MUTU 68
Mwana wa Mulungu Ndiye “Kuwala kwa Dziko”
YESU ANAFOTOKOZA KUTI MWANA NDI NDANI
N’CHIFUKWA CHIYANI YESU ANANENA KUTI AYUDA ANALI AKAPOLO?
Pa tsiku lomaliza la Chikondwerero cha Misasa, lomwe linali tsiku la 7, Yesu anapita kukaphunzitsa kukachisi koma pa nthawiyi anali kumbali ina ya kachisiyo yomwe inkadziwika kuti “malo a zopereka.” (Yohane 8:20; Luka 21:1) Malowa anali kubwalo lina la kachisiyo komwe kunkakhala azimayi ndipo n’kumene anthu ankaponya zopereka.
Usiku uliwonse pa nthawi yonse ya chikondwereroyi, malowa ankawala kwambiri chifukwa kunali zoikapo nyale zikuluzikulu zokwana 4. Choikapo nyale chilichonse chinali ndi beseni lalikulu lodzaza ndi mafuta. Nyalezo zinkawala kwambiri moti zinkaunikira malo aakulu ndithu. Zimene Yesu ananena ziyenera kuti zinakumbutsa anthu mmene malowa ankawalira usiku. Iye anati: “Ine ndine kuwala kwa dziko. Wonditsatira ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala nako kuwala kwa moyo.”—Yohane 8:12.
Koma Afarisi anatsutsa zimene Yesu ananenazi. Iwo ananena kuti: “Iwe umadzichitira wekha umboni koma umboni wakowo si woona ayi.” Yesu anawayankha kuti: “Ngakhale kuti ndimadzichitira ndekha umboni, umboni wanga ndi woona, chifukwa ndikudziwa kumene ndinachokera ndi kumene ndikupita. Koma inu simukudziwa kumene ndinachokera ndi kumene ndikupita.” Anawauzanso kuti: “M’chilamulo chanu chomwechi analembamo kuti, ‘Umboni wa anthu awiri ndi woona.’ Ineyo pandekha ndimadzichitira umboni, ndipo Atate amene anandituma amandichitiranso umboni.”—Yohane 8:13-18.
Posonyeza kuti sankagwirizana ndi zimene Yesu ananena, Afarisiwo anamufunsa kuti: “Atate wako ali kuti?” Yesu anawayankha kuti: “Inu simukundidziwa ine kapena Atate wanga. Mukanandidziwa ine, mukanadziwanso Atate wanga.” (Yohane 8:19) Ngakhale kuti Afarisiwo ankafuna kuti Yesu amangidwe, palibe aliyense amene anamuyandikira kuti amugwire.
Kenako Yesu anabwerezanso zimene ananena zija kuti: “Ine ndikuchoka ndipo mudzandifunafuna, koma mudzafabe m’tchimo lanu. Kumene ine ndikupita inu simungathe kukafikako.” Ayudawo sanamvetse zimene Yesu ananena moti anayamba kudabwa n’kuyamba kufunsana kuti: “Kodi akufuna kudzipha? Nanga n’chifukwa chiyani akunena kuti, ‘Kumene ine ndikupita inu simungathe kukafikako?’” Iwo sanamvetse zimene Yesu ankatanthauza chifukwa sankadziwa kumene anachokera. Koma Yesu anafotokoza kuti: “Inu ndinu ochokera pansi pano, ine ndine wochokera kumwamba. Inu ndinu ochokera m’dziko lino, ine si wochokera m’dziko lino.”—Yohane 8:21-23.
Ponena mawu amenewa Yesu anasonyeza kuti anali kumwamba asanabwere padziko lapansi komanso kuti iye anali Mesiya kapena kuti Khristu, amene atsogoleri achipembedzowa ankamuyembekezera. Komabe, iwo anamufunsa monyoza kuti: “Kodi iwe ndiwe ndani?”—Yohane 8:25.
Ngakhale kuti Ayudawa ankatsutsa komanso kukana zimene Yesu anawauza, iye anawayankha kuti: “N’chifukwa chiyani ndikudzivuta kulankhula nanu?” Komabe anayamba kufotokoza za Atate wake komanso chifukwa chimene Ayuda ankayenera kumvera zimene Mwana ankanena. Iye anati: “Amene anandituma ine amanena zoona. Zimene ndinamva kwa iye, zomwezo ndikuzilankhula m’dzikoli.”—Yohane 8:25, 26.
Mosiyana ndi Ayuda omwe sankakhulupirira Mulungu, Yesu analankhula zinthu zimene zinasonyeza kuti ankakhulupirira kwambiri Atate wake chifukwa ananena kuti: “Mukadzamukweza Mwana wa munthu, pamenepo mudzadziwa kuti ine ndine amene munali kumuyembekezera uja, ndi kutinso sindichita kanthu mongoganiza ndekha. Koma ndimalankhula zinthu izi ndendende mmene Atate anandiphunzitsira. Ndipo amene ananditumayo ali ndi ine. Iye sandisiya ndekha, chifukwa ndimachita zinthu zomukondweretsa nthawi zonse.”—Yohane 8:28, 29.
Komabe Ayuda ena anakhulupirira Yesu ndipo iye anawauza kuti: “Mukamasunga mawu anga nthawi zonse, ndiye kuti ndinudi ophunzira anga. Mudzadziwa choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.”—Yohane 8:31, 32.
Yesu atanena kuti choonadi chidzakumasulani, Ayuda ena anadabwa. Iwo anamutsutsa pomuuza kuti: “Ifetu ndife ana a Abulahamu ndipo sitinakhalepo akapolo a munthu. Tsopano iwe ukunena bwanji kuti, ‘Mudzamasulidwa’?” Ayudawo ankadziwa kuti nthawi zina ankatsatira miyambo komanso zikhulupiriro zachikunja koma ankakana zoti anali akapolo. Koma Yesu anawauza mosabisa mawu kuti pa nthawiyo anali akadali akapolo. Iye anawauza kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, Aliyense wochita tchimo ndi kapolo wa tchimo.”—Yohane 8:33, 34.
Ayudawo anataya mwayi waukulu chifukwa chokana kuvomereza kuti anali akapolo a uchimo. Yesu ananena kuti: “Kapolo sakhala m’banjamo kwamuyaya, mwana ndiye amakhalamo kwamuyaya.” (Yohane 8:35) Kapolo sankakhala ndi mwayi wolandira nawo cholowa ndipo ankatha kumuthamangitsa nthawi iliyonse. Mwana wobadwa m’banjalo kapena amene waleredwa m’banjalo, ndi amene ankakhala m’banjamo “kwamuyaya” kapena kuti kwa moyo wake wonse.
Choncho kudziwa zoona zenizeni zokhudza Mwanayo n’kumene kukanathandiza anthu kuti amasuke ku imfa yomwe inabwera chifukwa cha uchimo. N’chifukwa chake Yesu ananena kuti: “Ngati Mwana wakumasulani, mudzakhaladi omasuka.”—Yohane 8:36.