Maphunziro—Agwiritsireni Ntchito Kutamanda Yehova
“Iye wolankhula zochokera kwa iye yekha afuna ulemu wa mwini yekha. Iye wakufuna ulemu wa iye amene anamtuma, yemweyu ali woona.”—YOHANE 7:18.
1. Kodi ndi liti ndipo ndi motani mmene maphunziro anayambira?
MAPHUNZIRO anayamba kalekale. Anayamba pamene Yehova Mulungu, Mphunzitsi ndi Mlangizi Wamkulukuluyo, anali atangotha kumene kulenga Mwana wake woyamba. (Yesaya 30:20; Akolose 1:15) Ameneyu ndiye Munthu amene anaphunzira kwa Mlangizi Wamkulukulu mwiniyo! Pa zaka zikwi zambiri zimene anayanjana mwathithithi ndi Atate wake, Mwana ameneyo—amene anadziŵidwa monga Yesu Kristu—analandira maphunziro amtengo wapatali ponena za mikhalidwe, ntchito, ndi zifuno za Yehova Mulungu. Pambuyo pake, pamene anali munthu padziko lapansi, Yesu anakhoza kunena kuti: ‘Sindichita kanthu kwa ine ndekha, koma monga anandiphunzitsa Atate, ndilankhula izi.’—Yohane 8:28.
2-4. (a) Malinga ndi kunena kwa Yohane chaputala 7, kodi panali mikhalidwe yotani pamene Yesu anafika pa Phwando la Misasa mu 32 C.E.? (b) Kodi nchifukwa ninji Ayuda anazizwa pa kuphunzitsa kwa Yesu?
2 Kodi Yesu anagwiritsira ntchito motani maphunziro amene analandira? Mu utumiki wake wonse wapadziko lapansi wa zaka zitatu ndi theka, iye mosatopa anauza ena zimene anaphunzira. Komabe, anachita zimenezi ndi chifuno china chachikulu m’maganizo. Ndipo chinali chotani? Tiyeni tipende mawu a Yesu mu Yohane chaputala 7, mmene anafotokozamo zonse ziŵiri magwero ndi chifuno cha chiphunzitso chake.
3 Lingalirani za mkhalidwe wake. Munali mu mphakasa ya 32 C.E., pafupifupi zaka zitatu Yesu atabatizidwa. Ayuda anasonkhana mu Yerusalemu kaamba ka Phwando la Misasa. Pamasiku angapo oyamba a phwandolo, anthu ananena zambiri ponena za Yesu. Pamene phwandolo linafika pakati pake, Yesu anakwera naloŵa m’kachisi nayamba kuphunzitsa. (Yohane 7:2, 10-14) Monga mmene anachitira nthaŵi zonse, anasonyezadi kuti anali Mphunzitsi wamkulu.—Mateyu 13:54; Luka 4:22.
4 Vesi 15 la Yohane chaputala 7 limati: “Chifukwa chake Ayuda anazizwa, nanena, Ameneyu adziŵa bwanji zolemba, wosaphunzira?” Kodi mukudziŵa chifukwa chake iwo anazizwa? Yesu sanapite kusukulu iliyonse ya arabi, chotero anali wosaphunzira—malinga ndi kuganiza kwawo! Komabe, Yesu anali wokhoza kupeza ndi kuŵerenga zigawo m’Malembo Opatulika mosavuta. (Luka 4:16-21) Aha, Mgalileya wopala matabwa ameneyu anawalangizadi za Chilamulo cha Mose! (Yohane 7:19-23) Kodi zimenezi zinatheka bwanji?
5, 6. (a) Kodi Yesu analongosola motani za magwero a chiphunzitso chake? (b) Kodi Yesu anagwiritsira ntchito maphunziro ake m’njira yotani?
5 Monga momwe timaŵerengera m’mavesi 16 ndi 17, Yesu anafotokoza kuti: “Chiphunzitso changa sichili changa, koma cha iye amene anandituma ine. Ngati munthu aliyense afuna kuchita chifuniro Chake, adzazindikira za chiphunzitsocho, ngati chichokera kwa Mulungu, kapena ndilankhula zochokera kwa ine ndekha.” Iwo anafuna kudziŵa kuti Yesu anaphunzitsidwa ndi yani, ndipo anawauza poyera kuti maphunziro ake anachokera kwa Mulungu!—Yohane 12:49; 14:10.
