Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Ku Betaniya, m’Nyumba ya Simoni
PAMENE Yesu achoka ku Yeriko, iye akulinga ku Betaniya. Ulendowo ukutenga mbali yokulira ya tsikulo, popeza uli kukwezeka kwa makilomita 19 modutsa minda yovuta. Yeriko ali chifupifupi mamita 250 pansi pa malekezero a nyanja, ndipo Betaniya ali mamita 760 pamwamba pa malekezero a nyanja. Mungakumbukire kuti Betaniya, ndiko kwawo kwa Lazaro ndi alongo ake. Mudzi waung’onowo uli pa mtunda wa chifupifupi makilomita atatu kuchokera ku Yerusalemu, ukumakhala kumbali yotsetsereka yakum’mawa kwa Phiri la Azitona.
Ambiri afika kale mu Yerusalemu kaamba ka Paskha. Iwo abwera msanga kuti adzadziyeretse iwo eni mwamwambo. Mwinamwake iwo akhudza mitembo kapena achita chinachake chomwe chawapangitsa kukhala odetsedwa. Chotero akutsatira dongosolo lokhazikitsidwa la kudziyeretsa iwo eni kotero kuti akondwerere Paskha molandirika. Pamene ofika msangawa asonkhana pa kachisipo, ambiri akulingalira ngati Yesu adzabwera ku Paskha.
Yerusalemu ali malo apakati a mkangano wonena za Yesu. Nchodziŵika kuti atsogoleri achipembedzo akufuna kumgwira iye ndi kumupha. M’chenicheni, iwo apereka malamulo akuti ngati alipo aliyense wodziŵa kumene ali, ayenera kuwawuza iwo. Nthaŵi zitatu miyezi ya posachedwapa—pa Phwando la Misasa, pa Phwando la Kukonzanso, ndipo pambuyo pa kuukitsa Lazaro—atsogoleri amenewa anayesera kumupha. Chotero, anthu akuzizwa kuti, kodi Yesu adzadzivumbula kwa nthaŵi inanso? “Muyesa bwanji inu” iwo akufunsana wina ndi mnzake. “Sadzadza ku phwando kodi?”
Pa nthaŵiyo, Yesu afika ku Betaniya masiku asanu ndi limodzi lisanafike Paskha, yomwe iri pa Nisani 14 mogwirizana ndi kalenda Yachiyuda. Yesu akufika ku Betaniya Lachisanu madzulo, pomwe pali pamayambiriro pa Nisani 8. Iye sakanaupanga ulendo wa ku Betaniya pa Loŵeruka chifukwa chakuti kuyenda pa la Sabata—kuyambira pa kuloŵa kwa dzuŵa Lachisanu mpaka kuloŵa kwa dzuŵa Loŵeruka—kuli koletsedwa mwa lamulo Lachiyuda. Yesu mwinamwake akupita kunyumba ya Lazaro, monga momwe anachitira kalelo, ndi kugona kumeneko Lachisanu.
Komabe, nzika ina ya m’Betaniya akumuitana Yesu ndi mabwenzi ake ku chakudya chamadzulo Loŵeruka madzulo. Munthuyo ali Simoni, yemwe kale anali wakhate, yemwe poyambirirapo mwinamwake anachiritsidwa ndi Yesu. Lazaro ali pakati pa awo akuseyama pa chakudya ndi Yesu. M’kusungirira mkhalidwe wake wachangu, Malita akutumikira alendowo. Koma, mwapadera, Mariya akupereka chisamaliro kwa Yesu, nthaŵi ino m’njira yomwe ikudzutsa mkangano.
Mariya atsegula nsupa ya alabastero, kapena fulasiki yaing’ono, yomwe imanyamula theka la kilogramu ya mafuta onunkhira, “anardo weniweni.” Iwo ali a mtengo wapatali kwenikweni. Ndithudi, mtengo wake uli wofanana ndi malipiro a chaka chathunthu! Pamene Mariya atsanulira mafutawo pamutu pa Yesu ndi pa mapazi ake ndi kupukuta mapazi ake ndi tsitsi lake, fungo lonunkhiralo likudzadza mnyumba monsemo.
Ophunzirawo akukwiya ndi kufunsa kuti: “Chifukwa ninji kuwononga koteroko?” Kenaka Yudase Iskariyote akunena kuti: “Nanga mafuta onunkhirawa sanagulitsidwe chifukwa ninji ndi malupiya a theka mazana atatu, ndi kupatsidwa kwa osauka?” Koma Yudase sali wodera nkhaŵa konse ponena za osauka, popeza iye wakhala akuba kuchokera m’thumba la zoikamo losungidwa ndi ophunzirawo.
Yesu akuchinjiriza Mariya. “Mleke iye,” iye akulamula tero. “Muvutiranji mkaziyu? Popeza andichitira ine ntchito yabwino. Pakuti nthaŵi zonse muli nawo aumphawi pamodzi nanu; koma simuli ndi ine nthaŵi yonse. Pakuti mkaziyo, mmene anathira mafuta awa pathupi panga, wandichitiratu ichi pa kuikidwa kwanga. Indetu ndinena kwa inu, kumene kuli konse uthenga wabwino udzalalikidwa m’dziko lonse lapansi, ichi chimene mkaziyo anachitachi chidzakambidwanso chikumbukiro chake.”
Tsopano Yesu wakhala mu Betaniya kwa maola oposa 24, ndipo mphekesera ya kukhalapo kwake yafalikira. Chotero, ambiri akudza kunyumba ya Simoni kudzawona Yesu, koma akudzanso kudzawona Lazaro. Chotero akulu ansembe akupereka uphungu wakupha osati kokha Yesu komanso Lazaro. Ichi chiri chifukwa chakuti anthu ambiri akuika chikhulupiriro mwa Yesu chifukwa cha kuwona wamoyo uja yemwe anamuukitsa kwa akufa! Zowonadi, atsogoleri achipembedzo amenewa ali oipa chotani nanga! Yohane 11:55-12:11; Mateyu 26:6-13; Marko 14:3-9; Machitidwe 1:12.
◆ Kodi ndi liti pamene Yesu akufika m’Betaniya, ndipo nkuti kumene iye mwachidziŵikire akuthera Sabata?
◆ Kodi ndi kukambitsirana kotani komwe kukuchitika pa kachisi, ndipo nchifukwa ninji?
◆ Kodi nkachitidwe kotani ka Mariya komwe kakudzutsa mkangano, ndipo kodi ndimotani mmene Yesu akumuchinjirizira mkaziyo?
◆ Kodi nchiyani chimene chikusonyeza ukulu wa kuipa kwa ansembe aakulu?