Tsatirani Kuunika kwa Dziko
“Iye wonditsata ine . . . adzakhala nako kuunika kwa moyo.”—YOHANE 8:12.
1. Kodi kuunika nkofunika motani?
KODI tikanachitanji ngati panalibe kuunika? Tayerekezerani kudzuka tsiku lirilonse la maola 24 kwa chaka chonse muli mumdima. Tayerekezerani dziko lopanda mawonekedwe a chinthu, popeza kuti popanda kuunika palibe mawonekedwe a chinthu. Ndithudi, ngati panalibe kuunika, ifenso sitikanakhalako! Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti, mum’chitidwe wotchedwa photosynthesis, zomera zobiriŵira zimagwiritsira ntchito kuunika kupangira chakudya chimene timadya—dzinthu, ndiwo, ndi zipatso. Ndithudi, nthaŵi zina timadya nyama yazinyama. Koma zinyamazo zinadya zomera kapena zinyama zina zimene zinadya zomera. Chotero, miyoyo yathu ya kuthupi njodalira kotheratu pa kuunika.
2. Kodi pali magwero akuunika amphamvu otani, ndipo kodi zimenezi zikutiuzanji ponena za Yehova?
2 Kuunika kwathu kumachokera kudzuŵa, limene lili nyenyezi. Ngakhale kuti dzuŵa lathu limatulutsa mlingo waukulu wa kuunika, lili chabe nyenyezi yaukulu pang’ono. Zambiri zili zokulirapo. Ndipo khamu la nyenyezi limene tikukhalamo lotchedwa Mlalang’amba, lili ndi nyenyezi zoposa mamiliyoni zikwi zana limodzi. Kuwonjezerapo, pali makamu a nyenyezi mamiliyoni zikwi osaŵerengeka m’chilengedwe chonse. Ndidongosolo lalikulu chotani nanga la nyenyezi! Ndiukulu wotani nanga wa kuunika kotuluka m’zimenezi! Yehova ali magwero amphamvu chotani nanga a kuunika amene analenga zonsezi! Yesaya 40:26 amati: “Kwezani maso anu kumwamba, muwone amene analenga izo, amene atulutsa khamu lawo ndi kuziŵerenga; azitcha zonse maina awo, ndi mphamvu zake zazikulu, ndi popeza ali wolimba mphamvu, palibe imodzi isoŵeka.”
Mtundu Wina wa Kuunika
3. Kodi kuunika kwauzimu kochokera kwa Yehova kuli kofunika motani?
3 Yehova alinso Magwero a kuunika kwa mtundu wina, kumene kumatikhozetsa kukhala ndi kuwona kwauzimu, kuunikiridwa kwauzimu. Dikishonale ina imamasulira mawu akuti “kuunikira” motere: “Kupereka chidziŵitso: kulangiza; kupereka chidziŵitso chauzimu.” Imamasulira “kuunikiridwa” kukhala: “kumasulidwa ku umbuli ndi kupulukira.” Kuunikiridwa kwauzimu kochokera kwa Yehova kumaperekedwa kupyolera mwa chidziŵitso cholongosoka cha Mawu ake, Baibulo. Ndicho chimatikhozetsa kudziŵa amene Mulungu ali ndi chimene zifuno zake zili. “Pakuti Mulungu amene anati, Kuunika kudzaŵala kutuluka mumdima, ndiye amene anaŵala m’mitima yathu kutipatsa chiŵalitsiro cha chidziŵitso cha ulemerero wa Mulungu pankhope pa Yesu Kristu.” (2 Akorinto 4:6) Chotero, chowonadi cha Mawu a Mulungu chimatimasula ku umbuli ndi kupulukira. Yesu anati: “Mudzazindikira chowonadi, ndipo chowonadi chidzakumasulani.”—Yohane 8:32.
4, 5. Kodi chidziŵitso chochokera kwa Yehova chimakhala motani kuunika m’miyoyo yathu?
