N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kusonkhana?
“Tsiku ndi tsiku anali kusonkhana kukachisi.”—MAC. 2:46.
1-3. (a) Kodi Akhristu asonyeza bwanji kuti misonkhano ndi yofunika? (Onani chithunzi pamwambapa.) (b) Kodi tikambirana chiyani m’nkhaniyi?
PAMENE mtsikana wina dzina lake Corinna anali ndi zaka 17, mayi ake anamangidwa. Kenako nayenso anamangidwa n’kutumizidwa ku Siberia, komwe kunali kutali kwambiri ndi kwawo. Kumeneko anali ngati kapolo moti nthawi zina ankagwira ntchito panja, kunja kukuzizira kwambiri. Ngakhale zinali chonchi, Corinna ndi mlongo wina ankayesetsabe kupita kukasonkhana.
2 Corinna anati: “Tinkachoka madzulo pafamu yomwe tinkagwira ntchito, n’kuyenda ulendo wamakilomita 25 kukakwera sitima. Tinkakwera sitimayo 2 koloko m’mbandakucha ndipo tinkayenda kwa maola 6. Kenako tikatsika tinkayendanso makilomita 10 kuti tikafike pamalo omwe tinkasonkhana.” Ngakhale kuti ankayenda ulendo wautali chonchi, Corinna sankadandaula. Iye anati: “Tinkaphunzira Nsanja ya Olonda komanso tinkaimba nyimbo. Misonkhanoyi inkatilimbikitsa kwambiri.” Ngakhale kuti pankatenga masiku atatu kuti alongowa abwererenso kuntchito yawo, amene ankawayang’anira sankadziwa n’komwe kuti anachoka.
3 Kuyambira kale atumiki a Yehova amaona kuti kusonkhana n’kofunika. Mwachitsanzo, mpingo wachikhristu utangokhazikitsidwa kumene, Akhristu “anali kusonkhana kukachisi” tsiku ndi tsiku. (Mac. 2:46) Inunso muyenera kuti mumaona kuti kusonkhana n’kofunika kwambiri. Komabe Akhristu onse amakumana ndi mavuto omwe angawalepheretse kusonkhana. Zinthu monga ntchito, kutanganidwa komanso kutopa chifukwa cha zimene timachita tsiku ndi tsiku, zingapangitse kuti tizivutika kupita kumisonkhano. Ndiye kodi tingatani kuti tizisonkhana nthawi zonse?[1] Nanga tingathandize bwanji amene timaphunzira nawo Baibulo kuti aziona kuti misonkhano ndi yofunika? M’nkhaniyi tikambirana zifukwa 8 zosonyeza kuti kusonkhana n’kofunika. Zifukwazi tingaziike m’magulu atatu awa: (1) Zokhudza inuyo (2) Zokhudza anthu ena (3) Zokhudza Yehova.[2]
KODI MISONKHANO IMATITHANDIZA BWANJI?
4. Kodi misonkhano imatithandiza bwanji kuphunzira za Yehova?
4 Timaphunzira zambiri. Msonkhano uliwonse wampingo umatithandiza kuphunzira za Yehova. Mwachitsanzo, posachedwa mipingo yambiri yakhala ikuphunzira buku lakuti, Yandikirani kwa Yehova pa Phunziro la Baibulo la Mpingo. M’bukuli taphunzira za makhalidwe a Mulungu. Tinkalimbikitsidwanso ndi mayankho ochokera pansi pa mtima a abale ndi alongo ndipo izi zatithandiza kuti tizikonda kwambiri Atate wathu wakumwamba. Tikakhala pamisonkhano n’kumamvetsera nkhani, zitsanzo komanso kuwerenga Baibulo timamvetsa bwino Mawu a Mulungu. (Neh. 8:8) Mwachitsanzo, taganizirani mfundo zothandiza zimene mumapeza mukamakonzekera komanso kumvetsera mfundo zazikulu mlungu uliwonse.
