Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Yesu anati: “Zochimwa za anthu alionse muwakhululukira, zikhululukidwa kwa iwo; za iwo amene muzigwiritsa, zagwiritsidwa.” Kodi mawu ameneŵa amatanthauza kuti Akristu angakhululukire machimo?
Palibe umboni wa m’Malemba umene umatisonyeza kuti Akristu alionse, kapena ngakhale akulu oikidwa m’mipingo, ali ndi ulamuliro wochokera kwa Mulungu wa kukhululukira machimo. Komabe, zimene Yesu ananena kwa ophunzira ake pa Yohane 20:23, wogwidwa mawu pamwambapa, zimasonyeza kuti Mulungu anapatsa atumwi mphamvu zapadera pa nkhaniyi. Ndipo mawu a Yesu pamenepo angagwirizane ndi zimene ananena pa Mateyu 18:18 ponena za zigamulo za kumwamba.
Akristu angakhululukire milandu ina, mogwirizana ndi uphungu wa mtumwi Paulo wolembedwa pa Aefeso 4:32: “Mukhalirane okoma wina ndi mzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Kristu anakhululukira inu.” Panopa Paulo anali kunena za mavuto aumwini pakati pa Akristu, monga kulankhula kosasamala. Iwo ayenera kuyesetsa kuthetsa nkhanizi, akumakhululukirana wina ndi mzake. Kumbukirani mawu a Yesu akuti: “Chifukwa chake ngati ulikupereka mtulo wako pa guwa lansembe, ndipo pomwepo ukakumbukira kuti mbale wako ali ndi kanthu pa iwe, usiye pomwepo mtulo wako ku guwako, nuchoke, nuyambe kuyanjana ndi mbale wako, ndipo pamenepo idza nupereke mtulo wako.”—Mateyu 5:23, 24; 1 Petro 4:8.
Komabe, mawu a pa Yohane 20:23 akupereka lingaliro lakuti Yesu anali kunena za machimo aakulu, monga zimene ananenanso kwa anthu amodzimodziwa zikusonyezera. Tiyeni tione chifukwa chake.
Patsiku limene anaukitsidwa, Yesu anaonekera kwa ophunzira m’chipinda chotsekedwa m’Yerusalemu. Nkhaniyo imati: “Chifukwa chake Yesu anatinso kwa iwo, Mtendere ukhale ndi inu; monga Atate wandituma ine, inenso ndituma inu. Ndipo pamene anati ichi anawapumira, nanena nawo, Landirani mzimu woyera. Zochimwa za anthu alionse muwakhululukira, zikhululukidwa kwa iwo; za iwo amene muzigwiritsa, zagwiritsidwa.”—Yohane 20:21-23.
Mwachionekere, ophunzira otchulidwawo kwenikweni anali atumwi okhulupirikawo. (Yerekezerani ndi vesi 24.) Mwa kuwapumira ndi kunena kuti, “Landirani mzimu woyera,” Yesu mophiphiritsira anawadziŵitsa kuti posachedwa mzimu woyera udzatsanuliridwa pa iwo. Yesu ananenanso kuti adzakhala ndi ulamuliro wa kukhululukira machimo. Motero, mfundo zake ziŵirizo zikugwirizana, chimodzi chikumatsogolera ku chinzake.
Masiku makumi asanu pambuyo pa kuukitsidwa kwake, patsiku la Pentekoste, Yesu anatsanula mzimu woyera. Kodi zimenezo zinakwaniritsa chiyani? Chinthu chimodzi ndicho chakuti, awo amene analandira mzimuwo anabadwanso monga ana auzimu a Mulungu okhala ndi chiyembekezo cha kukakhala olamulira anzake a Kristu kumwamba. (Yohane 3:3-5; Aroma 8:15-17; 2 Akorinto 1:22) Koma kutsanuliridwa kwa mzimu kumeneko kunachita zambiri. Ena amene anaulandira anakhala ndi mphamvu za zozizwitsa. Mwa njira imeneyo ena anatha kulankhula zinenero za kwina zimene sanadziŵe. Ena anatha kulosera. Komabe enanso anatha kumachiza odwala kapena kuukitsira akufa ku moyo.—1 Akorinto 12:4-11.