4 Yehova, Magwero a kuunikira kwauzimu kowona, ali “wakudziŵa mwangwiro.” (Yobu 37:16) Ndiponso, Salmo 119:105 limati ponena za Mulungu: “Mawu anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga.” Chotero iye angathe kuunikira mwauzimu osati phazi limodzi lokha la miyoyo yathu patsogolo pathu komanso njira ya mtsogolo. Popanda kuunikako, moyo ukafanana ndi kuyendetsa galimoto lopanda nyale zakutsogolo pa msewu wokhotakhota wa m’mapiri kapena kwina kulikonse pa usiku wamdima. Kuunika kwauzimu kochokera kwa Mulungu kungafaniziridwe ndi kuunika kwa nyale zakutsogolo za galimoto. Kuunikako kumawalitsira njira kotero kuti tikhoze kuwona bwino kumene tikupita.
5 Ulosi wa pa Yesaya 2:2-5 umasonyeza kuti m’nthaŵi yathu Mulungu akusonkhanitsa m’mitundu yonse anthu ofuna kuunika kwauzimu kuti aphunzire ndi kuchita kulambira kowona. Vesi 3 limati: “Adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m’mayendedwe ake.” Vesi 5 limaitanira ofunafuna chowonadi kuti: “Tiyeni, tiyende m’kuŵala kwa Yehova.”
6. Kodi kuunika kochokera kwa Yehova potsirizira pake kudzatitsogolera kuti?
6 Chotero, Yehova ali magwero a mitundu iŵiri ya kuunika yofunika ku moyo: kwakutupi ndi kwauzimu. Kuunika kwakuthupi kumathandiza mathupi athu kukhala amoyo tsopano, mwinamwake kwa zaka 70 kapena 80 kapena kuposapo. Koma kuunika kwauzimu kumatitsogolera ku moyo wamuyaya pa dziko lapansi la paradaiso. Kuli monga momwe Yesu adanenera m’pemphero kwa Mulungu kuti: “Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu wowona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.”—Yohane 17:3.
Dziko mu Mdima Wauzimu
7. Kodi nchifukwa ninji timafunikira kuunikiridwa mwauzimu tsopano kuposa ndi kale lonse?
7 Lerolino tifunikira kuunika kwauzimu kuposa ndi kale lonse. Maulosi monga Mateyu chaputala 24 ndi 2 Timoteo chaputala 3 amasonyeza kuti tili pafupi ndi mapeto a dongosolo lino lazinthu. Ameneŵa ndi maulosi ena adaneneratu zinthu zochititsa mantha zimene zachitika m’nthaŵi yathu, kutidziŵitsa kuti tili mu “masiku otsiriza.” Mogwirizana ndi maulosiwo, zaka za zana lino zawona masoka osaneneka. Upandu ndi chiwawa zawonjezereka kowopsa. Nkhondo zapha anthu oposa mamiliyoni zana. Nthenda, zonga AIDS yowopsayo, zakantha mamiliyoni, ndipo pafupifupi 160,000 afa kale ndi AIDS mu United States mokha. Moyo wabanja wanyonyotsoka ndipo makhalidwe abwino m’zakugonana amawonedwa kukhala achikale.
8. Kodi ndimkhalidwe uti umene ukuyang’anizana ndi anthu tsopano, ndipo chifukwa ninji?
8 Mlembi wamkulu wakale wa Mitundu Yogwirizana Javier Pérez de Cuéllar anati: “Mkhalidwe wapadziko ukupereka umboni wokwanira wakuti umphaŵi [ukulepheretsa] kugwirizana kwa zitaganya za anthu.” Ananena kuti “anthu oposa [mamiliyoni chikwi] chimodzi tsopano akukhala muumphaŵi wotheratu” ndi kuti “zimenezi zawonjezera nkhondo za chiwawa.” “Mavuto aakulu” ameneŵa, iye anatero, “amalepheretsa njira zothetsera mavuto zimene maboma angagwiritsire ntchito.” Ndipo mtsogoleri wa gulu lina lotchuka anatsimikiza kuti: “Vuto lalikulu koposa limene likuyang’anizana ndi anthu nlakuti anthuwo akhala osalamulirika.” Ngowona chotani nanga mawu a Salmo 146:3: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye.”