5. Kodi misonkhano yakuthandizani bwanji kutsatira mfundo za m’Baibulo komanso kuti muzilalikira mogwira mtima?
5 Misonkhano imatithandizanso kuti tizitsatira mfundo za m’Baibulo pa moyo wathu. (1 Ates. 4:9, 10) Chitsanzo cha zimenezi ndi mfundo zimene timaphunzira pa Phunziro la Nsanja ya Olonda. Kodi inuyo munaphunzirapo mfundo zina zimene zinakuthandizani kusintha zolinga, kukhululukira Mkhristu mnzanu kapena kuyamba kupemphera kuchokera pansi pa mtima? Misonkhano imene timakhala nayo mkati mwa mlungu imatithandizanso kuti tizilalikira mwaluso komanso kuphunzitsa mfundo za m’Baibulo mogwira mtima.—Mat. 28:19, 20.
6. Kodi inuyo mumalimbikitsidwa ndi zinthu ziti pamisonkhano?
6 Timalimbikitsidwa. Zinthu za m’dzikoli zikhoza kutitopetsa komanso kusokoneza ubwenzi wathu ndi Yehova. Koma misonkhano ya mpingo imatilimbikitsa kwambiri. (Werengani Machitidwe 15:30-32.) Pamisonkhano timaphunziranso zokhudza kukwaniritsidwa kwa maulosi a m’Baibulo. Izi zimatithandiza kuti tisamakayikire kuti zimene Mulungu walonjeza zidzachitikadi. Anthu amene amatilimbikitsa si okamba nkhani okha. Timalimbikitsidwanso kumva abale ndi alongo akuyankha komanso kuimba mochokera pansi pa mtima. (1 Akor. 14:26) Tikamachezanso ndi abale ndi alongo misonkhano isanayambe komanso ikatha, timaona kuti sitili tokha ndipo timasangalala.—1 Akor. 16:17, 18.
7. Kodi chimachitika n’chiyani tikamasonkhana?
7 Timalandira mzimu woyera. Yesu Khristu ataukitsidwa n’kupita kumwamba ananena kuti: “Ali ndi makutu amve zimene mzimu ukunena ku mipingo.” (Chiv. 2:7) Izi zikusonyeza kuti Yesu amagwiritsa ntchito mzimu woyera potsogolera mpingo. Akhristufe timafunika mzimu woyera kuti uzitithandiza kupewa mayesero, kulalikira molimba mtima ndiponso kusankha zinthu mwanzeru. Choncho tiyeni tiziyesetsa kupezeka pamisonkhano n’cholinga choti tilandire mzimu woyera.
KODI MUMATHANDIZA BWANJI ENA MUKAMASONKHANA?
8. Kodi tikamasonkhana, kuyankha komanso kuimba nyimbo timathandiza bwanji ena? (Onaninso bokosi lakuti, “Akapita Kumisonkhano Amalimbikitsidwa Kwambiri.”)
8 Timasonyeza kuti timakonda abale athu. Abale ndi alongo athu akukumana ndi mavuto ambiri. N’chifukwa chake mtumwi Paulo analemba kuti: “Tiyeni tiganizirane.” Kenako ananena kuti tingachite zimenezi ‘tikamasonkhana pamodzi.’ (Aheb. 10:24, 25) Choncho, tikamafika pamisonkhano timasonyeza kuti timaganizira abale athu komanso timawaona kuti ndi ofunika kwambiri. Komanso tikamayankha ndiponso kuimba nyimbo mochokera pansi pamtima timalimbikitsa abale athu.—Akol. 3:16.
9, 10. (a) Kodi mawu a Yesu a pa Yohane 10:16 akusonyeza bwanji kuti kusonkhana n’kofunika? (b) Kodi tikamasonkhana timathandiza bwanji Akhristu amene amatsutsidwa ndi achibale awo omwe si Mboni?