6 Kodi Yesu anagwiritsira ntchito maphunziro ake motani? Monga momwe kwalembedwera pa Yohane 7:18, Yesu anati: ‘Iye wolankhula zochokera kwa iye yekha afuna ulemu wa mwini yekha. Iye wakufuna ulemu wa iye amene anamtuma, yemweyu ali woona, ndipo mwa iye mulibe chosalungama.’ Kunali koyenera chotani nanga kuti Yesu anagwiritsira ntchito maphunziro ake kulemekeza Yehova, “Iye wakudziŵa mwangwiro”!—Yobu 37:16.
7, 8. (a) Kodi maphunziro ayenera kugwiritsiridwa ntchito motani? (b) Kodi zolinga zinayi zazikulu za maphunziro oyenera nzotani?
7 Motero timapeza phunziro lofunika kwa Yesu—maphunziro ayenera kugwiritsiridwa ntchito, osati kaamba ka kudzipezera ulemu wa ife eni, koma kutamanda Yehova. Palibenso njira ina yabwino kwambiri yogwiritsira ntchito maphunziro kuposa imeneyi. Nangano, mungagwiritsire ntchito motani maphunziro kutamanda Yehova?
8 Kuphunzitsa kumatanthauza “kulangiza ndi malangizo oikika ndi kuyang’anira kuyesedwa makamaka kwa maluso, umisiri, kapena ntchito.” Tsopano tiyeni tikambitsirane zolinga zazikulu zinayi za maphunziro oyenera ndi mmene chilichonse chingagwiritsidwire ntchito pa kutamanda Yehova. Maphunziro oyenera ayenera kutithandiza (1) kuŵerenga bwino, (2) kulemba bwino, (3) kukula m’maganizo ndi m’makhalidwe, ndi (4) kuphunzira ntchito yofunika pa moyo wa tsiku ndi tsiku.
Kuphunzira Kuŵerenga Bwino
9. Kodi nchifukwa ninji kukhala woŵerenga wabwino kuli kofunika?
9 Choyamba ndicho kuphunzira kuŵerenga bwino. Kodi nchifukwa ninji kukhala woŵerenga bwino kuli kofunika kwambiri? The World Book Encyclopedia imafotokoza kuti: “Kuŵerenga . . . nkofunika pa kuphunzira ndipo kuli limodzi la maluso ofunika koposa pa moyo wa tsiku ndi tsiku. . . . Oŵerenga aluso amachirikiza kuyamba kwa mtundu wokhuphuka ndi wantchito. Panthaŵi imodzimodziyo, iwo eniwo amakhala ndi moyo wokwanira ndi wokhutiritsa kwambiri.”
10. Kodi kuŵerenga Mawu a Mulungu kumatithandiza motani kukhala ndi moyo wokwanira ndi wokhutiritsa kwambiri?
10 Ngati kuŵerenga wamba kungatithandize kukhala ndi moyo “wokwanira ndi wokhutiritsa kwambiri,” koposa chotani nanga kuŵerenga Mawu a Mulungu! Kuŵerenga kotero kumatsegula maganizo ndi mitima yathu kuti malingaliro ndi zifuno za Yehova ziloŵemo, ndipo kumvetsa bwino zimenezi kumachititsa moyo wathu kukhala ndi tanthauzo. Ndiponso, “mawu a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita,” amatero Ahebri 4:12. Pamene tiŵerenga Mawu a Mulungu ndi kuwasinkhasinkha, timayandikira kwambiri kwa Mlembi wake, ndipo timasonkhezereka kupanga masinthidwe m’moyo wathu kuti timkondweretse kwambiri. (Agalatiya 5:22, 23; Aefeso 4:22-24) Timaumirizikanso kuuza ena choonadi chamtengo wapatali chimene timaŵerenga. Zonsezi zimabweretsa chitamando kwa Mlangizi Wamkulukuluyo, Yehova Mulungu. Kunena zoona, palibe njira ina yabwino kwambiri kuposa imeneyi imene tingagwiritsirire ntchito luso lathu la kuŵerenga!
