Lingaliro la Baibulo
‘Kusakhala a Dziko Lapansi’ Kodi Kumatanthauzanji?
M’ZAKA za zana lachinayi C.E., anthu zikwi zambiri odzitcha Akristu anasiya katundu wawo, achibale awo, ndi kakhalidwe kawo nkumakakhala kwa okha m’zipululu za Igupto. Anadzatchedwa kuti aankhore, liwu lochokera ku Chigiriki lakuti a·na·kho·reʹo, kutanthauza kuti “ndichoka.” Wolemba mbiri wina akulongosola kuti iwo anadzipatula kwa anzawo. Aankhorewo anaganiza kuti mwa kudzipatula kwa anthu, anali kumvera lamulo lachikristu la ‘kusakhala a dziko lapansi.’—Yohane 15:19.
Baibulo limalangizadi Akristu kuti ‘asachitidwe maŵanga ndi dziko lapansi.’ (Yakobo 1:27) Malemba amachenjeza momveka bwino kuti: “Akazi achigololo inu, kodi simudziŵa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.” (Yakobo 4:4) Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti Akristu afunikira kukhala aankhore, kumadzipatula kwa ena m’lingaliro lenileni? Kodi ayenera kumatalikirana ndi anthu amene samagwirizana nawo pazikhulupiriro zawo zachipembedzo?
Akristu Samadzipatula kwa Anthu Ena
Lingaliro la kusakhala a dziko lapansi lafotokozedwa m’nkhani zambiri za Baibulo zimene zimasonyeza kuti Akristu afunikira kudzipatula kwa anthu ‘osadziŵa’ Mulungu. (Yerekezerani ndi 2 Akorinto 6:14-17; Aefeso 4:18; 2 Petro 2:20.) Chotero Akristu oona, mwanzeru amapeŵa maganizo, kalankhulidwe, ndi khalidwe losemphana ndi njira zolungama za Yehova, monga kukhumba mwadyera chuma, kutchuka, ndi kupambanitsa kukonda zokondweretsa, monga mmene dziko limachitira. (1 Yohane 2:15-17) Amalekananso ndi dziko mwa kukhala chete pankhani zankhondo ndi zandale zadziko.
Yesu Kristu anati ophunzira ake ‘sadzakhala a dziko lapansi.’ Komanso anapemphera kwa Mulungu kuti: “Sindipempha kuti muwachotse iwo m’dziko lapansi, koma kuti muwasunge iwo kuletsa woipayo.” (Yohane 17:15) Mwachionekere, Yesu sanafune kuti ophunzira ake azidzipatula kwa anthu ena, kupeŵa kulankhula ndi aliyense wosakhala Mkristu. Ndithudi, kudzipatula kungalepheretse Mkristu kukwaniritsa ntchito yake yolalikira ndi kuphunzitsa “pabwalo ndi m’nyumba m’nyumba.”—Machitidwe 20:20; Mateyu 5:16; 1 Akorinto 5:9, 10.
Uphungu wakuti akhale osachitidwa maŵanga ndi dziko lapansi sumapatsa Akristu chifukwa chilichonse chodzionera monga oposa ena. Oopa Yehova amada “kudzikuza.” (Miyambo 8:13) Agalatiya 6:3 amati “ngati wina ayesa ali kanthu pokhala ali chabe, adzinyenga yekha.” Amene amadziona ngati oposa anzawo akudzinyenga okha chifukwa “onse anachimwa, napereŵera pa ulemerero wa Mulungu.”—Aroma 3:23.
‘Samachitira Mwano Munthu Aliyense’
M’tsiku la Yesu kunali anthu amene anali kunyoza onse omwe sanali a zipembedzo zawo. Ena a iwo anali Afarisi. Anali odziŵa bwino Chilamulo cha Mose ngakhalenso tinthu tating’onong’ono tamwambo wachiyuda. (Mateyu 15:1, 2; 23:2) Ankadzitama chifukwa chotsatira mosamalitsa miyambo yambiri yachipembedzo. Afarisi ankachita ngati kuti anali oposa ena chabe chifukwa cha nzeru zawo ndi udindo wawo wachipembedzo. Anasonyeza mzimu wawo wakuti ndi opatulika ndipo onyansidwa ndi ena mwa kunena kuti: “Khamu ili losadziŵa chilamulo, likhala lotembereredwa.”—Yohane 7:49.
