Tsiku Loyenera Kulikumbukira
‘Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa ine mukakhale nawo mtendere. M’dziko lapansi mudzakhala nacho chivuto, koma limbikani mtima; ndalilaka dziko lapansi ine.’—YOHANE 16:33.
1, 2. Kodi nditsiku liti m’mbiri yonse limene liri lapadera pamasiku onse, ndipo chifukwa ninji?
DZIKO lerolino liri nzambiri zonena pankhani ya mtendere. Kumapeto kwa Nkhondo Yadziko ya II, mtendere unagwirizanitsidwa ndi V-E Day ndi V-J Day.a Chaka ndi chaka, Kirisimasi imapangitsa anthu kuganizira za ‘mtendere padziko lapansi.’ (Luka 2:14) Koma pali tsiku limodzi m’mbiri yonse ya anthu limene liri lapadera kuposa onse. Ndilo tsiku pamene Yesu Kristu analankhula mawu ogwidwa ali pamwambapa. Mwa masiku mamiliyoni aŵiri ndi kuposapo amene mtundu wa anthu wakhala pano padziko lapansi, liri tsiku lokhalo limene linasintha kotheratu njira ya mtundu wa anthu kaamba ka ubwino wawo wamuyaya.
2 Tsiku lalikulu limenelo linali Nisani 14 pa kalenda Yachiyuda. M’chaka cha 33 cha Nyengo Yathu, Nisani 14 inayamba pakuloŵa kwa dzuŵa pa April 1. Tiyeni tipende zochitika za tsiku losaiŵalikalo.
Ndiyeno Nisani 14!
3. Kodi Yesu anagwiritsira ntchito motani maola omalizira ameneŵa?
3 Pamene kamdima kachita bii, mwezi wathunthu ukuŵala monga chikumbutso chakuti Yehova amadziŵa nthaŵi ndi nyengo. (Machitidwe 1:7) Ndipo kodi mukuchitikanji m’chipinda chosanjacho m’mene Yesu ndi atumwi ake 12 asonkhana kaamba ka phwando la Paskha wa Ayuda wa chaka ndi chaka? Pamene Yesu akonzekera ‘kuchoka kutuluka m’dziko lino lapansi, kumka kwa Atate, mmene anakonda ake a iye yekha a m’dziko lapansi, anawakonda kufikira chimaliziro.’ (Yohane 13:1) Kodi achita motani zimenezi? Mwa mawu apakamwa ndi chitsanzo, Yesu apitiriza kukhomereza mwa ophunzira ake mikhalidwe imene idzawathandiza kulilaka dziko.
Kuvala Kudzichepetsa ndi Chikondi
4. (a) Kodi ndimotani mmene Yesu anasonyezera ophunzira ake mkhalidwe wofunika kwambiri? (b) Kodi tidziŵa bwanji kuti Petro anatengapo phunziro lalikulu la kufunika kwa kudzichepetsa?
4 Atumwiwo adakali ndi mzimu wina wachikhumbo chakaduka ndi kunyada umene ayenera kutaya. Chotero Yesu atenga thaulo nadzimanga m’chiuno ndi kuyamba kusambitsa mapazi awo. Aka sikachitidwe ka kudzichepetsa kongoyerekezera, monga zimene papa wa Chikristu Chadziko amachita ku Roma chaka ndi chaka. Ndithudi ayi! Kudzichepetsa kowona ndikudzikhutula kochokera mumtima wodzichepetsa ‘umene uyesa anzake oposa iye mwini.’ (Afilipi 2:2-5) Poyamba, Petro aiphonya mfundoyo, nakana kulola Yesu kusambitsa mapazi ake. Koma atawongoleredwa, apempha Yesu kusambitsa thupi lake lonse. (Yohane 13:1-10) Komabe, Petro ayenera kuti anatengapo phunziro. Zaka zingapo pambuyo pake, tiwona kuti iye apatsa ena uphungu woyenera. (1 Petro 3:8, 9; 5:5) Nkofunika chotani nanga lerolino kuti tonsefe tikhale ngati akapolo m’kudzichepetsa chifukwa cha Kristu!—Onaninso Miyambo 22:4; Mateyu 23:8-12.
