Chilungamo Osati Miyambo Yapakamwa
“Ngati chilungamo chanu sichichuluka koposa chija cha alembi ndi Afarisi, mwanjira iriyonse simudzalowa ufumu wakumwamba.”—MATEYU 5:20, “NW.”
1, 2. Kodi chinachitika nchiyani Yesu asanapereke Ulaliki wake wa pa Phiri?
YESU anali anachezera usiku wonse paphiri. Nyenyezi zinali mbuu m’mwamba. Nyama zausiku zazing’onozing’ono zinkawayulawayula m’thengo. Chakum’mawa madzi a Nyanja ya Galileya ankakhapira pagombe mwabata. Komatu Yesu anakumva pang’ono kuphokosera kwabwinoku, kokhalitsa bata komuzungulira. Iye anachezera usiku wonse akupemphera kwa Atate wake wakumwamba, Yehova. Iye anafunikira chitsogozo cha Atate wake. Tsiku lomwe linali kutsogolo kwake linali lowopsyadi.
2 Kum’mawa kunawonetsera kuwala kosonyeza kuti kukucha. Mbalame zinayamba kuwuluka, zikumalira mwadongosolo. Maluwa amthengo anandengumitsidwa mwabata ndi mphepo. Pamene cheza choyamba chadzuŵa chinawalikira m’chizimezime, Yesu anawaitana ophunzira ake kudza kwa iye ndipo pakati pawo anasankhapo 12 kuti akhale atumwi ake. Atangotero, iye limodzi ndi onsewo, anatsikira kunsi kwa phiri. Makamu a anthu adayamba kale kuwonedwa akubwera piringupiringu kuchokera ku Galileya, Turo ndi Sidoni, Yudeya ndi Yerusalemu. Iwo anabwera kudzachiritsidwa matenda awo. Mphamvu yopatsidwa ndi Yehova inkatuluka mwa Yesu pamene ambiri anamkhudza ndi kuchiritsidwa. Iwo anabweranso kudzamva mawu ake omwe anali ngati mankhwala ochiritsa miyoyo yawo yovutitsidwa.—Mateyu 4:25; Luka 6:12-19.
3. Kodi nchifukwa ninji ophunzira ndi makamu ankayembekezera molakalaka kufuna kumva pamene Yesu anayamba kulankhula?
3 M’misonkhano yawo ya kuphunzitsa wamba, arabi anazoloŵera kukhala pansi, ndipo m’mawa mwa ngululu yeniyeniyi ya 31 C.E., ichi nchimene Yesu anachichita, mwachiwonekere pamalo athyathyathya pamwamba pa phiri. Pamene ophunzira ake ndi makamuwo anawona chimenechi, iwo anazindikira kuti chinthu china chapadera chinali m’njira, chotero anasonkhana momzungulira namayembekezera kanthu kena. Pamene iye anayamba kulankhula, iwo ankayembekezera mawu ake molakalaka; pamene anamaliza pambuyo pake, iwo anatsala ozizwitsidwa ndi zimene anazimva. Tiyeni tiwone chifukwa chake.—Mateyu 7:28.
Mitundu Iŵiri ya Chilungamo
4. (a) Kodi ndi mitundu iŵiri iti ya chilungamo yomwe inkakambitsiridwapo? (b) Kodi nchiyani chimene chinali chifuno chake cha miyambo yapakamwayi, ndipo kodi chinakwaniritsidwa?
4 Mu Ulaliki wake wa pa Phiri, wosimbidwa ponse paŵiri pa Mateyu 5:1–7:29 ndi pa Luka 6:17-49, Yesu anasiyanitsa magulu aŵiriwa mosabisa kukhala: alembi ndi Afarisi ndiyeno anthu wamba amene anatsenderezedwa ndi iwo. Iye analankhula za mitundu iŵiri ya chilungamo, chilungamo chonyenga cha Afarisi ndi chilungamo chowona cha Mulungu. (Mateyu 5:6, 20) Chilungamo chodzipangira cha Afarisi chinazikidwa m’miyambo yapakamwa. Iyi inayambidwa m’zaka za zana lachiŵiri B.C.E. monga “chotetezera Chilamulo” kuchichinjiriza kuloŵereredwa ndi Chihelene (miyambo Yachigiriki). Iyi inadzalingaliridwa kukhala mbali ya Chilamulo. Kwenikweni, alembi anaipendadi miyambo yapakamwayi kukhala yaikulu kuposa Chilamulo. Mishnah ikuti: “Kulabadira mawu a Alembi [miyambo yawo yapakamwa] kunagwira ntchito mwathithithi kwenikweni kuposa kulabadira mawu a Chilamulo cholembedwa.” Chotero, mmalo mwa kukhala “chotetezera Chilamulo” kuti chichinjirizidwe, miyambo yawo inafooketsa Chilamulo ndikuchipanga kukhala chopanda pake, mongatu mmene Yesu ananenera kuti: “Bwino mukaniza lamulo la Mulungu, kuti musunge mwambo wanu.”—Marko 7:5-9; Mateyu 15:1-9.
