Yehova Amasunga Anthu Amene Amamudalira
“Chifundo chanu ndi choonadi chanu zindisunge chisungire.”—SALMO 40:11.
1. Kodi Mfumu Davide anapempha kuti Yehova amuchitire chiyani, ndipo kodi pakali pano Yehova akuliyankha bwanji pempholi?
MFUMU DAVIDE ya Israyeli wakale ‘inayembekeza Yehova’ ndi mtima wonse ndipo motero inanena kuti Yehova ‘anamva kufuula kwake.’ (Salmo 40:1) Nthawi zambirimbiri, Davide anaona mmene Yehova anasungira anthu omukonda. N’chifukwa chake Davide anapempha kuti nthawi zonse Yehova azimusunga. (Salmo 40:11) Davide ali m’gulu la amuna ndi akazi okhulupirika olonjezedwa “kuuka koposa,” motero pakali pano iye ndi wosungika m’chikumbumtima cha Yehova kudikirira kudzalandira mphoto imeneyi. (Ahebri 11:32-36) Choncho tsogolo lake n’lotsimikizika m’njira yabwino kuposa ina iliyonse. Dzina lake linalembedwa mu “buku la chikumbutso” la Yehova.—Malaki 3:16.
2. Kodi Malemba amatithandiza bwanji kumvetsa tanthauzo la kusungidwa ndi Yehova?
2 Ngakhale kuti anthu okhulupirika otchulidwa mu Ahebri chaputala 11 anakhalako Yesu Kristu asanabwere padziko lapansi, iwowa ankakhala moyo wogwirizana ndi zimene Yesu anaphunzitsa, zakuti: “Iye wokonda moyo wake adzautaya; ndipo wodana ndi moyo wake m’dziko lino lapansi adzausungira ku moyo wosatha.” (Yohane 12:25) Motero, n’zoonekeratu kuti kusungidwa ndi Yehova sikutanthauza kutetezedwa kuti tisavutike kapena kuzunzidwa. Kumatanthauza kukhala otetezeka mwauzimu kuti tithe kukhala ndi mbiri yabwino ndi Mulungu.
3. Kodi pali umboni wotani wakuti Kristu Yesu anasungidwa ndi Yehova, ndipo kodi zotsatira zake zinali zotani?
3 Yesu mwini ananyozedwa ndi kuzunzidwa koopsa, ndipo mapeto ake adani ake anamupha m’njira yochititsa manyazi kwambiri komanso yopweteka mosaneneka. Komatu zimenezi sizikutsutsana ndi lonjezo limene Mulungu ananena loti adzasunga Mesiya. (Yesaya 42:1-6) Kuukitsidwa kwa Yesu patsiku lachitatu pambuyo pophedwa imfa yochititsa manyazi ija, kumatsimikizira kuti, monga mmene anachitira ndi Davide, Yehova anamva kufuula kwa Yesu pofuna thandizo. Poyankha kufuulaku, Yehova anam’patsa mphamvu zom’thandiza kukhalabe wokhulupirika. (Mateyu 26:39) Posungidwa m’njira imeneyi, Yesu anapeza moyo wosafa kumwamba, ndipo anthu ochuluka zedi amene akhulupirira nsembe ya dipo apeza chiyembekezo cha moyo wosatha.
4. Kodi Akristu odzozedwa ndiponso a “nkhosa zina” ayenera kudalira malonjezo otani?
4 Tisakayike n’komwe kuti monga mmene Yehova analili panthawi ya Davide ndi Yesu, Iye n’ngofunitsitsabe kusunga atumiki ake masiku ano. (Yakobo 1:17) Abale a Yesu odzozedwa ochepa chabe amene adakali padziko lapansi pano ayenera kudalira lonjezo la Yehova lakuti: “Cholowa chosavunda ndi chosadetsa ndi chosafota, [chili] chosungikira m’Mwamba inu, amene musungidwa ndi mphamvu ya Mulungu mwa chikhulupiriro, kufikira chipulumutso chokonzeka kukavumbulutsidwa nthawi yotsiriza.” (1 Petro 1:4, 5) A “nkhosa zina,” omwe ali ndi chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi, ayeneranso kudalira Mulungu ndi lonjezo limene ananena kudzera mwa wamasalmo, lakuti: “Kondani Yehova, Inu nonse okondedwa ake: Yehova asunga okhulupirika.”—Yohane 10:16; Salmo 31:23.