11. Kodi nchiyani chimene chiyenera kuphatikizidwa m’programu yoyenera ya phunziro laumwini?
11 Kaya tikhale wachichepere kapena wachikulire, timalimbikitsidwa kuphunzira kuŵerenga bwino, pakuti kuŵerenga kumathandiza kwambiri pa moyo wathu wachikristu. Kuwonjezera pa kuŵerenga Mawu a Mulungu nthaŵi zonse, programu yoyenera ya phunziro laumwini iyenera kuphatikizapo kupenda lemba la m’Baibulo mu Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku, kuŵerenga Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, ndi kukonzekera misonkhano yachikristu. Ndipo bwanji nanga za utumiki wachikristu? Mwachionekere, kulalikira poyera, kupanga maulendo obwereza pa anthu okondwerera, ndi kuchititsa maphunziro a Baibulo apanyumba zonsezo zimafuna luso la kuŵerenga bwino.
Kuphunzira Kulemba Bwino
12. (a) Kodi nchifukwa ninji kuphunzira kulemba bwino kuli kofunika? (b) Kodi nkulemba kuti kwakukulu koposa kumene kunachitika?
12 Cholinga chachiŵiri nchakuti maphunziro oyenera ayenera kutithandiza kuphunzira kulemba bwino. Kulemba sikumangopereka mawu ndi malingaliro athu kwa ena komanso kumawasunga. Zaka mazana ambirimbiri zapitazo, amuna ena achiyuda 40 analemba mawu pagumbwa kapena pazikopa amene anapanga Malemba ouziridwa. (2 Timoteo 3:16) Kunena zoona uku kunali kulemba kwakukulu koposa kumene kunachitikapo! Mosakayikira Yehova anayang’anira kukopedwa ndi kubwerezanso kukopa kwa mawu opatulikawo kwa zaka mazana ambiri, kwakuti afika kwa ife ali odalirika. Kodi sitili oyamikira kuti Yehova anachititsa mawu ake kulembedwa, m’malo mwa kudalira pa kuwapatsira kwa ena ndi pakamwa?—Yerekezerani ndi Eksodo 34:27, 28.
13. Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti Aisrayeli anadziŵa kulemba?
13 M’nthaŵi zakale, magulu ena opeza bwino okha, onga ngati alembi ku Mesopotamiya ndi Igupto, ndiwo amene anali ophunzira. Mosiyana kwambiri ndi mitundu ina, mu Israyeli aliyense analimbikitsidwa kuphunzira. Lamulo la pa Deuteronomo 6:8, 9 kwa Aisrayeli la kulemba pamphuthu za nyumba zawo, ngakhale kuti mwachionekere linali lophiphiritsira, limasonyeza kuti iwo ankadziŵa kulemba. Ana anaphunzitsidwa kulemba pausinkhu waung’ono. Kalenda ya Gezer, chimodzi cha zitsanzo zakale kwambiri za malembo a Chihebri chakale, imalingaliridwa ndi akatswiri ena kukhala chipangizo chokumbutsa mwana wasukulu.
14, 15. Kodi ndi njira zina ziti zimene zili zopindulitsa ndi zoyenera zogwiritsirira ntchito luso la kulemba?
14 Koma kodi ife tingagwiritsire ntchito motani luso lathu la kulemba mwanjira yopindulitsa ndi yoyenera? Ndithudi, mwa kulemba mfundo pamisonkhano yachikristu yampingo, yadera, ndi yachigawo. Kalata, ngakhale yolembedwa “mwachidule,” ingapereke chilimbikitso kwa munthu amene akudwala kapena ingasonyeze chiyamikiro chathu kwa mbale kapena mlongo amene anatikomera mtima kapena anatichezetsa. (1 Petro 5:12) Ngati wina mumpingo wataya wokondedwa wake mu imfa, kalata yachidule kapena khadi ‘lingatitonthozere’ munthuyo. (1 Atesalonika 5:14, NW) Mlongo wina wachikristu amene amake anamwalira chifukwa cha kansa anafotokoza kuti: “Mnzanga wina anandilembera kalata yabwino. Zimenezo zinandithandizadi chifukwa chakuti ndinkaiŵerenga mobwerezabwereza.”
15 Njira yabwino koposa yogwiritsirira ntchito luso lathu la kulemba ndiyo kutamanda Yehova mwa kulemba kalata yopereka umboni wa Ufumu. Nthaŵi zina kungakhale kofunika kulemberana ndi anthu okondwerera chatsopano okhala kumadera akutali. Matenda angakuletseni kwakanthaŵi kupita kunyumba ndi nyumba. Mwina kalata inganene zimene mukananena naye maso ndi maso.
