Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
◼ Kodi kalembedwe ka Yohane 21:15 mu New World Translation nkolondola popeza kamasiyana ndi matembenuzidwe ena?
New World Translation imati: “Kodi umandikonda ine koposa izi?” pamene kuli kwakuti matembenuzidwe ena, monga ngati Baibulo la Revised Union Nyanja Version limati: “Kodi undikonda ine koposa awa?” Ndi lalembedwe kati kamene kali kolondola?
Yesu wowukitsidwayo anali pa Nyanja ya Galileya pamene anadzutsa funso iri. Yankho la Petro kwa iye linali lakuti: ‘Inde, Ambuye, mudziŵa kuti ndikukondani inu.’ Ananena naye: ‘Dyetsa ana a nkhosa anga.’ “—Yohane 21:15.
Pronauni ya Chigriki, ya unyinji touʹton, ingatembenuzidwe monga “izi” kapena “awa.” Monga chotulukapo chake, ophunzira alingalira matanthauzo othekera atatu kaamba ka funso la Yesu:
1. Kodi umandikonda ine kuposa mmene umakondera ophunzira ena awa?
2. Kodi umandikonda ine kuposa mmene ophunzira awa amandikondera ine?
3. Kodi umandikonda ine kuposa zinthu izi, monga ngati nsomba?
Tiyeni tilingalire pa zitatu zimenezi ndi kuwona chimene chiri chothekera kwenikweni.
Nambala 1. Mowona mtima, Akristu oŵerengeka angalingalire Kristu kukhala akufunsa kuti, ‘Kodi umandikonda ine kuposa mmene umakondera ophunzira?’ Ndithudi tiyenera! Chingawoneke chachilendo mwapadera kufunsa Petro funso loterolo. Iye anali ali m’ngalawa ndi ophunzira ena asanu ndi mmodzi, koma pamene iye anazindikira Yesu pa gombe, Petro anasiya ophunzirawo ndi kusambira kupita ku gombe. Akumasonyeza kugwirizana kofananako, pamene Kristu anafunsa ngati ophunzirawo anafuna kuchoka ndi awo omwe anakhumudwitsidwa, Petro ananena kuti iye anali wogamulapo kukhala ndi Yesu.—Yohane 6:66-69; 21:7, 8.
Nambala 2. Bwanji ponena za kuthekera kwakuti Yesu anatanthauza kuti, ‘Petro, kodi uli ndi chikondi chokulira kaamba ka ine kuposa chimene ophunzira awa ena ali nacho?’ Ochitira ndemanga ambiri akonda kawonedwe kameneka, popeza Petro kumayambiriro anadzinenera kuti iye anali wokhulupirika mokulira kwa Yesu kuposa ena. (Mateyu 26:33-35) Komabe, kumvetsetsa Yohane 21:15 m’njira imeneyi kumafunikira kuti verebu losatchulidwa ligwiritsiridwe ntchito, monga ngati “Kodi umandikonda ine kuposa mmene awa [amachitira]?” Koma verebu lowonjezereka loterolo siliri m’funso la Yesu, ndipo limapereka mavuto a galamala. M’kuwonjezerapo, chikawoneka kukhala chachilendo kwa Yesu kufunsa Petro kuyerekeza kukulira kwa chikondi chake ku kukulira kwa chikondi chimene ena angakhale nacho. Kodi Yesu sanawongolere atumwiwo pamene anagwera mu mkangano?—Marko 9:33-37; 10:35-44; Luka 22:24-27.
Kenaka, kodi chingakhale kuti, Nambala 3 inali imene Yesu anali kufunsa, ‘Kodi umandikonda ine kukposa zinthu izi, monga ngati nsomba?’ Kuthekera kumeneku kukuyenerera njira mu imene funso lalembedwera m’Chigriki, popeza kuti Petro anali kufunsidwa kusankha pakati pa zinthu ziŵiri (pakati pa Yesu ndi “izi”). Funso loterolo likakhalanso loyenerera m’chiyang’aniro chakale cha Petro. Iye anali mmodzi wa ophunzira oyambirira kutsatira Yesu. (Yohane 1:35-42) Mwachidziŵikire, ngakhale ndi tero, Petro sanatsatire Yesu pa nthaŵi yomweyo kwa nthaŵi yonse. M’malomwake, iye anabwerera ku usodzi wake wa nsomba. Chotero, miyezi ingapo pambuyo pake Yesu anamuitana Petro kuchoka ku bizinesi imeneyo kukhala ‘msodzi wa anthu.’ (Mateyu 4:18-20; Luka 5:1-11) Mosasamala kanthu za chimenechi, pambuyo pa imfa ya Yesu, Petro anabwereranso ku ntchito imeneyi, akumawuza ena a ophunzirawo kuti: “Ndinka kukasodza.”—Yohane 21:2, 3.
Chotero chiridi chothekera kuti Yesu anali kubweretsa m’maganizo kwa Petro kufunika kwa kupanga chosankha chotsimikizirika. Nchiyani chimene iye akaika patsogolo koposa m’moyo—kukhala wotsatira wa Yesu kapena kulondola ntchito, monga mmene chalingaliridwa ndi nsomba zowunjikidwa patsogolo pawo? Kodi ndi malo ofunika otani amene nsomba, makoka, ngalawa, ndi kuyanjana ndi asodzi anzake zinali nawo mu mtima wa Petro? Kodi Petro mowonadi akasiya zinthu zosangalatsa zimenezi kuika patsogolo chikondi chake kaamba ka Kristu ndi kudyetsa “ana a nkhosa” a Yesu kotsatirapo?—Yohane 21:17.
Tingadzifunse ife eni funso lofananalo lokhudza ‘zinthu izi’ zomwe zingatikoke ife, monga ngati ntchito yathu kapena bizinesi yosangalatsa, kusangalala kwathu ndi maphunziro a kudziko, nyumba yathu, kapena mtundu wathu wokondeka wa zosangulutsa. Mowona mtima tingasinkhesinkhe: ‘Kodi ndimakonda Yesu kuposa chirichonse kapena zonse za zinthu izi?’ Yesu anasonyeza kuti ngati yakho lathu liri inde, tidzalisonyeza ilo mwa kudyetsa “ana a nkhosa.”
Chingawonedwe kuti kalembedwe ka New World Translation kali chotero m’chigwirizano ndi mawu ozungulira lemba ndi ziphunzitso zonse za Yesu.
[Mawu a Chithunzi patsamba 31]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.