5. Kodi ndilamulo la Yesu lotani limene linasonyeza kufunika kwa mkhalidwe wina wofunika kwambiri?
5 Mmodzi wa atumwi 12 amenewo satengapo kanthu pa uphungu wa Yesu umenewo. Ameneyo ndiye Yudase Isikariote. Pamene chakudya cha Paskha chiri pakati, mzimu wa Yesu ukuvutika, azindikira Yudase kukhala womupereka, ndipo amtulutsamo. Ndipambuyo pazimenezi pamene Yesu awuza ophunzira ake 11 okhulupirikawo kuti: ‘Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake. Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.’ (Yohane 13:34, 35) Ilitu ndilamulo latsopano, losonyezedwa ndi chitsanzo chopambana cha Yesu iyemwini! Pamene nthaŵi ya imfa yake yopereka nsembe ifika, Yesu asonyeza chikondi chapadera. Agwiritsira ntchito mphindi yoyenera iriyonse kuphunzitsa ndi kulimbikitsa ophunzirawo. Pambuyo pake, agogomezera kufunika kwa chikondi, nati: ‘Lamulo langa ndi ili, kuti mukondane wina ndi mnzake, monga ndakonda inu. Palibe munthu ali nacho chikondi choposa ichi, chakuti munthu ataya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.’—Yohane 15:12, 13.
‘Njira ndi Chowonadi ndi Moyo’
6. Kodi nchonulirapo chotani chimene Yesu aikira ophunzira ake apamtima?
6 Yesu awuza okhulupirika 11 amenewo kuti: ‘Mtima wanu usavutike; mukhulupirira Mulungu, khulupirirani inenso. M’nyumba ya Atate wanga alimo malo okhalamo ambiri. Ngati sikudali kutero, ndikadakuwuzani inu; pakuti ndipita kukukonzerani inu malo.’ (Yohane 14:1, 2) Maloŵa akakhala mu ‘ufumu wa kumwamba.’ (Mateyu 7:21) Yesu afotokoza mmene gulu la ophunzira okhulupirika apamtima ameneŵa lingachifikire chonulirapo chawo. Iye akuti: ‘Ine ndine njira, ndi chowonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa ine.’ (Yohane 14:6) Izi zimagwiranso ntchito kwa anthu amene adzapeza moyo wosatha padziko lapansi.—Chivumbulutso 7:9, 10; 21:1-4.
7-9. Kodi nchifukwa ninji Yesu anadzitcha ‘njira ndi chowonadi ndi moyo’?
7 Yesu ndiye “njira.” Njira imodzi yokha yofikira kwa Mulungu m’pemphero ndiyo mwa Yesu Kristu. Yesu iyemwini awatsimikizira ophunzira ake kuti Atate adzawapatsa chirichonse chimene apempha m’dzina la Yesu. (Yohane 15:16) Mapemphero opyolera m’mafano kapena “oyera mtima” achipembedzo kapena odzala ndi mawu akuti Tikuwoneni Mayi Mariya ndi mawu ena opembedzera obwerezedwabwerezedwa—samamvedwa konse kapena kulandiridwa ndi Atate. (Mateyu 6:5-8) Ndiponso, ponena za Yesu, timaŵerenga pa Machitidwe 4:12 kuti: ‘Palibe chipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo lakumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.’
8 Yesu ndiye ‘chowonadi.’ Mtumwi Yohane anati ponena za iye: ‘Mawu anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinawona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi chowonadi.’ (Yohane 1:14) Yesu anakhala chowonadi cha mazanamazana a maulosi a m’Malemba Achihebri mwakuwakwaniritsa. (2 Akorinto 1:20; Chivumbulutso 19:10) Iye anadziŵikitsa chowonadi polankhula kwa ophunzira ake ndi makamu a anthu amene anamvetsera, pokangana ndi atsogoleri achipembedzo onyenga, ndi mwa chitsanzo cha moyo wake.
9 Yesu ndiye “moyo.” Monga Mwana wa Mulungu, Yesu anati: ‘Iye amene akhulupirira Mwanayo ali nawo moyo wosatha; koma iye amene sakhulupirira Mwanayo sadzawona moyo, koma mkwiyo wa Mulungu ukhala pa iye.’ (Yohane 3:36) Chikhulupiriro chozikidwa pa nsembe ya Yesu chimatsogolera ku moyo wosatha—moyo wosakhoza kufa kumwamba kwa “kagulu ka nkhosa” ka Akristu odzozedwa ndi moyo wamuyaya padziko lapansi laparadaiso kwa khamu lalikulu la “nkhosa zina.”—Luka 12:32; 23:43; Yohane 10:16.
