Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Ophunzira Ambiri Asiya Kutsatira Yesu
YESU akuphunzitsa mu sunagoge mu Kapernao ponena za mbali yake monga mkate wowona wochokera kumwamba. Nkhani yake mwachiwonekere iri kufutukula kwa kukambitsirana komwe kunayamba ndi anthu pamene anam’peza iye pakubwerera kwawo kuchokera ku mbali ya kum’mawa ya Nyanja ya Galileya, kumene iwo anali atadya kuchokera ku mikate ndi nsomba zoperekedwa mozizwitsa.
Yesu akupitiriza ndi ndemanga yake, kunena kuti: “Mkate umene ndidzaupatsa ine, ndiwo thupi langa, ukhale moyo wa dziko lapansi.” Kokha zaka ziŵiri pambuyo pake, mu ngululu ya 30 C.E., Yesu anauza Nikodemo kuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero kuti anapereka Mwana wake monga Mpulumutsi. Chotero, Yesu tsopano akusonyeza kuti aliyense wa dziko la mtundu wa anthu yemwe adya mophiphiritsira thupi lake, mwa kusonyeza chikhulupiriro mwa nsembe imene iye adzapereka posachedwapa, angalandire moyo wosatha.
Anthuwo, ngakhale kuli tero, akukhumudwa pa mawu a Yesu. “Akhoza bwanji ameneyo kutipatsa ife kudya thupi lake?” iwo akufunsa. Yesu akufuna amvetseri ake kumvetsetsa kuti kudya kwa thupi lake kudzachitidwa m’njira yophiphiritsira. Chotero, kugogomezera ichi, iye akunena chinachake chimene chiri chokanidwanso ngati chitatengedwa m’tanthauzo lenileni.
“Ngati simukudya thupi la Mwana wa munthu ndi kumwa mwazi wake,” Yesu akulengeza, “mulibe moyo mwa inu nokha. Iye wakudya thupi langa ndi kumwa mwazi wanga ali nawo moyo wosatha, ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza, pakuti thupi langa ndi chakudya ndithu, ndi mwazi wanga ndi chakumwa ndithu. Iye wakudya thupi langa ndi kumwa mwazi wanga akhala mwa Ine ndi Ine mwa iye.”
Zowona, ngati Yesu pano anali kulingalira za kudya anthu, chiphunzitso chake chikanamveka choipa koposa. Koma, ndithudi, Yesu sanali kupititsa patsogolo kudya thupi kwenikweni kapena kumwa mwazi. Iye anali kokha kugogomezera kuti awo onse amene akalandira moyo wosatha ayenera kusonyeza chikhulupiriro mu nsembe imene iye akaipanga pamene apereka thupi lake la munthu langwiro ndi kuthira mwazi wake wamoyo. Komabe, ngakhale ambiri a ophunzira ake sakupanga kuyesera kwa kumvetsetsa chiphunzitso chake ndipo chotero akutsutsa: “Mawu awa ndi osautsa; akhoza kumva awa ndani?”
Podziŵa kuti ambiri a ophunzira ake akung’ung’udza, Yesu anena kuti: “Ichi mukhumudwa nacho? Nanga bwanji ngati mukawona Mwana wa munthu alikukwera kumene anali kale lomwe? . . . Mawu amene ndalankhula ndi inu ndiwo mzimu, ndi moyo. Koma pali ena mwa inu amene sakhulupirira.”
Yesu akupitiriza: “Chifukwa cha ichi ndinati kwa inu, kuti palibe munthu angathe kudza kwa ine, koma ngati kupatsidwa kwa iye ndi Atate.” Ndi chimenecho, ambiri a ophunzira ake akuchoka ndipo sakumutsatiranso iye. Chotero Yesu atembenukira kwa atumwi ake 12 ndi kufunsa: “Nanga inunso mufuna kuchoka?”
Petro akuyankha: “Ambuye, tidzamuka kwa yani? Inu muli nawo mawu a moyo wosatha. Ndipo ife tikhulupirira, ndipo tidziŵa kuti Inu ndinu Woyera wa Mulungu.” Ndichisonyezero chabwino cha kukhulupirika chotani nanga, ngakhale kuti Petro ndi atumwi ena angakhale asanamvetsetse chiphunzitso cha Yesu pa nkhaniyo!
Ngakhale kuti anasangalatsidwa ndi yankho la Petro, Yesu akuyang’ana: “Kodi sindinakusankhani khumi ndi aŵiri, ndipo mwa inu mmodzi ali mdyerekezi?” Iye akulankhula ponena za Yudase Isikariote. Mothekera pa nsongayi Yesu akuzindikira mwa Yudase “chiyambi,” kapena kuyambika, kwa njira yolakwa.
Yesu wangokhumudwitsa kumene anthu mwakukana kuyesayesa kwawo kwa kum’panga iye mfumu, ndipo iwo angapereke chifukwa, ‘Kodi iyeyu angakhale Mesiya motani ngati sadzatenga kaimidwe koyenerera ka Umesiya?’ Ichi, nachonso, chidzakhala nkhani yatsopano m’malingaliro mwa anthuwo. Yohane 6:51-71; 3:16.
◆ Yesu akupereka thupi lake kaamba ka yani, ndipo ndimotani mmene awa ‘amadyera thupi lake’?
◆ Ndi mawu owonjezereka otani a Yesu amene akukhumudwitsa anthu, komabe nchiyani chimene iye akugogomezera?
◆ Pamene ambiri asiya kutsatira Yesu, nchiyani chimene chiri yankho la Petro?