MUTU 89
Anaphunzitsa ku Pereya Ali pa Ulendo Wopita ku Yudeya
KUOPSA KOKHUMUDWITSA ENA
MUZIKHULULUKA KOMANSO MUZIKHALA NDI CHIKHULUPIRIRO
Yesu ‘atawoloka Yorodano’ anakhala m’chigawo cha Pereya kwa kanthawi. (Yohane 10:40) Kenako anachoka m’derali n’kuyamba kulowera chakum’mwera ku mzinda wa Yerusalemu.
Pa nthawiyi Yesu anali ndi ophunzira ake komanso “khamu lalikulu la anthu.” Pa gululi panalinso anthu ena ochimwa komanso okhometsa misonkho. (Luka 14:25; 15:1) Alembi ndi Afarisi omwe ankatsutsa zimene Yesu ankanena komanso kuchita analinso pagululo. Alembi ndi Afarisiwa ayenera kuti ankaganizira zinthu zambiri Yesu atawafotokozera fanizo la nkhosa yotayika, la mwana wotayika komanso la munthu wachuma ndi Lazaro.—Luka 15:2; 16:14.
Poganizira zimene anthu amene ankamutsutsa komanso kumunyogodola anachita, Yesu anayamba kulankhula ndi ophunzira ake. Anawafotokozera mfundo zina zomwe anawaphunzitsa ali ku Galileya.
Mwachitsanzo Yesu ananena kuti: “N’zosatheka kuti pakhale popanda zopunthwitsa. Koma tsoka kwa munthu amene zopunthwitsazo zimadzera mwa iye! . . . Samalani ndithu. Ngati m’bale wako wachita tchimo um’dzudzule, ndipo akalapa umukhululukire. Ngakhale akuchimwire maulendo 7 pa tsiku, n’kubwera kwa iwe maulendo 7, kudzanena kuti, ‘Ndalapa ine,’ umukhululukire ndithu.” (Luka 17:1-4) N’kutheka kuti mfundo imene Yesu anaitchula pomalizirayi inakumbutsa Petulo funso limene anafunsa lokhudza kukhululukira m’bale wake maulendo 7.—Mateyu 18:21.
Kodi ophunzirawo anachitadi zimene Yesu ananena? Atamuuza Yesu kuti: “Tiwonjezereni chikhulupiriro,” iye anawauza kuti: “Mukanakhala ndi chikhulupiriro chofanana ndi kanjere ka mpiru kuchepa kwake, mukanatha kuuza mtengo wa mabulosi uwu kuti, ‘Zuka pano, kadzibzale m’nyanjamo!’ ndipo ukanakumverani.” (Luka 17:5, 6) Choncho ngakhale munthu atakhala ndi chikhulupiriro chochepa chonchi akhoza kuchita zinthu zazikulu.
Yesu anapitiriza kuphunzitsa atumwi ake kufunika kokhala odzichepetsa komanso kuti asamadzione kuti ndi ofunika kwambiri. Iye anati: “Ndani wa inu angauze kapolo wake amene wangofika kumene kuchokera ku ntchito yolima kapena yoweta nkhosa kuti, ‘Fika kutebulo kuno msanga udzadye’? Kodi sadzamuuza kuti, ‘Ndikonzere chakudya chamadzulo, uvale epuloni ndi kunditumikira kufikira nditamaliza kudya ndi kumwa, pambuyo pake iwenso udye ndi kumwa’? Ndipo munthuyo sangamuyamike kapoloyo chifukwa zimene wachitazo ndi ntchito yake, si choncho kodi? Chimodzimodzi inunso, mukachita zonse zimene munapatsidwa ngati ntchito yanu, muzinena kuti, ‘Ife ndife akapolo opanda pake. Tangochita zimene tinayenera kuchita.’”—Luka 17:7-10.
Mtumiki wa Mulungu aliyense ayenera kumvetsa kufunika koika pa malo oyamba zimene Mulungu amafuna. Ayeneranso kukumbukira kuti ali ndi mwayi wapadera wolambira Mulungu monga mmodzi wa anthu a m’banja la Mulungu.
Yesu atangomaliza kunena mawu amenewa, panafika munthu wina amene anatumidwa ndi Mariya komanso Marita. Mariya ndi Marita anali azichemwali ake a Lazaro ndipo ankakhala ku Betaniya wa ku Yudeya. Munthuyo anabwera ndi uthenga wakuti: “Ambuye! amene mumamukonda uja akudwala.”—Yohane 11:1-3.
Ngakhale kuti Yesu anamva zoti Lazaro, yemwe anali mnzake, akudwala kwambiri sanasokonezeke maganizo chifukwa cha chisoni. M’malomwake ananena kuti: “Kudwala kumeneku si kwa imfa chabe, koma n’kopatsa Mulungu ulemerero, kuti mwa kudwalako, Mwana wa Mulungu alemekezeke.” Yesu anakhalabe kumene analiko masiku ena awiri kenako anauza ophunzira ake kuti: “Tiyeni tipitenso ku Yudeya.” Koma ophunzirawo sanagwirizane ndi zimenezi ndipo anamufunsa kuti: “Rabi, posachedwapa Ayudeya anafuna kukuponyani miyala, ndiye mukufuna kupitanso komweko kodi?”—Yohane 11:4, 7, 8.
Yesu anayankha kuti: “Kodi usana suli ndi maola 12? Munthu akayenda masana palibe chimamupunthwitsa, chifukwa amaona kuwala kwa dzikoli. Koma munthu akayenda usiku, amapunthwa pa chinachake chifukwa mwa iye mulibe kuwala.” (Yohane 11:9, 10) Ponena zimenezi iye ankatanthauza kuti nthawi imene Mulungu anamupatsa kuti achite utumiki wake inali isanathe. Choncho Yesu ankafunika kugwiritsa ntchito nthawi yochepa yomwe anali nayo mwanzeru.
Yesu ananenanso kuti: “Bwenzi lathu Lazaro ali m’tulo akupumula, koma ndikupita kumeneko kukamudzutsa ku tulo take.” Chifukwa chakuti ophunzira a Yesu ankaganiza kuti Lazaro wagona kuti apume moti achira, iwo ananena kuti: “Ambuye, ngati iye akupumula, apeza bwino.” Koma Yesu anawauza mosapita m’mbali kuti: “Lazaro wamwalira, . . . Tsopano tiyeni tipite kwa iye.”—Yohane 11:11-15.
Tomasi ankadziwa kuti Yesu akhoza kukaphedwa ku Yudeya komabe pofuna kumulimbikitsa, anauza ophunzira anzakewo kuti: “Ifenso tiyeni tipite, kuti tikafere naye limodzi.”—Yohane 11:16.