N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kunena Zoona?
PAMENE Manfred anali ndi zaka 18, anayamba kugwira ntchito ya muofesi, ngakhale kuti sanali kuidziwa bwinobwino ntchitoyo.a Kampani yomwe ankagwirako ntchitoyo inakonza zoti iye ndi anzake ena azipita ku koleji kukaphunzira za ntchitoyo masiku awiri pamlungu. Tsiku lina anaweruka mwamsanga. Malinga ndi malamulo a kampaniyo, antchitowo anafunika kubwerera ku ntchito n’kukagwira ntchito mpaka nthawi yowerukira. M’malo mwake, onse anapita kokasangalala, kupatulako Manfred amene anabwerera ku ntchito. Zinangochitika kuti, bwana wa kampaniyo amene ankayang’anira antchitowo anabwera ku ofesiko. Atamuona Manfred, anam’funsa kuti: “N’chifukwa chiyani suli m’kalasi? Ndipo anzako ali kuti?” Kodi Manfred akanayankha kuti chiyani?
Vuto limene anakumana nalo Manfred si lachilendo. Kodi anafunika kunena zoona kapena kunama kuti awabise anzakewo? Akananena zoona, akanawaika anzakewo m’mavuto ndipo zikanapangitsa kuti asamamukonde. Kodi ndi bwino kunama pa zochitika ngati zimenezi? Kodi inuyo mukanatani? Tikambabe za Manfred, koma choyamba tiyeni tione zimene tiyenera kuzindikira pamene tikuganiza zoti tinene zoona kapena ayi.
Choonadi ndi Bodza Zimatsutsana Kwambiri
Pachiyambi cha mbiri ya anthu, chilichonse chinkachitika mogwirizana ndi choonadi. Panalibe kupotoza kapena kukhotetsa choonadi. Mlengi wathu Yehova, ndi “Mulungu wa choonadi.” Mawu ake ndiwo choonadi, iyeyo sanganame, ndipo amadana ndi kunama ndiponso anthu onama.—Salmo 31:5; Yohane 17:17; Tito 1:2.
Ngati zinthu zinali choncho, nanga kunama kunachokera kuti? Yesu Khristu anapereka yankho lenileni pamene anauza atsogoleri achipembedzo omwe ankamutsutsa ndiponso omwe ankafuna kumupha kuti: “Inu ndinu ochokera kwa atate wanu Mdyerekezi, ndipo mukufuna kuchita zokhumba za atate wanu. Iyeyo ndi wopha anthu chiyambire kupanduka kwake, ndipo sanakhazikike m’choonadi, chifukwa mwa iye mulibe choonadi. Pamene akunena bodza, amalankhula za m’mutu mwake, chifukwa iye ndi wabodza komanso tate wake wa bodza.” (Yohane 8:44) Apa Yesu anali kunena za nkhani yomwe inachitika m’munda wa Edene pamene Satana anachititsa anthu awiri oyamba kusamvera Mulungu ndi kukhala akapolo a uchimo ndi imfa.—Genesis 3:1-5; Aroma 5:12.
Mawu a Yesuwa akusonyezeratu kuti Satana ndi “tate wake wa bodza,” amene anayambitsa kunama ndi bodza. Satana akadali wolimbikitsa kunama wamkulu, ndipo “akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” Ndipo ndiye amene ali ndi mlandu waukulu pamavuto onse amene bodza, lomwe lafalikira, labweretsa kwa anthu masiku ano.—Chivumbulutso 12:9.
Kutsutsana kwakukulu pakati pa choonadi ndi bodza, komwe kunayamba ndi Satana Mdyerekezi, kukupitirirabe masiku ano. Ndipo kumakhudza magulu osiyanasiyana a anthu komanso munthu aliyense payekha. Moyo umene munthu amakhala umasonyeza kuti ali ku mbali ya choonadi kapena ku mbali ya bodza. Amene ali ku mbali ya Mulungu amakhala moyo wotsatira choonadi cha Mawu a Mulungu, Baibulo. Aliyense amene satsatira njira ya choonadi, mosadziwa kapenanso mwadala, amagwa m’manja mwa Satana chifukwa choti “dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.”—1 Yohane 5:19; Mateyo 7:13, 14.
N’chifukwa Chiyani Anthu Ambiri Amanama?
Mfundo yakuti “dziko lonse” lili m’manja mwa Satana ikusonyeza chifukwa chimene anthu ambiri amanenera bodza. Komabe tingafunse kuti, ‘N’chifukwa chiyani Satana, “tate wake wa bodza” anayamba kunama?’ Satana ankadziwa kuti Yehova ndi Wolamulira woyenerera wa zonse zomwe analenga, kuphatikizapo anthu awiri oyamba. Komabe, Satana anafuna kuti udindo wapadera umenewu, umene sunali womuyenerera, ukhale wake. Chifukwa cha dyera ndiponso kufuna kutchuka, iye anafuna kulanda malo a Yehova. Pofuna kukwaniritsa zimenezi, Satana anagwiritsa ntchito bodza ndi chinyengo.—1 Timoteyo 3:6.
