NKHANI YOPHUNZIRA 16
Tizitsatira Mfundo za Choonadi Pakachitika Maliro
‘Timadziwa mawu ouziridwa oona kapena abodza.’—1 YOH. 4:6.
NYIMBO NA. 73 Tithandizeni Kukhala Olimba Mtima
ZIMENE TIPHUNZIREa
1-2. (a) Kodi Satana wakhala akupusitsa bwanji anthu? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?
SATANA ndi “tate wake wa bodza” ndipo wakhala akunamiza anthu kuyambira pamene anthu oyamba analengedwa. (Yoh. 8:44) Mabodza ena ndi okhudza imfa ndipo ena ndi okhudza zimene zimachitika pambuyo pa imfa. Zinthu zambiri zimene anthu amakhulupirira masiku ano zimachokera pa mabodza amenewa. Chifukwa cha zimenezi, abale ndi alongo amafunika “kumenya mwamphamvu nkhondo yachikhulupiriro” ngati munthu wamwalira m’banja lawo kapena m’dera limene amakhala.—Yuda 3.
2 Ngati zoterezi zitakuchitikirani, kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti muzitsatirabe zimene Baibulo limanena pa nkhani ya imfa? (Aef. 6:11) Nanga mungatani kuti mulimbikitse komanso kuthandiza Mkhristu amene akukakamizidwa kuti achite nawo miyambo yomwe sisangalatsa Mulungu? Munkhaniyi tikambirana malangizo a Yehova amene angatithandize. Choyamba, tiyeni tikambirane zimene Baibulo limanena pa nkhani ya imfa.
ZIMENE ZIMACHITIKA MUNTHU AKAMWALIRA
3. Kodi zotsatira za bodza loyambirira zinali zotani?
3 Cholinga cha Mulungu sichinali choti anthu azifa. Koma kuti Adamu ndi Hava asafe, anafunika kumvera lamulo losavuta limene Yehova anawapatsa. Anawauza kuti: “Zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu uzidya ndithu. Koma usadye zipatso za mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa. Chifukwa tsiku limene udzadya, udzafa ndithu.” (Gen. 2:16, 17) Koma kenako, Satana anabwera kudzalankhula ndi Hava ndipo anagwiritsa ntchito njoka. Iye anati: “Kufa simudzafa ayi.” N’zomvetsa chisoni kuti Hava anamvera bodzali n’kudya chipatsocho. Kenako mwamuna wake anadyanso. (Gen. 3:4, 6) Izi zinachititsa kuti uchimo ndi imfa zifalikire kwa anthu onse.—Aroma 5:12.
4-5. Kodi Satana akufalitsanso bodza liti?
4 Mogwirizana ndi zimene Mulungu ananena, Adamu ndi Hava anafa. Koma Satana sanasiye kunena mabodza okhudza imfa. Pa nthawi ina, iye anayamba kufalitsa mabodza ena. Bodza lina ndi lakuti munthu akamwalira, thupi ndi limene limafa koma mzimu wake umapitirizabe kukhala ndi moyo. Kuyambira kalekale, anthu ambiri akhala akukhulupirira bodza limeneli.—1 Tim. 4:1.
5 N’chifukwa chiyani anthu ambiri amakhulupirira bodzali? Satana amadziwa mmene anthu ambiri amamvera pa nkhani ya imfa ndiye amapezerapo mwayi kuti awapusitse. Anthufe tinalengedwa kuti tisamafe choncho sitifuna kufa. (Mlal. 3:11) Tonse timaona kuti imfa ndi mdani wathu.—1 Akor. 15:26.
6-7. (a) Kodi Satana wakwanitsa kubisira anthu zoona zake pa nkhani ya imfa? Fotokozani (b) Kodi mfundo za m’Baibulo zimatithandiza bwanji?
6 Koma ngakhale kuti Satana wachita zonsezi, zoona zake pa nkhani ya imfa sizinabisike. Panopa anthu ambiri akudziwa komanso kuuza anzawo zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani ya imfa komanso zimene zidzachitikire akufa. (Mlal. 9:5, 10; Mac. 24:15) Kudziwa zoona pa nkhani ya akufa kumatilimbikitsa ndipo kumatithandiza kuti tisiye kuchita mantha kapena kukayikakayika. Mwachitsanzo, sitiopa anthu akufa kapena kuopa kuti chinachake chingawachitikire. Timadziwa kuti iwo kulibe ndipo sangavulaze aliyense. Zimangokhala ngati agona tulo teniteni. (Yoh. 11:11-14) Timadziwa kuti akufa sadziwanso za nthawi imene ikudutsa. Choncho ngakhale anthu amene anafa kalekale kwambiri akadzaukitsidwa adzangoganiza kuti nthawi imene yadutsa ndi yochepa kwambiri.
