Zimene Zolengedwa “Zanzeru Mwachibadwa” Zingatiphunzitse
KUTSUKULUZA MPWEYA, kuletsa madzi kuundana, kuchotsa mchere m’madzi, ndi kugwiritsira ntchito namalowe ndizo zinthu zimene zakhala zodziŵika kwambiri kwa anthu m’zaka za zana la 20. Komabe, zinaliko pakati pa nyama zaka zikwi zambiri kalelo. Inde, anthu amapindula mwa kuphunzira za zolengedwa zotero “zanzeru [mwachibadwa, NW].” (Miyambo 30:24-28; Yobu 12:7-9) Nyama zina zikuoneka kuti zakhala aphunzitsi osalankhula kwa anthu, ndipo kuzipenda kumakondweretsa.
Kodi tingapindule mwa kupenda mikhalidwe ya nyama zina? Chabwino, Yesu Kristu anafanizira otsatira ake ndi nkhosa, njoka, nkhunda, ndipo ngakhale dzombe. Kodi anali kuganiza chiyani pamene anafanizira otsatira ake ndi zolengedwa zimenezi? Tiyeni tione.
“Nkhosa Zanga Zimva Mawu Anga”
Nkhosa zimatchulidwa m’Baibulo nthaŵi zoposa 200. Malinga ndi kufotokoza kwa Smith’s Bible Dictionary, “nkhosa ndiyo chizindikiro cha kufatsa, kuleza mtima, ndi kugonjera.” Mu Yesaya chaputala 53, Yesu mwiniyo mwaulosi anafanizidwa ndi nkhosa. Nzoyenera chotani nanga kuti anafanizira otsatira ake ndi nyama imodzimodziyo! Koma kodi ndi mkhalidwe uti wa nkhosa makamaka umene Yesu anali kuganiza?
“Nkhosa zanga zimva mawu anga, ndipo ine ndizizindikira, ndipo zinditsata ine,” Yesu anatero. (Yohane 10:27) Motero Yesu anasonyeza kufatsa kwa ophunzira ake ndi kufunitsitsa kwawo kumtsatira. Nkhosa zenizeni zimamvera mbusa wawo ndi kumtsatira mwaufulu. Ndiponso mbusayo amalikondanso kwambiri gulu la nkhosalo.
Nkhosa zingakhale zomwazikana m’dambo pamene zikudya msipu, koma nkhosa iliyonse simatayana ndi gulu lonselo. Chifukwa chake, pamene nyamazo zizindikira kuti palibe chisungiko kapena ziwopsezedwa, “zimasonkhana pamodzi mwamsanga,” likutero bukulo Alles für das Schaf (Zonse Kaamba ka Nkhosa). Ngati nkhosa zikuthaŵa kupeŵa ngozi, zimatero monga gulu, zikumaima nthaŵi ndi nthaŵi kuona mmene mkhalidwe ulili. “Kuthaŵa pang’onopang’ono kumalola ana ndi nyama zofookerapo kuyendera limodzi ndi zinazo. Gululo limazipatsanso ngakhale chitetezo chapadera.” Kodi khalidwe limeneli likutiphunzitsanji?
Akristu oona lerolino sali omwazikana pakati pa magulu ndi mipatuko ya Dziko Lachikristu. M’malo mwake, ali m’gulu limodzi. Mkristu aliyense amakonda kwambiri gulu limeneli la Mulungu, ndipo zimenezi zimachirikiza umodzi wa gulu la Mboni za Yehova. Kutagwa tsoka—kaya ndi matenda aakulu, nkhondo, kapena tsoka lachilengedwe—kodi wolambira aliyense amayang’ana kuti kaamba ka chitsogozo ndi chitetezo? Ku gulu la Yehova, limene limapereka chitetezo chauzimu.