16, 17. (a) Kodi nchokumana nacho chotani chimene chikusonyeza phindu la kulemba kalata yopereka umboni wa Ufumu? (b) Kodi mungasimbe chokumana nacho chofanana ndi chimenechi?
16 Talingalirani za chokumana nacho chotsatira. Zaka zambiri zapitazo Mboni ina inalemba kalata yopereka umboni wa Ufumu kwa mkazi wamasiye amene imfa ya mwamuna wake inalengezedwa m’nyuzipepala yakumaloko. Iyeyo sanayankhe. Ndiyeno, m’November 1994, pambuyo pa zaka zoposa 21, Mboniyo inalandira kalata yochokera kwa mwana wamkazi wa mkaziyo. Mwanayo analemba kuti:
17 “Mu April 1973, munalembera kalata amayi yowatonthoza pa imfa ya atate. Panthaŵiyo ndinali ndi zaka zisanu ndi zinayi. Amayi anaphunziradi Baibulo, koma mpaka lero sanakhalebe mtumiki wa Yehova. Koma, kuphunzira kwawo kunandichititsa kupeza choonadi. Mu 1988, ndinayamba kuphunzira Baibulo—patapita zaka 15 pambuyo pa kulandira kalata yanu. Pa March 9, 1990, ndinabatizidwa. Ndikuthokozani kwambiri pa kalata yanu ya zaka zambiri zapitazo ndipo ndili wokondwa kukudziŵitsani kuti mbewu zimene munafesazo zinakula ndi thandizo la Yehova. Amayi anandipatsa kalata yanu kuti ndisunge, ndipo ndikufuna kukudziŵani. Ndikukhulupirira kuti kalatayi idzakufikani.” Kalata ya mwanayo, imene inalinso ndi keyala ndi nambala za telefoni, inafikadi kwa Mboni imene inalemba kalatayo zaka zambiri zapitazo. Talingalirani mmene mtsikanayo anadabwira pamene analandira telefoni kuchokera kwa Mboniyo—imene imalembabe makalata kuuza ena za chiyembekezo cha Ufumu!
Kukula m’Maganizo, m’Makhalidwe, ndi Mwauzimu
18. M’nthaŵi za Baibulo, kodi makolo anawaphunzitsa motani ana awo kukula m’maganizo ndi m’makhalidwe?
18 Cholinga chachitatu nchakuti maphunziro oyenera afunikira kutithandiza kukula m’maganizo ndi m’makhalidwe. M’nthaŵi za Baibulo limodzi la mathayo oyamba a makolo linali kuphunzitsa ana kukula m’maganizo ndi m’makhalidwe. Ana sanangophunzitsidwa kuŵerenga ndi kulemba, komanso anaphunzitsidwa makamaka Chilamulo cha Mulungu, chimene chinakhudza zochita zawo zonse m’moyo. Chotero, maphunziro anaphatikizapo malangizo a mathayo awo achipembedzo ndi mapulinsipulo a ukwati, maunansi a banja, ndi chikhalidwe cha zakugonana, ndiponso mathayo awo kulinga kwa anthu anzawo. Maphunziro otero sanangowathandiza kukula m’maganizo ndi m’makhalidwe komanso mwauzimu.—Deuteronomo 6:4-9, 20, 21; 11:18-21.
19. Kodi nkuti kumene tingapeze maphunziro amene angatisonyeze makhalidwe abwino koposa otsatira ndi amene angatithandize kukula mwauzimu?
19 Bwanji nanga za lerolino? Maphunziro abwino akusukulu ngofunika. Amatithandiza kukula m’maganizo. Koma kodi tingatembenukire kuti kaamba ka maphunziro amene angatisonyeze miyezo ya makhalidwe yabwino kwambiri imene tiyenera kutsatira ndi imene ingatithandize kukula mwauzimu? Mumpingo wachikristu, tili ndi programu ya maphunziro ateokrase amene samapezeka kwina kulikonse padziko lapansi. Mwa phunziro lathu laumwini la Baibulo ndi zofalitsidwa zozikidwa pa Baibulo ndiponso malangizo operekedwa pamisonkhano yampingo, yadera, ndi yachigawo, tingalandire maphunziro opitiriza amtengo wapatali ameneŵa—maphunziro aumulungu—kwaulere! Kodi amatiphunzitsanji?
