Mamiliyoni Amene Ngakufa Tsopano Adzakhalanso ndi Moyo
MAMILIYONI amene ngakufa tsopano adzakhalanso ndi moyo—ndi chiyembekezo chodzutsa mtima chotani nanga! Koma kodi ndi zowona? Kodi nchiyani chimene chingakukhutiritseni? Kuti mukhulupirire lonjezo, muyenera kukhala wotsimikiza kuti amene akupanga lonjezoyo akufunitsitsa ndipo ali wokhoza kulikwaniritsa. Pamenepa, kodi ndani amene akulonjeza kuti mamiliyoni amene ngakufa tsopano adzakhalanso ndi moyo?
Mu ngululu ya 31 C.E., Yesu Kristu molimbika mtima ananena kuti anapatsidwa mphamvu ndi Yehova Mulungu youkitsa akufa. Yesu analonjeza kuti: “Pakuti monga Atate aukitsa akufa, nawapatsa moyo, momwemonso Mwana apatsa moyo iwo amene Iye afuna. Musazizwe ndi ichi, kuti ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda adzamva mawu ake [a Yesu], nadzatulukira.” (Yohane 5:21, 28, 29) Inde, Yesu Kristu analonjeza kuti mamiliyoni amene ngakufa tsopano adzakhalanso ndi moyo pa dziko lapansili ndi kukhala ndi chiyembekezo cha kukhalapo kosatha. (Yohane 3:16; 17:3; yerekezerani Salmo 37:29 ndi Mateyu 5:5.)a Popeza kuti Yesu anapanga lonjezo limeneli, nkwanzeru kulingalira kuti iye ali wofunitsitsa kulikwaniritsa. Koma kodi ali wokhoza kutero?
Mogwirizana ndi mbiri ya Baibulo, kufikira nthaŵi imene Yesu anapanga lonjezo limenelo, iye anali asanaukitsepo aliyense. Koma zochepera pa zaka ziŵiri pambuyo pake, iye anasonyeza mwamphamvu kuti ponse paŵiri ngofunitsitsa ndipo ali wokhoza kuukitsa.
‘Lazaro, Tuluka!’
Chidali chochitika chogwira maganizo. Lazaro adadwala mwakayakaya. Alongo ake aŵiri, Mariya ndi Marita, anatumiza uthenga kwa Yesu, amene adali kutsidya lina la Mtsinje wa Yordano: “Ambuye, onani, amene mumkonda adwala.” (Yohane 11:3) Inde, Yesu adakondadi banja limeneli kwabasi. Iye adali mlendo wawo kunyumba kwawo mu Betaniya, mwinamwake mobwerezabwereza. (Luka 10:38-42; yerekezerani ndi Luka 9:58.) Koma tsopano bwenzi lapamtima la Yesu linali kudwala kwambiri.
Komabe, kodi Mariya ndi Marita anayembekera kuti Yesu achitenji? Iwo sanampemphe kubwera ku Betaniya. Koma adadziŵa kuti Yesu anamkonda Lazaro. Kodi Yesu sakafuna kukawona bwenzi lake lodwalalo? Mosakaikira anayembekezera kuti Yesu akamchiritsa mozizwitsa. Ndiiko komwe, panthaŵiyi mu uminisitala wake, Yesu anali atachita zozizwitsa zambiri zochiritsa, ndiponso mtunda sunali choletsa kwa iye. (Yerekezerani ndi Mateyu 8:5-13.) Kodi iye akachita zochepa kwa bwenzi lapamtima loterolo? Modabwitsa, m’malo mopita mwamsanga ku Betaniya, Yesu anakhala kumene anali kwa masiku aŵiri otsatira.—Yohane 11:5, 6.