Kupirira Chizunzo
10. Kodi nchifukwa ninji tifunikira ‘kulilaka dziko,’ ndipo nchilimbikitso chotani chimene Yesu anapereka pazimenezi?
10 Awo amene ali ndi chiyembekezo chakukhala m’dongosolo latsopano la Yehova ayenera kulimbana ndi dziko limene “ligona mwa woipayo,” Satana Mdyerekezi. (1 Yohane 5:19) Pamenepo, ngolimbikitsa chotani nanga mawu a Yesu pa Yohane 15:17-19! Iye alengeza kuti: ‘Zinthu izi ndilamulira inu, kuti mukondane wina ndi mnzake. Ngati dziko lapansi lida inu, mudziŵa kuti lidada ine lisanayambe kuda inu. Mukadakhala a dziko lapansi, dziko lapansi likadakonda zake za lokha; koma popeza simuli a dziko lapansi, koma ine ndinakusankhani inu mwa dziko lapansi, chifukwa cha ichi likudani inu.’ Akristu owona akhala akudedwa kufikira ndi chaka chino cha 1992, ndipo timakondwera chotani nanga kuwona zitsanzo zabwino za awo amene apitiriza kuchirimika, modzichepetsa akupeza nyonga pansi pa dzanja lamphamvu la Mulungu! (1 Petro 5:6-10) Tonsefe tikhoza kupirira mayesero mwakusonyeza chikhulupiriro mwa Yesu, amene akumaliza kukambitsirana kwake ndi mawu otonthoza mtima aŵa: ‘M’dziko lapansi mudzakhala nacho chivuto, koma limbikani mtima; ndalilaka dziko lapansi ine.’—Yohane 16:33.
Kuyambitsa Pangano Latsopano
11. Kodi Yeremiya analoseranji ponena za pangano latsopano?
11 Madzulowo, litatha phwando la Paskha, Yesu alankhula za pangano latsopano. Mneneri Yeremiya ananeneratu chimenechi zaka mazana ambiri pasadakhale, nati: ‘Tawonani, masiku adza, ati Yehova, ndipo ndidzapangana pangano latsopano ndi nyumba ya Israyeli, ndi nyumba ya Yuda . . . ndidzaika chilamulo changa mkati mwawo, ndipo m’mtima mwawo ndidzachilemba; ndipo ndidzakhala Mulungu wawo, nadzakhala iwo anthu anga. . . . ndidzakhululukira mphulupulu yawo, ndipo sindidzakumbukira tchimo lawo.’ (Yeremiya 31:31-34) Pa Nisani 14, 33 C.E., nsembe imene itheketsa kugwira ntchito kwa pangano latsopano limeneli iyenera kuperekedwa!
12. Kodi ndimotani mmene Yesu anayambitsira pangano latsopano, ndipo kodi limatheketsa chiyani?
12 Yesu awuza okhulupirika 11 amenewo kuti wakhala akulakalaka kwambiri kudya nawo Paskha ameneyu. Ndiyeno atenga mtanda wa mkate, ayamikira, naunyema, ndi kuwapatsa iwo, ndi kunena: ‘Ichi ndithupi langa lopatsidwa chifukwa cha inu; Chitani ichi chikumbukiro changa.’ M’njira yofananayo, awapatsira chikho cha vinyo wofiira, nanena: ‘Chikho ichi ndipangano latsopano m’mwazi wanga wothiridwa chifukwa cha inu.’ (Luka 22:15, 19, 20) Pangano latsopanolo liyamba kugwira ntchito “ndi mwazi wa mtengo wake wapatali,” woposa kutalitali mwazi wa nyama wowazidwa kukhozetsa kugwira ntchito kwa pangano la Chilamulo la Israyeli! (1 Petro 1:19; Ahebri 9:13, 14) Awo oloŵetsedwa m’pangano latsopano amakhululukidwa machimo awo kotheratu. Chifukwa chake, iwo angayeneretsedwe kukhala a 144,000, amene alandira choloŵa chosatha monga Israyeli wauzimu.—Agalatiya 6:16; Ahebri 9:15-18; 13:20; Chivumbulutso 14:1.
‘Chikumbukiro Changa’
13. (a) Kodi tiyenera kusinkhasinkha pachiyani m’nthaŵi ya Chikumbutso? (b) Kodi ndani okha amene ayenera kudyako ziphiphiritsozo, ndipo chifukwa ninji?
