MUTU 117
Chakudya Chamadzulo cha Ambuye
MATEYU 26:21-29 MALIKO 14:18-25 LUKA 22:19-23 YOHANE 13:18-30
YESU ANANENA KUTI YUDASI NDI AMENE AMUPEREKE
YESU ANAYAMBITSA MWAMBO WOKUMBUKIRA IMFA YAKE
Asanachite mwambo wa Pasika, Yesu anaphunzitsa atumwi ake khalidwe la kudzichepetsa pamene anawasambitsa mapazi. Ndiyeno mwambo wa Pasikawo utatha, Yesu ananena mawu amene Davide analosera akuti: “Munthu amene ndinali kukhala naye mwamtendere, amene ndinali kumukhulupirira, munthu amene anali kudya chakudya changa, wakweza chidendene chake kundiukira.” Kenako ananena kuti: “Mmodzi wa inu andipereka.”—Salimo 41:9; Yohane 13:18, 21.
Atumwi anayang’anana ndipo anayamba kufunsa kuti: “Ambuye, kodi ndine kapena?” Nayenso Yudasi Isikariyoti anafunsa nawo. Popeza kuti Yohane anakhala pafupi ndi Yesu, Petulo anauza Yohane kuti afunse kuti munthuyo ndi ndani. Choncho Yohane anayandikira Yesu n’kumufunsa kuti: “Ambuye, mukunena ndani?”—Mateyu 26:22; Yohane 13:25.
Yesu anayankha kuti: “Ndi amene ndimupatse chidutswa cha mkate chimene ndisunse.” Ndiyeno Yesu anatenga mkate n’kusunsa m’mbale ina imene inali patebulopo n’kupatsa Yudasi kenako ananena kuti: “Mwana wa munthu akuchokadi, monga Malemba amanenera za iye, koma tsoka kwa munthu amene akupereka Mwana wa munthu! Zikanakhala bwino munthu ameneyu akanapanda kubadwa.” (Yohane 13:26; Mateyu 26:24) Kenako Satana anayamba kulamulira maganizo a Yudasi. Chifukwa chakuti Yudasi ankachita zinthu zachinyengo analola kuti Satana amugwiritse ntchito ndipo zimenezi zinachititsa kuti akhale “mwana wa chiwonongeko.”—Yohane 6:64, 70; 12:4; 17:12.
Kenako Yesu anauza Yudasi kuti: “Zimene wakonza kuchita, zichite mwamsanga.” Popeza kuti Yudasi ankasunga bokosi la ndalama, atumwi enawo anaganiza kuti Yesu ankamuuza kuti: “‘Ugule zofunikira zonse za chikondwerero,’ kapena kuti apereke kenakake kwa osauka.” (Yohane 13:27-30) M’malomwake Yudasi ananyamuka kuti akapeze njira yoperekera Yesu.
Usiku umene anachita mwambo wa Pasika, Yesu anayambitsa mwambo wina watsopano. Anatenga mkate, anapemphera, anaunyema n’kuupereka kwa atumwi ake kuti adye. Atawapatsa ananena kuti: “Mkate uwu ukuimira thupi langa limene likuperekedwa chifukwa cha inu. Muzichita zimenezi pondikumbukira.” (Luka 22:19) Atumwiwo ankapatsirana mkatewo kuti aliyense adye.
Kenako Yesu anatenga kapu ya vinyo, anapemphera n’kuipereka kwa atumwi ake. Aliyense ankati akamwa ankapereka kapuyo kwa mnzake kuti amwe. Pamene atumwiwo ankamwa vinyoyo Yesu ananena kuti: “Kapu iyi ikutanthauza pangano latsopano pamaziko a magazi anga, amene adzakhetsedwa chifukwa cha inu.”—Luka 22:20.
Pochita zimenezi Yesu anakhazikitsa mwambo wokumbukira imfa yake ndipo otsatira ake ayenera kuchita mwambo umenewu chaka chilichonse pa Nisani 14. Akamachita mwambo umenewu amakumbukira zimene Yesu komanso Atate wake anachita pothandiza anthu okhulupirika kuti adzamasuke ku uchimo ndi imfa. Mwambo wa Pasika unkakumbutsa Ayuda kuti Mulungu anawapulumutsa koma mwambo wa tsopano umene Yesu anayambitsawu umasonyeza kuti Mulungu anakonza njira yopulumutsira anthu onse amene angakhulupirire Yesu.
Yesu ananena kuti magazi ake “adzakhetsedwa chifukwa cha anthu ambiri kuti machimo akhululukidwe.” Ena mwa anthu amene adzakhululukidwe machimo awo ndi atumwi ake komanso anthu ena okhulupirika. Anthu amenewa ndi amene akalamulire ndi Yesu mu Ufumu wa Atate ake.—Mateyu 26:28, 29.