Lazaro anamwalira nthaŵi ina uthengawo utatumizidwa, mwinamwake pa nthaŵi imene Yesu ankalandira uthengawo. (Yerekezerani ndi Yohane 11:3, 6, 17.) Koma sipanafunikire uthenga wina wowonjezereka. Yesu anadziŵa pamene Lazaro anamwalira, ndipo anafuna kuchitapo kanthu. Akumalankhula za imfa ya Lazaro, anauza ophunzira ake kuti: “Lazaro bwenzi lathu ali m’tulo; koma ndimuka kukamuukitsa iye tulo take.” (Yohane 11:11) Papitapo Yesu anali ataukitsa anthu aŵiri kwa akufa, m’chochitika chirichonse mwamsanga pambuyo pa kufa kwa munthuyo.b Komabe, pa nthaŵi ino zikakhala zosiyana. Pamene pomalizira pake Yesu akufika ku Betaniya, bwenzi lake lakhala lomwalira kwa masiku anayi. (Yohane 11:17, 39) Kodi Yesu angaukitse winawake amene wakhala womwalira kwa nthaŵi yaitali motero ndipo amene thupi lake layamba kuwola?
Pamene anamva kuti Yesu akubwera, Marita, mkazi wokangalika, anathamanga kukamchingamira. (Yerekezerani ndi Luka 10:38-42.) Mwamsanga atakumana ndi Yesu, mtima wake unamsonkhezera kunena kuti: “Ambuye, mukadakhala kuno mlongo wanga sakadafa.” Komabe, anasonyeza chikhulupiriro chake: “Ndidziŵa kuti zinthu ziri zonse mukapempha Mulungu, adzakupatsani Mulungu.” Pokhudzidwa ndi chisoni chake, Yesu anamtsimikizira kuti: “Mlongo wako adzauka.” Pamene mkaziyo anasonyeza chikhulupiriro chake m’chiukiriro chakutsogolo, Yesu momvekera anamuuza kuti: “Ine ndine kuuka ndi moyo: wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo.”—Yohane 11:20-25.
Pamene anafika kumandako, Yesu analamula kuti mwala wotseka manda uchotsedwe. Poyamba Marita anatsutsa nati: “Ambuye, adayamba kununkha: pakuti wagona masiku anayi.” Koma Yesu anamtsimikizira nati: “Kodi sindinati kwa iwe, kuti, ngati ukhulupira, udzawona ulemerero wa Mulungu?” Kenaka, pambuyo popemphera mofuula, analamula nati: “Lazaro, tuluka.” Lazaro anatuluka ndi lamulo la Yesu, ngakhale kuti anali womwalira kwa masiku anayi!—Yohane 11:38-44.
Kodi Zinachitikadi?
Mbiri ya kuuka kwa Lazaro yalembedwa mu Uthenga Wabwino wa Yohane monga nsonga yowona ya m’mbiri. Tsatanetsatane wake ngwowonekeratu kotero kuti sangakhale nthano wamba. Kukaikira mbiri yake kukakhala kukaikira zozizwitsa zonse za Baibulo, kuphatikizapo chiukiriro cha Yesu Kristu iyemwini.c Ndipo kukana chiukiriro cha Yesu ndiko kukana chikhulupiriro chonse Chachikristu.—1 Akorinto 15:13-15.
Kwenikwenidi, ngati mwavomereza kukhalapo kwa Mulungu, simuyenera kukhala ndi vuto kusonyeza chikhulupiriro m’chiukiriro. Kuti tichitire chitsanzo: Munthu angajambule pa tepi ya video pangano logawa chuma chamasiye ndi chipangano, ndipo pambuyo pakumwalira kwake achibale ake ndi mabwenzi angamuwone ndi kumumvadi, pamene akulongosola mmene katundu wake ayenera kusamaliridwa. Zaka zana limodzi zapitazo, chinthu choterocho chinali chosalingalirika. Ndipo kwa anthu ena amene akukhala kumalo akutali a dziko, “chozizwitsa” cha kujambula pa video nchosamveka. Ngati malamulo abwino asayansi okhazikitsidwa ndi Mlengi angagwiritsiridwe ntchito ndi anthu kupanga chinthu chowoneka ndi chomveka choterocho, kodi Mlengiyo sayenera kukhala wokhoza kupanga zoposa pamenepo? Pamenepa, kodi sizanzeru kuti Iye amene analenga moyo ndiwokhoza kuukitsa munthu mwa kupanganso umunthu wake m’thupi lopangidwa chatsopano?