5. (a) Kodi ndiuti womwe unali mkhalidwe wa anthu wamba amene anabwera kudzamva Yesu, ndipo kodi analingaliridwa motani ndi alembi ndi Afarisi? (b) Kodi nchiyani chimene chinaipanga miyambo yapakamwayi kukhala katundu wolemetsa pamapewa a anthu ogwira ntchito?
5 Anthu wamba amene anathamangira kukamva Yesu anali anjala mwauzimu, pokhala “okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.” (Mateyu 9:36) Ndi kunyada kodzitama alembi ndi Afarisi anawanyoza iwo, akumawatcha ʽam-ha·ʼaʹrets (anthu a m’dziko), ndikuwapeputsa kukhala mbuli, ochimwa otembereredwa osayenerera chiukiriro chifukwa chakuti sanasunge miyambo yapakamwa. Podzafika m’nthaŵi ya Yesu miyambo imeneyi inali itakhala yambirimbiri ndipo inakhala chinthu chopinga zedi chonga kulamulira munthu kuti azingotolatola nyena za nsabwe—yodzaladi ndi miyambo yakudya nthaŵi—kwakuti palibe munthu wogwira ntchito akanatha kuilabadira. Nkosadabwitsa kuti Yesu anatsutsa miyamboyi kukhala ‘akatundu olemera pamapewa a anthu.’—Mateyu 23:4; Yohane 7:45-49.
6. Kodi chinali chochititsa chidwi nchiyani ndi chitsutso chotsegulira cha Yesu, ndipo kodi chinasonyeza kusintha kotani kwa ophunzira ake ndi kwa alembi ndi Afarisi?
6 Chotero pamene Yesu anakhala pansi m’mbali mwa phiri, anthu omwe anayandikira pafupi kudzamvetsera anali ophunzira ake ndi makamu anjala yauzimu. Anthuwa ayenera kukhala anakumva kutsutsa kwake koyambirirako kukhala kochititsa chidwi. ‘Achimwemwe ali osauka, achimwemwe ali akumva njala, achimwemwe ali akulira, achimwemwe ali odedwa.’ Koma kodi ndani amene angakhale achimwemwe pamene ali osauka, akumva njala, akulira, ndi kudedwa? Ndipo masoka analengezedwa kwa omwe anali achuma, odya bwino, oseka, ndi okhumbiridwa! (Luka 6:20-26, NW) M’mawu ochepa okha, Yesu anasintha kudzikweza konse kwamwambo ndi miyezo ya anthu yovomerezedwayo. Kunali kusintha maudindo kwadzawoneni, kogwirizana ndi mawu a Yesu apambuyo pake awa: ‘Pakuti yense wakudzikuza yekha adzachepetsedwa; koma wodzichepetsa yekha adzakulitsidwa.’—Luka 18:9-14.
7. Kodi mawu otsegulira a Yesu anali ndi chiyambukiro chotani pa khamu la anthu anjala yauzimu omvetsera Yesu?
7 Mosiyana ndi alembi ndi Afarisi odzikhutiritsa okha, awo obwera kwa Yesu m’mawa mmenemu anali ozindikira za mkhalidwe wawo wauzimu womvetsa achisoni. Mawu ake otsegulira anawapatsa chiyembekezo: “Achimwemwe ali awo ozindikira kusowa kwawo kwauzimu, popeza kuti ufumu wakumwamba uli wawo.” Ndipo mzimu wawo udakondwa chotani nanga pamene iye anawonjezera kuti: “Achimwemwe ali awo akumva njala ndi ludzu la chilungamo, popeza kuti adzakhutitsidwa”! (Mateyu 5:3, 6, NW; Yohane 6:35; Chibvumbulutso 7:16, 17) Inde, adzakhutitsidwa ndi chilungamo, koma osati ndi chinyengo cha Afarisi.
