Kodi Winawake Anawonapo Mulungu?
KHOLO lolemekezedwa Abrahamu, yemwe anakhalako zaka 1,900 asanabadwe Yesu Kristu, anawonedwa motentha ndi Mlengi wathu kotero kuti anatchedwa “bwenzi la Mulungu.” (Yakobo 2:23, Byington) Ngati winawake anapatsidwa mwaŵi wakuwona Mulungu, ndithudi Abrahamu akanakhala munthu ameneyo. Chabwino, pa chochitika chinachake, alendo atatu anabwera kwa iye ndi uthenga waumulungu. Abrahamu analonjera mmodzi wa iwo monga Yehova. Kodi ichi chikutanthauza kuti Abrahamu m’chenicheni anawona Mulungu?
Mbiri imeneyi ikupezeka pa Genesis 18:1-3. Pamenepo timaŵerenga kuti: “Ndipo Yehova anamuwonekera iye pa mitengo yathundu ya ku Mamre, pamene anakhala pa khomo la hema wake pakutentha dzuŵa. Ndipo anatukula maso ake, nayang’ana, tawonani, anthu atatu anaima pandunji pake; pamene anawona iwo, anawathamangira kuchoka ku khomo la hema kukakomana nawo, nawerama pansi. Kenaka anati: ‘Yehova, ngatitu tsopano, ndapeza ufulu pamaso panu, musapitirira pa kapolo wanu.’” (NW)
Pambuyo pake, pamene Abrahamu ndi alendo ake atatu anali kuyang’ana Sodomu kuchokera pamalo okwezeka, aŵiri anachoka kukayendera mzindawo. Versi 22 kenaka likunena kuti: “Koma Yehova, anaimabe pamaso pa Abrahamu.” Chingawoneke kuchokera apa kuti Mulungu anali ndi Abrahamu m’thupi lenileni la umunthu. Ichi chiri chimene anthu ena amanena amene amakhulupirira kuti Mulungu ndi Yesu Kristu ali amodzi ndipo munthu mmodzimodziyo.
Ponena za Genesis 18:3, wophunzira Baibulo Melancthon W. Jacobus analemba kuti: “Pano Mulungu akuwoneka kwanthaŵi yoyamba m’zolembedwa monga munthu pakati pa anthu, kusonyeza kutsimikizirika kwa Kukhalapo Kwake, ndi unansi Wake ndi anthu, ndipo mwakachitidweka kutsimikizira ukholo wa chigwirizano cha Umulungu ndi ubwenzi.” Awo okhala ndi nsonga imeneyi m’kawonedwe amamaliza kuti Abrahamu m’chenicheni anawona Yehova ndi maso ake akuthupi ndipo kuti anthu omwe anawona Yesu Kristu anawonanso Mulungu. Koma kodi awa ndiwo mapeto ogwirizana ndi Baibulo?
Chimene Yesu Ananena
M’malo mwakulengeza kuti iye anali Mulungu mwakuthupi, Yesu Kristu anati: “Ndine Mwana wa Mulungu.” (Yohane 10:36) Monga Woimira wangwiro wa Yehova Mulungu, Yesu ananenanso kuti: “Sindikhoza kuchita kanthu kwa ine ndekha, monga momwemo ndimva ndiweruza; ndipo maweruzidwe anga ali olungama, chifukwa chakuti sinditsata chifuniro changa, koma chifuniro cha iye wondituma ine.” (Yohane 5:30) Pamene Yesu anali pa mtengo wozunzirapo, iye anapemphera kwa Mlengi wamkulu kumwamba, akumamutcha iye monga “Mulungu wanga, Mulungu wanga.” (Mateyu 27:46) Pambuyo pa kuwukitsidwa kwake, Yesu anauza Mariya wa Magadala: “Ndikwera kunka kwa Atate wanga ndi Atate wanu ndi Mulungu wanga ndi Mulungu wanu.” (Yohane 20:1, 17) Popeza Yesu Kristu sanali Mulungu wosandulika, palibe aliyense amene anawona Yesu amene anganene kuti anawona Mulungu.