Chozizwitsa cha kubwezeretsedwa ku moyo cha Lazaro chinathandizira kuwonjezera chikhulupiriro mwa Yesu ndi chiukiriro. (Yohane 11:41, 42; 12:9-11, 17-19) M’njira yokhudza maganizo, chimavumbulanso kufunitsitsa ndi chikhumbo cha Yehova ndi Mwana wake cha kuukitsa.
‘Mulungu Adzakhumba’
Chivomerezo cha Yesu ku imfa ya Lazaro chikuvumbula mbali yachifundo kwambiri ya Mwana wa Mulungu. Malingaliro ake ozama pa chochitikacho akusonyeza mowonekera chikhumbo chake chakuya cha kuukitsa akufa. Timaŵerenga kuti: “Mariya, pofika pamene panali Yesu, mmene anamuona Iye, anagwa pa mapazi ake, nanena ndi Iye, Ambuye, mukadakhala kuno Inu, mlongo wanga sakadamwalira. Pamenepo Yesu, pakumuona iye alikulira, ndi Ayuda akumperekeza iye alikulira, anadzuma mumzimu, navutika mwini, nati, Mwamuika iye kuti? Ananena ndi Iye, Ambuye, tiyeni, mukaone. Yesu analira. Chifukwa chake Ayuda ananena, Taonani, anamkondadi!”—Yohane 11:32-36.
Chisoni chochokera mumtima cha Yesu chikusonyezedwa pano ndi mawu atatu: “anadzuma,” “navutika,” ndi “analira.” Mawu achinenero choyambirira ogwiritsiridwa ntchito ndi mtumwi Yohane polemba chochitika chokhudza mtimacho amasonyeza ukulu umene Yesu anavutitsidwa ndi maganizo.
Liwu Lachigiriki lolembedwa “anadzuma” n’lochokera ku mneni (em·bri·maʹo·mai) amene amasonyeza kusonkhezeredwa mopweteka, kapena mozama. William Barclay wochitira ndemanga Baibulo ananena kuti: “M’Chigiriki chanthaŵi zonse kugwiritsira ntchito kwanthaŵi zonse kwa [em·bri·maʹo·mai] kuli kulira kwa kavalo. Panopa lingangotanthauza kuti malingaliro ozama oterowo anakhudza Yesu kotero kuti kudzuma kosalamulirika kunatuluka mumtima Mwake.”
Mawu otembenuzidwa “navutika” amachokera ku liwu Lachigiriki lakuti (ta·rasʹso) limene limatanthauza kusokonezeka. Mogwirizana ndi The New Thayer’s Greek-English Lexicon of the New Testament, limatanthauza “kupangitsa wina kusokonezeka kwa mkati, . . . kuyambukira ndi kupweteka kwakukulu kapena chisoni.” Mawu akuti “analira” amachokera ku mneni Wachigiriki (da·kryʹo) amene amatanthauza “kugwetsa misozi, kulira mwakachetechete.” Kumeneku nkosiyana ndi “kulira” kwa Mariya ndi Ayuda amene ali naye, kotchulidwa pa Yohane 11:33. Pamenepo liwu Lachigiriki (lochokera ku klaiʹo) logwiritsiridwa ntchito limatanthauza kulira momveka kapena mofuula.d
Pamenepo, Yesu anakhudzidwa mozama ndi imfa ya bwenzi lake lapamtima Lazaro ndi kuwona mlongo wa Lazaro akulira. Mtima wa Yesu unadzazidwa ndi chisoni kotero kuti maso ake anadzala ndi misozi. Chimene chiri chosangalatsa kwambiri nchakuti papitapo Yesu anaukitsa ena aŵiri. Ndipo pa chochitikachi iye akufuna kuchita zofananazo kwa Lazaro. (Yohane 11:11, 23, 25) Komabe, iye “analira.” Pamenepa, kubwezeretsa anthu ku moyo sikuli kokha chinthu chongochita kwa Yesu. Malingaliro ake achifundo ndi ozama osonyezedwa pa chochitikachi mowonekera akusonyeza chikhumbo chake chachikulu cha kuchotsapo ziyambukiro zosakaza za imfa.