Kusungidwa Mwauzimu
5, 6. (a) Kodi anthu a Mulungu akhala akusungidwa bwanji masiku ano? (b) Kodi odzozedwa ali ndi ubwenzi wotani ndi Yehova, nanga bwanji za amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi pano?
5 Masiku ano, Yehova wakonza njira zosungira anthu ake mwauzimu. Ngakhale kuti sawateteza kuti asamazunzidwe ndiponso kuti asamakumane ndi mavuto ndi masoka a m’moyo uno, iye mokhulupirika, amawathandiza ndiponso amawalimbikitsa kuti ateteze ubwenzi wolimba umene ali nawo ndi Yehovayo. Maziko a ubwenzi umenewu ndiwo chikhulupiriro chawo pa dipo limene Mulungu anapereka. Ena mwa Akristu okhulupirikawa adzozedwa ndi mzimu wa Mulungu kuti akalamulire limodzi ndi Kristu kumwamba. Mulungu amawaona kuti ndi olungama monga ana ake auzimu, ndipo mawu otsatirawa amanena za iwowa: “Anatilanditsa ife ku ulamuliro wa mdima, natisunthitsa kutilowetsa m’ufumu wa Mwana wa chikondi chake; amene tili nawo mawomboledwe mwa Iye, m’kukhululukidwa kwa zochimwa zathu.”—Akolose 1:13, 14.
6 Baibulo limatsimikizira Akristu ena ambirimbiri okhulupirika kuti nawonso angathe kupindula ndi dipo limene Mulungu anapereka. Limati: “Mwana wa munthu sanadza kutumikiridwa, koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la kwa anthu ambiri.” (Marko 10:45) Akristu amenewa amayembekezera kuti nthawi ikadzakwana adzapeza “ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.” (Aroma 8:21) Pakali pano, ubwenzi umene ali nawo paokhapaokha ndi Mulungu amauona kuti n’ngwamtengo wapatali kwambiri ndipo amayesetsa moona mtima kuulimbitsa.
7. Kodi Yehova amagwiritsira ntchito njira yotani posunga anthu ake mwauzimu masiku ano?
7 Njira imodzi imene Yehova amasungira anthu ake mwauzimu ndiyo kukonza njira yowaphunzitsira nthawi zonse. Zimenezi zimawathandiza kuti apitirize kuchidziwa bwino kwambiri choonadi. Yehova amatitsogoleranso nthawi zonse kudzera m’Mawu ake, gulu lake, ndiponso mzimu wake woyera. Motsogoleredwa ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” anthu a Mulungu padziko lonse ali ngati banja limodzi. Gulu la kapolo limathandiza banja la atumiki a Yehova m’njira yauzimu komanso m’njira zina zofunikira, mosaganizira kanthu za dziko kapena kupeza kwa anthu a m’banjali.—Mateyu 24:45.
8. Kodi Yehova amawakhulupirira motani atumiki ake okhulupirika, ndipo zimenezi zimawatsimikizira chiyani?
8 Yehova sanateteze Yesu kwa adani ake, ndipo masiku ano satetezanso Akristu m’njira imeneyi. Koma zimenezi sizisonyeza kuti Mulungu sawayanja. M’malomwake zimasonyeza kuti Mulungu amawakhulupirira kuti iwo azikhala ku mbali yake pa nkhani yaikulu yakuti ndani ali woyenera kulamulira chilengedwe chonse. (Yobu 1:8-12; Miyambo 27:11) Yehova sangataye anthu amene ali okhulupirika kwa iye, “pakuti Yehova akonda chiweruzo, ndipo sataya okondedwa ake: asungika kosatha.”—Salmo 37:28.
Kusungidwa ndi Chifundo Ndiponso Choonadi
9, 10. (a) Kodi choonadi cha Yehova chimasunga bwanji anthu ake? (b) Kodi Baibulo limasonyeza bwanji kuti Yehova amasunga anthu ake okhulupirika, mwa chifundo chake?