Nanga bwanji masiku ano? Kodi si zoona kuti dyera ndi kudzikonda ndi zimene zikuchititsabe kuti anthu ambiri azinama? Mabizinesi adyera, ndale zakatangale, ndiponso chipembedzo chonyenga zadzadza ndi chinyengo, mabodza, machenjera, ndi ukamberembere. Chifukwa chiyani? Kodi si chifukwa chakuti anthu nthawi zambiri amasonkhezeredwa ndi dyera ndi maganizo ofuna kutchuka kapena kupeza chuma, mphamvu, kapena udindo, zimene sakuyenerera kukhala nazo? Wolamulira wanzeru, Mfumu Solomo ya ku Isiraeli, anachenjeza kuti: “Wokangaza kulemera sadzapulumuka chilango.” (Miyambo 28:20) Ndipo mtumwi Paulo analemba kuti: “Kukonda ndalama ndi muzu wa zopweteka za mtundu uliwonse.” (1 Timoteyo 6:10) Tinganenenso chimodzimodzi za kufunitsitsa mphamvu kapena udindo monyanyira.
Chifukwa china chimene chimachititsa kunama ndicho mantha, kuopa zotsatira za zimene tachita kapena kuopa zimene ena angaganize ngati tinena zoona. Mwachibadwa, anthu amafuna kuti ena aziwakonda kapena kugwirizana nawo. Koma kufuna zimenezi kungawachititse kupotoza choonadi, mwina pang’ono chabe, ndi cholinga chofuna kuphimba zolakwa, kubisa mfundo zochititsa manyazi, kapenanso mwina pongofuna kukondweretsa ena. Mogwirizana ndi zimenezi, Solomo analemba kuti: “Kuopa anthu kutchera msampha; koma wokhulupirira Yehova adzapulumuka.”—Miyambo 29:25.
Kukhala Wokhulupirika kwa Mulungu wa Choonadi
Kodi Manfred anamuyankha bwanji bwana wake uja? Manfred ananena zoona. Anati: “Aphunzitsi anatiwerutsa mofulumira, ndiye ine ndabwera kudzagwira ntchito. Koma za enawo, sindingathe kuwayankhira. Mwina mungadzawafunse nokha.”
Manfred akanatha kuyankha mochenjera n’kupereka yankho lonama, kuti adzitchukitse kwa antchito anzake aja. Koma anaona kuti ndi bwino kunena zoona. Manfred ndi wa Mboni za Yehova. Kunena zoona kunam’chititsa kuti akhale ndi chikumbumtima choyera. Kunachititsanso kuti bwana wake azim’khulupirira. Monga mbali ya kum’phunzitsa ntchito, Manfred anamuika ku dipatimenti imene kunali zinthu zamtengo wapatali monga ndolo, zibangili ndi zina zotero, imene kawirikawiri anthu omwe akuphunzira kumene ntchito sankawalola kugwirako ntchito. Patapita zaka 15 Manfred anapatsidwa udindo wapamwamba pakampaniyo, ndipo bwana yemwe uja anamuimbira foni kum’thokoza ndipo anam’kumbutsanso za nkhani imeneyi, yosonyeza kuti ndi munthu wonena zoona nthawi zonse.
Popeza Yehova ndi Mulungu wonena zoona, aliyense amene akufuna kukhala pa ubwenzi wolimba ndi iye, ayenera ‘kutaya chinyengo’ ndi ‘kulankhula zoona.’ Mtumiki wa Mulungu ayenera kukonda choonadi. Munthu wina wanzeru analemba kuti: “Mboni yokhulupirika sidzanama.” Komabe, kodi bodza n’chiyani?—Aefeso 4:25; Miyambo 14:5.
Kodi Bodza N’chiyani?
Kunena bodza lililonse n’kusanena zoona, koma sikuti kusanena zoona kulikonse n’kunena bodza. Chifukwa chiyani? Mtanthauziramawu wina amati bodza ndilo, “kunena chinthu chimene ukudziwa kapena ukukhulupirira kuti si choona n’cholinga chonyenga munthu wina.” Zoonadi, bodza limaphatikizapo cholinga chonyenga munthu wina. Choncho, kulankhula zinthu zimene si zoona mosadziwa, monga kuuza munthu wina mfundo kapena manambala olakwika mosadziwa, si zofanana ndi kunama.
