Maphunziro Opezeka m’Zozizwitsa za Yesu
“NDIPO tsiku lachitatu panali ukwati m’Kana wa m’Galileya; . . . ndipo Yesu yemwe ndi akuphunzira ake anaitanidwa ku ukwatiwo. Ndipo pakutha vinyo, amake wa Yesu ananena naye, Alibe vinyo.” Chochitika chimenechi chinapereka maziko kwa Yesu akuchita chozizwitsa chake choyamba.—Yohane 2:1-3.
Kodi vuto lotero silinali laling’ono kwambiri ndi losanunkha kanthu kwakuti silinayenere kuperekedwa kwa Yesu? Katswiri wina wa Baibulo akufotokoza kuti: “Kummaŵa kulandira alendo kunali ntchito yopatulika . . . Kulandira alendo kwenikweni, makamaka pa ukwati, kunafuna zakudya ndi zakumwa zambiri. Chakudya [chitatha] pa ukwati, banjalo ndi okwatirana achicheperewo amakhala amanyazi nthaŵi zonse.”
Chotero Yesu anachitapo kanthu. Iye anaona “pamenepo mitsuko yamiyala isanu ndi umodzi yoikidwako monga mwa mayeretsedwe a Ayuda.” Mwambo wa kusamba m’manja asanayambe kudya unali wofala pakati pa Ayuda, ndipo panafunikira madzi ochuluka ogwiritsira ntchito awo amene analipo. “Dzazani mitsukoyo ndi madzi,” Yesu analamula awo amene anali kutumikira alendo. Yesu sanali “mkulu wa phwando,” koma iye analankhula kwa iwo mwachindunji ndi mwaukumu. Nkhaniyo imati: “Koma pamene mkuluyo analaŵa madzi[wo, anali atasanduka vinyo, NW].”—Yohane 2:6-9; Marko 7:3.
Zingaonekere kukhala zachilendo kuti kanthu kofala kwambiri konga ukwati kakakhala maziko a chozizwitsa choyamba cha Yesu, komano chochitikacho chimavumbula zambiri ponena za Yesu. Iye anali mbeta, ndipo panthaŵi ina yotsatira anafotokoza za maubwino a umbeta kwa ophunzira ake. (Mateyu 19:12) Komabe, kukhalapo kwake pa phwando laukwati kunavumbula kuti sanali munthu wotsutsa ukwati. Anali wachikatikati, wochirikiza makonzedwe aukwati; anauona kukhala kanthu kolemekezeka m’maso mwa Mulungu.—Yerekezerani ndi Ahebri 13:4.
Yesu sanali wodzimana wouma mtima monga munthu amene anasonyezedwa ndi akatswiri ojambula zithunzi a tchalitchi pambuyo pake. Mwachionekere iye anali wosangalala kukhala pakati pa anthu ndipo sanaipidwe ndi macheza. (Yerekezerani ndi Luka 5:29.) Motero machitidwe ake anapereka chitsanzo kwa otsatira ake. Yesu iye mwini anasonyeza kuti iwo sakafunikira kukhala oziya mosayenera kapena osakondwera—monga ngati kuti chilungamo chinatanthauza kupanda chimwemwe. Mosiyana ndi zimenezo, pambuyo pake Akristu analamulidwa kuti: “Kondwerani mwa Ambuye nthaŵi zonse.” (Afilipi 4:4) Lerolino Akristu amachita mosamala kuti asunge kusanguluka pamalo pake poyenera. Amapeza chisangalalo mu utumiki wa Mulungu, koma mwa kutsatira chitsanzo cha Yesu, nthaŵi zina amapeza nthaŵi ya kuchezerana wina ndi mnzake.
Onaninso mkhalidwe wachikondi wa Yesu. Iye analibe chomkakamiza chilichonse chochitira chozizwitsa. Panalibe ulosi wofunikira kukwaniritsidwa m’nkhaniyi. Malinga ndi nkhaniyi, Yesu anangosonkhezeredwa ndi nkhaŵa ya amake ndi mkhalidwe wochititsa chisoni wa okwatiranawo. Anasamala za malingaliro awo ndipo anafuna kuwapeŵetsa kuchita manyazi. Kodi zimenezo sizimakulitsa chidaliro chanu chakuti Kristu amakukondanidi—ngakhale m’mavuto anu a tsiku ndi tsiku?—Yerekezerani ndi Ahebri 4:14-16.