Popeza mawu a Yesu pa Yohane 20:22 anasonyeza za kutsanuliridwa kwa mzimu woyera kumeneku pa ophunzirawo, mawu ake ogwirizanitsidwa onena za kukhululukira machimo akuoneka kuti akutanthauza kuti atumwi anapatsidwa ulamuliro wapadera wa kukhululukira machimo kapena kusakhululukira kuchokera kwa Mulungu kupyolera mwa ntchito ya mzimu.—Onani Nsanja ya Olonda, yachingelezi ya March 1, 1949, tsamba 78.
Baibulo silimasimba zonse ponena za nthaŵi iliyonse pamene atumwi anagwiritsira ntchito ulamuliro umenewu, komanso silimasonyeza zochitika zonse pamene iwo anagwiritsira ntchito mphatso yozizwitsa ya kulankhula m’malirime, kulosera, kapena kuchiritsa.—2 Akorinto 12:12; Agalatiya 3:5; Ahebri 2:4.
Chochitika chimodzi chimene chinaloŵetsamo ulamuliro wa atumwi wa kukhululukira kapena kusakhululukira machimo chinakhudza Hananiya ndi Safira, amene ananyenga mzimu. Petro, amene anamva Yesu akulankhula zimene timaŵerenga pa Yohane 20:22, 23, anavumbula Hananiya ndi Safira. Petro choyamba analankhula kwa Hananiya, amene anamwalira pomwepo. Pamene Safira analoŵa pambuyo pake napitiriza ndi chinyengocho, Petro ananena chiweruzo chake. Petro sanakhululukire tchimo lake koma iye anati: “Taona, mapazi awo a iwo amene anaika mwamuna wako ali pakhomo, ndipo adzakunyamula kutuluka nawe.” Iyenso anamwalira pamenepo.—Machitidwe 5:1-11.
Pachochitika chimenechi mtumwi Petro anagwiritsira ntchito ulamuliro wapadera kusonyeza kusakhululukiradi tchimo, chidziŵitso chozizwitsa chakuti Mulungu sakanakhululukira tchimo la Hananiya ndi Safira. Atumwi akuonekanso kuti anali ndi chidziŵitso choposa chaumunthu pa milandu imene anali otsimikiza kuti machimo akhululukidwa pamaziko a nsembe ya Kristu. Motero atumwi osonkhezeredwa ndi mzimuwo ankatha kunena za kukhululukidwa kapena kugwiritsa kwa machimo.a
Zimenezi sizikutanthauza kuti akulu onse odzozedwa ndi mzimu kalelo anali ndi ulamuliro wa zozizwitsa umenewu. Tingadziŵe zimenezi kuchokera pa zimene mtumwi Paulo ananena za mwamuna amene anachotsedwa mumpingo wa Akorinto. Paulo sananene kuti, ‘Ndakhululukira machimo a mwamunayo’ kapena ngakhale kunena kuti, ‘Ndikudziŵa kuti mwamunayu wakhululukidwa kumwamba, motero mulandireninso.’ M’malo mwake, Paulo analimbikitsa mpingo wonse kukhululukira Mkristu wobwezeredwayu ndi kumsonyeza chikondi. Paulo anawonjezera kuti: “Amene mumkhululukira kanthu, inenso nditero naye.”—2 Akorinto 2:5-11.
Pamene munthuyo anabwezeretsedwa mumpingo, abale onse achikristu anali kumkhululukira mlingaliro la kusamsungira kanthu kukhosi pa zimene anali atachita. Komabe, choyamba, anafunikira kulapa ndi kubwezeretsedwa. Kodi zimenezo zinali kuchitika motani?