Komanso, tiyenera kuona ngati munthu amene akufunsayo n’ngofunikadi kumuuza choonadi chonse. Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti Manfred anafunsidwa funso lomwe lija ndi bwana wa kampani ina. Kodi Manfred akanafunika kumuuza nkhaniyo mwatsatanetsatane? Ayi. Chifukwa chakuti bwanayo sakanakhala woyenerera kuuzidwa zinthuzo, Manfred sakanakhala ndi chifukwa chomuuzira zimenezo. Komabe, ngakhale pa nthawi ngati imeneyi, kukanakhala kulakwa kumuuza bodza.
Kodi Yesu Khristu anapereka chitsanzo chotani pa nkhani imeneyi? Panthawi ina, Yesu anali kucheza ndi anthu osakhulupirira amene anaonetsa kuti anali ndi chidwi ndi maulendo ake. Anthuwo anamulangiza kuti, “Bwanji munyamuke mupite ku Yudeya.” Kodi Yesu anawayankha chiyani? Anati: “Inuyo kwezekani mtunda mupite ku chikondwereroko [ku Yerusalemu]; ine sindipitako pakali pano, chifukwa nthawi yanga yoyenera sinafike.” Koma patangopita kanthawi pang’ono, Yesu anapitadi ku Yerusalemu ku chikondwereroko. N’chifukwa chiyani anawayankha choncho? Anthuwo sanafunikire kudziwa tsatanetsatane wa kumene iye anali. Choncho ngakhale kuti Yesu sananene bodza, sanawauze zonse pofuna kuchepetsa mavuto amene anthuwo akanam’bweretsera iyeyo kapena otsatira ake. Limeneli silinali bodza chifukwa mtumwi Petulo analemba za Khristu kuti: “Sanachite tchimo, ndipo m’kamwa mwake simunapezeke chinyengo.”—Yohane 7:1-13; 1 Petulo 2:22.
Nanga bwanji Petuloyo? Usiku umene Yesu anagwidwa, kodi Petulo sananame katatu n’kukana kuti sankamudziwa Yesu? Inde, Petulo anaopa anthu ndipo ananama. Koma nthawi yomweyo analira “mopwetekedwa mtima kwambiri” kenako analapa, ndipo tchimo lake linakhululukidwa. Komanso anaphunzirapo kanthu pa cholakwa chakecho. Patapita masiku angapo, analankhula za Yesu molimba mtima ndipo anakaniratu kuleka kulankhula za iye pamene akuluakulu achiyuda anamuopseza ku Yerusalemu. Inde, kulephera kwa Petulo kwa kanthawi ndi kusintha mwamsanga ziyenera kukhala zolimbikitsa kwa tonsefe, amene tingachite mantha mosavuta pamene tafooka ndiponso kupunthwa m’mawu kapena m’zochita.—Mateyo 26:69-75; Machitidwe 4:18-20; 5:27-32; Yakobe 3:2.
Choonadi Chidzakhala ku Nthawi Zonse
Lemba la Miyambo 12:19 limati: “Mlomo wa ntheradi ukhazikika nthawi zonse; koma lilime lonama likhala kamphindi.” Inde, zolankhula zoona zimakhalitsa. Ndipo anthu amakhala ndi ubwenzi wolimba ndi wosangalatsa akamalankhula zoona nthawi zonse ndi kuchita zinthu zogwirizana ndi zimenezo. Zoonadi, munthu akamalankhula zoona amapindula nthawi yomweyo. Kupindula kwake kumaphatikizapo kukhala ndi chikumbumtima choyera, mbiri yabwino, ndiponso ubwenzi wolimba mu ukwati, m’banja, ndi anzanu, ndiponso ngakhale pabizinesi.
Koma bodza silichedwa kuululika. Lilime labodza linganyenge anthu kwa kanthawi, koma bodza silingapambane mpaka kalekale. Kuwonjezera apo, Yehova, Mulungu wa choonadi, waika malire a nthawi imene walola kuti bodza ndiponso amene amalimbikitsa bodzalo akhalepo. Baibulo limalonjeza kuti Yehova adzathetsa mphamvu ya Satana Mdyerekezi, tate wake wa bodza, amene akusokeretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu. Yehova posachedwapa adzathetsa mabodza onse ndi onse onena bodza.—Chivumbulutso 21:8.
Kudzakhaladi mpumulo waukulu “lilime la ntheradi” likadzakhazikika ku nthawi zonse!
[Mawu a M’munsi]
a Si dzina lake lenileni.
[Mawu Otsindika patsamba 5]
Dyera ndiponso kufuna kutchuka n’zimene zimachititsa anthu ambiri kunama
[Mawu Otsindika patsamba 6]
Kunena bodza lililonse n’kusanena zoona, koma sikuti kusanena zoona kulikonse n’kunena bodza
[Chithunzi patsamba 6]
Kodi tikuphunzira chiyani pa mfundo yoti Petulo anakana Khristu?
[Chithunzi patsamba 7]
Anthu akamalankhula zoona amakhala ndi ubwenzi wolimba ndi wosangalatsa