MUTU 18
Ntchito ya Yesu Inayamba Kuwonjezeka Kuposa ya Yohane
MATEYU 4:12 MALIKO 6:17-20 LUKA 3:19, 20 YOHANE 3:22-4:3
OPHUNZIRA A YESU ANAYAMBA KUBATIZA ANTHU
YOHANE M’BATIZI ANAPONYEDWA M’NDENDE
M’chaka cha 30 C.E., mwambo wa Pasika utatha, Yesu ndi ophunzira ake anachoka ku Yerusalemu koma sanabwerere kwawo ku Galileya. Anapita ku Yudeya komwe anakabatiza anthu ambiri. Pamene zimenezi zinkachitika n’kuti Yohane M’batizi atagwira ntchito yobatiza anthu kwa pafupifupi chaka chimodzi. Pa nthawiyi Yohane anali akadali ndi ena mwa ophunzira ake, mwina pafupi ndi mtsinje wa Yorodano.
Yesu sankabatiza anthu koma ophunzira ake ndi amene ankagwira ntchitoyi ndipo iye ankangowatsogolera. Pa nthawi imeneyi, Yesu ndi Yohane ankaphunzitsa Ayuda amene alapa machimo awo chifukwa chozindikira kuti sanatsatire Chilamulo cha Mulungu chomwe chinali pangano pakati pa Yehova ndi Aisiraeli.—Machitidwe 19:4.
Koma ophunzira a Yohane anayamba kuchitira nsanje Yesu ndipo anauza Yohane kuti: “[Yesu] amene munali naye . . . akubatiza ndipo anthu onse akupita kwa iye.” (Yohane 3:26) Koma Yohane sanachitire Yesu nsanje. Iye ankasangalala kuti ntchito ya Yesu inkayenda bwino ndipo ankafunanso kuti ophunzira akewo azisangalala nawo. Iye anawakumbutsa kuti: “Inu nomwe ndinu mboni zanga pamawu amene ndinanena kuti, ‘Ine sindine Khristu, koma, ndinatumizidwa monga kalambulabwalo wake.’” Pofuna kuwathandiza ophunzira akewo kuti amvetse mfundo imeneyi anawauza fanizo. Iye anati: “Iye amene ali ndi mkwatibwi ndiye mkwati. Koma mnzake wa mkwati, akaimirira ndi kumvetsera zimene akunena, amakhala n’chimwemwe chochuluka chifukwa cha mawu a mkwatiyo. Choncho chimwemwe changa chasefukiradi.”—Yohane 3:28, 29.
Miyezi ingapo m’mbuyomu, Yohane, yemwe anali ngati mnzake wa mkwati, anasangalala pothandiza ophunzira ake kuti amudziwe Yesu. Ena mwa ophunzira a Yohane anayamba kuyenda ndi Yesu ndipo kenako anadzadzozedwa ndi mzimu woyera. Pa nthawiyi, Yohane ankafunanso kuti ophunzira amene anali nawo akhale otsatira a Yesu. Ndipotu ntchito yaikulu ya Yohane inali yokonza njira kuti Yesu adzagwire ntchito imene Yehova anamutuma padziko lapansi. N’chifukwa chake Yohane ananena kuti: “Ameneyo ayenera kumawonjezereka, koma ine ndiyenera kucheperachepera.”—Yohane 3:30.
Patapita nthawi, Yohane wina, amene anali atayamba kale kuyenda ndi Yesu, anafotokoza kumene Yesu anachokera komanso udindo waukulu umene anali nawo pothandiza anthu kuti adzapulumuke. Iye anati: “Wochokera kumwamba ali woposa ena onse. . . . Atate amakonda Mwana wake ndipo anapereka zinthu zonse m’manja mwake. Iye wokhulupirira mwa Mwanayo ali nawo moyo wosatha. Wosamvera Mwanayo sadzauona moyowu, koma mkwiyo wa Mulungu ukhalabe pa iye.” (Yohane 3:31, 35, 36) Mfundo imeneyi ndi yofunika kwambiri ndipo anthu ayenera kuidziwa.
Pasanapite nthawi yaitali, Yohane M’batizi atanena kuti ntchito yake iyamba kuchepa, anamangidwa ndi Mfumu Herode. Herode anali atakwatira Herodiya, yemwe anali mkazi wa m’bale wake, dzina lake Filipo. Herode anaponya Yohane m’ndende chifukwa chakuti anali atamudzudzula poyera chifukwa chokwatira mlamu wake. Yesu atamva kuti Yohane wamangidwa, iye ndi ophunzira ake anachoka ku Yudeya ‘n’kupita ku Galileya.’—Mateyu 4:12; Maliko 1:14.