‘Kudziyesera Olungama Pamaso pa Anthu’ Nkosakwanira
8. Kodi nchifukwa ninji ena ayenera kukhala anadabwa mmene chilungamo chawo chikachulukira kuposa cha alembi ndi Afarisi, chikhalirechobe nchifukwa ninji chinafunikira kutero?
8 “Ngati chilungamo chanu sichichuluka koposa chija cha alembi ndi Afarisi,” Yesu akuti, “mwanjira iriyonse simudzalowa ufumu wakumwamba.” (Mateyu 5:17-20, NW; onani Marko 2:23-28; 3:1-6; 7:1-13.) Ena ayenera kukhala analingalira kuti: ‘Kodi pali munthu angakhale wolungama kuposa Afarisi? Iwo amasala kudya ndikupemphera ndi kusunga chachikhumi ndikupereka mphatso zaulere ndikuthera miyoyo yawo akuphunzira Chilamulo. Kodi chilungamo chathu chingapose bwanji chawo?’ Komatu chinafunikira kuchuluka. Afarisi pena adalidi okwezedwa kwabasi ndi anthu, koma osati ndi Mulungu. Nthaŵi ina Yesu anati kwa Afarisiwa: ‘Inu ndinu odziyesera nokha olungama pamaso pa anthu; koma Mulungu azindikira mitima yanu; chifukwa ichi chimene chikuzika mwa anthu chiri chonyansa pamaso pa Mulungu.’—Luka 16:15.
9-11. (a) Kodi ndiiti imene inali njira imodzi imene alembi ndi Afarisi analingalira kuti akalandira nayo kaimidwe kolungama pamaso pa Mulungu? (b) Kodi iwo anayembekezera kupeza chilungamo ndinjira ina iti yachiŵiri? (c) Kodi ndiiti imene inali njira yachitatu imene iwo anaiŵerengera, ndipo kodi mtumwi Paulo anati nchiyani chimene chinailepheretsa?
9 Arabi anadzipangira okha malamulo kuti adzipezere chilungamo. Limodzi linali kuyenerera chinthu kopezedwa mwa kukhala mbadwa ya Abrahamu: “Ophunzira a Abrahamu atate wathu amasangalala m’dziko lino ndikulowa m’dziko likudzalo.” (Mishnah) Mwinamwake Yohane Mbatizi anafuna kutsutsa mwambowu pamene anachenjeza Afarisi amene anadza kwa iye kuti: ‘Onetsani inu zipatso zakuyenera kutembenuka mtima: ndipo musamayesa kunena mwa inu nokha, Atate wathu tiri naye Abrahamu [ngati kuti kutero kokha kunali kokwanira].’—Mateyu 3:7-9; onaninso Yohane 8:33, 39.
10 Njira yachiŵiri yopezera chilungamo, iwo anati, inali yopereka mphatso zaulere. Mabuku aŵiri a Miyambo Yakalekale olembedwa ndi Ayuda opembedza m’zaka za zana lachiŵiri B.C.E. akuwunikira malingaliro a mwambowa. Ndemanga ina iyi ikupezeka mu Tobit: “Kupereka mphatso zaulere kumapulumutsa munthu ku imfa ndipo kumakhululukitsa chimo lirilonse.” (12:9, The New American Bible) Bukhu la Sirach (Ecclesiasticus) likuvomereza motere: “Madzi amazima laŵi la moto, ndipo mphatso zaulere zimaombola machimo.”—3:29, NAB.
11 Njira yachitatu imene iwo anafunira nayo chilungamo inali mwa ntchito za Chilamulo. Miyambo yawo yapakamwa inaphunzitsa kuti ngati mayendedwe ochuluka a munthu anali abwino, iye akapulumutsidwa. Chiweruzo “chimadalira pa ntchito zimene ziri zochuluka kaya zikhale zabwino kapena zoipa.” (Mishnah) Kuti ayanjidwe pa chiweruzo, nkhaŵa yawo inaikidwa pa “kupeza kuyenerera kumene kukapambana machimo.” Ngati ntchito zabwino za munthu zinapambana ntchito zake zoipa ndi imodzi, iye akapulumutsidwa—ngati kuti Mulungu anaweruza mwa kuŵerenga zochita zawo zochepa zonse! (Mateyu 23:23, 24) Pofotokoza lingaliro lolondola, Paulo analemba motere: ‘Chifukwa kuti pamaso [pa Mulungu] palibe munthu adzayesedwa wolungama ndi ntchito za lamulo.’ (Aroma 3:20) Motsimikizirika, chilungamo Chachikristu chiyenera kuchuluka kuposa cha alembi ndi Afarisi!