9. Kodi ndani kwenikweni amene akuchititsa mdima umene waphimba mtundu wa anthu, ndipo ndani angatichotsere chisonkhezero chimenechi?
9 Mkhalidwe lerolino uli monga momwe Yesaya 60:2 adanenera kuti: “Pakuti tawona, mdima udzaphimba dziko lapansi, ndi mdima wa bii mitundu ya anthu.” Mdima umenewo wophimba anthu ochuluka a padziko lapansi wachititsidwa ndi kusalandira kwawo kuunika kwauzimu kochokera kwa Yehova. Ndipo Satana Mdyerekezi ndi ziŵanda zake, adani aakulu a Mulungu wa kuunika, ndiwo ochititsa mdima wauzimu. Ndiwo “maulamuliro . . . a dziko lapansi a mdima uno.” (Aefeso 6:12) Monga momwe 2 Akorinto 4:4 akunenera, Mdyerekezi ali “mulungu wa nthaŵi ino ya pansi pano,” amene “[wachititsa] khungu maganizo awo a osakhulupirira, kuti chiŵalitsiro cha uthenga wabwino wa ulemerero wa Kristu, amene ali chithunzithunzi cha Mulungu, chisawaŵalire.” Palibe ulamuliro wa munthu umene ungachotse chisonkhezero cha Satana pa dziko lapansi. Mulungu yekha angathe.
“Kuŵala Kwakukulu”
10. Kodi Yesaya ananenera motani kuti m’tsiku lathu kuunika kukaŵalira mtundu wa anthu?
10 Komabe, ngakhale kuti mdima waukulu ukuphimba unyinji wa anthu, nawonso Mawu a Mulungu pa Yesaya 60:2, 3 analosera kuti: “Yehova adzakutulukira, ndi ulemerero wake udzawoneka pa iwe. Ndipo amitundu adzafika kwa kuunika kwako, ndi mafumu kwa kuyera kwa kutuluka kwako.” Izi zili zogwirizana ndi ulosi wa Yesaya chaputala 2, umene unalonjeza kuti kulambiridwa kowona kounikiridwa kwa Yehova, kukakhazikika m’masiku omaliza ano, ndipo, pa mavesi 2 ndi 3 pamanena kuti, “mitundu yonse idzasonkhana kumeneko. Ndipo anthu ambiri adzanka, nati, Tiyeni tikwere kunka ku phiri la Yehova,” ndiko kuti, kumka ku kulambira kwake kowona kokwezeka. Chotero ngakhale kuti dziko likulamuliridwa ndi Satana, kuunika kochokera kwa Mulungu kukuŵalitsidwa ndipo kukuwonjola anthu ochuluka ku mdima.
11. Kodi ndani amene akakhala woposa onse m’kuŵalitsira kuunika kwa Yehova, ndipo Simeoni anamsonyeza motani?
11 Ulosi wa pa Yesaya 9:2 unaneneratu kuti Mulungu akatumiza munthu wina m’dziko kudzaŵalitsira kuunika kwake. Uwo umati: “Anthu amene anayenda mumdima, awona kuŵala kwakukulu; iwo amene anakhala m’dziko la mthunzi wa imfa, kuŵala kwatulukira kwa iwo.” “Kuŵala kwakukulu” kumeneku ndiko Wolankhulira wa Yehova, Yesu Kristu. Yesu anati: “Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi; iye wonditsata ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala nako kuunika kwa moyo.” (Yohane 8:12) Ena anadziŵa zimenezi ngakhale pamene Yesu anali mwana wang’ono. Luka 2:25 amanena kuti mwamuna wina wotchedwa Simeoni anali “wolungama mtima ndi wopemphera” ndi kuti ‘mzimu woyera unali pa iye.’ Pamene Simeoni anawona khandalo Yesu, iye anati m’pemphero kwa Mulungu: “Maso anga adawona chipulumutso chanu, chimene munakonza pamaso pa anthu onse, kuunika kukhale chivumbulutso cha kwa anthu a mitundu.”—Luka 2:30-32.
