Abusa Achikondi, Nkhosa Zokhulupirira
M’NTHAŴI za Baibulo chiyanjo chathithithi pakati pa mbusa ndi nkhosa zake chinali cha mwambo. Kaŵirikaŵiri mbusa anali mwinamwake mwini wa nkhosa kapena chiwalo cha banja la mwiniwake. M’mawa iye ankapita ku khola ndi kuitana nkhosa zake kuchoka pakati pa nkhosa zosiyanasiyana zotsekeredwa m’menemo. Iye anadziŵa nkhosa zake; izo zinadziŵa liwu lake. Iye sanazikakamize izo—iye anazitsogolera ndipo izo zinam’tsatira. Ku udzu wobiriŵira ndi madzi otsitsimula iye anazitsogolera izo. Mu mphepo yoipa usiku, iye anakhoza mwinamwake kuzibweza izo ku khola kapena kuzifunda izo mu phanga. Mu mphepo yabwino, iye anathera usiku wonse ndi izo pansi pa nyenyezi—mongadi mmene zinaliri m’ngululu ya chaka cha 2 B.C.E. pamene abusa anali “kukhala kubusa ndi kuyang’anira zoŵeta zawo usiku.”—Luka 2:8.
Ngati nkhosa imodzi inasokera, mbusa ankaifunafuna kufikira ataipeza iyo. (Luka 15:4) Zinazo 99 sizinamkhutiritse iye kufikira yosowayo itabwezeretsedwa.
Chiyanjo cha mbusa wa kum’mawa ku nkhosa zake chinali chozama m’malingaliro, popeza kuti mmodzi wa iwo anachitira umboni kuti: “Kutaika kwa nkhosa kunabweretsa chisoni ku mtima wanga. Pamene imodzi ya izo inakhala yodwala kapena inagulitsidwa, ndinasisima chifukwa chakuti ndinkasowa bwenzi yemwe ndinasamalira ndi yemwe anandisamalira ine. Pansi pa mtambo wowala ndi wonyezimira wa m’maiko a m’Baibulo, panakhala, monga mmene zinaliri kwa ine, pakati pa mbusa ndi nkhosa zake kugwirizana kwa kumvana ndi chikondi. Okha m’malo a kutali, popanda munthu aliyense pafupi, m’maora a mtendere kapena ovuta, mbusa ndi nkhosa amasangalala ndi moyo wofanana.”
Mbusa wokhulupirika anali wochinjiriza wopanda mantha. Iye anamenyera achifwamba omwe anadza kudzaba. Iye anapitikitsa nyama za kuthengo zomwe zinadza kaamba ka kudzasakaza. Ndipo monga mbusa wachichepere Davide, iye anali wolondola kukhala pafupi kwenikweni ndi miyala yoponyela. (1 Samueli 17:34-36, 49; onaninso Oweruza 20:16.) Ngati nkhosa inadyedwa, mbusa anayesetsa kufunkha zidutswa za mafupa kapena zikopa kuti apange chokumbukira kaamba ka nyama yosowayo. Ichi chinali makamaka tero ngati mbusayo anali wolembedwa ntchito—popanda chitsimikiziro choterocho iye akanakaikiridwa kukhala ataiba iyo.—Eksodo 22:12-15; yerekezani ndi Amosi 3:12.
Nkhosa zinakhulupirira abusa awo. Zambiri zinapatsidwa maina olongosola—yamakutu otambasuka, yonenepa mchira, yakuda pamaso, yoyera kwenikweni. Pamene mbusa anaitana maina awo, izo zinayankha. Wofufuza mmodzi anafuna kutsimikizira chimenechi pamene iye ankapita pakati pa gulu la nkhosa. Iye akusimba zotsatirazi: “Ine kenaka ndinamufunsa iye [mbusa] kuti aitane imodzi ya nkhosa zake. Iye anatero, ndipo mwamsanga iyo inachoka pabusa pake ndi pa zinzake, ndi kuthamangira ku manja a mbusayo, yokhala ndi zizindikiro za kusangalala, ndi chimvero cha mwamsanga chomwe sindinawonepo ndi kale lonse mwa nyama ina iriyonse. Chirinso chowona kuti m’dzikoli, ‘mlendo sizidzamtsatira, koma zidzamthawa.’”
Yesu anatsimikizira zochulukira za zomwe zangotchulidwazi pamene anazidziŵikitsa iyemwini monga Mbusa Wabwino wa otsatira ake onga nkhosa kuti: “Nkhosa zimva mawu ake; ndipo aitana nkhosa za iye yekha maina awo, nazitsogolera kunja [kwa khola]. Pamene atulutsa zonse za iye yekha, azitsogolera; ndi nkhosa zonse zimtsata iye; chifukwa zidziŵa mawu ake. Koma mlendo sizidzamtsata, koma zidzamthawa; chifukwa sizidziŵa mawu a alendo. Ine ndine mbusa wabwino; ndipo ndizindikira zanga, ndi zanga zindizindikira ine, monga Atate andidziŵa ine, ndi ine ndimdziŵa Atate; ndipo nditaya moyo wanga chifukwa cha nkhosa.”—Yohane 10:3-5, 14, 15.
Osati kokha Kristu Yesu komanso Yehova Mulungu akulozeredwa monga mbusa. “Yehova ndiye mbusa wanga,” anatero wamasalmo. Monga wotero Iye limodzinso ndi Yesu amasonyeza kudera nkhaŵa kwachikondi kaamba ka “nkhosa za pa busa pake.” Ponena za iye kwalembedwa kuti: “Iye adzadyetsa zoŵeta zake ngati mbusa, nadzasonkhanitsa ana a nkhosa pachapa pake, nadzawatengera pa chifuwa chake, ndipo adzatsogolera bwino bwino zimene ziyamwitsa.”—Masalmo 23:1; 100:3; Yesaya 40:11.
Koma kwa abusa onyenga omwe amazunza nkhosa zake, Yehova akunena kuti: “Ndidzalanditsa nkhosa zanga pakamwa pawo, zisakhale chakudya chawo.”—Ezekieli 34:10.
Mkawonedwe ka makhalidwe ndi chiphunzitso cha abusa a chipembedzo amakono, kodi iwo amalinga motani m’maso mwa Yehova? Nkhani yotsatira ikulingalira chimenechi.
[Mawu Otsindika patsamba 27]
“Munthu ndani wa inu ali nazo nkhosa makumi khumi, ndipo pakutaika imodzi ya izo, sasiya nanga m’chipululu zinazo makumi asanu ndi anayi mphambu zisanu ndi zinayi, nalondola yotaikayo kufikira aipeza? Ndipo pamene adaipeza, aisenza pa mapewa ake wokondwera.”—Luka 15:4, 5.