NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MULANDIRA MPHATSO YAIKULU IMENE MULUNGU WAPEREKA?
Kodi Mungasonyeze Bwanji Kuti Mumayamikira Mphatso Imeneyi?
“Chikondi chimene Khristu ali nacho chimatikakamiza . . . Iye anaferanso onse kuti amene ali moyo asakhale moyo wongodzisangalatsa okha, koma akhale moyo wosangalatsa amene anawafera.”—2 Akorinto 5:14, 15.
MUNTHU akalandira mphatso yapamwamba kwambiri amafunika kuyamikira. Yesu anasonyeza mfundo imeneyi pambuyo pochiritsa anthu 10 odwala matenda oopsa a khate. Mmodzi yekha “anabwerera, akutamanda Mulungu mokweza mawu.” Ndiyeno Yesu anafunsa kuti: “Amene ayeretsedwa si anthu 10 kodi? Nanga ena 9 ali kuti?” (Luka 17:12-17) Apa tikuphunzira kuti tikhoza kuiwala mosavuta zinthu zabwino zimene ena atichitira.
Dipo ndi mphatso yaikulu komanso yabwino kuposa iliyonse imene tingalandire. Ndiye kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira zimene Mulungu watichitira?
Muyenera kudziwa bwino Mulungu. Sikuti dipo limachititsa kuti munthu aliyense apeze moyo wosatha popanda kuchita chilichonse. Yesu anapemphera kwa Mulungu kuti: “Moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.” (Yohane 17:3) Tiyerekeze kuti inuyo mwamva kuti munthu wina anapulumutsa moyo wanu muli mwana, kodi simungafufuze za munthuyo komanso chimene chinamuchititsa kuti akupulumutseni? Yehova Mulungu anapereka mphatso ya dipo kuti apulumutse moyo wathu ndipo amafuna kuti timudziwe komanso tikhale naye pa ubwenzi. N’chifukwa chake Baibulo limatilimbikitsa kuti: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.”—Yakobo 4:8.
Muzisonyeza kuti mumakhulupirira nsembeyo. Mawu a Mulungu amanena kuti: “Wokhulupirira mwa Mwanayo ali nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:36) Kodi munthu amene amakhulupirira Mwanayo amatani? Amachita zinthu zosonyeza kuti amakhulupirira dipo. (Yakobo 2:17) Kodi ndi zinthu ziti zimene tiyenera kuchita? Mphatso imakhala ya munthu ngati wailandira. Choncho ifenso tiyenera kuchita zinthu zosonyeza kuti talandira dipolo. Tingachite zimenezi pophunzira zimene Mulungu amafuna kuti tichite n’kumachitadi zomwezo.a Tiyenera kupempha Mulungu kuti atikhululukire zimene talakwitsa komanso kutithandiza kuti tisamadziimbebe mlandu. Tikamapemphera, tisamakayikire kuti Mulungu adzathandiza anthu amene amakhulupirira dipo kuti m’tsogolomu adzapeze mtendere komanso zinthu zizidzawayendera bwino.—Aheberi 11:1.
Muzipezeka pamwambo wokumbukira imfa ya Yesu. Yesu anayambitsa mwambo wokumbukira imfa yake umene tiyenera kuchita chaka ndi chaka. Ponena za mwambo umenewu, iye anati: “Muzichita zimenezi pondikumbukira.” (Luka 22:19) A Mboni za Yehova adzachita mwambo wokumbukira imfa ya Yesu Lachiwiri pa 11 April 2017, dzuwa litalowa. Pulogalamu yonse ndi ya ola limodzi ndipo padzakambidwa nkhani yofotokoza mmene imfa ya Yesu ingatithandizire panopa komanso m’tsogolo. Chaka chatha, anthu pafupifupi 20 miliyoni padziko lonse anapezeka pa mwambowu. Tikukupemphani kuti mudzapezeke pa mwambowu posonyeza kuti mumayamikira mphatso yaikulu imene Mulungu anatipatsa.
a Kuphunzira Baibulo ndi njira yabwino yotithandiza kudziwa Mulungu komanso kukhala naye pa ubwenzi. Kuti mudziwe mmene mungaphunzirire Baibulo, funsani wa Mboni za Yehova kapena pitani pawebusaiti ya www.jw.org.