Kodi uphungu wa Baibulo umaperekedwa motani? M’zofalitsa monga Nsanja ya Olonda ndi magazini anzake, Galamukani! Magazini ameneŵa ndi misonkhano yachikristu zimapereka ngakhale thandizo lapadera kwa aja ofuna chisamaliro chowonjezereka, monga ana a nkhosa ndi nkhosa zofookerapo m’gulu. Mwachitsanzo, chisamaliro chimaperekedwa kwa makolo opanda mnzawo ndi aja ochita tondovi. Chotero, kuli kwanzeru chotani nanga kuŵerenga magazini onse, kupezeka pamsonkhano uliwonse wa mpingo, ndi kugwiritsira ntchito zimene timaphunzira! Motero timasonyeza kufatsa ndi chikondi chachikulu ku gulu la Mulungu.—1 Petro 5:2.
“Ochenjera Monga Njoka, Ndi Oona Mtima Monga Nkhunda”
Smith’s Bible Dictionary imati “Kummaŵa konse njoka inagwiritsiridwa ntchito monga chizindikiro cha mphamvu yoipa, cha mzimu wa kusamvera.” Komabe, mawu akuti “nkhunda yanga” anali kusonyeza chikondi. (Nyimbo ya Solomo 5:2) Pamenepo, kodi Yesu anali kuganiza chiyani pamene analimbikitsa otsatira ake kukhala “ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda”?—Mateyu 10:16.
Yesu anali kupereka malangizo a kulalikira ndi kuphunzitsa. Ophunzira ake anayenera kuyembekezera anthu ena kumvetsera ndipo ena kukana. Oŵerengeka adzachita chidwi, pamene ena adzakana uthenga wabwino. Ndipo ena adzazunza atumiki oona ameneŵa a Mulungu. (Mateyu 10:17-23) Kodi ophunzirawo akanachita motani ndi chizunzo?
Mu Das Evangelium des Matthäus (Uthenga Wabwino wa Mateyu), Fritz Rienecker, ponena za Mateyu 10:16, akunena kuti: “Kuchenjera . . . kuyenera kugwirizana ndi umphumphu, kuona mtima, ndi kuwongoka mtima, kuti kangachitike kanthu kena kamene kangapatse adani chifukwa chabwino chodandaulira. Oimira a Yesu ali pakati pa adani ankhanza, amene salingalira ena ndi amene amaukira atumwiwo popanda chifundo ndipo atangopeza mpata pang’ono. Chifukwa chake, kuli kofunika—monga njoka—kuyang’anira adani, ndi kupenda mkhalidwewo maso ndi nzeru zili zatcheru; kulamulira mkhalidwewo popanda machenjera kapena chinyengo, kukhala oyera ndi oona m’mawu ndi ntchito ndipo motero kusonyeza kuti ali monga nkhunda.”
Kodi atumiki amakono a Mulungu angaphunzireponji pa mawu a Yesu opezeka pa Mateyu 10:16? Lerolino, anthu amachita ndi uthenga wabwino mofanana kwambiri ndi mmene anachitira m’zaka za zana loyamba. Atayang’anizana ndi chizunzo, Akristu oona afunikira kuchenjera ngati njoka ndi kukhala oyera mtima ngati nkhunda. Akristu samachita chinyengo kapena kusaona mtima koma amakhala osanyenga, enieni, ndi oona mtima polengeza uthenga wa Ufumu kwa ena.
Mwachitsanzo: Mabwenzi kuntchito, achichepere kusukulu, kapena ngakhale a pabanja lanu angamanene mawu oipa ponena za zikhulupiriro zanu monga Mboni ya Yehova. Zimene zingabwere m’maganizo zingakhale kubwezera ndi mawu ofanana mwa kuwanyodola ndi mawu oŵaŵa pa chikhulupiriro chawo. Koma kodi kumeneko ndi kukhala woona mtima? Kutalitali. Ngati musonyeza okusulizaniwo kuti zokamba zawo sizikukhudza khalidwe lanu labwino, mwina iwo angasinthe. Pamenepo mudzakhala wochenjera ndi wopanda liwongo—‘wochenjera monga njoka, komabe woona mtima monga nkhunda.’