12. Kodi ndiliti ndipo ndimotani mmene Yesu anayambira kuchotsa chophimba chochititsa mdima anthu?
12 Yesu atangobatizidwa, anayamba kuchotsa pa mtundu wa anthu chophimba cha mdima. Mateyu 4:12-16 amatiuza kuti zimenezi zinakwaniritsa Yesaya 9:1, 2, amene analankhula za “kuŵala kwakukulu” kumene kukayamba kuŵalira anthu oyenda mumdima wauzimu. Mateyu 4:17 amati: “Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kulalikira, ndi kunena, Tembenukani mitima, pakuti ufumu wa kumwamba wayandikira.” Mwakulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu, Yesu anapereka chidziŵitso kwa anthu cha zifuno za Mulungu. Iye ‘anawonetsera poyera moyo ndi chosavunda mwa uthenga wabwino.’—2 Timoteo 1:10.
13. Kodi ndimotani mmene Yesu anadzifotokozera, ndipo kodi nchifukwa ninji anatero motsimikizirika?
13 Yesu mokhulupirika anaŵalitsira kuunika kwa Mulungu. Iye anati: “Ndadza ine kuunika ku dziko lapansi, kuti yense wokhulupirira ine asakhale mumdima. . . . Sindinalankhula mwa ine ndekha; koma Atate wondituma ine, yemweyu anandipatsa ine lamulo, limene ndikanene, ndi limene ndikalankhule. Ndipo, ndidziŵa kuti lamulo lake lili moyo wosatha.”—Yohane 12:44-50.
“Mwa Iye Munali Moyo”
14. Kodi Yesu akusonyezedwa motani pa Yohane 1:1, 2?
14 Inde, Yehova anatuma Mwana wake kudziko lapansi kudzakhala kuunika kosonyeza njira ya ku moyo wosatha. Tamverani mmene Yohane 1:1-16 akunenera zimenezi. Mavesi 1 ndi 2 (NW) amati: “Pachiyambi panali Mawu, ndipo Mawu anali ndi Mulungu, ndipo Mawu anali mulungu. Ameneyu anali pachiyambi ndi Mulungu.” Panopa Yohane akutchula Yesu asanakhale munthu dzina la ulemu lakuti “Mawu.” Limeneli likusonyeza ntchito imene anachita monga Wolankhulira wa Yehova Mulungu. Ndipo pamene Yohane akunena kuti “pachiyambi panali Mawu,” akutanthauza kuti Mawuyo anali chiyambi cha ntchito ya kulenga ya Yehova, “woyamba wa chilengo cha Mulungu.” (Chivumbulutso 3:14) Malo ake opambana koposa zolengedwa zina zonse za Mulungu amapereka chifukwa choyenera chakuti atchedwe “mulungu,” wamphamvuyo. Yesaya 9:6 amamutcha “Mulungu wamphamvu,” ngakhale kuti sali Mulungu Wamphamvuyonse.
15. Kodi nchidziŵitso chowonjezereka chotani chimene Yohane 1:3-5 amatipatsa ponena za Yesu?
15 Yohane 1:3 amati: “Zonse zinalengedwa ndi iye; ndipo kopanda iye sikunalengedwa kanthu kalikonse kolengedwa.” Akolose 1:16 amanena kuti “pakuti mwa iye, zinalengedwa zonse za m’mwamba, ndi za padziko.” Yohane 1:4 amati “mwa iye munali moyo; ndi moyowu unali kuunika kwa anthu.” Chotero mwa Mawuyo, mitundu yonse ya moyo inalengedwa; ndiponso mwa Mwana wake, Mulungu akutheketsa anthu ochimwa ndi omafa, kupeza moyo wosatha. Ndithudi Yesu ndiye wamphamvuyo amene Yesaya 9:2 amamutcha “kuŵala kwakukulu.” Ndipo Yohane 1:5 (NW) amati: “Kuunika kukuŵala mumdima, koma mdimawu sunakugonjetse.” Kuunika kumatanthauza chowonadi ndi chilungamo, mosiyana ndi mdima, umene umatanthauza mphulupulu ndi chisalungamo. Chotero Yohane akusonyeza kuti mdima sudzalaka kuunika.