9 M’pemphero lake limene linalembedwa mu Salmo 40, Davide anapempha kuti Yehova amusunge ndi chifundo komanso choonadi chake. Chifukwa cha choonadi ndiponso kukonda kwake chilungamo Yehova amanena malamulo ake momveka bwino. Anthu amene amatsatira malamulo amenewa amatetezedwa kwambiri ku zinthu zosautsa, zochititsa mantha, ndiponso mavuto amene anthu onyalanyaza malamulowa amakumana nawo. Mwachitsanzo, tingathe kudziteteza komanso kuteteza anthu amene timawakonda ku mavuto ambiri adzaoneni tikamapewa zinthu monga mankhwala osokoneza bongo, uchidakwa, chiwerewere, ndiponso zachiwawa. Ngakhale anthu amene amasochera pochoka m’njira ya Yehova ya choonadi, monga anachitira Davide pa nthawi zina, sayenera kukayika kuti Mulungu adakali “mobisalira” mwa ochimwa amene alapa. Anthu oterewa anganene mosangalala kuti: “M’nsautso mudzandisunga.” (Salmo 32:7) Izitu zikusonyeza kuti chifundo cha Mulungu n’chachikulu zedi.
10 Chitsanzo china cha chifundo cha Mulungu n’chakuti iye amachenjeza atumiki ake kuti azidzipatula ku dziko loipali, limene iye adzaliwononge posachedwapa. Baibulo limatiuza kuti: “Musakonde dziko lapansi, kapena za m’dziko lapansi. Ngati wina akonda dziko lapansi, chikondi cha Atate sichili mwa iye. Pakuti chilichonse cha m’dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi.” Pochita zinthu momvera chenjezo limeneli, tingathe kudzisungira moyo wathuwu kosatha, pakuti lembali limapitirira motere: “Ndipo dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthawi yonse.”—1 Yohane 2:15-17.
Kusungidwa ndi Kulingalira, Kuzindikira, Ndiponso Nzeru
11, 12. Longosolani mmene kulingalira, kuzindikira, ndiponso nzeru zimatisungira.
11 Solomo, mwana wa Davide, anauziridwa kulemba mawu awa kwa anthu ofuna kuyanjidwa ndi Mulungu: “Kulingalira kudzakudikira, kuzindikira kudzakutchinjiriza.” Iye anatinso: “Tenga nzeru . . . usasiye nzeru, ndipo idzakusunga; uikonde, idzakutchinjiriza.”—Miyambo 2:11; 4:5, 6.
12 Timazindikira zinthu tikamasinkhasinkha zimene tikuphunzira m’Mawu a Mulungu. Kusinkhasinkhaku kumatithandiza kukhala ozindikira kwambiri kuti tizitha kuona zinthu zimene zili zofunikira koposa. Zimenezi n’zofunika kwambiri, chifukwa choti monga mmene ambirife tikudziwira, mwina kudzera m’zinthu zimene takumanapo nazo, anthu amatha kugwa m’mavuto akalephera kudziwa kuti chofunika kwambiri n’chiyani. Zilibe kanthu kuti akuchita zimenezo mwadala kapena ayi. Dziko la Satanali limatikhumbiza zinthu zoti tiziyesetsa kuzipeza, zinthu monga chuma, kutchuka ndiponso mphamvu, koma Yehova amatilimbikitsa kuti tizilimbana ndi zinthu zofunika kwambiri zauzimu. Kulephera kuika zinthu zauzimu patsogolo kungachititse kuti mabanja apasuke, anthu adane, ndiponso kuti tiiwale zolinga zauzimu. Mapeto ake munthu angathe kukumana ndi zimene Yesu ananena zakuti: “Pakuti munthu apindulanji akadzilemezera dziko lonse, natayapo moyo wake?” (Marko 8:36) Motero, n’chinthu chanzeru kumvera malangizo a Yesu otsatirawa: “Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.”—Mateyu 6:33.
Kuopsa Kokhala Wodzikonda
13, 14. Kodi kudzikonda kumatanthauza chiyani, ndipo kodi n’chifukwa chiyani si nzeru kukhala munthu wodzikonda?