20. Kodi maphunziro aumulungu amatiphunzitsanji, ndipo amatulutsanji?
20 Pamene tiyamba kuphunzira Baibulo, timadziŵa ziphunzitso zoyambirira za Malemba, “mawu a chiyambidwe.” (Ahebri 6:1) Pamene tipitiriza, timadya “chakudya chotafuna”—ndiko kuti, choonadi chakuya. (Ahebri 5:14) Komanso kuwonjezera pa zimenezo, timaphunzira za mapulinsipulo aumulungu amene amatisonyeza kukhala ndi moyo mwanjira imene Mulungu amafuna. Mwachitsanzo, timaphunzira kupeŵa zizoloŵezi ndi machitachita amene ‘amadetsa thupi’ ndi kulemekeza ulamuliro ndi munthu wina ndi katundu wa ena. (2 Akorinto 7:1; Tito 3:1, 2; Ahebri 13:4) Ndiponso, timafika pa kuzindikira za kufunika kwake kwa kukhala oona mtima ndi kukhala akhama pantchito yathu ndi phindu la kutsatira malamulo a Baibulo a zakugonana. (1 Akorinto 6:9, 10; Aefeso 4:28) Pamene tipita patsogolo pa kugwiritsira ntchito mapulinsipulo ameneŵa m’moyo wathu, timakula mwauzimu, ndipo unansi wathu ndi Mulungu umakula. Ndiponso, khalidwe lathu laumulungu limatipangitsa kukhala nzika zabwino, kulikonse kumene timakhala. Ndipo zimenezi zingasonkhezere ena kulemekeza Magwero a chiphunzitso chaumulungu—Yehova Mulungu.—1 Petro 2:12.
Kuphunzira Ntchito ya Moyo wa Tsiku ndi Tsiku
21. Kodi ana anaphunzitsidwa ntchito zotani m’nthaŵi za Baibulo?
21 Cholinga chachinayi cha maphunziro oyenera ndicho kuphunzitsa munthu ntchito yofunika pa moyo wa tsiku ndi tsiku. Maphunziro operekedwa ndi makolo m’nthaŵi za Baibulo anaphatikizapo kuphunzitsa ntchito. Asungwana anaphunzitsidwa ntchito zapanyumba. Chaputala chomaliza cha Miyambo chimasonyeza kuti zimenezi zinali zambiri ndiponso zosiyanasiyana. Motero, asungwana ankadziŵa kupota ulusi, kuomba nsalu, ndi kuphika ndi kusamalira ntchito zina zapanyumba, kuchita malonda, ndi malonda a malo ndi minda. Kaŵirikaŵiri anyamata ankaphunzitsidwa ntchito za atate wawo, kaya ulimi kapena malonda kapena umisiri winawake. Yesu anaphunzira umisiri wa mitengo kwa Yosefe, atate wake omlera; motero, sanangotchedwa kuti “mwana wa mmisiri wa mitengo” komanso kuti “mmisiri wa mitengo.”—Mateyu 13:55; Marko 6:3.
22, 23. (a) Kodi maphunziro ayenera kukonzekeretsa ana chiyani? (b) Kodi cholinga chathu chiyenera kukhala chotani posankha maphunziro owonjezera pamene ali ofunika?
22 Lerolinonso, maphunziro oyenera amaphatikizapo kukonzekera kwa munthu kusamalira zofunika za banja mtsogolo. Mawu a mtumwi Paulo opezeka pa 1 Timoteo 5:8 amasonyeza kuti kupezera zosoŵa za banja la munthuwe kuli thayo lopatulika. Iye analemba kuti: “Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m’banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupira.” Pamenepo, maphunziro ayenera kukonzekeretsa ana za mathayo amene adzasenza m’moyo ndiponso kuwakonzekeretsa kukhala anthu akhama pantchito m’chitaganya.