7 Kunena zoona, zimene zimachitika munthu akamwalira n’zomveka komanso zosavuta kufotokoza. Komatu umu si mmene zilili ndi mabodza amene Satana amafalitsa. Mabodza amenewa amasokoneza anthu komanso kunyozetsa Mlengi wathu. Kuti timvetse mavuto amene abwera chifukwa cha mabodza a Satana, tiyeni tikambirane mafunso awa: Kodi mabodza a Satana anyozetsa bwanji Yehova? Kodi amalepheretsa bwanji anthu kukhulupirira nsembe ya dipo ya Khristu? Nanga achititsa bwanji anthu kuvutika komanso kumva chisoni kwambiri?
MABODZA A SATANA ABWERETSA MAVUTO AMBIRI
8. Malinga ndi Yeremiya 19:5, kodi bodza lina la Satana limanyozetsa bwanji Yehova?
8 Mabodza a Satana amanyozetsa Yehova. Ena mwa mabodzawa ndi akuti anthu akufa amakazunzidwa kumoto. Bodza limeneli limanyozetsa kwambiri Mulungu. Tikutero chifukwa chakuti limachititsa anthu kuganiza kuti Mulungu si wachikondi koma wankhanza ngati Satana. (1 Yoh. 4:8) Kodi inuyo mumamva bwanji mukaganizira zimenezi? Nanga mukuganiza kuti Yehova amamva bwanji? Pajatu Yehova amadana ndi nkhanza zamtundu uliwonse.—Werengani Yeremiya 19:5.
9. Kodi bodza la Satana limalepheretsa bwanji anthu kukhulupirira nsembe ya Khristu yofotokozedwa pa Yohane 3:16 ndi 15:13?
9 Mabodza a Satana amalepheretsa anthu kukhulupirira nsembe ya dipo ya Yesu. (Mat. 20:28) Bodza lina la Satana ndi lakuti mzimu wa munthu suufa. Zimenezi zikanakhala zoona, ndiye kuti anthu onse adzakhala ndi moyo wosatha. Zikanakhaladi choncho ndiye kuti Khristu sakanafunika kupereka moyo wake kuti tidzapeze moyo wosatha. Koma tizikumbukira kuti nsembe ya Khristu imasonyeza chikondi chapamwamba kwambiri kuposa chikondi chilichonse chimene anthufe tinasonyezedwa. (Werengani Yohane 3:16; 15:13.) Ndiye mukuganiza kuti Yehova ndi Mwana wake amamva bwanji akaona anthu akukhulupirira zimenezi?
10. Kodi mabodza a Satana achititsa bwanji anthu kuvutika komanso kumva chisoni kwambiri?
10 Mabodza a Satana amachititsa kuti anthu azivutika komanso kumva chisoni kwambiri. Makolo amene mwana wawo wamwalira amauzidwa kuti Mulungu watenga mwana wawoyo, mwina kuti akakhale mngelo kumwamba. Kodi bodza limeneli limachititsa kuti chisoni cha anthu chichepe kapena chiwonjezeke? Bodza lakuti anthu ena amapita kumoto lachititsa anthu kuganiza kuti palibe vuto kuzunza anzawo. Mwachitsanzo, anthu ena amene ankatsutsa zimene tchalitchi cha Katolika chimaphunzitsa, anakhomeredwa pamtengo kenako n’kuwotchedwa. Pofotokoza za nkhanza zimenezi, buku lina linafotokoza kuti ankawawotcha kuti alawe ululu wamoto n’kulapa n’cholinga choti akafa asadzapite kumoto. M’mayiko ambiri, anthu amalambira makolo akufa, kuwalemekeza komanso kuwapempha kuti awadalitse. Ena amachita zinthu kuti awasangalatse n’cholinga choti asawalange. Vuto ndi lakuti zinthu zimene anthu amakhulupirira chifukwa cha mabodzawa siziwalimbikitsa. M’malomwake, zimangowachititsa kuda nkhawa komanso kuchita mantha.
TIZITSATIRA MFUNDO ZOONA ZA M’BAIBULO
11. Kodi anzathu kapena achibale angachite zinthu ziti zomwe zingatilepheretse kutsatira mfundo za m’Baibulo?
11 Kukonda Mulungu ndi Mawu ake kumatilimbikitsa kumvera Yehova ngakhale pa nthawi imene achibale kapena anzathu akutikakamiza kuti tichite miyambo yokhudza anthu akufa. Mwina angatinyoze potinena kuti sitikonda kapena kulemekeza anthu amene amwalirawo. Mwinanso anganene kuti zochita zathu zingachititse kuti anthu akufawo avulaze anthu ena amoyo. Ndiye kodi tingatani kuti titsatirebe mfundo za choonadi? Tiyeni tikambirane mfundo zina za m’Baibulo zimene zingatithandize.