“Munamva Kuti Kunanenedwa”
12. (a) Kodi nkusintha kotani kuchoka pa njira yanthaŵi zonseyi ya kupereka zilozero ku Malemba Achihebri kumene Yesu anakupanga mu Ulaliki wake wa pa Phiri, ndipo kodi nchifukwa ninji? (b) Kodi tikuphunziranji m’kugwiritsira ntchito kwachisanu ndi chimodzi kwa mawu akuti “Kunanenedwa”?
12 Pamene Yesu poyambirira anagwira mawu kuchokera m’Malemba Achihebri, iye anati: “Kwalembedwa.” (Mateyu 4:4, 7, 10) Koma nthaŵi zisanu ndi imodzi mu Ulaliki wa pa Phiri, iye anayamba yomwe inamveka ngati ndemanga yochokera m’Malemba Achihebri ndi mawu akuti: “Kunanenedwa.” (Mateyu 5:21, 27, 31, 33, 38, 43) Kodi nchifukwa ninji? Chifukwa chakuti iye ankalozera ku Malemba monga momwe anamasulidwira mlingaliro la miyambo ya Afarisi imene inatsutsana ndi malamulo a Mulungu. (Deuteronomo 4:2; Mateyu 15:3) Ichi chamveketsedwa m’kulozera kwa Yesu kwa chisanu ndi chimodzi ndi komalizira uku mumpambowu: “Munamva kuti kunanenedwa, Uzikondana ndi mnansi wako, ndi kumuda mdani wako.” Koma panalibe lamulo la Mose limene linati, ‘Uzida mdani wako.’ Alembi ndi Afarisi ndiwo analinena. Uku kunali kumasulira kwawo Chilamulo kwa kukondana ndi mnansi wako—mnansi wako Wachiyuda, osati wina aliyense.
13. Kodi Yesu akuchenjeza motani motsutsana ngakhale ndi kuyamba mkhalidwe umene ungatsogolere kukupha kwenikweni?
13 Tsopano lingalirani yoyambirira ya mpambo umenewu wa ndemanga zisanu ndi imodzi. Yesu analengeza motere: “Munamva kuti kunanenedwa kwa iwo akale kuti, ‘Usaphe; koma yense wakupha adzakhala wopalamula mlandu woyenera kukaukamba kubwalo la milandu.’ Komabe, Ine ndinena kwa inu kuti yense wopitiriza kukwiyira mbale wake adzakhala wopalamula mlandu woyenera kukaukamba kubwalo la milandu.” (Mateyu 5:21, 22, NW) Mkwiyo utakhala mumtima ungatsogolere ku mawu onyoza ndipo zitatero ungafikitse ku chiweruzo cha kukanidwa, ndipo pomalizira pake ungatsogolere ku kachitidwe ka kupha kenikeniko. Mkwiyo wosungidwa kwanthaŵi yaitali mumtima ungakhale wakupha: ‘Yense wakudana ndi mbale wake ali wakupha munthu.’—1 Yohane 3:15.
14. Kodi ndimotani mmene Yesu akutipatsira uphungu kusalowa konse panjira yotsogolera ku chigololo?
14 Yesu chotsatira anati: ‘Munamva kuti kunanenedwa, Usachite chigololo; koma ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuyang’ana mkazi kumkhumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake.’ (Mateyu 5:27, 28) Kodi inuyo simudzachita chigololo? Pamenepo musalowemo konse m’njira yonkira kukachichita mwa kusunga malingaliro oganizira za icho. Chinjirizani mtima wanu, mmene mumakhala maziko a zinthu zoterezi. (Miyambo 4:23; Mateyu 15:18, 19) Yakobo 1:14, 15 akuchenjeza motere: ‘Koma munthu aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iyemwini chimkokera, nichimnyenga. Pamenepo chilakolako chitaima, chibala uchimo; ndipo uchimo, utakula msinkhu, ubala imfa.’ Nthaŵi zina anthu amati: ‘Musayambe kuchita chinthu chomwe simungathe kuchimaliza.’ Koma pankhani ino tiyenera kunena kuti: ‘Musayambe kuchita chinthu chomwe simungathe kuchileka.’ Ena amene akhala okhulupirika ngakhale pamene awopsyezedwa ndi imfa pamaso pa asilikali okonzekera kuwombera mfuti pambuyo pake agwera m’mbuna yoipa ya chisembwere cha kugonana.