9 Timagwirizana ndi Akhristu anzathu. (Werengani Yohane 10:16.) Yesu anati iyeyo ndi m’busa ndipo otsatira ake ndi gulu la nkhosa. Ndiye taganizirani izi, tiyerekeze kuti nkhosa ziwiri zili paphiri, ziwiri zili m’chigwa ndipo imodzi ikudya kudambo. Kodi tinganene kuti limeneli ndi gulu la nkhosa? Ayi. Nkhosa zimapanga gulu zikakhala pamodzi ndipo m’busa akhoza kuzitsogolera bwino. Mofanana ndi zimenezi, sitingatsatire m’busa wathu ngati tili ndi chizolowezi chosafika pamisonkhano. Tiyenera kusonkhana ndi Akhristu anzathu kuti tikhale nawo m’gulu lotsogoleredwa ndi “m’busa mmodzi.”
10 Komanso tikamasonkhana timakhala ngati banja limodzi logwirizana. (Sal. 133:1) Abale ndi alongo athu ena anakanidwa ndi makolo ndiponso achibale awo. Koma Yesu analonjeza anthu oterewa kuti adzawapatsa anthu oti aziwakonda komanso kuwasamalira. (Maliko 10:29, 30) Ndiyeno, tikamafika pamisonkhano timakhala bambo, mayi, mchimwene ndiponso mchemwali wa abale ndi alongo amenewa. Kuganizira kwambiri mfundo imeneyi kungatithandize kuti tiziyesetsa kupezeka pamisonkhano nthawi zonse.
YEHOVA AMASANGALALA TIKAMASONKHANA
11. Kodi misonkhano yathu imatithandiza bwanji kulemekeza Yehova?
11 Timalemekeza Yehova. Akhristufe tiyenera kutamanda, kulemekeza komanso kuthokoza Yehova chifukwa ndi Mlengi wathu. (Werengani Chivumbulutso 7:12.) Timachita zimenezi tikamapemphera, kuimba komanso kulankhula za Yehova pamisonkhano yathu. Timaona kuti ndi mwayi waukulu kutamanda Mulungu wathu chifukwa amatichitira zambiri.
12. Kodi Yehova amamva bwanji tikamamvera lamulo lake loti tizisonkhana?
12 Tiyeneranso kumvera Yehova. Iye anatilamula kuti tisasiye kusonkhana, makamaka masiku otsiriza ano. Yehova amasangalala kwambiri tikamamvera lamuloli. (1 Yoh. 3:22) Amaonanso zonse zimene timachita poyesetsa kuti tipezeke pamisonkhano.—Aheb. 6:10.
13, 14. N’chifukwa chiyani tinganene kuti misonkhano imatithandiza kukhala pa ubwenzi ndi Yehova komanso Yesu?
13 Timasonyeza kuti tikufuna kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu komanso Yesu. Tikakhala pamisonkhano, Mlangizi wathu wamkulu amatitsogolera pogwira ntchito Mawu ake, Baibulo. (Yes. 30:20, 21) Ngakhale anthu ena akafika pamisonkhano yathu amadziwa kuti ‘Mulungu ali pakati pathu.’ (1 Akor. 14:23-25) Zimene timaphunzira zimachokera kwa Yehova ndipo amatitsogolera ndi mzimu wake woyera. Tikakhala pamisonkhano timaona kuti Yehova amatikonda ndiponso amatisamalira. Choncho m’pomveka kunena kuti misonkhano imatithandiza kuti tikhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova.
14 Yesu anati: “Kulikonse kumene awiri kapena atatu asonkhana m’dzina langa, ine ndidzakhala pakati pawo.” (Mat. 18:20) Mawu a Yesuwa amagwiranso ntchito tikakhala pamisonkhano. Baibulo limati Khristu ndi Mutu wampingo ndipo amayenda pakati pa mipingo. (Chiv. 1:20–2:1) Izi zikusonyeza kuti Yehova ndi Yesu amakhala nafe pamisonkhano ndipo amatilimbikitsa. Yehova amasangalala kwambiri akaona kuti tikuyesetsa kukhala pa ubwenzi ndi Mwana wake komanso iyeyo.
