Mutu 28
Kugwirizana m’Chikondi
1. (a) Kodi mungakhale mbali ya gulu la Mulungu motani? (b) Kodi pamenepo muyenera kumvera lamulo lotani?
PAMENE MUKUWONJEZEKA m’kudziwa ndi kuzindikira Yehova Mulungu ndi zifuno zake, mudzafuna kugwirizana nthawi zonse ndi anthu amene ali ndi chikhulupiriro ndi chiyembekezo chimodzimodzichi. Mwa kutero, mudzakhala mbali ya gulu lowoneka la Mulungu, ubale weniweni Wachikristu. “Kondani gulu lonse la abale” pa nthawi imeneyo lidzakhala lamulo limene muyenera kumvera.—1 Petro 2:17; 5:8, 9.
2. (a) Kodi Yesu anapatsa omtsatira lamulo latsopano lotani? (b) Kodi kanenedweko “mukondane” ndi “wina ndi mnzake” kamasonyezanji mwachiwonekere? (c) Kodi kukhala ndi chikondi kuli kofunika motani?
2 Yesu Kristu anagogomezera mmene kuliri kufunika kuti omtsatira akondane. Iye anati kwa iwo: “Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane . . . Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunizira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” (Yohane 13:34, 35) Manenedwewo “mukondane” ndi “wina ndi mnzake” amasonyeza bwino lomwe kuti Akristu onse owona akakhala pamodzi m’kagulu kamodzi kapena gulu. (Aroma 12:5; Aefeso 4:25) Ndipo gulu limeneli likadziwika ndi chikondi chimene ziwalo zake ziri nacho kwa wina ndi mnzake. Ngati munthu alibe chikondi, chinthu chirichonse chimakhala chachabechabe.—1 Akorinto 13:1-3.
3. Kodi Baibulo limagogomezera motani kufunika kwa kukonda ndi kusamalira Akristu anzathu?
3 Chifukwa cha chimenecho, Akristu oyambirira anali kupatsidwa kawirikawiri zikumbutso zonga ngati zino: “Mukondane ndi chikondi chenicheni.” “Mulandirane wina ndi mnzake.” Chitiranani ukapolo.” “Mukhalirane okoma [mtima] wina ndi mnzake, a mtima wachifundo.” “Pitirizanibe kupirirana ndi kukhululukirana mwaufulu ngati aliyense ali ndi chifukwa chodandaulira ndi wina.” “Dzitonthozanani ndi kulimbikitsana.” “Khalani mumtendere mwa inu nokha.”—Aroma 12:10; 15:7; Agalatiya 5:13; Aefeso 4:32, NW; Akolose 3:13, 14; 1 Atesalonika 5:11, 13; 1 Petro 4:8; 1 Yohane 3:23; 4:7, 11.
4. (a) Kodi nchiyani chimene chikusonyeza kuti Akristu ayenera kukonda ena kuphatikiza pa “kukondana”? (b) Kodi makamaka Akristu ayenera kukonda yani?
4 Komabe, zimenezi sizikutanthauza kuti Akristu owona ayenera kukonda kokha ziwalo zinzawo za gulu la Mulungu. Iwo ayenera kukondanso ena. Baibulo, kunena zowona, limawafulumiza kuwonjezeka “m’chikondano wina ndi mnzake ndi kwa anthu onse.” (1 Atesalonika 3:12; 5:15) Popereka lingaliro loyenera lokhazikika, mtumwi Paulo analemba kuti: “Tiyeni tichite chimene chiri chabwino kwa onse, koma makamaka kwa awo ogwirizana nafe m’chikhulupiriro.” (Agalatiya 6:10, NW) Motero pamene kuli kwakuti Akristu ayenera kukonda onse, kuphatikizapo adani awo, iwo makamaka ayenera kukonda ziwalo zinzawo za gulu la Mulungu, abale ndi alongo awo auzimu.—Mateyu 5:44.