13 Mwachibadwa anthu amakhala ndi mtima wochita zinthu zowakomera. Komano kukulitsa kwambiri mtima umenewu, kumabweretsa mavuto. Motero, Yehova amatilangiza kuti tizipewa kudzikonda kuti ubwenzi wathu ndi Iyeyo usungike. Kudzikonda kumatanthauza “kumangoganizira za zolakalaka, ndiponso zofuna zako zokha basi.” Kodi umu si mmene anthu ambiri alili masiku ano? N’zochititsa chidwi kuti Baibulo linalosera kuti mu “masiku otsiriza” a dongosolo loipa la Satanali, anthu “adzakhala odzikonda okha.”—2 Timoteo 3:1, 2.
14 Akristu amazindikira kuti n’chinthu chanzeru kumvera lamulo la Baibulo lakuti tiziganizira ena n’kumawakonda mmene timadzikondera ife eni. (Luka 10:27; Afilipi 2:4) Anthu ambiri amaona kuti izi n’zosatheka kuzikwanitsa, komatu zimenezi n’zofunika kwambiri kuti maukwati athu aziyenda bwino, kuti tizigwirizana ndi anthu a m’banja mwathu, komanso anzathu. Motero mtumiki weniweni wa Yehova sayenera kulola kuti chibadwa chofuna kuti zinthu zizingomukomera chimulowerere moti n’kuchita kufika pomuiwalitsa zinthu zina zofunika kwambiri. Chinthu choyamba pa zinthu zimenezi ndicho zinthu zokhudza Mulungu wake Yehova.
15, 16. (a) Kodi mzimu wofuna kuti zinthu zizingotikomera ifeyo ungam’chititse munthu zotani, ndipo perekani chitsanzo cha amene anatero? (b) Kodi munthu akamafulumira kuweruza ena, n’chiyani kwenikweni chimene amakhala akuchita?
15 Mtima wodzikonda ungachititse munthu kudziona ngati wolungama kuposa ena, motero munthuyo angakhale womva zake zokha, n’kusanduka wodzikuza. Baibulo limanena zoona kuti: “Uli wopanda mawu owiringula, munthu iwe, amene uli yense wakuweruza; pakuti mmene uweruza wina, momwemo udzitsutsa iwe wekha, pakuti iwe wakuweruza, umachita zomwezo.” (Aroma 2:1; 14:4, 10) Atsogoleri achipembedzo a m’nthawi ya Yesu ankadziona kuti n’ngolungama kwambiri moti ankaona kuti angathe kum’loza chala Yesu ndi ophunzira ake. Potero, anadziveka okha udindo wokhala oweruza. Chifukwa chosaona zolakwa zawo, chiweruzo chawocho chinawatembenukira iwo omwewo.
16 Yudasi, wotsatira wa Yesu amene anam’pereka, analola kuti kamzimu koweruza ena kam’kulire. Panthawi imene anali ku Betaniya, pamene Mariya, mlongo wa Lazaro Mariya anadzoza Yesu ndi mafuta onunkhira, Yudasi sanagwirizane nazo mpang’ono pomwe. Mopsa mtima iye anati: “Nanga mafuta onunkhira awa sanagulitsidwa chifukwa ninji ndi marupiya atheka mazana atatu, ndi kupatsidwa kwa osauka?” Koma Baibulo limafotokoza kuti: “Koma ananena ichi si chifukwa analikusamalira osauka, koma chifukwa anali mbala, ndipo pokhala nalo thumba, amaba zoikidwamo.” (Yohane 12:1-6) Tisakhale ngati Yudasi kapena atsogoleri achipembedzo aja, amene ankafulumira kuweruza ena, n’kupezeka kuti nkhani ikuwatembenukira iwo omwewo.