Yohane, mtumwi amene Yesu anamkonda mwapadera, anatsimikizira chenicheni chakuti atumwi sanali kuwona Mulungu pamene anayang’ana kwa Yesu. Pansi pa kuuziridwa Yohane ananena kuti: “Kulibe munthu anawona Mulungu nthaŵi zonse.” (Yohane 1:18) Ndani, chotero, amene Abrahamu anawona? Chokumana nacho cha Mose chidzatithandiza ife kupeza yankho.
Mmene Mose Anawonera Mulungu
Mose panthaŵi imodzi analongosola chikhumbo cha kufuna kuwona Mulungu. Pa Eksodo 33:18-20, timaŵerenga kuti: “‘Ndiwonetsenitu [Mose] ulemerero wanu.’ Koma iye [Mulungu] anati: ‘Ndidzapititsa ukoma wanga wonse pamaso pako, ndipo ndidzatchula dzina la Yehova pamaso pako; ndipo ndidzachitira ufulu amene ndidzamchitira ufulu; ndi kuchitira chifundo amene ndidzamchitira chifundo.’ Ndipo anawonjezera kuti: ‘Sungathe kuwona nkhope yanga, pakuti palibe munthu adzandiwona ine ndi kukhala ndi moyo.’”
Chimene Mulungu anamulola Mose kuwona chinali ulemerero Wake. Maversi 21-23 amanena kuti: “Ndipo anati Yehova: ‘Tawona pali inepo pali malo, ndipo uime pathanthwe, ndipo kudzakhala pakupitira ulemerero wanga, ndidzakuika mu mpata wa thanthwe, ndi kukuphimba ndi dzanja langa, mpaka nditapitirira. Ndipo pamene ndichotsa dzanja langa udzawona m’mbuyo mwanga; koma nkhope yanga siidzawoneka.’”
M’chigwirizano ndi chimene Yehova nauza Mose ndi chimene mtumwi Yohane ananena, Mose sanawone thupi kapena mkhalidwe wathupi wa Mulungu. Zonse zimene Mose anawona zinali ulemerero wa kukhalapo kwaumulungu ukudutsa. Ngakhale pamenepo iye anayenera kuchinjirizidwa mwaumulungu. Mwachiwonekere, sanali Mulungu iyemwini amene Mose anawona.
Pamene Mose analankhula kwa Mulungu “pamaso ndi pamaso,” monga mmene chanenedwera pa Eksodo 33:11, iye sanali m’kugwirizana kowonana ndi Yehova. Katchulidwe kameneka kamasonyeza mtundu mu umene Mose analankhula ndi Mulungu, osati chimene anawona. Kulankhula ndi Mulungu “kopenyana ndi maso” kumasonyeza kukambitsirana kwa njira ziŵiri. Mofananamo, munthu angakambitsirane mwanjira ziŵiri pa lamya popanda kuwona munthu winayo.
Pamene Mose analankhula ndi Mulungu ndi kulandira malangizo kuchokera kwa iye, kulankhulanako sikunali kupyolera mwa masomphenya, monga mmene kaŵirikaŵiri zinaliri ndi aneneri ena. Ichi chikudziŵidwa pa Numeri 12:6-8, pamene timaŵerenga kuti: “Ndipo anati: ‘Tamvani tsopano mawu anga; pakakhala mneneri pakati pa inu, ine Yehova ndidzizindikiritsa kwa iye m’masomphenya, ndinena naye m’kulota. Satero mtumiki wanga Mose! Ndiye wokhulupirika m’nyumba mwanga monse. Ndimanena naye pakamwa ndi pakamwa, mowonekera, osati mophiphiritsa; ndipo amapenyerera mawonekedwe a Yehova.’” Ndi mlingaliro lotani mmene Mose anawonera “mawonekedwe a Yehova”?