5. Kodi nchiyani chimene chikusonyeza kuti Akristu owona, m’nthawi zakale ndi lerolino, adziwika ndi chikondi chawo?
5 Akristu oyambirira anadziwika kwambiri ndi chikondi chimenechi chimene iwo anali nacho kwa wina ndi mnzake. Malinga ndi wolemba wa m’zaka za zana lachiwiri Tertullian, anthu ankanena za iwo kuti: ‘Wonani mmene iwo akukondanirana, ndi mmene iwo aliri okonzekera kuferana! Chikondi choterocho chimawonekanso pakati pa Akristu owona lerolino. Koma kodi zimenezi zimatanthauza kuti sipamakhala mavuto ndi zovuta pakati pa Akristu owona?
ZOTULUKAPO ZA KUPANDA UNGWIRO
6. Kodi nchifukwa ninji nthawi zina ngakhale Akristu owona amachimwirana?
6 Mwa kuphunzira kwanu Baibulo mukuzindikira kuti tonsefe talandira kupanda ungwiro kuchokera kwa makolo athu oyambirira, Adamu ndi Hava. (Aroma 5:12) Motero tiri oyedzamira ku kuchita choipa. “Timakhumudwa tonse nthawi zambiri,” Baibulo limatero. (Yakobo 3:2, NW; Aroma 3:23) Ndipo muyenera kudziwa kuti ziwalo za gulu la Mulungu zirinso zopanda ungwiro ndipo nthawi zina zimachita zinthu zimene siziri zabwino. Kumeneku kungachititse mavuto ndi zovuta ngakhale pakati pa Akristu owona.
7. (a) Kodi nchifukwa ninji Euodiya ndi Suntuke anafunikira kuuzidwa kuti “alingirire ndi mtima umodzi”? (b) Kodi nchiyani chimene chikusonyeza kuti, kwakukulukulu, amenewa anali akazi Achikristu abwino kwambiri?
7 Lingalirani mkhalidwewo ndi akazi awiri otchedwa Euodiya ndi Suntuke mumpingo woyambirira wa Afilipi. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndidandaulira Euodiya, ndidandaulira Suntuke, alingirire ndi mtima umodzi mwa Ambuye.” Kodi nchifukwa ninji Paulo analimbikitsa akazi awiri amenewa kuti “alingirire ndi mtima umodzi”? Mwachiwonekere, panali vuto pakati pawo. Baibulo silikusimba chimene ilo linali. Mwina mwake iwo m’njira ina anali kuchitirana nsanje. Komabe, kwakukulukulu, amenewa anali akazi abwino. Iwo adali Akristu kwa nthawi yaitali, zaka zambiri asanagwirizane ndi Paulo m’ntchito yolalikira. Motero iye analembera kalata mpingowo, kuti: “Muthandize akazi awa amene anakangalika nane pamodzi mu uthenga wabwino.”—Afilipi 4:1-3.
8. (a) Kodi ndivuto lotani limene linabuka pakati pa Paulo ndi Barnaba? (b) Ngati mukanakhala mulipo ndipo mudawona vuto limeneli, kodi mukananenanji?
8 Pa nthawi ina vuto linabukanso pakati pa mtumwi Paulo ndi tsamwali wake woyenda naye Barnaba. Pamene iwo anali pafupi kunyamuka pa ulendo wawo wachiwiri waumishonale, Barnaba anafuna kutenga mbale wake Marko. Komabe Paulo sanafune kutenga Marko, popeza kuti Marko adawasiuya napita kunyumba mkati mwa ulendo wawo woyamba waumishonale. (Machitidwe 13:13) Baibulo limati: “Ndipo panali kupsetsana mtima, kotero kuti analekana wina ndi mnzake.” (Machitidwe 15:37-40) Kodi mungayerekezere zimenezo! Ngati mukanakhala muliko ndipo mudawona “kupsetsana mtima” kumeneku, kodi mukadanena kuti Paulo ndi Barnaba sanali mbali ya gulu la Mulungu chifukwa cha mmene iwo anachitira?