13 Chikumbutso chapachaka cha 1,960 cha imfa ya Yesu chidzafika pa April 17, 1992. Pamene detilo likuyandikira, ndibwino kuti tisinkhesinkhe pazonse zimene nsembe yangwiro ya Yesu ikuzitheketsa. Makonzedwe ameneŵa amakweza nzeru ya Yehova ndi chikondi chake pa mtundu wa anthu. Umphumphu wa Yesu wosagwedera, kufikiradi imfa yoŵaŵa, umalemekeza Yehova ndi kutsutsa chitonzo cha Satana chakuti zolengedwa Zake zaumunthu nzolakwa ndipo zidzalephera pansi pa chiyeso. (Yobu 1:8-11; Miyambo 27:11) Ndi mwazi wake wansembe, Yesu akukhala nkhoswe ya pangano latsopano, limene liri chiŵiya cha Yehova chosankhira ‘mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwiniwake.’ Pamene adakali padziko lapansi, ameneŵa ‘alalikira zoposazo’ za Mulungu wawo, Yehova, amene ‘anawaitana atuluke mumdima, aloŵe kuunika kwake kodabwitsa.’ (1 Petro 2:9; yerekezerani ndi Eksodo 19:5, 6.) Moyenerera, iwo okha ndiwo amadyako ziphiphiritso za Chikumbutsocho chaka ndi chaka.
14. Kodi mamiliyoni a openyererawo amapindula motani?
14 Pa Chikumbutso cha chaka chatha, 10,650,158 anapezekapo kuzungulira dziko lonse, koma mwa ameneŵa 8,850 okha—osakwanira chigawo chimodzi mwa khumi cha 1 peresenti—ndiwo anadyako ziphiphiritsozo. Pamenepo, kodi phwando limeneli nlaphindu lanji kwa mamiliyoni openyererawo? Phindu lake nlalikulu zedi! Ngakhale kuti samadyako, iwo amapindula mwauzimu mwakugwirizana ndi gulu la abale lapadziko lonse, pamene akumvetsera zinthu zazikulu zonse zimene Yehova akukwaniritsa kupyolera m’nsembe ya Mwana wake.
15. Kodi ena amene saali odzozedwa amapindula motani ndi nsembe ya Yesu?
15 Ndiponso, mtumwi akutiuza pa 1 Yohane 2:1, 2 kuti: ‘Nkhoswe tiri naye kwa Atate, ndiye Yesu Kristu wolungama; ndipo iye ndiye chiwombolo cha machimo athu; koma osati athu okha, komanso a dziko lonse lapansi.’ Inde, pamene kuli kwakuti nsembe ya Yesu choyamba imapindula a kagulu ka Yohane oloŵetsedwa m’pangano latsopanolo, imatheketsanso kukhululukidwa machimo kwa ‘dziko lonse.’ Ndiyo ‘nsembe ya chiwombolo’ ya machimo a dziko lonse la mtundu wa anthu amene asonyeza chikhulupiriro m’mwazi wokhetsedwa wa Yesu, umene umawatsegulira njira ku chiyembekezo chosangalatsa cha moyo wosatha padziko lapansi laparadaiso.—Mateyu 20:28.
“Mu Ufumu wa Atate Wanga”
16. (a) Kodi Yesu ndi oloŵa nyumba anzake akuchitanji tsopano? (b) Kodi nchiyani chikufunika lerolino kwa onse otsalira odzozedwa ndi a khamu lalikulu?
16 Akupitiriza kulimbikitsa atumwi ake, Yesu asonya ku tsiku pamene adzamwa mophiphiritsira vinyo wa mpesa watsopano ndi ophunzira ake mu Ufumu wa Atate wake. (Mateyu 26:29) Awauza kuti: “Inu ndinu amene mwakhala nane chikhalire m’mayesero anga; ndipo ndipangana nanu pangano, monga Atate anapangana nane pangano, la ufumu, kuti mukadye ndi kumwa pagome langa mu ufumu wanga, ndi kukhala pamipando yachifumu ndi kuweruza mafuko khumi ndi aŵiri a Israyeli.” (Luka 22:28-30, NW) Chiyambire pamene Yesu anatenga mphamvu ya Ufumu kumwamba mu 1914, tikhoza kunena kuti chiŵerengero chachikulu cha oloŵa nyumba pamodzi ndi Yesu, osonkhanitsidwa kwa zaka mazana ambiri, anaukitsidwa kale, “kukhala pamipando yachifumu” pamodzi naye. (1 Atesalonika 4:15, 16) Tsiku likufika mofulumira lakuti angelo amasule ‘mphepo zinayi’ za ‘chisautso chachikulu’! Panthaŵiyo, kusindikizidwa chizindikiro kwa a 144,000 a Israyeli wauzimu ndi kusonkhanitsidwa kwa mamiliyoni a khamu lalikulu kudzakhala kutamalizidwa. Onseŵa ayenera kusunga umphumphu, monga momwe Yesu anachitira, kotero kuti akalandire mphotho ya moyo wosatha.—Chivumbulutso 2:10; 7:1-4, 9.