Mose anawona “mawonekedwe a Yehova” pamene iye, Aroni, ndi amuna ena anali pa Phiri la Sinai. Pa Eksodo 24:10, palembedwa kuti: “Ndipo anapenya Mulungu wa Israyeli ndipo pansi pa mapazi ake panali ngati mayalidwe oyera a miyala yasafiri, ndi ngati thupi la thambo loti mbe.” Koma kodi ndimotani mmene Mose ndi amuna ena anafikira pa “kuwona Mulungu wa Israyeli,” popeza Mulungu anauza iye kuti, “Palibe munthu angandiwone ndi kukhala ndi moyo”? Versi 11 likulongosola, popeza limanena kuti: “Koma sanatulutse dzanja lake pa akulu ena a Israyeli, [koma anali ndi masomphenya a Mulungu wowona, NW] ndipo anapenya anadya namwa.” Chotero mawonekedwe a Mulungu amene Mose ndi ena anawona anali mwa masomphenya.
Oimira a Ungelo
Sichinakhale choyenerera kwa Mlengi wamkulu wa chilengedwe kubwera pansi kuchokera ku malo okhazikika kumwamba ndi cholinga chofuna kupereka uthenga kwa anthu ena. Pambali pa zochitika zitatu zolembedwa pamene mawu a Mulungu anamveka pamene Mwana wake anali padziko lapansi, Yehova nthaŵi zonse anagwiritsira ntchito angelo kutumiza mauthenga Ake. (Mateyu 3:17; 17:5; Yohane 12:28) Ngakhale Lamulo limene Mulungu anapereka kwa mtundu wa Israyeli pa Phiri la Sinayi linatumizidwa kupyolera mwa angelo, ngakhale kuti Mose anaimiridwa kukhala akulankhula mwachindunji kwa Mulungu iyemwini. Ponena za ichi, mtumwi Paulo analemba kuti: “Nanga Chilamulo tsopano? Chinawonjezeka chifuno chifukwa cha zolakwa, kufikira ikadza mbewu imene adailonjezera; ndipo chidakonzeka ndi angelo m’dzanja la nkhoswe.”—Agalatiya 3:19.
Kuti Mose m’chenicheni analankhula ndi mngelo yemwe mwaumwini anaimira Mulungu kukusonyezedwanso pa Machitidwe 7:38, pamene pamanena kuti: “Uyu ndiye amene anali mu mpingo m’chipululu pamodzi ndi mngelo wakulankhula naye m’phiri la Sinai, ndi makolo athu.” Mngelo ameneyo mwaumwini anali wolankhulira wa Yehova Mulungu, Mlengi, ndipo chotero analankhula kwa Mose ngati kuti anali Mulungu iyemwini akulankhula.
Mngelo amene anapereka uthenga wa Mulungu kwa Mose pa chitsamba choyaka moto analinso wolankhulira. Iye anazindikiritsidwa monga mngelo wa Yehova pa Eksodo 3:2, pamene timauzidwa kuti: “Ndipo [mngelo wa Yehova, NW] anawonekera m’chirangali chamoto chotuluka mkati mwa chitsamba.” Versi 4 likunena kuti: “Pamene Yehova anawona kuti adapatuka kukapenya, Mulungu ali mkati mwa chitsamba anamuitana.” Mu Versi 6, wolankhulira wa ungelo ameneyo kaamba ka Mulungu anati: “Ine ndine Mulungu wa atate wako, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake ndi Mulungu wa Yakobo.” Chotero pamene anali kulankhula ndi woimira waumwini ameneyo wa Mulungu, Mose analankhula ngati kuti anali kulankhula ndi Yehova iyemwini.—Eksodo 4:10.