9. (a) Kodi Petro anachita tchimo lanji, ndipo kodi nchiyani chimene chinamchititsa kuchita motere? (b) Kodi Paulo anachitanji pamene anawona zimene zinalinkuchitika?
9 Pa nthawi ina mtumwi Petro analakwa. Analeka kuyanjana kwambiri ndi Akristu a mwa Amitundu chifukwa cha kuwopa kusawonedwa bwino ndi ena a Akristu Achiyuda amene molakwa anali kunyoza abale awo a mwa Amitundu. (Agalatiya 2:11-14) Pamene mtumwi Paulo anawona zimene Petro anali kuchita, anatsutsa khalidwe losayenera la Petro pamaso pa awo onse okhalapo. Kodi mukanamva bwanji ngati mukanakhala Petro?—Ahebri 12:11.
KUTHETSA ZOVUTA NDI CHIKONDI
10. (a) Kodi Petro anachita motani pamene anawongoleredwa? (b) Kodi tingaphunzirenji m’chitsanzo cha Petro?
10 Petro akadakwiya ndi Paulo. Iye akadakhumudwa ndi njira imene Paulo adamuwongolerera pamaso pa onse. Koma iye sanatero. (Mlaliki 7:9) Petro anali wodzichepetsa. Analandira chiwongolerocho, ndipo iye sanachilole kuchititsa kukonda kwake Paulo kuzirala. (1 Petro 3:8, 9) Wonani mmene Petro pambuyo pake anatchulira Paulo m’kalata ya chilimbikitso kwa Akristu anzake: “Yesani kulekerera kwa Ambuye wathu chipulumutso; monganso mbale wathu wokondedwa Paulo, monga mwa nzeru zopatsidwa kwa iye, anakulemberani.” (2 Petro 3:15) Inde, Petro analola chikondi kukwirira vutolo, limene m’chochitika chino lidachokera m’khalidwe lake lolakwa.—Miyambo 10:12.
11. (a) Mosasamala kanthu za kupsetsana kwawo mitima, kodi ndimotani mmene Paulo ndi Barnaba anasonyezera kuti iwo anali Akristu owona? (b) Kodi tingapindule motani ndi chitsanzo chawo?
11 Bwanji ponena za vutolo pakati pa Paulo ndi Barnaba? Limenelinso linathetsedwa ndi chikondi. Pakuti pambuyo pake, pamene Paulo analembera kalata mpingo wa ku Korinto, iye anatchula Barnaba kukhala wantchito mnzake weniweni. (1 Akorinto 9:5-6) Ndipo ngakhale Paulo akuwonekera kukhala anali ndi chifukwa chabwino chokayikirira phindu la Marko monga tsamwali woyenda naye, mnyamata ameneyu pambuyo pake anakhwima kufikira pakuti Paulo anatha kulembera kalata Timoteo kuti: “Tenga Marko nudze naye, pakuti iye ngwopindulitsa kwa ine kaamba ka kutumikira.” (2 Timoteo 4:11, NW) Tingapindule ndi chitsanzo cha kuthetsa kusagwirizana chimenechi.
12. (a) Kodi nchifukwa ninji tingayerekezere kuti Euodiya ndi Suntuke anathetsa kusamvana kwawo? (b) Malinga ndi kunena kwa Agalatiya 5:13-15, kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kuti Akristu athetse kusamvana kwawo m’chikondi?