Popeza kuti mtsuko uliwonse unali wa “miyeso iŵiri kapena itatu” ya madzi, chozizwitsa cha Yesu chinali cha vinyo wochuluka kwambiri—mwinamwake malita 390 (magaloni 105)! (Yohane 2:6) Kodi nchifukwa ninji panafunika wochuluka chotero? Yesu sanali kuchirikiza kuledzera, kanthu kena kamene Mulungu amatsutsa. (Aefeso 5:18) M’malo mwake, anali kusonyeza kuoloŵa manja konga kwa Mulungu. Popeza kuti vinyo anali chakumwa chofala, aliyense amene anatsala akanadzagwiritsiridwa ntchito panthaŵi ina.—Yerekezerani ndi Mateyu 14:14-20; 15:32-37.
Akristu oyambirira anatsanzira chitsanzo cha Yesu cha kuoloŵa manja. (Yerekezerani ndi Machitidwe 4:34, 35.) Ndipo anthu a Yehova lerolino mofananamo amalimbikitsidwa ‘kupatsa.’ (Luka 6:38) Komabe, chozizwitsa choyamba cha Yesu chilinso ndi tanthauzo la ulosi. Chimasonyeza za nthaŵi imene ili mtsogolo pamene Mulungu adzakonza mooloŵa manja “phwando la zinthu zonona, phwando la vinyo wa pamitsokwe,” akumachotseratu njala.—Yesaya 25:6.
Komabe, bwanji nanga za zozizwitsa zambiri zimene Yesu anachita zimene zinaphatikizapo machiritso akuthupi? Kodi tingaphunzirenji mu izo?
Kuchita Zabwino pa Sabata
“Tauka, yalula mphasa yako, nuyende.” Yesu analankhula mawu ameneŵa kwa munthu amene anali wodwala kwa zaka 38. Cholembedwa cha Uthenga Wabwino chimapitiriza kuti: “Ndipo pomwepo munthuyu anachira, nayalula mphasa yake, nayenda.” Modabwitsa, si onse amene anakondwera ndi kusintha kumeneku. Cholembedwacho chimanena kuti: “Ayuda analondalonda Yesu, popeza anachita izo dzuŵa la Sabata.”—Yohane 5:1-9, 16.
Sabata linalinganizidwira kukhala tsiku la kupuma ndi la kusangalala kwa onse. (Eksodo 20:8-11) Komabe, m’tsiku la Yesu, linakhala la malamulo ocholoŵana ndi opsinja opangidwa ndi anthu. Katswiri Alfred Edersheim analemba kuti m’zigawo za malamulo a Sabata zazitali za Talmud, “zinthu zina zikufotokozedwa mwamphamvu monga ngati zofunika kwambiri pachipembedzo, zimene munthu wanzeru sangazilingalire konse kukhala zofunika kwambiri.” (The Life and Times of Jesus the Messiah) Arabi anachititsa malamulo achabechabe ndi osinthasintha, amene analamulira mbali iliyonse ya moyo wa Myuda kukhala nkhani ya moyo ndi imfa—kaŵirikaŵiri ndi kusasamala kwankhalwe malingaliro a anthu. Lamulo limodzi la Sabata loperekedwa linali lakuti: “Ngati nyumba yagwera munthu ndipo anthu akukayikira ngati munthu alimo, kapena ngati ali wamoyo kapena wakufa, kapena ngati ndi wakunja kapena Mwisrayeli, iwo angachotse muluwo pa iye. Ngati ampeza wamoyo angachotse kwambiri muluwo pa iye; koma ngati wafa, amsiye.”—Tractate Yoma 8:7, The Mishnah, lotembenuzidwa ndi Herbert Danby.
Kodi Yesu anaona motani kuumirira gwagwagwa pamalamulo achabechabeko? Pamene anaimbidwa mlandu wa kuchiritsa pa Sabata, iye anati: “Atate wanga amagwira ntchito kufikira tsopano, inenso ndigwira ntchito.” (Yohane 5:17) Yesu sanali kuchita ntchito yolembedwa kuti adzilemeretse. M’malo mwake, anali kuchita chifuniro cha Mulungu. Monga momwe Alevi analoledwera kupitiriza kuchita utumiki wawo wopatulika pa Sabata, iye moyenerera anachita ntchito zake zopatsidwa ndi Mulungu monga Mesiya popanda kuswa Chilamulo cha Mulungu.—Mateyu 12:5.