Popeza kuti Yesu ali ‘chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe cha Yehova Mulungu,’ molondola sitiyembekezera zochepa kuchokera kwa Atate wathu wakumwamba. (Ahebri 1:3) Ponena za kufunitsitsa kwa Yehova kwa kuukitsa, munthu wokhulupirika Yobu anati: “Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi? . . . Mukadaitana, ndipo ndikadakuyankhani; Mukadakhumba ntchito ya manja anu.” (Yobu 14:14, 15) Liwu la chinenero choyambirira lolembedwa “mukadakhumba” limasonyeza kulakalaka kofunitsitsa ndi kukhumba. (Genesis 31:30; Salmo 84:2) Mwachiwonekere, mofunitsitsa Yehova ayenera kukhala akuyembekezera chiukiriro.
Kodi tingakhulupiriredi lonjezo la chiukiriro? Chabwino, palibe chikaikiro chakuti Yehova ndi Mwana wake ali ofunitsitsa ndipo okhoza kulikwaniritsa ilo. Kodi zimenezi zimatanthauzanji kwa inu? Muli ndi chiyembekezo cha kukhala wogwirizananso ndi akufa okondedwa pompano pa dziko lapansi pansi pa mikhalidwe yamtendere!
Chimenecho tsopano ndicho chiyembekezo cha Roberta (wotchulidwa m’nkhani yapita). Zaka zambiri pambuyo pa imfa ya amayi ake, Mboni za Yehova zinamthandiza kuphunzira Baibulo mosamalitsa. Iye akukumbukira kuti: “Pambuyo pophunzira za chiyembekezo cha chiukiriro, ndinalira. Zinali zosangalatsa kudziŵa kuti ndidzawawonanso amayi.” Ngati mtima wanu ukukhumba kudzawonanso wokondedwa, mosakaikira mungakonde kudziŵa zambiri ponena za chiyembekezo chimenechi. Kutsimikizirika kwa chiyembekezo chimenechi kwalongosoledwa mwatsatanetsatane pa masamba 18-28 a magazine ano.
[Mawu a M’munsi]
a Onani nkhani yakuti “Sonyezani Chikhulupiriro kaamba ka Moyo Wosatha,” masamba 23-8.
b Mkati mwa nthaŵi imene inapitapo Yesu atapanga lonjezo lolembedwa pa Yohane 5:28, 29 ndi imfa ya Lazaro, Yesu anaukitsa mwana wamwamuna wa mkazi wamasiye wa ku Nayini ndi mwana wamkazi wa Jairo.—Luka 7:11-17; 8:40-56.
c Onani mutu 6, “The Miracles—Did They Really Happen?” m’bukhu lakuti The Bible—God’s Word or Man’s? lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
d Mosangalatsa, liwu Lachigiriki kaamba ka kulira momveka (klaiʹo) lagwiritsidwa ntchito kwa Yesu pa chochitika pamene ananeneratu za kudza kwa chiwonongeko cha Yerusalemu. Cholembera cha Luka chikuti: “Ndipo mmene anayandikira, anaona mudziwo [Yerusalemu] naulirira.”—Luka 19:41.
[Chithunzi patsamba 5]
Kuukitsa mwana wa Jairo kwa Yesu kumapereka maziko a chikhulupiriro m’chiukiriro cha mtsogolo cha akufa
[Chithunzi patsamba 6]
Yesu anakhudzidwa mozama ndi imfa ya Lazaro
[Chithunzi patsamba 7]
Chisangalalo cha awo amene adzachitira umboni chiukiriro chidzakhala ngati chisangalalo cha mkazi wamasiye wa ku Nayini pamene Yesu anaukitsa mwana wake wakufa