15. Kodi tikamapezeka pamisonkhano timasonyeza bwanji kuti timafuna kumvera Yehova?
15 Timasonyeza kuti tili kumbali ya ulamuliro wa Mulungu. Yehova amatilamula kuti tizisonkhana koma satikakamiza. (Yes. 43:23) Choncho tikamasonkhana timasonyeza kuti timamukonda kwambiri komanso tili kumbali ya ulamuliro wake. (Aroma 6:17) Mwachitsanzo, abwana athu akhoza kutiuza kuti tigwirebe ntchito pa nthawi imene timasonkhana. Nthawi zinanso boma lingatiletse kusonkhana n’kulamula kuti wochita zimenezi amangidwa kapena apatsidwa chilango choopsa. Apo ayi tikhoza kutengeka ndi zosangalatsa mpaka kuiwala nazo misonkhano. Pa zochitika zonsezi munthu amayenera kusankha kuti amvera ndani. (Mac. 5:29) Koma Yehova amasangalala kwambiri tikasankha kumumvera.—Miy. 27:11.
TIZIYESETSA KUPEZEKA PAMISONKHANO
16, 17. (a) Kodi tikudziwa bwanji kuti Akhristu oyambirira ankaona kuti kusonkhana n’kofunika kwambiri? (b) Kodi M’bale Gangas ankamva bwanji akakhala pamisonkhano?
16 Akhristu oyambirira anapitiriza kusonkhana pambuyo pa msonkhano wa pa Pentekosite mu 33 C.E. Baibulo limati: ‘Iwo anapitiriza kulabadira zimene atumwiwo anali kuphunzitsa ndipo tsiku ndi tsiku anali kusonkhana kukachisi.’ (Mac. 2:42, 46) Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “anapitiriza kulabadira,” amasonyeza kuti ankachita khama kwambiri. Mu ulamuliro wa Aroma sizinali zapafupi kuti Akhristu azisonkhana. Kuwonjezera apo, atsogoleri achipembedzo achiyuda ankawatsutsa kwambiri. Komabe iwo sanabwerere m’mbuyo.
17 Masiku ano, pali atumiki a Yehova ambiri amene amaona kuti misonkhano ndi yofunika. Mwachitsanzo, M’bale George Gangas, amene anatumikira m’Bungwe Lolamulira kwa zaka 22, ananena kuti: “Munthune ndimalimbikitsidwa ndikasonkhana ndi abale ndipo ndimasangalala kwabasi. Ndimakonda kufika mofulumira pamisonkhano ndipo ikatha sindichoka msanga. Ndikamacheza ndi anthu a Yehova ndimamva bwino kwambiri ndipo ndimaona kuti ndili ndi abale anga enieni m’Paradaiso wauzimu.” Iye ananenanso kuti: “Maganizo anga onse amakhala pa misonkhano basi.”
18. Kodi inuyo mumamva bwanji mukaganizira za misonkhano, nanga muyesetsa kuchita chiyani?
18 Kodi inunso mumamva chonchi mukaganizira zosonkhana kuti mulambire Yehova? Ngati ndi choncho, yesetsani kuti musamaphonye misonkhano. Mukatero mudzafanana ndi Mfumu Davide amene analemba kuti: “Yehova, ine ndimakonda nyumba imene inu mumakhala.”—Sal. 26:8.
^ [1] (ndime 3) Abale ndi alongo athu ena amalephera kusonkhana nthawi zonse chifukwa cha mavuto monga matenda aakulu. Abale ndi alongowa ayenera kudziwa kuti Yehova amamvetsa mavuto awo ndipo amayamikira zimene amayesetsa kuchita pomulambira. Akulu angapeze njira yothandizira abalewa. Mwachitsanzo, angawathandize kuti azimvetsera misonkhano pa foni kapena kuwajambulira kuti amvetsere ali kunyumba.
^ [2] (ndime 3) Onani bokosi lakuti, “N’chifukwa Chiyani Timasonkhana?”