko ndi Yohane akuvomereza kuti malayawo anali ndi mawonekedwe ofiirira. Cheza cha kuŵala ndi malowo ziyenera kukhala zitapangitsa malayawo kupereka mawonekedwe osiyanasiyana, ndipo olemba Uthenga Wabwinowo anatchula mawonekedwe amene anali owonekera kwambiri kwa iwo kapena kwa amene anawawuza nkhaniyo. Kusiyana kwakung’onoko kumasonyeza kuti olembawo anali anthu osiyana ndipo kumatsimikizira kuti panalibe chinyengo.
▪ Kodi ndani amene ananyamula mtengo wozunzirapo wa Yesu?
Yohane (19:17) anati: “Ndipo anasenza [mtengo wozunzirapo, NW] yekha, natuluka kumka ku malo otchedwa Malo-a-bade, amene atchedwa m’Chihebri, Golgota.” Koma Mateyu (27:32), Marko (15:21), ndi Luka (23:26) amati ‘pamene anali kutuluka, Simoni wa ku Kurene anakakamizidwa kunyamula [mtengo wozunzirapo, NW].’ Yesu ananyamuladi mtengo wake wozunzirapo, monga momwe Yohane ananenera. Komabe, m’cholembedwa chake chachidule, Yohane sanaphatikizepo mfundo yakuti Simoni pambuyo pake anapatsidwa ntchito yakunyamula mtengowo. Motero, zolembedwa za Uthenga Wabwino zimagwirizana m’zimenezi.
▪ Kodi ndimotani mmene Yudasi Isikareote anafera?
Mateyu 27:5 amanena kuti Yudasi anadzimangirira, pamene Machitidwe 1:18 amati “anagwa chamutu, naphulika pakati, ndi matumbo ake onse anakhuthuka.” Pamene Mateyu akuwonekera kukhala akufotokoza mtundu wa kudzipha, Machitidwe akulongosola zotulukapo zake. Mwachiwonekere Yudasi anamangirira chingwe panthambi ya mtengo, nakoloŵeka khwekwe m’khosi mwake, ndipo anayesa kudzinyonga mwakulumpha patherezi. Kukuwonekera kuti chingwecho chinaduka kapena nthambi ya mtengoyo inathyoka kotero kuti anagwa chamutu naphulika pamiyala yomwe inali pansipo. Malo ozungulira Yerusalemu amapangitsa lingaliro loterolo kukhala lomveka.
Kodi Mudzaziwona Motani Nkhanizo?
Ngati tikumana ndi nkhani zowonekera kukhala zotsemphana m’Baibulo, ndibwino kuzindikira kuti anthu kaŵirikaŵiri amanena zinthu zimene zimawonekera kukhala zotsutsana koma zimalongosoledwa kapena kumvedwa mosavuta. Mwachitsanzo, mwini bizinesi angalembe kalata kwa munthu wina mwakulankhula mawu kwa mlembi wake oika m’kalatayo. Atafunsidwa, akhoza kunena kuti iye anatumiza kalatayo. Koma popeza kuti mlembi wake ndiye anataipa ndi kutumiza kalatayo, akhoza kunena kuti iye ndiye anaitumiza. Mofananamo, sikunali kutsutsana pamene Mateyu (8:5) ananena kuti kenturiyo anadza kudzapempha kwa Yesu, pamene kuli kwakuti Luka (7:2, 3) ananena kuti mwamunayo anatumiza omuimira.
Zitsanzo zimene zaperekedwazo zimasonyeza kuti zovuta za m’Baibulo zikhoza kuthetsedwa. Motero, pali chifukwa chabwino chokhalira ndi kaimidwe kamaganizo kabwino kulinga ku Malemba. Mzimu woterowo unathokozedwa m’mawu aŵa opezeka m’Baibulo labanja lofalitsidwa m’chaka cha 1876:
“Mkhalidwe woyenera wochitira ndi zovuta zimenezo ndiwo, kuzichotsa monga momwe kungathekere, ndi kumamatira ndi kugonjera ku chowonadi, ngakhale pamene chokaikiritsa chirichonse sichitheka kuchotsedwapo. Tiyenera kutsanzira chitsanzo cha atumwi, amene, pamene ena a ophunzira anakhumudwa ndi zimene anatcha ‘mawu osautsa,’ kuti amkane Kristu, anakaniza chitsutso chirichonse ndi mawu akuti: ‘Ambuye tidzamuka kwa yani? Inu muli nawo mawu a moyo wosatha. Ndipo ife tikhulupirira, ndipo tidziŵa kuti inu ndinu Kristuyo, Mwana wa Mulungu wamoyo.’ . . . Pamene tiwona kuti chowonadi chikuwonekera kukhala chikutsutsana ndi chowonadi china, tiyeni tiyese kuzigwirizanitsa, ndipo chisonyezeni kwa onse kuti chimagwirizanika.”—Yohane 6:60-69.
Kodi mudzakhala ndi kaimidwe koteroko? Pambuyo pakupenda zitsanzo zoŵerengeka chabe zosonyeza kugwirizana kwa Malemba, tikhulupirira kuti mukuvomerezana ndi wamasalmo amene anati kwa Mulungu: “Chiŵerengero cha mawu anu ndicho chowonadi.” (Salmo 119:160) Mboni za Yehova zimakhala ndi lingaliro limenelo ponena za Baibulo lonse ndipo zimakhala zokondwa kupereka zifukwa zakukhulupirira kwanu. Bwanji osakambitsirana nazo bukhulo losafanana ndi lina lirilonse? Uthenga wake wotonthoza mtima ungakudzazeni ndi chiyembekezo chowona ndi chimwemwe.
[Chithunzi patsamba 7]
Kodi munafunsapo Mboni za Yehova chifukwa chake zimakhulupirira Baibulo?