M’mutu 6 wa Oweruza, timapeza chitsanzo china cha mwamuna wolankhula kwa Mulungu kupyolera mwa woimira wa ungelo. Versi 11 limazindikiritsa wonyamula uthengayo monga “mngelo wa Yehova.” Pamenepo timaŵerenga kuti: “Pamenepo anadza [mngelo wa Yehova, NW] nakhala patsinde pa thundu wokhala m’Ofira, wa Yosasi M’abieziri, ndi mwana wake Gideoni analikuwomba tirigu mopondera mphesa, awabisire Amidyani.” Mthenga ameneyu, “mngelo wa Yehova,” pambuyo pake akuimiridwa ngati kuti anali Yehova Mulungu iyemwini. Mu maversi 14 ndi 15, timaŵerenga kuti: “Pamenepo Yehova anamtembenukira [Gideoni] nati: ‘Muka nayo mphamvu yako iyi, nupulumutse Israyeli m’dzanja la Midyani. Sindinakutuma ndine kodi?’ Ndipo anati kwa iye: ‘Ha! Yehova. Ndidzapulumutsa Israyeli ndichiyani?’” Chotero mngelo wovala thupi la umunthu wowonedwa ndi Gideoni ndi amene analankhula naye akuimiridwa m’mbiri ya Baibulo ngati kuti anali Mulungu iyemwini. Mu versi 22, Gideoni akunena kuti: “Ndawona [mngelo, NW] wa Yehova maso ndi maso!” Mngelo analankhula mwachindunji chimene Mulungu anamuuza iye kulankhula. Chotero, Gideoni analankhula ndi Mulungu kupyolera mwa wolankhulira wa ungelo ameneyu.
Lingalirani, kachiŵirinso, nkhani ya Manowa ndi mkazi wake, makolo a Samsoni. Mbiri imeneyi imalankhulanso za mthenga wa ungelo ngati “mngelo wa Yehova” ndi “mngelo wa Mulungu wowona.” (Oweruza 13:2-18) Mu versi 22, Manowa ananena kwa mkazi wake kuti: “Tidzafa ndithu, pakuti tawona Mulungu.” Ngakhale kuti iye sanawonedi kwenikweni Yehova Mulungu, Manowa anadzimva mwanjira imeneyi chifukwa iye anawona wolankhulira waumwini wokhala m’thupi laumunthu wa Mulungu.
“Palibe Munthu Anawona Mulungu”
Tsopano chiri chothekera kumvetsetsa chifukwa chimene Abrahamu analankhula ndi wolankhulira wa ungelo wovala thupi laumunthu wa Mulungu ngati kuti anali kulankhula ndi Yehova Mulungu iyemwini. Popeza mngelo ameneyo analankhula mwachindunji chimene Mulungu anamfuna kunena kwa Abrahamu ndipo anali pamenepo mwaumwini kumuimira Iye, cholembera cha Baibulo chinakhoza kunena kuti “Yehova anawonekera kwa iye.”—Genesis 18:1.
Kumbukirani kuti wolankhulira wa ungelo wa Mulungu angatumize mauthenga Ake mwachindunji monga mmene lamya kapena wailesi imaperekera mawu athu kwa munthu wina. Chotero, chingamvetsetsedwe mmene Abrahamu, Mose, Manowa, ndi ena analankhulira ndi angelo ovala thupi laumunthu ngati kuti anali kulankhula ndi Mulungu. Pamene kuli kwakuti anthu oterowo anali okhoza kuwona angelo amenewa ndi ulemerero wa Yehova wounikiridwa ndi iwo, iwo sanali okhoza kuwona Mulungu. Chotero, ichi sichimatsutsana mwanjira iriyonse ndi mawu a mtumwi Yohane: “Kulibe munthu anawona Mulungu nthaŵi yonse.” (Yohane 1:18) Zimene amuna amenewo anawona anali oimira a ungelo ndipo osati Mulungu iyemwini.