16. Kodi ndimotani mmene Yohane Mbatizi anasonyera ukulu wa ntchito ya Yesu?
16 Tsopano Yohane akupereka zigomeko pa mavesi 6 mpaka 9: “Kunali munthu, wotumidwa ndi Mulungu: dzina lake ndiye Yohane [Mbatizi]. Iyeyu anadza mwa umboni kudzachita umboni za kuunikaku, kuti onse akakhulupirire mwa iye. Iye [Yohane] sindiye kuunikaku, koma anatumidwa kukachita umboni wa kuunikaku [Yesu]. Uku ndiko kuunika kwenikweni, kumene kuunikira anthu onse akuloŵa m’dziko lapansi.” Yohane anasonya kwa Mesiya wakudzayo napereka otsatira ake kwa Iye. M’kupita kwanthaŵi, anthu a mitundu yonse anapatsidwa mpata wakulandira kuunika. Chotero Yesu sanadzere kudzapindulitsa Ayuda okha, koma kupindulitsa mtundu wonse wa anthu—olemera kapena osauka, mosasamala kanthu za fuko.
17. Kodi Yohane 1:10, 11 amatiuzanji za mkhalidwe wauzimu wa Ayuda m’tsiku la Yesu?
17 Mavesi 10 ndi 11 amapitiriza kuti: “Anali m’dziko lapansi, ndi dziko linalengedwa ndi iye, koma dziko silinamzindikira iye. Anadza kwa zake za iye yekha, ndipo ake a mwini yekha sanamlandire iye.” Yesu, m’kukhalapo kwake asanakhale munthu, anali mwa amene dziko la mtundu wa anthu linalengedwa. Komabe, pamene anali pa dziko lapansi, anakanidwa ndi unyinji wa anthu a mtundu wake, Ayuda. Iwo sanafune kuti kuipa kwawo ndi chinyengo zivumbulidwe. Anakonda mdima mmalo mwa kuunika.
18. Kodi ndimotani mmene Yohane 1:12, 13 amasonyezera kuti ena akafikira kukhala ana a Mulungu ndi choloŵa chapadera?
18 Yohane akuti pa mavesi 12 ndi 13: “Koma onse amene anamlandira iye, kwa iwo anapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lake; amene sanabadwa ndi mwazi, kapena ndi chifuniro cha thupi, kapena ndi chifuniro cha munthu, koma cha Mulungu.” Mavesi ameneŵa amasonyeza kuti choyamba, otsatira a Yesu sanali ana a Mulungu. Kristu asanadze padziko lapansi, anthu analibe mwaŵi wakukhala ana ake otero kapena wa chiyembekezo cha kumwamba. Koma mwa mtengo wansembe ya dipo ya Kristu imene iwo anakhulupirira, anthu ena analandiridwa kukhala ana ndipo anakhoza kukhala ndi chiyembekezo cha moyo monga mafumu limodzi ndi Kristu mu Ufumu wa kumwamba wa Mulungu.
19. Kodi nchifukwa ninji Yesu ali m’malo abwino koposa kuŵalitsira kuunika kwa Mulungu, monga momwe kwasonyezedwera pa Yohane 1:14?
19 Vesi 14 limafotokoza kuti: “Ndipo Mawu anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinawona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate.” Ali padziko lapansi, Yesu anaŵalitsira ulemerero wa Mulungu umene Mwana wachisamba wa Mulungu yekha akanasonyeza. Chifukwa chake, mwanjira yapadera, iye anali woyeneretsedwa bwino koposa kuvumbulira anthu Mulungu ndi zifuno Zake.