Machiritso atsiku la Sabata a Yesu anasonyezanso poyera alembi ndi Afarisi Achiyuda kukhala ‘opambanitsa kukhala olungama’—aliuma ndi osaganiza moyenera. (Mlaliki 7:16) Ndithudi, sichinali chifuniro cha Mulungu kuti ntchito zabwino zizichitidwa chabe pamasiku ena akutiakuti a mlungu; ndiponso Mulungu sanalinganize kuti Sabata likhale lopanda pake mwa kuumirira malamulo. Yesu anati pa Marko 2:27: “Sabata linaikidwa chifukwa cha munthu, si munthu chifukwa cha Sabata.” Yesu anakonda anthu, osati malamulo osautsa.
Motero ndi bwino kuti Akristu lerolino asakhale aliuma kapena oumirira pa malamulo m’kuganiza kwawo. Awo amene ali ndi ulamuliro mu mpingo amapeŵa kulemetsa ena ndi malamulo aumunthu omkitsa. Chitsanzo cha Yesu chimatilimbikitsanso kufunafuna mipata yochitira zabwino. Mwachitsanzo, Mkristu sayenera konse kulingalira kuti adzauza ena choonadi cha Baibulo kokha pamene ali mu utumiki wa kukhomo ndi khomo wolinganizidwa kapena pamene ali papulatifomu. Petro akuti, Mkristu ayenera kukhala ‘wokonzeka nthaŵi zonse kuchita chodzikanira pa yense wakumufunsa chifukwa cha chiyembekezo chili mwa iye.’ (1 Petro 3:15) Kuchita zabwino kulibe malire.
Phunziro la Chifundo
Chozizwitsa china chapadera chalembedwa pa Luka 7:11-17. Malinga nkunena kwa nkhaniyo, Yesu “anapita kumudzi, dzina lake Nayini; ndipo ophunzira ake ndi mpingo waukulu wa anthu anapita naye.” Ngakhale lerolino, manda angaonedwe kummwera chakummaŵa kwa mudzi wamakono Wachiluya wa Nein. “Ndipo pamene anayandikira ku chipata cha mudziwo,” mosakayikira khomo la mzindawo la kummaŵa, anamva phokoso. “Onani, anthu analikunyamula munthu wakufa, mwana wamwamuna mmodzi yekha, amake ndiye mkazi wamasiye; ndipo anthu ambiri a kumudzi anali pamodzi naye.” H. B. Tristram ananena kuti “mwambo woikira maliro sunasinthe” kuyambira m’nthaŵi zakale, akumawonjezera kuti: “Ndaona akazi oyenda patsogolo pa chithatha, otsogoleredwa ndi akazi olira olembedwa ntchito. Amaponyera mikono yawo m’mwamba, kukudzula tsitsi lawo, akumalira ndi kugwedeza thupi kowopsa, ndipo amatchula dzina la womwalirayo mofuula.”—Eastern Customs in Bible Lands.
Pakati pa chipwirikiti choterocho panali mkazi wamasiye wolira amene nkhope yake yeniyeniyo inasonyeza kuŵaŵidwa mtima kwakukulu. Pokhala atatayikiridwa kale ndi mwamuna, anaona mwana wake wamwamunayo monga, m’mawu a mlembiyo Herbert Lockyer, “ndodo ya ukalamba wake, ndi chitonthozo cha kusukidwa kwake—mchirikizo ndi mzati wapanyumba. Potayikiridwa ndi mwana wake wamwamuna mmodzi yekhayo, mchirikizo wotsala unachotsedwa.” (All the Miracles of the Bible) Kodi Yesu anachita motani? M’mawu ondondomekedwa bwino a Luka, “pamene Ambuye anamuona, anagwidwa ndi chifundo chifukwa cha iye, nanena naye, Usalire.” Mawu akuti “anagwidwa ndi chifundo” atengedwa ku liwu Lachigiriki limene kwenikweni limatanthauza kuti “matumbo.” Limatanthauza “kuvutika mumtima kwakukulu.” (Vine’s Expository Dictionary of Old and New Testament Words) Inde, mtima wa Yesu unakhudzidwa kwambiri.