17 ndi bokosi. (a) Ngati wodzozedwa akanidwa monga wosakhulupirika, kodi ndani angamloŵe m’malo moyenerera? (b) Kodi nkhani za mu The Watchtower mu 1938 zinaŵalitsa kuunika kosangalatsa kotani ponena za kulinganizidwa ndi kufutukuka kwapambuyo pake kwa gulu lateokratiki padziko lapansi?
17 Bwanji ngati odzozedwa ena alephera kusunga umphumphu wawo? Panthaŵi yakumapeto imeneyi, osakhulupirika oterowo mosakaikira akakhala ochepa okha. Moyenerera, aliyense akaloŵetsedwa pamalo awo, osati wotengedwa mwa obatizidwa chatsopano, koma mwa awo amene akhala chikhalire ndi Yesu m’mayesero ake kwa zaka zambiri za utumiki wokhulupirika. Kuunikira koŵala kwauzimu kumene kunadza mwa The Watchtower m’ma 1920 ndi ma 1930 kumasonyeza kuti kusonkhanitsidwa kwa otsalira odzozedwa kwakukulukulu kunamalizidwa mkati mwa nyengo imeneyo. Awo amene ‘anatsuka zovala zawo, naziyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa’ chiyambire pamenepo ali ndi chiyembekezo chosangalatsa chosiyana. Kupyolera mwa Kristu, mzimu wa Yehova umawatsogolera ku “akasupe a madzi a moyo” m’dziko lapansi Laparadaiso.—Chivumbulutso 7:10, 14, 17.
Pemphero Logwira Mtima Koposa
18. Kodi ndimaphunziro aakulu otani amene titengapo pa pemphero la Yesu pa Yohane mutu 17?
18 Yesu atseka phwando la Chikumbutsolo ndi ophunzira ake mwakupereka pemphero logwira mtima lolembedwa pa Yohane 17:1-26. Iye choyamba apemphera kuti Atate wake amlemekeze pamene akusunga umphumphu kufikira mapeto. Mwanjirayi Yehova adzalemekezedwanso, dzina lake likuyeretsedwa—kuchotseredwa chitonzo chonse. Ndithudi, munthu wangwiroyo Yesu atsimikizira kuti zolengedwa za Mulungu zaumunthu zikhoza kusungabe umphumphu, ngakhale poyang’anizana ndi chiyeso chachikulu koposa. (Deuteronomo 32:4, 5; Ahebri 4:15) M’kuwonjezerapo, imfa ya Yesu yansembe imatsegula mwaŵi waukulu kwa ana a Adamu. Yesu akuti: ‘Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe inu Mulungu wowona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.’ Nkofunika chotani nanga kupeza chidziŵitso cholongosoka chonena za Yehova Mulungu ndi Mwana wake, Mwanawankhosa wa Mulungu, amene anapereka moyo wake kaamba ka kulemekezedwa kwa Yehova ndi chipulumutso cha mtundu wa anthu! (Yohane 1:29; 1 Petro 2:22-25) Kodi mumayamikira nsembe yachikondi yopambana imeneyo kumlingo wokhoza kudzikhutula inu mwini kwa Yehova ndi kuutumiki wake wamtengo wapatali?
