MUTU 55
Anthu Ambiri Anakhumudwa ndi Zimene Yesu Ananena
KUDYA MNOFU NDIPONSO KUMWA MAGAZI AKE
ANTHU AMBIRI ANAKHUMUDWA NDIPO ANASIYA KUMUTSATIRA
Ali m’sunagoge wa ku Kaperenao, Yesu anaphunzitsa zoti iyeyo ndi chakudya chochokera kumwamba. Pa nthawiyi Yesu anabwereza zimene anauza anthu amene anabwera kuchokera ku chigawo chakum’mawa kwa nyanja ya Galileya. Anthuwa ndi amene Yesu anawadyetsa mozizwitsa aja.
Yesu ananenanso kuti: “Makolo anu anadya mana m’chipululu koma anamwalirabe.” Pofuna kusiyanitsa mana ndi chakudya chochokera kumwamba, iye anafotokoza kuti: “Ine ndine chakudya chamoyo chotsika kumwamba. Ngati wina adyako chakudya chimenechi adzakhala ndi moyo kosatha. Ndipotu chakudya chimene ndidzapereke kuti dzikoli lipeze moyo, ndicho mnofu wangawu.”—Yohane 6:48-51.
Pakati pa mwezi wa March ndi April mu 30 C.E., Yesu anauza Nikodemo kuti Mulungu anakonda kwambiri dziko lapansi moti anatumiza Mwana wake kuti adzapulumutse anthu. Koma pa nthawiyi Yesu anafotokoza za kufunika kodya mnofu wake zomwe zinkatanthauza kukhulupirira nsembe imene anali atatsala pang’ono kuipereka. Kukhulupirira nsembeyi ndi njira yokhayo yopezera moyo wosatha.
Koma anthuwo sanagwirizane ndi zimene Yesu ananenazi, moti ankafunsana kuti: “Kodi munthu uyu angathe bwanji kutipatsa mnofu wake kuti tidye?” (Yohane 6:52) Yesu sankanena zoti anthu adyedi thupi lake lenileni. Tikutero chifukwa cha zimene kenako ananena.
Yesu ananena kuti: “Mukapanda kudya mnofu wa Mwana wa munthu ndi kumwa magazi ake, mulibe moyo mwa inu. Wakudya mnofu wanga ndi kumwa magazi anga ali nawo moyo wosatha, . . . Pakuti mnofu wanga ndi chakudya chenicheni, ndipo magazi anga ndi chakumwa chenicheni. Munthu wakudya mnofu wanga ndi kumwa magazi anga, iyeyo ndi ine timakhala ogwirizana.”—Yohane 6:53-56.
Tangoganizani mmene Ayudawo anakhumudwira atamva zimenezi. Mwina anthuwa ankaganiza kuti Yesu ankanena kuti azidya anthu anzawo kapena kuphwanya lamulo la Mulungu loletsa kudya magazi. (Genesis 9:4; Levitiko 17:10, 11) Komatu Yesu sankatanthauza zimenezi. Iye ankatanthauza kuti aliyense amene akufuna kudzakhala ndi moyo wosatha ayenera kukhulupirira nsembe yomwe anali atatsala pang’ono kuipereka. Yesu anapereka nsembeyi pamene analolera kuti thupi lake lopanda uchimo komanso magazi ake ziperekedwe monga nsembe. Koma ophunzira ake ambiri sanamvetse zimene Yesu ankaphunzitsa moti ena ananena kuti: “Mawu amenewa ndi ozunguza. Ndani angamvetsere zimenezi?”—Yohane 6:60.
Yesu ataona kuti ena mwa ophunzira ake akung’ung’udza anawafunsa kuti: “Kodi mawuwa mwakhumudwa nawo? Nanga zidzakhala bwanji mukadzaona Mwana wa munthu akukwera kupita kumene anali poyamba? . . . Mawu amene ndakuuzaniwa ndiwo mzimu ndiponso ndiwo moyo. Koma pali ena mwa inu amene sakukhulupirira.” Atanena mawu amenewa ambiri mwa ophunzira akewo anachoka ndipo anasiya kumutsatira.—Yohane 6:61-64.
Ndiyeno Yesu anafunsa atumwi ake 12 kuti: “Inunso mukufuna kupita kapena?” Petulo anayankha kuti: “Ambuye, tingapitenso kwa ndani? Inu ndi amene muli ndi mawu amoyo wosatha. Ife takhulupirira ndipo tadziwa kuti inu ndinu Woyera wa Mulungu.” (Yohane 6:67-69) Zimene Petulo anayankha zinasonyeza kuti iyeyo komanso atumwi enawo anali okhulupirika ngakhale kuti nawonso sanamvetse zimene Yesu ankaphunzitsa pa nkhani imeneyi.
Yesu anasangalala ndi zimene Petulo anayankhazo ndipo ananena kuti: “Ine ndinakusankhani inu 12, si choncho kodi? Komatu mmodzi wa inu ndi wonenera anzake zoipa.” (Yohane 6:70) Pamenepa Yesu ankanena za Yudasi Isikariyoti. N’kutheka kuti pa nthawi imeneyi Yesu anadziwa zoti Yudasi wayamba kumukonzera chiwembu.
Komabe Yesu anasangalala kudziwa kuti Petulo ndiponso atumwi ake ena sanasiye kuyenda naye komanso kugwira nawo ntchito yopulumutsa anthu yomwe iye ankagwira.