Amake a Yesu mwiniyo mwachionekere anali amasiye, chotero anadziŵa bwino kwambiri za kupweteka kwa kuferedwa potayikiridwa ndi atate wake omlera, Yosefe. (Yerekezerani ndi Yohane 19:25-27.) Mkazi wamasiyeyo sanachite kumchonderera. Yesu anachita chifundo mwa iye yekha. “Anayandikira, nakhudza chithatha,” mosasamala kanthu kuti pansi pa Chilamulo cha Mose kugwira mtembo kunadetsa munthu. (Numeri 19:11) Kupyolera mwa mphamvu zake zozizwitsa, Yesu akanatha kuchotsa chochititsa chidetso! “Iye anati, Mnyamata iwe, ndinena ndi iwe, Tauka. Ndipo wakufayo anakhala tsonga, nayamba kulankhula. Ndipo anampereka kwa amake.”
Nkhani imeneyi ili ndi phunziro la chifundo losonkhezera maganizo chotani nanga! Akristu safunikira kutsanzira mkhalidwe wopanda chikondi ndi wankhalwe wosonyezedwa mkati mwa “masiku otsiriza” ano. (2 Timoteo 3:1-5) Mosiyana ndi zimenezo, 1 Petro 3:8 amalimbikitsa kuti: “Chotsalira, khalani nonse a mtima umodzi, ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni.” Pamene mnansi wathu aferedwa kapena akhala ndi wina wodwala kwambiri, sitingathe kuukitsa munthuyo kapena kuchiritsa wodwalayo. Koma chifundo chingatisonkhezere kupereka thandizo labwino ndi chitonthozo, mwina mwake mwa kungopezekapo kwathu ndi kulira nawo.—Aroma 12:15.
Chiukiriro chosonkhezera mtima chimenechi chochitidwa ndi Yesu chimasonyezanso za mtsogolo—nthaŵiyo pamene “onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatulukira”! (Yohane 5:28, 29) Kuzungulira pa dziko lonse lapansi, oferedwa adzasonyezedwa chifundo cha Yesu mwachindunji pamene anakubala amene anamwalira, atate, ana, ndi mabwenzi abwerera kuchokera kumanda!
Maphunziro a Zozizwitsa
Pamenepo, nkwachionekere kuti zozizwitsa za Yesu sizinali chabe zisonyezero zongokondweretsa zamphamvu. Zinalemekezanso Mulungu, zikumapereka chitsanzo kwa Akristu amene amalimbikitsidwa ‘kulemekeza Mulungu.’ (Aroma 15:6) Zinalimbikitsa kuchita zabwino, kusonyeza kuoloŵa manja, ndi kusonyeza chifundo. Chofunika koposa nchakuti, zinatumikira monga njira yooneratu ntchito zamphamvu zamtsogolo zoti zidzachitidwe mu Ulamuliro wa Zaka Chikwi wa Kristu.
Pamene anali pa dziko lapansi, Yesu anachita ntchito zake zamphamvu kudera lochepa kwambiri. (Mateyu 15:24) Monga Mfumu yolemekezedwa, ulamuliro wake udzafutukukira pa dziko lonse lapansi! (Salmo 72:8) Kalelo, awo amene analandira machiritso ozizwitsa ndi ziukiriro potsirizira pake anafa. Mu ufumu wake wakumwamba, uchimo ndi imfa zidzachotsedwa kotheratu, zikumatsegula njira ya moyo wosatha. (Aroma 6:23; Chivumbulutso 21:3, 4) Inde, zozizwitsa za Yesu zimasonyeza za kudza kwa mtsogolo mwaulemerero. Mboni za Yehova zathandiza mamiliyoni ambiri kukulitsa chiyembekezo chenicheni cha kukhala mbali yake. Kufikira pamene nthaŵiyo ifika, ha, ndi kulaŵiratu kwabwino kwambiri chotani nanga kumeneko kwa zimene ziti zichitike posachedwapa kumene kumasonyezedwa ndi zozizwitsa za Yesu Kristu!
[Chithunzi patsamba 7]
Yesu asandutsa madzi kukhala vinyo