12 Eya, bwanji ponena za Euodiya ndi Suntuke? Kodi iwo anathetsa kusamvana kwawo, akumalola chikondi kukwirira machimo alionse amene iwo angakhale atachitirana? Baibulo silikutiuza chimene potsirizira pake chinawachitikira. Koma, kukhala kwawo akazi abwino amene adagwira ntchito mogwirizana ndi Paulo mu uminisitala wake Wachikristu, tingaganizire moyenerera kuti iwo analandira modzichepetsa uphungu woperekedwawo. Pamene kalata ya Paulo inalandiridwa, tingangoyerekezera kupita kwawo kwa wina ndi mnzake ndi kuthetsa vuto lawo mu mzimu wa chokondi.—Agalatiya 5:13-15.
13. Kodi Yehova Mulungu amapereka chitsanzo chotani m’kusonyeza chikondi?
13 Inu, nanunso, mumgawone kukhala kovuta kugwirizana ndi munthu wina, kapena anthu, mumpingo. Ngakhale kuli kwakuti iwo angakhale atatsaliridwa ulendo wautali m’kukulitsa mikhalidwe yengakhale atatsaliridwa ulendo wautali m’kukulitsa mikhalidwe yeniyeni Yachikristu, ganizirani izi: Kodi Yehova Mulungu amayembekezera kufikira anthu atasiya njira zawo zonse zoipa asanawakonde? Ayi; Baibulo limati: “Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha m’menemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Kristu adatifera ife.” (Aroma 5:8) Tifunikira kutsatira chitsanzo cha Mulungu chimenecho ndi kusonyeza chikondi kwa awo amene akuchita zinthu zoipa ndi zopusa.—Aefeso 5:1, 2; 1 Yohane 4:9-11; Salmo 103:10.
14. Kodi Yesu anapereka uphungu wotani wonena za kusakhala wopeza zifukwa pa ena?
14 Popeza kuti tonsefe ndife opanda ungwiro kwenikweni, Yesu anaphunzitsa kuti sitiyenera kukhala opeza zifukwa pa ena. Zowona, ena amakhala ndi zolakwa, koma nafenso tiri nazo. “Upenya bwanji kachitsotso kali m’diso la mbale wako, koma mtanda uli m’diso la iwe mwini suuganizira?” anatero Yesu. (Mateyu 7:1-5) Mwa kukumbukira uphungu wanzeru woterowo, tidzathandizidwa kugwirizana ndi abale ndi alongo athu.
15. (a) Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kuti tikhululukire ena ngakhale pamene tiri ndi chifukwa chodandaulira nawo? (b) M’fanizo lake m’Mateyu chaputala 18, kodi Yesu anaphunzitsa motani kufunika kwa kukhala wokhululukira?
15 Nkofunika kotheratu kuti tikhale achifundo ndi okhululukira. Zowona, mungakhale ndi chifukwa chenicheni chodandaulira ndi mbale wina kapena mlongo wina. Koma kumbukirani uphungu Wabaibulowo: “Pitirizanibe kupirirana ndi kukhululukirana mwaufulu ngati aliyense ali ndi chifukwa chodandaulira ndi wina.” Koma kodi nchifukwa ninji muyenera kukhululukira ena pamene muli ndi chifukwa chenicheni chodandaulira ndi iwo? Chifukwa chakuti “Yehova anakukhulukirani mwaufulu,” limayankha Baibulo. (Akolose 3:13, NW) Ndipo ngati titi tilandire chikhululukiro chake, Yesu anati, tiyenera kukhululukira ena. (Mateyu 6:9-12, 14, 15) Yehova, mofanana nd mfumu m’limodzi la mafanizo a Yesu, watikhululukira zikwizikwi za nthawi, motero kodi sitingakhululukire abale athu nthawi zowerengeka?—Mateyu 18:21-35; Miyambo 19:11.
16. (a) Malinga ndi kunena kwa 1 Yohane 4:20, 21, kodi kukonda Mulungu kukugwirizana motani ndi kukonda Akristu anzathu? (b) Kodi nkachitidwe kotani kamene kali kofunika ngati mbale wanu ali ndi kanthu kena kwa inu?