12. Tchulani miyambo ina yokhudza akufa imene imasemphana ndi Malemba.
12 “Lekanani” ndi zikhulupiriro zosemphana ndi Malemba. (2 Akor. 6:17) Ku Caribbean, anthu amakhulupirira kuti munthu akamwalira, mzimu wake umakhala m’deralo ndipo umalanga anthu onse amene ankamuchitira zoipa. Ena amanena kuti mzimuwo ukhoza kubweretsa mavuto m’dera lonse. M’mayiko ena a ku Africa, anthu amasonkha moto usiku wonse panyumba imene pali maliro. Ena amati zimenezi zimathandiza kuti mizimu yoipa isabwere panyumbapo. Koma anthu a Yehovafe sitichita nawo miyambo kapena kukhulupirira zinthu zimene zinayamba chifukwa cha mabodza a Satana.—1 Akor. 10:21, 22.
13. Mogwirizana ndi Yakobo 1:5, kodi mungatani ngati simukudziwa zoyenera kuchita pa miyambo inayake?
13 Ngati simukudziwa zoyenera kuchita pa miyambo inayake muyenera kupemphera kwa Yehova kuti akupatseni nzeru. (Werengani Yakobo 1:5.) Kenako mungafufuze m’mabuku athu. Mwinanso tingafunse akulu mumpingo wathu. Iwo sangakusankhireni zochita koma angakukumbutseni mfundo za m’Baibulo ngati zimene tikukambiranazi. Mukamachita zimenezi, mumaphunzitsa ‘mphamvu zanu za kuzindikira’ kuti muzitha “kusiyanitsa choyenera ndi chosayenera.”—Aheb. 5:14.
14. Kodi tingapewe bwanji kukhumudwitsa ena?
14 “Chitani zonse kuti zibweretse ulemerero kwa Mulungu. Pewani kukhala okhumudwitsa.” (1 Akor. 10:31, 32) Tikamasankha zoyenera kuchita pa nkhani ya miyambo inayake tiziganiziranso mmene zingakhudzire anthu ena, makamaka Akhristu anzathu. Tiyenera kupewa kukhumudwitsa ena. (Maliko 9:42) Ngati zingatheke, tizipewanso kukhumudwitsa anthu omwe si Akhristu. Ndipo ngati ndife achikondi, tidzayesetsa kulankhula mwaulemu n’cholinga choti Yehova alemekezeke. Si bwino kukangana ndi anthu kapena kunyoza zimene amakhulupirira. Tizikumbukira kuti chikondi ndi champhamvu kwambiri. Tikamasonyeza chikondi polankhula ndi anthu mwaulemu komanso mowaganizira, tikhoza kufewetsa mitima ya anthu amene amadana nafe.
15-16. (a) Kodi kuuziratu anthu zimene timakhulupirira kungatithandize bwanji? Perekani chitsanzo. (b) Kodi tingatsatire bwanji mawu a Paulo a pa Aroma 1:16?
15 Anthu m’dera lanu azidziwa kuti ndinu a Mboni za Yehova. (Yes. 43:10) Ngati achibale ndi anthu am’dera lanu amadziwa zoti ndinu a Mboni za Yehova, zimakhala zosavuta kuthana ndi mavuto amene angayambitse mikangano. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi m’bale wina wa ku Mozambique dzina lake Francisco. Iye anati: “Ine ndi mkazi wanga Carolina titangophunzira choonadi tinauziratu achibale athu kuti tasiya kulambira akufa. Zinthu zinavuta kwambiri pamene mchemwali wake wa Carolina anamwalira. M’dera lathu muli mwambo wosambitsa maliro. Pamwambowu, wachibale wapafupi kwambiri amafunika kugona masiku atatu pamalo pamene anatayira madzi osambitsira malirowo. Anthu amanena kuti zimenezi zimathandiza kuti mzimu wa wakufayo usakwiye. Ndiyeno achibale a Carolina ankafuna kuti iye achite zimenezi.”
16 Kodi Francisco ndi mkazi wake anatani? Francisco anati: “Popeza timakonda Yehova ndipo sitifuna kumukhumudwitsa, tinakana kuchita zimenezi. Achibale a Carolina anakwiya kwambiri. Iwo ananena kuti sitilemekeza akufa choncho asiyiratu kutiyendera kapena kutithandiza. Popeza tinawafotokozera kale nkhaniyi, zinathandiza kuti tisakambirane nawo pa nthawi yovutayi. Achibale ena anali kumbali yathu n’kukumbutsa anzawo zimene tinafotokoza kale. Patapita nthawi, mitima yawo inakhala m’malo ndipo tinagwirizananso. Ndipo ena anafika pobwera kunyumba kwathu kudzapempha mabuku.” Tiyeni tonse tisamachite manyazi kutsatira mfundo za m’Baibulo zokhudza akufa.— Werengani Aroma 1:16.