Afarisi anali nalo ngakhale dzina lonyozera anthu osakhala Afarisi. Dzina lachihebri lakuti ʽam ha·ʼaʹrets poyamba anali kuligwiritsira ntchito bwino potchula anthu ena onse. Koma m’kupita kwa nthaŵi atsogoleri achipembedzo odzitukumulawo a Yuda anasintha lingaliro la ʽam ha·ʼaʹrets nkukhala lonyoza. A zipembedzo zina, kuphatikizapo odzitcha Akristu, agwiritsira ntchito mawu onga “akunja” (pagan) ndi “amitundu” (heathen) monyoza potchula anthu a zikhulupiriro zachipembedzo zina.
Komabe, kodi Akristu a m’zaka za zana loyamba anawaona bwanji aja amene anali asanalandire Chikristu? Ophunzira a Yesu analangizidwa kuchita ndi osakhulupirira “mofatsa” ndi “mwaulemu waukulu.” (2 Timoteo 2:25; 1 Petro 3:15, NW) Mtumwi Paulo anasonyeza chitsanzo chabwino pazimenezi. Anali wofikirika, osati wodzitukumula. M’malo modzikweza pakati pa ena, anali wodzichepetsa ndi wolimbikitsa. (1 Akorinto 9:22, 23) M’kalata yake youziridwa yolembera Tito, Paulo akutilangiza kuti ‘tisachitire mwano munthu aliyense, tisakhale andewu, tikhale aulere, nitionetsere chifatso chonse pa anthu onse.’—Tito 3:2.
M’Baibulo liwu lakuti “wosakhulupirira” nthaŵi zina limagwiritsiridwa ntchito potchula anthu osakhala Akristu. Komabe, palibe umboni wakuti liwu lakuti “wosakhulupirira” linagwiritsiridwa ntchito monga dzina kapena chizindikiro chawo choyenera iyayi. Ndithudi, silinagwiritsiridwe ntchito mopeputsa kapena monyoza anthu osakhala Akristu, pakuti zimenezo zikanakhala zosemphana ndi mapulinsipulo a Baibulo. (Miyambo 24:9) Lerolino Mboni za Yehova zimapeŵa kukhala zaukali kapena zodzitukumula pochita ndi osakhulupirira. Zimaona kuti ndi mwano kutchula achibale kapena anansi osakhala Mboni ndi mawu onyoza. Zimamvera uphungu wa Baibulo wakuti: “Kapolo wa Ambuye . . . akhale . . . waulere pa onse.”—2 Timoteo 2:24.
‘Chitirani Onse Chokoma’
Nkofunika kuzindikira ngozi za kuyanjana ndi dziko, makamaka ndi aja amene alibiretu ulemu pa malamulo a Mulungu. (Yerekezerani ndi 1 Akorinto 15:33.) Komabe, pamene Baibulo likulangiza kuti ‘tichitire onse chokoma,’ liwu lakuti “onse” likuphatikizapo amene siali Akristu. (Agalatiya 6:10) Mwachionekere, Akristu a m’zaka za zana loyamba anadya pamodzi ndi osakhulupirira. (1 Akorinto 10:27) Choncho, lero Akristu amachita mosamala ndi anthu osakhulupirira, amawaona ngati anthu anzawo.—Mateyu 22:39.
Kungakhale kulakwa kuganiza kuti munthu wina ngwachabe kapena woipa chabe chifukwa chakuti sadziŵa choonadi cha Baibulo. Mikhalidwe ndi anthu amasiyana. Chotero, Mkristu aliyense ayenera kudziŵa malire amene angadziikire pocheza ndi osakhulupirira. Komabe, sikoyenera ndipo malemba samavomereza kuti Mkristu achite kudzipatula kwenikweni monga anachitira aankhore kapena kuti adzione ngati woposa ena monga anadzionera Afarisi.