Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Pa Phwando la Misasa
YESU wakhala wotchuka mkati mwa chifupifupi zaka zitatu kuyambira ubatizo wake. Zikwi zambiri zawona zozizwitsa zake, ndipo maripoti onena za machitachita ake afalikira kuzungulira dziko lonse. Tsopano, pamene anthu akusonkhana kaamba ka Phwando la Misasa mu Yerusalemu, iwo akumufunafuna iye kumeneko. “Ali kuti uja?” iwo akufuna kudziŵa.
Yesu wakhala maziko a mtsutsano. “Ali wabwino,” ena akutero. “Iai, koma asocheretsa khamu la anthuwo,” ena akutsutsa tero. Pali nkhani yotsutsana yokulira ya mtunduwu mkati mwa masiku otsegulira a phwandolo. Komabe palibe aliyense amene ali ndi kulimba mtima kwa kulankhula poyera m’malo mwa Yesu. Ichi chiri chifukwa chakuti anthu akuwopa chidzudzulo chochokera kwa atsogoleri a Chiyuda.
Pamene phwandolo liri pafupi kutha, Yesu afika. Iye apita ku kachisi, kumene anthu adabwitsidwa ndi mphamvu zake zozizwitsa za kuphunzitsa. Popeza kuti Yesu sanapezekepo ku maphunziro a urabi, Ayuda akuzizwa: “Ameneyo adziŵa bwanji zolemba, wosaphunzira?”
“Chiphunzitso changa sichiri changa,” Yesu akulongosola, “koma cha iye amene anandituma ine. Ngati munthu aliyense afuna kuchita chifuniro chake, adzazindikira za chiphunzitsocho, ngati chichokera kwa Mulungu kapena ndilankhula zochokera kwa ine ndekha.” Chiphunzitso cha Yesu chimagwirizana mwathithithi ndi lamulo la Mulungu. Chotero, chiyenera kukhala chotsimikizirika kuti iye akufunafuna ulemerero wa Mulungu, osati wake. “Si Mose kodi anakupatsani inu chilamulo?” Yesu akufunsa. Ndipo mwa njira ya kuwadzudzula, iye akupitiriza kunena kuti: “Ndipo kulibe mmodzi mwa inu anachita chilamulo.”
“Mufuna kundipha chifukwa ninji?” Yesu kenaka akuwafunsa iwo.
Khamulo, mwinawake alendo ku phwandolo, anali osadziŵa za zoyesayesa zimenezo. Iwo akulingalira icho kukhala chosalingaliridwa kuti winawake angafune kupha mphunzitsi wabwino kwambiri woteroyo. Chotero iwo akukhulupirira kuti chinachake chiyenera kukhala cholakwika ndi Yesu kuti iye alingalire chimenechi. “Muli ndi chiwanda,” iwo akutero. “Afuna ndani kukuphani inu?”
Atsogoleri a Chiyuda akufuna kuti Yesu aphedwe, ngakhale kuti khamu silingazindikire za icho. Pamene Yesu anachiritsa munthu pa Sabata chaka chimodzi ndi theka zapita, atsogoleriwo anayesera kumupha iye. Chotero Yesu tsopano akuloza ku kusalingalira kwawo mwa kuwafunsa iwo kuti: “Ngati alandira mdulidwe tsiku la Sabata, kuti chilamulo cha Mose chisapasulidwe, kodi mundikwiira ine, chifukwa ndam’chiritsadi munthu tsiku la Sabata? Musaweruze monga mwa mawonekedwe, koma weruzani chiweruziro cholungama.”
Nzika za Yerusalemu, zomwe zikudziŵa za mkhalidwewo, tsopano zikunena kuti: “Kodi suyu amene afuna kumupha? Ndipo tawona amalankhula poyera, ndipo sanena kanthu kwa iye. Kapena kodi akulu adziŵa ndithu kuti ndiye Kristu ameneyo?” Nzika za Yerusalemu zimenezi zikulongosola chifukwa chimene iwo sakukhulupirira kuti Yesu ndiye Kristu: “Koma ameneyo tidziŵa uko achokera; koma Kristu akadzadza, palibe mmodzi adzadziŵa uko achokera.”
Yesu akuyankha: “Mundidziŵa ine, ndiponso mudziŵa uko ndichokera. Ndipo sindinadza ine ndekha, koma iye wondituma ine amene inu simumdziŵa, ali wowona. Ine ndimdziŵa iye; chifukwa ndiri wochokera kwa iye, nandituma ine iyeyu.” Pamenepo anafuna kumugwira iye, mwinamwake kuti amuike m’ndende kapena kumupha iye. Komabe iwo sakupambana chifukwa siiri nthaŵi kaamba ka Yesu kuti afe.
Komabe, ambiri aika chikhulupiriro mwa Yesu, monga mmenedi ayenera kutero. Nkulekelanji, popeza kuti iye anayenda pamadzi, kukhalitsa bata mphepo, kutontholetsa namondwe pa nyanja, mozizwitsa kudyetsa zikwi pa mikate yochepa ndi tinsomba, kuchiritsa odwala, kupangitsa opunduka kuyenda, kutsegula maso a akhungu, kuchiritsa akhate, ndipo ngakhale kuwukitsa akufa. Chotero iwo akufunsa: “Pamene Kristu akadza kodi adzachita zizindikiro zambiri zoposa zimene adazichita ameneyo?”
Pamene Afarisi amva khamulo likung’ung’udza zinthuzi, iwo ndi akulu ansembe atumiza nduna kukagwira Yesu. Yohane 7:11-32.
◆ Ndi liti pamene Yesu afika pa phwando, ndipo ndi nkhani yotani imene iri pamenepo ponena za iye?
◆ Nchifukwa ninji chingakhale chakuti ena akunena kuti Yesu ali ndi chiwanda?
◆ Ndi kawonedwe kotani ka Yesu kamene nzika za Yerusalemu ziri nako?
◆ Nchifukwa ninji ambiri akuika chikhulupiriro mwa Yesu?