15. Kodi ndimotani mmene kaimidwe ka Yesu pa chisudzulo kanasiyaniratu ndi konenedwa m’miyambo yapakamwa ya Ayuda?
15 Tsopano tatiyeni ku ndemanga yachitatu ya Yesu. Iye anati: ‘Kunanenedwanso, [Yense wakusudzula mkazi wake ampatse iye chikalata cha chilekaniro, NW]: koma ine ndinena kwa inu, kuti yense [wakusudzula, NW] mkazi wake, kosati chifukwa cha chigololo, amchititsa chigololo: ndipo amene adzakwata [wosudzulidwayo, NW] [ndiko kuti, munthu wosudzulidwa pa zifukwa zosakhala za chisembwere cha kugonana] achita chigololo.’ (Mateyu 5:31, 32) Ayuda ena anachita mwachinyengo ndi akazi awo ndipo anawasudzula pazifukwa zazing’ono kwenikweni. (Malaki 2:13-16; Mateyu 19:3-9) Miyambo yapakamwa inamlola mwamuna kusudzula mkazi wake “ngakhale ngati sanam’phikire bwino chakudya” kapena “ngati iye anapeza wina wokongolapo kuposa mkaziyo.”—Mishnah.
16. Kodi ndi kachitidwe kotani Kachiyuda kamene kanapangitsa kulumbira kukhala kopanda pake, ndipo kodi ndi kaimidwe kotani kamene Yesu anatenga?
16 M’lingaliro lofanana ndi ili, Yesu anapitiriza motere: ‘Ndiponso, munamva kuti kunanenedwa kwa iwo akale, Usalumbire [popanda kukwaniritsa, NW] . . . koma ine ndinena kwa inu, Musalumbire konse.’ Panthaŵiyi Ayuda ankagwiritsira ntchito molakwa malumbiro ndipo ankapereka malumbiro ambiri pa zinthu zazing’ono popanda kuzikwaniritsa. Koma Yesu anati: ‘Musalumbire konse . . . Koma manenedwe anu akhale Inde, inde; Iai, iai.’ Lamulo lake linali lopepuka: Khalani wonena zowonadi nthaŵi zonse, osafunikira kutsimikizira mawu anu ndi lumbiro. Kulumbira kusiireni kunkhani zina.—Mateyu 5:33-37; yerekezerani ndi 23:16-22.
17. Kodi ndinjira yabwinopo iti kuposa “diso kulipa diso, ndi dzino kulipa dzino” imene Yesu anaphunzitsa?
17 Chotsatira Yesu anati: “Munamva kuti kunanenedwa, Diso kulipa diso, ndi dzino kulipa dzino: koma ndinena kwa inu, Musakanize munthu woipa; koma amene adzakupanda iwe pa tsaya lako lamanja, umtembenuzire linanso.” (Mateyu 5:38-42) Yesu panopa sakutanthauza nkhonya yolinganizidwira kuvulaza koma akutanthauza pama lonyoza lomenyedwa ndi kumbuyo kwa dzanja. Musadziluluze nokha mwakuyamba kubwezerana minyozo. Peŵani kubwezera choipa ndi choipa. Mmalo mwake, bwezerani zabwino, ndipo mwakutero mudzakhala ‘mukugonjetsa zoipa pakuchita zabwino.’—Aroma 12:17-21.
18. (a) Kodi Ayuda anachisintha motani chilamulo chonena za kukonda mnansi wako, koma kodi Yesu analowereramo motani? (b) Kodi ndiliti limene linali yankho la Yesu kwa munthu wachilamulo wina amene anafuna kuika polekezera kugwiritsiridwa ntchito kwa “mnansi”?
18 M’chitsanzo chachisanu ndi chimodzi ndipo chomalizira, Yesu anasonyeza momvekera bwino mmene Chilamulo cha Mose chinafooketsedwera ndi miyambo ya arabi motere: “Munamva kuti kunanenedwa, Uzikondana ndi mnansi wako, ndi kumuda mdani wako: koma Ine ndinena kwa inu, Kondanani nao adani anu, ndi kupempherera iwo akuzunza inu.” (Mateyu 5:43, 44) Chilamulo cha Mose cholembedwa sichinaike polekezera chikondi: “Uzikonda mnansi wako monga udzikonda wekha.” (Levitiko 19:18) Anali Afarisi amene anatsekereza lamulo ili, ndipo m’kupatuka kwawo pa iyo iwo anaika polekezera liwu lakuti “mnansi” kwa anthu omwe anasunga miyamboyo. Zidatero kuti pamene Yesu pambuyo pake anakumbutsa wachilamulo wina za lamulo la ‘kukonda mnansi wanu monga inueni,’ munthuyo m’mawu ake anazemba motere: “Mnansi wanga ndani?” Yesu anamuyankha mwa kufotokoza fanizo la Msamariya wachifundo—dzipangeni nokha mnansi kwa okufunani.—Luka 10:25-37.