20. Malinga ncholembedwa cha Yohane 1:15, kodi Yohane Mbatizi akutiuzanji za Yesu?
20 Kenako, mtumwi Yohane akulemba mu vesi 15 kuti: “Yohane [Mbatizi] achita umboni za iye, nafuula nati, Uyu ndiye amene ndinanena za iye, Wakudzayo pambuyo panga analipo ndisanabadwe ine.” Yohane Mbatizi ndiye anayamba kubadwa ndipo panapita pafupifupi miyezi isanu ndi umodzi Yesu asanabadwe monga munthu. Koma Yesu anachita ntchito zochuluka kwambiri kuposa Yohane, kotero kuti anaposa Yohane m’njira iriyonse. Ndipo Yohane anavomereza kuti Yesu anakhalako iye asanatero, popeza kuti Yesu analiko asanakhale munthu.
Mphatso Zochokera kwa Yehova
21. Kodi Yohane 1:16 amaneneranji kuti talandira “chisomo chosinthana ndi chisomo”?
21 Yohane 1:16 amagomeka kuti: “Chifukwa mwakudzala kwake tinalandira ife tonse, chisomo chosinthana ndi chisomo.” Ngakhale kuti anthu amabadwira muuchimo chifukwa cha kuulandira mwacholoŵa kuchokera kwa Adamu, Yehova walinganiza kuwononga dongosolo loipa lino, kupulumutsa mamiliyoni kuloŵa m’dziko latsopano, kuukitsa akufa, ndi kuchotsa uchimo ndi imfa, akumatheketsa moyo wamuyaya m’paradaiso wa pa dziko lapansi. Madalitso onsewa ngosawayenerera, osakhoza kupezedwa ndi anthu ochimwa pa iwo okha. Ali mphatso zochokera kwa Yehova kupyolera mwa Kristu.
22. (a) Kodi mphatso yaikulu koposa ya Mulungu imatheketsa chiyani? (b) Kodi nchiitano chotani chimene chaperekedwa kwa ife m’buku lomalizira la Baibulo?
22 Kodi mphatso yaikulu koposa imene imatheketsa zonsezi nchiyani? “Mulungu anakonda dziko lapansi [mtundu wa anthu] kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Chotero, chidziŵitso cholongosoka cha Mulungu ndi Mwana wake, “Mkulu wa moyo,” chiri chofunika kwa awo amene afuna kuunika kwauzimu ndi moyo wosatha. (Machitidwe 3:15) Ndicho chifukwa chake buku lomalizira la Baibulo limapereka chiitano chotsatirachi kwa onse amene amakonda chowonadi ndi amene amafuna moyo: “Idzani. Ndipo wakumva anene, Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.”—Chivumbulutso 22:17.
23. Kodi anthu onga nkhosa adzachitanji pamene afika ku kuunika?
23 Anthu odzichepetsa onga nkhosa, sadzangobwera ku kuunika kwa dziko koma adzatsatira kuunikako: “Nkhosa zimtsata iye; chifukwa zidziŵa [mamvekedwe a chowonadi mu] mawu ake.” (Yohane 10:4) Ndithudi, iwo amakondwera ‘kulondola mapazi ake mosamalitsa’ chifukwa amadziŵa kuti kuchita tero kudzatanthauza moyo kwa iwo.—1 Petro 2:21.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi ndimitundu iŵiri ya kuunika yotani imene imachokera kwa Yehova?
◻ Kodi nchifukwa ninji kuunikira kwauzimu kuli kofunika kwambiri lerolino?
◻ Kodi Yesu anali “kuŵala kwakukulu” motani?
◻ Kodi Yohane chaputala 1 amatiuzanji za Yesu?
◻ Kodi ndimphatso zotani zimene zimadza kwa otsatira kuunika kwa dziko?
[Chithunzi patsamba 10]
Simeoni anatcha Yesu ‘kuunika kochotsera amitundu chophimba’