23 Kodi tiyenera kupeza maphunziro ochuluka motani? Zimenezi zimasiyanasiyana m’maiko. Koma ngati olemba ntchito afuna maphunziro ena owonjezera pa amene amafunidwa ndi lamulo, zili kwa makolo kulangiza ana awo popanga chosankha ponena za maphunziro owonjezera kapena kosi, akumapenda zonse ziŵiri mapindu ake ndi kuipa kwake zimene maphunziro owonjezera amenewo angakhale nazo. Koma kodi cholinga cha munthu posankha maphunziro pamene ali ofunika chiyenera kukhala chotani? Ndithudi sindicho chakuti apeze chuma, ulemu, kapena chitamando. (Miyambo 15:25; 1 Timoteo 6:17) Kumbukirani phunziro limene tapeza m’chitsanzo cha Yesu—maphunziro ayenera kugwiritsiridwa ntchito kutamanda Yehova. Ngati tisankha maphunziro owonjezera, cholinga chathu chiyenera kukhala kupeza ndalama zodzichirikizira mokwanira kuti titumikire Yehova bwino lomwe mu utumiki wachikristu.—Akolose 3:23, 24.
24. Kodi tapeza phunziro lotani kwa Yesu limene sitiyenera kuiŵala?
24 Chotero, tiyeni tichite khama pa kuyesayesa kwathu kupeza maphunziro oyenera akusukulu. Tiyeni tigwiritsire ntchito mokwanira mwaŵi wa programu yopitiriza ya maphunziro aumulungu, amene akuperekedwa m’gulu la Yehova. Ndipo tisaiŵaletu phunziro lofunika limene taphunzira kwa Yesu Kristu, munthu wophunzira koposa aliyense amene anakhalako padziko lapansi—maphunziro ayenera kugwiritsiridwa ntchito, osati kudzipezera thamo, koma kutamanda Mlangizi wamkulukuluyo, Yehova Mulungu!
Kodi Yankho Lanu Nlotani?
◻ Kodi Yesu anagwiritsira ntchito motani maphunziro ake?
◻ Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kuphunzira kuŵerenga bwino?
◻ Kodi tingagwiritsire ntchito bwino motani luso la kulemba kutamanda Yehova?
◻ Kodi chiphunzitso chaumulungu chimatithandiza motani kukula ponse paŵiri m’makhalidwe ndi mwauzimu?
◻ Kodi ndi ntchito zotani zimene maphunziro oyenera ayenera kuphatikizapo?
[Bokosi patsamba 13]
Thandizo Lopindulitsa Aphunzitsi
Pa Msonkhano Wachigawo wa “Atamandi Achimwemwe” mkati mwa 1995/96, Watch Tower Society inatulutsa brosha latsopano lotchedwa Mboni za Yehova ndi Maphunziro. Brosha lamasamba 32 limeneli, lazithunzithunzi zamaonekedwe achibadwa lafalitsidwa makamaka kaamba ka aphunzitsi. Pofika pano latembenuzidwa m’zinenero 58.
Kodi chifuno cha kutulutsa brosha la aphunzitsili nchiyani? Kuti liwathandize kumvetsetsa zikhulupiriro za ophunzira amene ali ana a Mboni za Yehova. Kodi broshalo limanenanji? M’njira yomveka bwino ndi yolimbikitsa, limalongosola za malingaliro athu pankhani zonga maphunziro owonjezera, masiku akubadwa nd Krisimasi, ndi kuchitira suluti mbendera. Broshalo limatsimikiziranso aphunzitsi kuti timafuna kuti ana athu achite bwino kwambiri pamaphunziro awo ndi kuti tili ofunitsitsa kugwirizana ndi aphunzitsi, tikumasoyeza chidwi chachikulu m’maphunziro a ana athu.
Kodi brosha la Maphunziro lingagwiritsiridwe ntchito motani? Popeza kuti linalinganizidwira aphunzitsi, tiyeni tikambitsirane za ilo ndi aphunzitsi, ahedimasitala, ndi akuluakulu ena a sukulu. Brosha limeneli lithandizetu aphunzitsi onsewo kumvetsa malingaliro athu ndi zikhulupiriro ndi chifukwa chake ife nthaŵi zina timasankha kukhala osiyana ndi ena. Makolo akulimbikitsidwa kugwiritsira ntchito broshalo monga maziko a kukambitsirana kwawo ndi aphunzitsi a ana awo.
[Chithunzi patsamba 10]
Mu Israyeli wakale maphunziro analemekezedwa