Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Alephera Kumugwira Iye
PAMENE phwando la misasa lidakali mkati, atsogoleri a chipembedzo atumiza nduna za apolisi kukagwira Yesu. Iye sakuyesera kubisala. Yesu akupitirizabe kuphunzitsa mwapoyera, akumanena kuti: “Katsala kanthaŵi ndiri ndi inu, ndipo ndimuka kwa iye wondituma ine. Mudzafunafuna ine, osandipeza, ndipo pomwe ndiri ine, inu simungathe kudzapo.”
Ayudawo sakumvetsetsa, ndipo chotero akudzifunsa iwo eni: “Adzanka kuti uyu kuti ife sitikampeza iye? Kodi adzamuka kwa a Heleni obalalikawo ndi kuphunzitsa a Heleni? Mawu awa amene anena nchiyani, ‘Mudzandifunafuna osandipeza ine, ndipo komwe ndiri ine, inu simungathe kudzapo’?” Yesu, ndithudi, akulankhula ponena za imfa yake yomayandikira ndi chiwukiriro kupita kumwamba, kumene adani ake sangathe kutsatira.
Tsiku lachisanu ndi chiŵiri ndipo lomalizira la phwandolo lifika. M’mawa mulimonse mwa phwandolo, wansembe anathira madzi, omwe anatenga kuchokera pa chidikha cha Silomu, kotero kuti anayenda kufika kunsi kwa guwa la nsembe. Moyenerera akumakumbutsa anthuwo za chikondwerero cha tsiku ndi tsiku ichi, Yesu anafuula: “Ngati pali munthu wakumva ludzu, adze kwa ine, namwe. Iye wokhulupirira ine monga chilembo chinati, ‘Mitsinje ya madzi a moyo idzayenda, kutuluka mkati mwake.’”
M’chenicheni, Yesu pano akulankhula ponena za zotulukapo zazikulu pamene mzimu woyera udzatsanulidwa. Chaka chotsatira kutsanuliridwa kwa mzimu woyera kumeneku kunawoneka pa Pentekoste. Pamenepo, mitsinje ya madzi a moyo inatuluka pamene ophunzira 120 anayamba kutumikira kwa anthu. Koma kufikira pa nthawiyo, palibe mzimu m’lingaliro lakuti palibe ndi mmodzi yemwe wa ophunzira a Yesu amene ali wodzozedwa ndi mzimu woyera ndipo kuitanidwa ku moyo wakumwamba.
M’kuyankha ku chiphunzitso cha Yesu, ena ayamba kunena kuti: “M’neneriyo ndi uyu ndithu,” mwachiwonekere akulozera kwa m’neneri wokulirapo kuposa Mose yemwe analonjezedwa kubwera. Ena akunena kuti: “Uyu ndi Kristu.” Koma ena akutsutsa: “Kodi Kristu adza kutuluka mu Galileya? Kodi sichinati chilembo kuti Kristu adza kutuluka mwa mbewu ya Davide, ndi kuchokera ku Betelehemu, ku mudzi kumene kunali Davide?”
Chotero mtsutsano unakula pakati pa khamulo. Ena akufuna kuti Yesu agwidwe, koma palibe amene akuika manja ake pa iye. Pamene nduna za polisi zibwerera popanda Yesu, akulu ansembe ndi Afarisi akufunsa kuti: “Simunamtenga iye bwanji?”
“Nthaŵi yonse palibe munthu analankhula chotero,” ndunazo zinayankha.
Odzazidwa ndi mkwiyo, atsogoleri a chipembedzo anayamba kutonza, kuimira molakwa, ndi kutcha maina. Iwo akuwopsya: “Kodi mwasokeretsedwa inunso? Kodi wina wa akulu anakhulupirira iye, kapena wa Afarisi? Koma khamu iri losadziŵa chilamulo, likhala lotembereredwa.”
Pa ichi, Nikodemo, Mfarisi ndi mtsogoleri wa Ayuda (kunena kuti, chiwalo cha Bwalo Lalikulu Lamilandu la Yuda), sakufuna kulankhula m’malo mwa Yesu. Mungakumbukire kuti zaka ziŵiri ndi theka zapitazo, Nikodemo anabwera kwa Yesu usiku ndi kusonyeza chikhulupiriro chake mwa iye. Tsopano Nikodemo akunena kuti: “Kodi chilamulo chathu chiŵeruza munthu, osayamba kumva iye, ndi kuzindikira chimene achita?”
Afarisi akwiitsidwa koposa kuti mmodzi wa iwo akulankhula m’njira ya kuchinjiriza Yesu. “Kodi iwenso uli wotuluka mu Galileya?” iwo akupereka ndemanga. “Santhula nuwone kuti mu Galileya sanawuka m’neneri.”
Ngakhale kuti Malemba sanena mwachindunji kuti mneneri adzatuluka ku Galileya, iwo akulozadi kwa Kristu kukhala akuchokera kumeneko, akumanena kuti “kuwala kwakukulu” kudzawoneka m’gawo iri. Ndipo mosiyana ndi malingaliro olakwa, Yesu anabadwira mu Betelehemu, ndipo anali mbadwa ya Davide. Pamene kuli kwakuti Afarisi mwinamwake akudziwa za ichi, iwo mwachidziwikire ali ndi liwongo la kufalitsa malingaliro olakwa amene anthu ali nawo ponena za Yesu. Yohane 7:32-52; Yesaya 9:1, 2; Mateyu 4:13-17.
◆ Nchiyani chimene chikuchitika m’mawa muliwonse mwa phwando, ndipo ndimotani mmene Yesu angakokere chisamaliro ku ichi?
◆ Nchifukwa ninji nduna zalephera kugwira Yesu, ndipo ndimotani mmene atsogoleri achipembedzo akuvomerezera?
◆ Kodi Nikodemo ndani, nchiyani chimene chiri mkhalidwe wake kulinga kwa Yesu, ndipo ndimotani mmene iye akuchitidwira ndi Afarisi anzake?
◆ Ndi umboni wotani umene ulipo wakuti Kristu adzabwera kuchokera ku Galileya?