16 Ife chabe sitingamatsatire chowonadi, ndipo pa nthawi imodzimodziyo kukhala tikuchitira abale ndi alongo anthu m’njira yopanda chikondi ndi yosakhululukira. (1 Yohane 4:20, 21; 3:14-16) Chotero, pamenepa, ngati mudzakhalanso ndi vuto ndi Mkristu mnzanu, musaleke kulankhula naye. Musasunge mkwiyo, koma thetsani nkhani mu mzimu wa chikondi. Ngati mwalakwira mbale wanu, khalani wokonzekera kupepesa ndi kupempha chikhululukiro.—Mateyu 5:23, 24.
17. Kodi njira yoyenera yotsatira njotani ngati munthu wina akulakwirani?
17 Koma bwanji ngati munthu wina akuyambani, kapena akulakwirani m’njira inayakenso? Baibulo limalangiza kuti: “Usanene, Ndidzamchitira zomwezo anandichitira ine.” (Miyambo 24:29; Aroma 12:17, 18) Yesu Kristu analangiza kuti: “Amene adzakupanda iwe pa tsaya lako lamanja, umtembenuzire linanso.” (Mateyu 5:39) Mbama silimalinganizidwa kuvulaza mwakuthupi, koma kokha kuyamba kapena kuputa. Yesu motero anali kuphunzitsa omtsatira kupewa kulowetsedwa m’nkhondo kapena mkangano. Koposa ndi “kubwezera chivulazo ndi chivulazo kapena kutukwana ndi kutukwana,” muyenera “kufunafuna mtendere ndi kuulondola.”—1 Petro 3:9, 11 NW; Aroma 12:14.
18. Kodi tiyenera kuphunziranji m’chitsanzo cha Mulungu cha kukonda anthu onse?
18 Kumbukirani kuti tiyenera “kukhala ndi chikondi kaamba ka gulu lonse la abale.” (1 Petro 2:17, NW) Yehova Mulungu amapereka chitsanzo. Iye ngwosasankha. Mitundu yonse njofanana m’maso mwake. (Machitidwe 10:34, 35; 17:26) Awo amene adzatetezeredwa kupyola “chisautso chachikulu” chikudzacho atengedwa “m’mitundu yonse ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe.” (Chivumbulutso 7:9, 14-17) Motero, motsanzira Mulungu, sitiyenera kukonda ena mochepa chifukwa chakuti ndiwo a fuko lina, mtundu kapena otsika, kapena ali ndi kawonekedwe kakhungu kena.
19. (a) Kodi tiyenera kuwona ndi kuchitira motani Akristu anzathu? (b) Kodi ndimwayi waukulu wotani umene ungakhale wathu?
19 Fikani pa kudziwa bwino awo onse okhala mumpingo Wachikristu, ndipo mudzafika pa kuwakonda ndi kuwazindikira. Wonani achikulire monga atate ndi amayi, achichepere monga abale ndi alongo. (1 Timoteo 5:1, 2) Ulidi mwayi kukhala mbali ya gulu la Mulungu lowonekera longa banja, limene ziwalo zake zimagwirizana bwino kwambiri pamodzi m’chikondi. Kudzakhala kwabwino kwambiri chotani nanga kukhala ndi moyo kosatha m’paradaiso padziko lapansi limodzi ndi banja lachikondi loterolo!—1 Akorinto 13:4-8.
[Chithunzi patsamba 233]
Kodi tingaphunzirenji m’chochitika chokhudza Euodiya ndi Suntuke?
[Chithunzi patsamba 235]
Kodi kukagana pakati pa Paulo ndi Barnaba kunatanthauza kuti iwo sanali ziwalo za gulu la Mulungu?
[Chithunzi patsamba 236]
Akristu owona amalola chikondi kukwirira zochititsa kudandaula
[Chithunzi patsamba 237]
Mkati mwa gulu la Mulungu, Akristu amasonkhezeredwa ndi chikondi kugwirizana monga ofanana