TIZILIMBIKITSA KOMANSO KUTHANDIZA ANTHU AMENE AFEREDWA
17. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tikhale bwenzi lenileni kwa Mkhristu mnzathu?
17 Mkhristu mnzathu akaferedwa tiyenera kuyesetsa kukhala “bwenzi lenileni . . . ndi m’bale amene anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.” (Miy. 17:17) Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tikhale “bwenzi lenileni” pa nthawi imene m’bale kapena mlongo akukakamizidwa kuti achite miyambo yosemphana ndi Malemba? Pali mfundo ziwiri za m’Baibulo zimene zingatithandize pa nkhaniyi.
18. N’chifukwa chiyani Yesu anagwetsa misozi, nanga tikuphunzira chiyani pa zimene anachitazi?
18 “Lirani ndi anthu amene akulira.” (Aroma 12:15) Nthawi zina tikakhala ndi munthu amene waferedwa timasowa chonena. Koma tizikumbukira kuti akangotiona tikulira zimawathandiza kudziwa kuti timawaganizira. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zimene Yesu anachita Lazaro atamwalira. Mariya, Marita ndi anthu ena ankalira. Patapita masiku 4, Yesu anafika ndipo nayenso anagwetsa misozi. Anachita zimenezi ngakhale kuti ankadziwa kuti amuukitsa Lazaro pasanapite nthawi yaitali. (Yoh. 11:17, 33-35) Kulira kwa Yesu kunasonyeza mmene Yehova anamveranso Lazaro atamwalira. Zimene anachitazi zinalimbikitsa kwambiri Mariya ndi Marita chifukwa anazindikira kuti iye amawakonda kwambiri. Abale athunso akazindikira kuti timawaganizira komanso kuwakonda, amadziwa kuti sali okha koma ali ndi anzawo amene angawathandize.
19. Kodi tingatsatire bwanji lemba la Mlaliki 3:7 polimbikitsa Mkhristu amene waferedwa?
19 Pali “nthawi yokhala chete ndi nthawi yolankhula.” (Mlal. 3:7) Njira ina yolimbikitsira Akhristu anzathu amene aferedwa ndi kumvetsera pamene akulankhula. Tiyenera kulola m’bale wathu amene waferedwa kufotokoza zimene zili mumtima mwake ndipo tisamakhumudwe ngati akulankhula “zopanda pake.” (Yobu 6:2, 3) Tikutero chifukwa choti munthuyo akhoza kukhala atapanikizika ndi zochita za achibale ake omwe si Mboni. Choncho tiyenera kupemphera naye. Tizipempha “wakumva pemphero” kuti amupatse mphamvu komanso nzeru. (Sal. 65:2) Ngati n’zotheka, tikhoza kuwerenga naye Baibulo. Apo ayi, tingawerenge nkhani yolimbikitsa ya m’mabuku athu kapena mbiri ya moyo wa munthu wina imene ingamulimbikitse.
20. Kodi tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?
20 Ndi mwayi waukulu kudziwa zoona pa nkhani ya imfa komanso chiyembekezo chakuti akufa adzauka. (Yoh. 5:28, 29) Choncho mawu ndi zochita zathu ziyenera kusonyeza kuti timatsatira mfundo za m’Baibulo. Tiziuzanso anthu zimene timakhulupirira mpata ukangopezeka. Munkhani yotsatira tidzaona njira ina imene Satana akupusitsira anthu. Njira yake ndi yokhudza kukhulupirira mizimu. Tidzakambirana chifukwa chake tiyenera kupewa miyambo komanso zosangalatsa zimene zingachititse kuti tikodwe mumsampha wa ziwanda.
NYIMBO NA. 24 Bwerani Kuphiri la Yehova
a Satana ndi ziwanda zake akhala akunamiza anthu pa nkhani ya zimene zimachitika munthu akamwalira. Mabodza amenewa achititsa kuti anthu azichita miyambo yosemphana ndi Malemba. Nkhaniyi itithandiza kuti tizikhalabe okhulupirika kwa Yehova pamene anthu akutikakamiza kuti tichite nawo miyamboyi.
b MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mayi akulira chifukwa choti waferedwa ndipo achibale ake omwe ndi a Mboni akumulimbikitsa.
c MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Pambuyo pofufuza miyambo yokhudza maliro, wa Mboni akufotokozera achibale ake zimene amakhulupirira.
d MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Akulu akulimbikitsa m’bale amene waferedwa.