PHUNZIRO 18
Kodi Akhristu Enieni Mungawadziwe Bwanji?
Anthu mabiliyoni ambirimbiri amanena kuti ndi Akhristu. Koma anthu amenewa amakhulupirira zinthu zosiyana ndiponso satsatira mfundo zofanana pa moyo wawo. Ndiye kodi Akhristu enieni tingawadziwe bwanji?
1. Kodi mawu akuti Mkhristu amatanthauza chiyani?
Mawu akuti Mkhristu amatanthauza wophunzira kapena kuti wotsatira wa Yesu Khristu. (Werengani Machitidwe 11:26.) Ndiye kodi Akhristu amasonyeza bwanji kuti ndi ophunzira a Yesu? Yesu anati: “Mukamasunga mawu anga nthawi zonse, ndiye kuti ndinudi ophunzira anga.” (Yohane 8:31) Zimenezi zikutanthauza kuti Akhristu enieni ayenera kutsatira zimene Yesu anaphunzitsa. Ndipo mofanana ndi Yesu yemwe ankagwiritsa ntchito Malemba pophunzitsa, zimene Akhristu enieni amakhulupirira zimachokeranso m’Baibulo.—Werengani Luka 24:27.
2. Kodi Akhristu enieni amasonyeza bwanji kuti amakonda ena?
Yesu anauza otsatira ake kuti “Mukondane monga mmene inenso ndakukonderani.” (Yohane 15:12) Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ankakonda ophunzira ake? Iye ankapeza nthawi yocheza nawo, kuwalimbikitsa komanso kuwathandiza. Ndipotu mpaka anafika powafera. (1 Yohane 3:16) N’chimodzimodzinso Akhristu enieni, iwo samangolankhula za chikondi, koma amachita zinthu zosonyeza kuti amakonda anzawo. Zolankhula ndi zochita zawo zimasonyeza kuti ndi anthu achikondidi.
3. Kodi ndi ntchito iti imene Akhristu enieni amaigwira mwakhama?
Yesu anapatsa ophunzira ake ntchito yoti azigwira. Iye “anawatumiza kukalalikira Ufumu wa Mulungu.” (Luka 9:2) Sikuti Akhristu oyambirira ankalalikira m’malo olambirira okha, koma ankalalikiranso m’malo opezeka anthu ambiri ndi m’nyumba za anthu. (Werengani Machitidwe 5:42; 17:17.) Masiku ano Akhristu enieni nawonso amalalikira mfundo za m’Baibulo kulikonse komwe angapeze anthu. Popeza amakonda anthu, iwo amasangalala kugwiritsa ntchito nthawi ndi mphamvu zawo pouzako ena uthenga wa m’Baibulo, womwe umatonthoza anthu ndi kuwapatsa chiyembekezo.—Maliko 12:31.
FUFUZANI MOZAMA
Onani zimene zingakuthandizeni kusiyanitsa Akhristu enieni ndi anthu amene satsatira zimene Yesu anaphunzitsa komanso kuchita.
4. Amafufuza choonadi cha m’Baibulo
Anthu ena amene amati ndi Akhristu samaona kuti choonadi cha m’Baibulo ndi chofunika ndipo samachigwiritsa ntchito pa moyo wawo. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso lotsatirali.
Kodi matchalitchi ena a Chikhristu amaphunzitsa zinthu ziti zosiyana ndi zimene Yesu anaphunzitsa?
Yesu ankaphunzitsa choonadi chochokera m’Mawu a Mulungu. Werengani Yohane 18:37, kenako mukambirane funso ili:
Malinga ndi zimene Yesu ananena, kodi tingawazindikire bwanji Akhristu amene ali “kumbali ya choonadi”?
5. Amaphunzitsa choonadi cha m’Baibulo
Yesu asanabwerere kumwamba, anauza otsatira ake kuti azigwira ntchito yomwe ikuchitikabe masiku ano. Werengani Mateyu 28:19, 20 ndi Machitidwe 1:8, kenako mukambirane funso ili:
Kodi Akhristu akufunika kugwira ntchito yolalikira mpaka liti komanso kufikira pati?
6. Amachita zimene amaphunzitsa
N’chifukwa chiyani a Tom anafika povomereza kuti apeza choonadi? Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa.
Muvidiyoyi, n’chifukwa chiyani a Tom anasiya kupita ku chipembedzo chilichonse?
N’chiyani chinawathandiza kutsimikizira kuti apeza choonadi?
Ntchito zathu ndi zimene zimatichitira umboni. Werengani Mateyu 7:21, kenako mukambirane funso ili:
Kodi Yesu amaona kuti chofunika n’chiyani, kungonena zimene timakhulupirira kapena kuchita zimene timakhulupirirazo?
7. Amakondana
Kodi Akhristu alolerapo kuika moyo wawo pangozi chifukwa cha Akhristu anzawo? Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa.
Muvidiyoyi, n’chiyani chinachititsa kuti M’bale Likhwide alolere kuika moyo wake pangozi kuti M’bale Johansson asaphedwe?
Kodi mukuganiza kuti anachita zinthu ngati Mkhristu weniweni?
Werengani Yohane 13:34, 35, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi Akhristu enieni ayenera kuchita bwanji zinthu ndi anthu amitundu ina kapenanso ochokera ku mayiko ena?
Nanga angachite bwanji zimenezi pa nthawi yankhondo?
ZIMENE ENA AMANENA: “Akhristu ena akhala akuchita zinthu zoipa kwambiri, ndiye zingatheke bwanji kuti chipembedzo chawo chikhale chabwino?”
Kodi munthu wotereyu mungamuwerengere lemba liti lomwe lingamuthandize kuzindikira Akhristu enieni?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Akhristu enieni amatsatira zimene Baibulo limaphunzitsa pa moyo wawo, amasonyezana chikondi chololera kuvutikira ena komanso amalalikira choonadi cha m’Baibulo.
Kubwereza
Kodi zimene Akhristu enieni amakhulupirira zimachokera kuti?
Kodi Akhristu enieni amasonyeza khalidwe liti limene lingatithandize kuwazindikira?
Kodi Akhristu enieni amagwira ntchito iti?
ONANI ZINANSO
Dziwani zambiri zokhudza gulu la anthu omwe amayesetsa kutengera chitsanzo cha Yesu Khristu komanso kutsatira zimene anaphunzitsa.
Onani zimene zinathandiza munthu wina yemwe anali sisitere kuti akhale m’banja lokondana lapadziko lonse.
“Ankagwiritsa Ntchito Baibulo Poyankha Funso Lililonse” (Nsanja ya Olonda, April 1, 2014)
Onani zimene Akhristu enieni amachita posonyeza kuti amakonda Akhristu anzawo omwe akufunikira chithandizo.
Kuthandiza Abale Athu Kukachitika Ngozi Zam’chilengedwe—Kachigawo Kake (3:57)
Yesu anafotokoza zinthu zomwe zingathandize anthu kuzindikira otsatira ake. Fufuzani kuti muone mmene Akhristu oyambirira ndi Akhristu enieni masiku ano amakwaniritsira zimenezi.
“Kodi Mungawadziwe Bwanji Akhristu Oona?” (Nsanja ya Olonda, March 1, 2012)