“Maonekedwe a Dzombelo Anafanana ndi Akavalo Okonzeka Kukachita Nkhondo”
Magazini a GEO akusimba kuti mu 1784, South Africa anasakazidwa ndi “[dzombe] lochuluka koposa limene silinaonekepo m’mbiri yolembedwa.” Dzombelo linaphimba dera la makilomita 5,200 mbali zonse zinayi, limene ukulu wake uli pafupifupi kuŵirikiza kasanu kuposa Hong Kong. Smith’s Bible Dictionary ikunena kuti dzombe “limasakaza moipa zomera m’maiko amene limapitako.”
M’vumbulutso lake lopatsidwa ndi Mulungu la zinthu zochitika “tsiku la Ambuye,” Yesu anagwiritsira ntchito masomphenya a dzombe. Ponena za ilo, kunanenedwa kuti: “Maonekedwe a dzombelo anafanana ndi akavalo okonzeka kukachita nkhondo.” (Chivumbulutso 1:1, 10; 9:3-7) Kodi tanthauzo la chizindikiro chimenechi linali lotani?
Mboni za Yehova kwa nthaŵi yaitali zadziŵa kuti dzombe la m’Chivumbulutso chaputala 9 limaimira atumiki odzozedwa a Mulungu padziko lapansi m’zaka za zana lino.a Akristu ameneŵa apatsidwa ntchito yochita—kulalikira uthenga wa Ufumu padziko lonse lapansi ndi kupanga ophunzira. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Zimenezi zimafuna kuti iwo agonjetse zopinga ndi kulimbikira pantchito yawo. Kodi nchiyaninso china chimene chikanaphiphiritsira zimenezi bwino lomwe kuposa dzombe losagonjalo?
Ngakhale kuti siliposa masentimita asanu m’litali, dzombe kaŵirikaŵiri limayenda mtunda wa makilomita 100 kapena 200 patsiku. Dzombe la m’chipululu lingaposedi pamenepo kufika pamtunda wa makilomita 1,000. GEO ikufotokoza kuti “mapiko ake amakupiza nthaŵi 18 pasekondi imodzi ndipo mpaka maola 17 patsiku—chinthu chimene kachilombo kena kalikonse sikangachite.” Ha, kacholengedwa kakang’ono kameneka kali ndi ntchito yaikulu chotani nanga!
Monga gulu, Mboni za Yehova nzolimba powanditsa uthenga wabwino wa Ufumu. Tsopano zikulalikira m’maiko oposa 230. Atumiki a Mulungu ameneŵa agonjetsa zovuta zambiri kuti atengemo mbali m’ntchito imeneyi. Kodi amakumana ndi zothetsa nzeru zotani? Zoŵerengeka za izo ndizo tsankhu, ziletso za lamulo, matenda, kulefulidwa, ndi chitsutso cha achibale. Koma palibe chimene chaletsa kupita kwawo patsogolo. Amaumirira pantchito yawo imene Mulungu anawapatsa.
Pitirizani Kusonyeza Mikhalidwe Yachikristu
Inde, Yesu anafanizira otsatira ake ndi nkhosa, njoka, nkhunda, ndi dzombe. Zimenezi nzoyenereradi m’tsiku lathu. Chifukwa? Chifukwa mapeto a dongosolo ili la zinthu ayandikira, ndipo zothetsa nzeru zikukulirakulira kuposa ndi kale lonse.
Pokumbukira mawu a fanizo a Yesu, Akristu oona amagwirizana zolimba ndi gulu la Mulungu ndipo modzichepetsa amalandira uphungu kuchokera ku gulu la Yehova. Amakhala osamala ndi atcheru m’mikhalidwe imene ingapinge ntchito zawo zachikristu, pamene kuli kwakuti amakhala opanda liwongo m’zinthu zonse. Ndiponso, amalimbikira kuchita chifuniro cha Mulungu poyang’anizana ndi zopinga. Ndipo amapitiriza kuphunzira ku zolengedwa zina “zanzeru mwachibadwa.”
[Mawu a M’munsi]
a Onani Revelation—Its Grand Climax At Hand!, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., mutu 22.