Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Kuphunzitsa Kowonjezereka pa Tsiku Lachisanu ndi Chiŵiri
TSIKU lotsirizira la Phwando la Misasa, tsiku lachisanu ndi chiŵiri, likuchitikabe. Yesu akuphunzitsira m’mbali ya kachisi yotchedwa “mosungira ndalama.” Umu mwachiwonekere muli m’dera lotchedwa Chipinda cha Akazi kumene kuli chigawo m’chimene anthu amaikako zopereka zawo.
Usiku uliwonse mkati mwa phwandolo, pali kusonyeza kwa kuwunika kwapadera m’chigawochi cha kachisi. Mitengo yaikulu inayi yokhala ndi nyali yaikidwa pano, iriyonse yokhala ndi mbale zinayi zodzaza ndi mafuta. Kuwunika kochokera ku mbale 16 zimenezi za mafuta owunikira kuli kwamphamvu mokwanira kokhoza kuwunikira malo ozungulirawo pa mtundu waukulu usiku. Chimene Yesu tsopano akunena chingakumbutse amvetseri ake ponena za tsikuli. “Ndine kuwunika kwa dziko lapansi,” Yesu analengeza tero. “Iye wonditsata ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala nako kuwunika kwa moyo.”
Afarisi atsutsa: “Muchita umboni wa inu nokha; umboni wanu suli wowona.”
M’kuyankha Yesu akunena kuti: “Ndingakhale ndichita umboni wa ine ndekha, umboni wanga uli wowona, chifukwa chakuti ndidziŵa kumene ndinachokera, ndi kumene ndimuka. Koma inu sumudziŵa kumene ndichokera ndi kumene ndimukako.” Iye akuwonjezera kuti: “Ine ndine wakuchita umboni wa ine ndekha ndipo Atate amene anandituma ine andichitira umboni.”
“Ali kuti Atate wanu?” Afarisi akufuna kudziŵa.
“Simudziŵa kapena ine kapena Atate wanga,” Yesu akuyankha tero. “Mukanandidziŵa ine, mukadadziŵanso Atate wanga.” Ngakhale kuti Afarisi akufunabe kumgwira Yesu, palibe aliyense yemwe akumkhudza.
“Ndimuka ine,” Yesu kachiŵirinso akunena tero. “Kumene ndimukako inu sumungadze.”
Pa ichi Ayuda ayamba kuzizwitsidwa: “Kodi adzadzipha yekha? Pakuti anena kuti, ‘Kumene ndimukako ine simungadze.’”
“Inu ndinu ochokera pansi pano,” Yesu akulongosola tero. “Ine ndine wochokera kumwamba. Inu ndinu a dziko lino lapansi; sindiri ine wa dziko lino lapansi.” Kenaka iye akuwonjezera kuti: “Ngati simundikhulupirira ine, mudzafa m’machimo anu.”
Ndithudi, Yesu, akulozera ku kukhalapo kwake asanakhale munthu ndi nsonga ya kuti iye ali Mesiya wolonjezedwayo, kapena Kristu. Ngakhale kuli tero, iwo akufunsa, mosakaikira ndi chikaikiritso chokulira: “Kodi ndinu yani?”
Pamaso pa kukana kwawo, Yesu akuyankha: “Nchifukwa ninji ndikulankhula kwa inu?” Komabe iye akupitiriza kunena kuti: “Iye wondituma ine ali wowona, ndipo zimene ndazimva kwa iye zomwezo ndilankhula kwa dziko lapansi.” Yesu akupitirizabe: “Pamene mutadzamkweza mwana wa munthu, pomwepo mudzazindikira kuti ine ndine, ndipo sindichita kanthu kwa ine ndekha, koma monga anandiphunzitsa Atate, ndilankhula izi. Ndipo wondituma ine ali ndi ine; sanandisiya ine pa ndekha; chifukwa ndichita ine zimene zimkondweretsa iye nthaŵi zonse.”
Pamene Yesu anena zinthu izi, ambiri aika chikhulupiriro mwa iye. Kwa iwo iye akunena kuti: “Ngati mukhala inu m’mawu anga, muli akuphunzira anga ndithu; ndipo mudzazindikira chowonadi, ndipo chowonadi chidzakumasulani.”
“Tiri mbewu ya Abrahamu,” otsutsa ake alowereramo, “ndipo sitinakhala akapolo a munthu nthaŵi iriyonse. Munena bwanji, ‘Mudzayesedwa aufulu’?”
Ngakhale kuti Ayuda akhala kaŵirikaŵiri pansi pa kulamuliridwa kwa chilendo, iwo samavomereza wodidikiza aliyense kukhala mbuye wawo. Iwo akana kuitanidwa akapolo. Koma Yesu akuchipanga kukhala chowonekera kuti iwo ndithudi ali akapolo. Mwanjira yotani? “Indetu, indetu ndinena kwa inu,” Yesu akutero, “yense wakuchita chimo ali kapolo wa chimolo.”
Kukana kuvomereza ukapolo wawo ku uchimo kukuika Ayuda m’malo owopsya. “Kapolo sakhala m’nyumba nthaŵi zonse,” Yesu akulongosola tero. “Mwana ndiye akhala nthaŵi yonse.” Popeza kuti kapolo alibe kuyenera kwa cholowa, iye angakhale m’ngozi ya kuthamangitsidwa nthaŵi iriyonse. Koma mwana m’chenicheni wobadwira mmenemo kapena kusungidwa mmenemo amakhala “kosatha,” uko ndiko kuti, malinga ngati iye ali wamoyo.
“Chotero ngati Mwana akumasunali inu,” Yesu akupitirizabe, “inu mudzakhala aufulu.” Chotero, chowonadi chimene chimamasula anthu chiri chowonadi chonena za Mwana, Yesu Kristu. Chiri kokha mwanjira ya nsembe ya moyo wangwiro wa munthu mmene aliyense angamasulidwire kuchoka ku uchimo wodzetsa imfa. Yohane 8:12-36.
◆ Ndi kuti kumene Yesu akuphunzitsa pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri? Kodi nchiyani chimene chikuchitika usiku umenewo, ndipo kodi ndimotani mmene ichi chikulongosolera kuphunzitsa kwa Yesu?
◆ Kodi nchiyani chimene Yesu akunena ponena za chiyambi chake, ndipo kodi nchiyani chimene ichi chiyenera kuvumbula ponena za kuzindikiridwa kwake?
◆ Ndi mwanjira yotani mmene Ayuda aliri akapolo, koma ndi chowonadi chotani chimene chidzawamasula iwo?