19. Kodi ndimotani mmene otsalira ndi khamu lalikulu angakhalire m’chigwirizano chamtengo wapatali?
19 Ndiponso, Yesu akupemphera kwa Atate wake Woyera kuti Iye ayang’anire ophunzira ake pamene akudzitsimikizira kusakhala mbali ya dziko, akumamatira ku mawu Ake monga chowonadi, ndi kusunga umodzi wamtengo wapatali ndi Atate ndi Mwana. Kodi pemphero limeneli silinayankhidwe modabwitsa kufikira m’tsiku lathu pamene otsalira odzozedwa ndi khamu lalikulu akutumikira pamodzi mogwirizana m’chikondi, pamene akusunga uchete kulinga ku dziko, chiwawa chake, ndi kuipa kwake? Ha, ngamtengo wapatali chotani nanga mawu omalizira a Yesu kwa Atate wake, Yehova! ‘Ndinazindikiritsa iwo dzina lanu, ndipo ndidzalizindikiritsa,’ anatero Yesu, ‘kuti chikondi chimene munandikonda nacho chikhale mwa iwo, ndi ine mwa iwo.’—Yohane 17:14, 16, 26.
20. Kodi nchifukwa ninji Nisani 14, 33 C.E., liridi tsiku loyenera kulikumbukira?
20 Atatuluka kupita ku munda wa Getsemane, Yesu akhala ndi mayanjano achidule, olimbikitsana ndi ophunzira ake. Kenako, adani ake afika namgwira! Tilibe mawu otha kulongosola kuvutika kwa Yesu, chisoni chake choswa mtima pachitonzo chokundikidwa pa Yehova, ndi umphumphu wake wopambana m’zonsezo. Yesu apirira kufikira mapeto, usiku wonse ndi mbali yaikulu ya maola amasana atsikulo. Iye asonyeza popanda chikaikiro kuti Ufumu wake suli mbali ya dziko. Ndipo ndi kupuma kwake komalizira, afuula kuti: “Kwatha.” (Yohane 18:36, 37; 19:30) Kulilaka kwake dziko kuli kotheratu. Nisani 14, 33 C.E., liridi tsiku loyenera kulikumbukira!
[Mawu a M’munsi]
a Victory in Europe Day (Tsiku la Chilakiko mu Yuropu) ndi Victory over Japan Day (Tsiku Lachilakiko pa Japani).
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi Yesu anaphunzitsanji ponena za kudzichepetsa ndi chikondi?
◻ Kodi ndimotani mmene Yesu anakhalira “njira ndi chowonadi ndi moyo”?
◻ Kodi pangano latsopano nlachifuno chotani?
◻ Kodi nchigwirizano chotani ndi chikondi zimene ziri pakati pa otsalira odzozedwa ndi khamu lalikulu?
[Bokosi patsamba 20]
Nzeru ya Solomo Wamkulu
Nkhani za mutu wakuti “Organization” (Kulinganizidwa kwa Gulu) m’makope a The Watchtower a June 1 ndi June 15, 1938, zinakhazikitsa malinganizidwe amaziko ateokratiki amene Mboni za Yehova zimatsatira kufikira ndi lero lomwe. Zinasonyeza nyengo yapadera ya kuwongolera ziphunzitso ndi kulinganizidwa kwa gulu kumene kunayamba mu 1919. (Yesaya 60:17) Poyerekezera nyengo imeneyo ya zaka 20 ndi zaka 20 zimene Solomo anamanga kachisi ndi nyumba yachifumu mu Yerusalemu, The Watchtower inati: “Malemba amasonyeza kuti, pambuyo pa programu ya Solomo yakumanga yazaka makumi aŵiri . . . , iye anayamba programu yakumanga m’dziko lake lonselo. (1 Maf. 9:10, 17-23; 2 Mbiri 8:1-10) Ndiyeno mfumu yaikazi ya ku Seba inabwera ‘kuchokera ku mbali zakutali za dziko kudzamva nzeru ya Solomo.’ (Mat. 12:42; 1 Maf. 10:1-10; 2 Mbiri 9:1-9, 12) Izi zimabutsa funso lakuti: Kodi nchiyani chimene chiri mtsogolo posachedwapa kaamba ka anthu a Yehova a padziko lapansi? Tidzadikirira ndi chidaliro chotheratu, ndipo tidzawona.” Chidaliro chimenecho sichinali cholakwika. Pansi pa kulinganiza kwa teokratiki, programu yapadziko lonse yakumanga kwauzimu yasonkhanitsa anthu oposa mamiliyoni anayi a khamu lalikulu. Mofanana ndi mfumu ya ku Seba, iwoŵa abwera kuchokera kumbali zadziko zakutali kudzamva za nzeru ya Solomo Wamkulu, Yesu Kristu—yoperekedwa kwa iwo kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.”—Mateyu 24:45-47.