17. Longosolani kuopsa kodzikuza kapena kodzithemba kwambiri.
17 N’zomvetsa chisoni kuti ngakhale kuti Akristu ena oyambirira sanali mbala ngati Yudasi, iwo ankanyada, n’kukhala odzikuza. Ponena za anthu oterewa, Yakobo analemba kuti: “Mudzitamandira m’kudzikuza kwanu.” Kenaka anati: “Kudzitamandira kuli konse kotero n’koipa.” (Yakobo 4:16) Kudzitama chifukwa cha zinthu zimene tachita kapena chifukwa cha maudindo apadera amene tili nawo muutumiki wa Yehova n’kungodzivutita. (Miyambo 14:16) Tikumbukire zimene zinam’chitikira mtumwi Petro, amene panthawi ina anadzithemba kwambiri n’kunena kuti: “Ngakhale onse adzakhumudwa chifukwa cha Inu, ine sindidzakhumudwa nthawi zonse. . . . Ngakhale ine ndikafa ndi Inu, sindidzakukanani Inu iyayi.” Kunena zoona, tilibe chilichonse chimene tingadzitamire. Chilichonse chomwe tili nacho tinachipeza mwa chifundo cha Yehova. Kukumbukira zimenezi kungatithandize kuti tisakhale odzikuza.—Mateyu 26:33-35, 69-75.
18. Kodi kunyada Yehova amakuona bwanji?
18 Baibulo limati “Kunyada kutsogolera kuonongeka; mtima wodzikuza ndi kutsogolera kupunthwa.” N’chifukwa chiyani limatero? Yehova anayankha kuti: “Kunyada, ndi kudzikuza . . . ndizida.” (Miyambo 8:13; 16:18) N’zosadabwitsa kuti Yehova anapsa mtima ndi “zipatso za mtima wolimba wa mfumu ya Asuri, ndi ulemerero wa maso ake okwezedwa.” (Yesaya 10:12) Yehova analanga mfumu imeneyi chifukwa cha zipatso kapena kuti kudzikuza kwa mtima wake. Posachedwapa, dziko lonse la Satanali, pamodzi ndi atsogoleri ake odzikuza, ooneka ndi osaoneka omwe, adzalangidwa. Tiyeni tipeweretu mzimu wodzithemba womwe adani a Yehova ali nawo.
19. Kodi anthu a Mulungu n’ngonyada komanso n’ngodzichepetsa m’njira yotani?
19 Akristu oona ayenera kunyada chifukwa chokhala atumiki a Yehova. (Yeremiya 9:24) Koma panthawi yomweyo, ayenera kukhala odzichepetsa. N’chifukwa chiyani ayenera kutero? Chifukwa chakuti “onse anachimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu.” (Aroma 3:23) Motero pofuna kuteteza mwayi wathu wotumikira Yehova, tiyenera kukhala ndi mzimu wa mtumwi Paulo, amene anati: “Kristu Yesu anadza ku dziko lapansi kupulumutsa ochimwa.” Kenaka anamaliza n’kunena kuti: “Wa iwowa ine ndine woposa.”—1 Timoteo 1:15.
20. Kodi Yehova amasunga motani anthu ake masiku ano, ndipo kodi adzawasunga motani m’tsogolo?
20 Poti anthu a Yehova amasangalala kusiya kaye zofuna zawo kuti atsogoze zofuna zake, tisakayikire n’komwe kuti iye apitiriza kuwasunga mwauzimu. Tisakayikirenso kuti chisautso chachikulu chikadzabwera, Yehova adzasunga anthu ake mwauzimu komanso adzawatetezadi zenizeni. Akadzalowa m’dziko latsopano la Mulungu, adzanena mosangalala kuti: “Taonani, uyu ndiye Mulungu wathu; tam’lindirira Iye, adzatipulumutsa; uyu ndiye Yehova, tam’lindirira Iye, tidzakondwa ndi kusekerera m’chipulumutso chake.”—Yesaya 25:9.
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi Mfumu Davide ndi Yesu Kristu anasungidwa motani?
• Kodi anthu a Yehova masiku ano amasungidwa motani?
• Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kukhala wodzikonda?
• Kodi zingatheke bwanji kukhala onyada koma tili odzichepetsa?
[Zithunzi patsamba 9]
Kodi Yehova anasunga bwanji Davide ndiponso Yesu?
[Zithunzi pamasamba 10, 11]
Kodi anthu a Mulungu amasungidwa m’njira zotani mwauzimu masiku ano?
[Zithunzi patsamba 12]
Ngakhale timanyada potumikira Yehova, tiyenera kudzichepetsa nthawi zonse