19. Kodi ndi kachitidwe kotani ka Yehova kulinga kwa oipa kamene Yesu anakayamikira kuti tikatsatire?
19 Popitiriza ndi ulaliki wake, Yesu analengeza kuti ‘Mulungu anasonyezera chikondi chake kwa oipa. Iye anawalitsira dzuwa ndi kuvumbitsira mvula yake pa iwo. Palibe chachilendo mutakonda okukondani. Oipa amazichita zimenezo. Ichi sichifunikira mphotho. Dzitsimikizireni nokha kukhala ana a Mulungu. Mutsanzireni. Dzipangeni nokha kukhala mnansi wa onse ndipo kondanani ndi mnansi wanu. Ndipo chotero “mukhale angwiro, monga Atate wanu wa Kumwamba ali wangwiro.”’ (Mateyu 5:45-48) Ndi muyezo wodzetsa chitokoso chotani nanga wofunikira kutsanzira! Ndipo ichi chikusonyeza kupereŵera kotani nanga kwa chilungamo cha alembi ndi Afarisi!
20. Mmalo mwa kuchotsapo Chilamulo cha Mose, kodi ndimotani mmene Yesu anakulitsira ndi kuzamitsa mphamvu yake ndikuchikweza?
20 Chotero pamene Yesu analozera ku mbali za Chilamulo ndikuwonjezera kuti, “Koma Ine ndinena kwa inu,” sanali kuchotsa Chilamulo cha Mose ndikuchilowa mmalo ndi chinachake. Ayi, koma anali kuzamitsa ndi kukulitsa mphamvu yake mwa kusonyeza mzimu wokhala kumbuyo kwake. Chilamulo chapamwamba chaubale chimapereka chiweruzo chakuti wopitiriza kukhala ndi chidani ngwakupha. Chilamulo chapamwamba cha chiyero chimatsutsa kuti kupitiriza nawo maganizo okhumbira ndiko chigololo. Chilamulo chapamwamba chaukwati chimaletsa kusudzulana kwachinyengo kuti ndiko njira yotsogolera ku kukwatirananso kwachigololo. Chilamulo chapamwamba cha chowonadi chimasonyeza kuti kulapa kobwerezabwereza nkosayenera. Chilamulo chapamwamba cha kudekha chimaletsa kubwezera. Chilamulo chapamwamba cha chikondi chimafuna chikondi chaumulungu chomwe chiribe polekezera.
21. Kodi kulangiza kwa Yesu konena za chilungamo chodzipangira cha arabi kunavumbulanji, ndipo kodi nchiyani chinanso chimene makamuwo anaphunzira?
21 Ha malamulo omwe sanamvedwepo ndi kale lonse ameneŵa anachititsa nthumanzi chotani nanga pamene analowa m’makutu a omvetserawo kwanthaŵi yoyamba! Iwo ayenera kukhala anatsimikizira chilungamo chodzipangiracho chomwe chidakhalapo mwa kudziika mu ukapolo ku miyambo ya arabi kukhala chopanda pake kotheratu chotani nanga! Koma pamene Yesu anapitiriza ndi Ulaliki wake wa pa Phiri, makamu akumva njala ndi ludzu la chilungamo cha Mulungu anafunikira kuphunzira mwapadera mochipezera, monga mmene nkhani yotsatira idzasonyezera.
Mafunso Akubwereramo
◻ Kodi nchifukwa ninji Ayuda anapanga miyambo yawo yapakamwa?
◻ Kodi ndi kusintha kwa dzawoneni kota- ni kumene Yesu anapanga m’chigwirizano ndi alembi ndi Afarisi ndi anthu wamba?
◻ Kodi ndimotani mmene alembi ndi Afarisi anayembekezera kupeza kaimidwe kolungama ndi Mulungu?
◻ Kodi nchiyani chimene Yesu anasonyeza kukhala njira yopeŵera dama ndi chigololo?
◻ Mwakusonyeza mzimu wokhala kumbuyo kwa Chilamulo cha Mose, kodi ndi miyezo yapamwamba yotani imene Yesu anakhazikitsa?