Pali machimo aakulu amene akulu a mpingo amafunikira kusamalira, monga kuba, kunama, kapena khalidwe loipa kwambiri. Iwo amayesa kuwongolera ndi kudzudzula ochimwa otero, kuwasonkhezera kuti alape. Koma ngati wina mosalapa amachita tchimo lalikulu, akulu ameneŵa amagwiritsira ntchito chitsogozo chaumulungu cha kuchotsa wochimwayo. (1 Akorinto 5:1-5, 11-13) Zimene Yesu ananena pa Yohane 20:23 sizimagwira ntchito pazochitika zotero. Akulu ameneŵa alibe mphatso za mzimu zozizwitsa, monga mphamvu za kuchiritsa odwala mwakuthupi kapena kuukitsa akufa; mphatso zimenezo zinakwaniritsa chifuno chake m’zaka za zana loyamba ndiyeno zinatha. (1 Akorinto 13:8-10) Ndiponso, akulu lerolino alibe ulamuliro wochokera kwa Mulungu wa kukhululukira machimo aakulu m’lingaliro la kutcha wochita tchimo lalikulu kukhala woyera pamaso pa Yehova. Kukhululukira kumeneku kuyenera kukhala kwa pamaziko a nsembe ya dipo, ndipo ali Yehova yekha amene angakhululukire pamaziko amenewo.—Salmo 32:5; Mateyu 6:9, 12; 1 Yohane 1:9.
Monga mmene zinalili pankhani ya mwamuna wa ku Korinto wakale, pamene wochita tchimo lalikulu akana kulapa, ayenera kuchotsedwa. Ngati pambuyo pake alapa ndi kusonyeza ntchito zoyenerana ndi kulapa, chikhululukiro chaumulungu nchotheka. (Machitidwe 26:20) Mumkhalidwe wotero, Malemba amapatsa akulu chifukwa chokhulupirira kuti Yehova wakhululukiradi wochimwayo. Ndiyeno, munthuyo atangobwezeretsedwa, akulu angamthandize mwauzimu kuti alimbe m’chikhulupiriro. Enanso mumpingo angakhululukire m’njira yofanana ndi imene Akristu a ku Korinto kalelo anakhululukira mwamuna wochotsedwa amene anabwezeretsedwa.
Posamalira nkhaniyi m’njira imeneyi, akulu samadzipangira miyezo yawoyawo ya chiweruzo. Iwo amagwiritsira ntchito mapulinsipulo a m’Baibulo ndi kutsatira mosamalitsa njira za m’Malemba zimene Yehova anapereka. Motero, kukhululukira kapena kusakhululukira kulikonse kwa akulu kuli mlingaliro la mawu a Yesu pa Mateyu 18:18 akuti: “Indetu ndinena ndi inu, Zilizonse mukazimanga padziko lapansi zidzakhala zomangidwa kumwamba: ndipo zilizonse mukazimasula padziko lapansi, zidzakhala zomasulidwa kumwamba.” Zochita zawo zidzangosonyeza mmene Yehova akuonera nkhaniyo molingana ndi zimene Baibulo limanena.
Motero, zimene Yesu ananena, monga momwe kwalembedwera pa Yohane 20:23, sizikutsutsana ndi Malemba ena onse, koma zikusonyeza kuti atumwi anapatsidwa ulamuliro wapadera ponena za kukhululukira machimo, mogwirizana ndi mbali yawo yapadera kuchiyambiyambi kwa mpingo wachikristu.
[Mawu a M’munsi]
a Ngakhale pamene Yesu anali asanamwalire ndi kupereka dipo, anali ndi ulamuliro wa kunena kuti machimo a munthu akhululukidwa—Mateyu 9:2-6; yerekezerani ndi “Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga” mu Nsanja ya Olonda ya June 1, 1995.