-
“Njira Choonadi ndi Moyo”‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’
-
-
MUTU 2
“Njira, Choonadi ndi Moyo”
1, 2. N’chifukwa chiyani n’zosatheka kuti munthu payekha afike kwa Yehova, nanga Yesu Khristu watichitira chiyani pofuna kutithandiza?
KODI munayamba mwasocherapo? Mwina mungakumbukire nthawi imene munkapita kukaona mnzanu kapena wachibale wanu ndipo munasochera. Ndiye mutasochera choncho, kodi munafunsira njira kwa munthu winawake? Kodi munamva bwanji ngati munthu wachifundoyo anakuuzani kuti: “Tiyeni ndikuperekezeni,” m’malo mongokuuzani mmene mungayendere? N’zosakayikitsa kuti munasangalala kwambiri.
2 Tinganene kuti Yesu Khristu anachita zinthu mofanana ndi munthu wachifundo ameneyu kwa aliyense wa ife. Patokha, sizikanatheka kuti tidziwe Mulungu komanso kuti tikhale naye pa ubwenzi. Chifukwa choti anthu padziko lonse lapansi anatengera uchimo ndi kupanda ungwiro, iwo amakhala ngati osochera ndipo ndi “otalikirana ndi moyo umene umachokera kwa Mulungu.” (Aefeso 4:17, 18) Choncho timafunikira kuti munthu wina atithandize kuti tidziwe Mulungu n’kumachita zinthu zimene zimamusangalatsa. Yesu ali ngati munthu wachifundo amene akutitsogolera njira. Kuwonjezera pa kutipatsa malangizo komanso kutithandiza kuti tipeze njira, iye anatipatsa chitsanzo choti titsanzire. Monga taonera m’mutu woyamba uja, Yesu akuitana aliyense wa ife kuti: ‘Bwera ukhale wotsatira wanga.’ (Maliko 10:21) Komanso anatipatsa zifukwa zomveka zotilimbikitsa kuti timutsatire. Pa nthawi ina, Yesu anati: “Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.” (Yohane 14:6) Tsopano tiyeni tikambirane zina mwa zifukwa zimene zikuchititsa kuti munthu athe kufika kwa Atate pokhapokha ngati atadzera mwa Mwana basi. Tikadziwa zifukwa zimenezo tiona zimene zikuchititsa kuti Yesu akhaledi “njira, choonadi ndi moyo.”
Yesu Ali ndi Udindo Wofunika Kwambiri Pokwaniritsa Cholinga cha Yehova
3. N’chifukwa chiyani anthu angafike kwa Mulungu kudzera mwa Yesu yekha?
3 Chifukwa choyamba ndiponso chofunika kwambiri n’chakuti anthu angafike kwa Mulungu kudzera mwa Yesu chifukwa Yehova anaona kuti n’zoyenera kupereka udindo wofunika kwambiriwu kwa Mwana wake.a Atate wamupatsa udindo wofunika kwambiri pokwaniritsa zolinga zake zonse. (2 Akorinto 1:20; Akolose 1:18-20) Kuti timvetse bwino za udindo umene Mwanayo wapatsidwa, tiganizire zimene zinachitika m’munda wa Edeni pamene anthu awiri oyambirira anagwirizana ndi Satana n’kupandukira Yehova.—Genesis 2:16, 17; 3:1-6.
4. Kodi zimene zinachitika m’munda wa Edeni zinayambitsa nkhani iti, nanga Yehova anachita chiyani kuti aithetse?
4 Zimene makolo athu anachita mogwirizana ndi Satana popandukira Mulungu m’munda wa Edeni, zinayambitsa nkhani yofunika kwambiri imene ikukhudza angelo komanso anthu. Nkhani yake ndi yakuti: ‘Kodi Mulungu amene dzina lake ndi Yehova ndi woyeradi, wabwino, wolungama komanso kuti zonse zimene amachita amazichita mwachikondi?’ Kuti athetse nkhani yofunikayi, Yehova anaganiza zoti atumize mwana wake wauzimu yemwenso ndi wangwiro padziko lapansi lino. Ntchito imene mwana ameneyu ankafunika kugwira inali yofunika kwambiri chifukwa ankayenera kupereka moyo wake dipo kuti apulumutse anthu komanso kuti ayeretse dzina la Atate wake. Kuti mavuto onse amene Satana anayambitsa m’munda wa Edeni athe, mwana amene akanasankhidwayo ankafunika kukhala wokhulupirika mpaka imfa. (Aheberi 2:14, 15; 1 Yohane 3:8) Koma Yehova anali ndi ana ambirimbiri auzimu komanso angwiro. (Danieli 7:9, 10) Kodi iye anasankha mwana uti kuti agwire ntchito yofunika kwambiri imeneyi? Yehova anasankha “Mwana wake wobadwa yekha,” amene kenako anayamba kutchedwa Yesu Khristu.—Yohane 3:16.
5, 6. Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti amakhulupirira Mwana wake, ndipo n’chifukwa chiyani amamukhulupirira?
5 Kodi tiyenera kudabwa chifukwa choti Yehova anasankha mwanayu? Ayi ndithu. Atate amakhulupirira kwambiri Mwana wake wobadwa yekha ameneyu. Zaka zambirimbiri Mwana wake asanabwere padziko lapansi, Yehova ananeneratu kuti Mwanayu adzakhalabe wokhulupirika ngakhale kuti adzakumana ndi mavuto ambiri. (Yesaya 53:3-7, 10-12; Machitidwe 8:32-35) Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Mofanana ndi anthu komanso angelo, Mwanayo anali ndi ufulu wosankha yekha zochita. Komabe Yehova ankamukhulupirira kwambiri Mwana wakeyo moti ananeneratu kuti adzakhala wokhulupirika. N’chifukwa chiyani ankamukhulupirira kwambiri choncho? N’chifukwa chakuti Yehova amamudziwa bwino Mwana wakeyo ndipo amadziwa kuti Mwanayo amafunitsitsa kuchita zinthu zomukondweretsa. (Yohane 8:29; 14:31) Mwanayo amakonda kwambiri Atate ndipo nayenso Yehova amakonda kwambiri Mwana wakeyo. (Yohane 3:35) Chikondi cha pakati pa Atate ndi Mwana wakeyo chimachititsa kuti azigwirizana komanso kukhulupirirana kwambiri, moti palibe chimene chingachititse kuti zimenezi zisinthe.—Akolose 3:14.
6 Popeza taona kuti Mwanayu ali ndi udindo wofunika kwambiri, Atate wake amamukhulupirira ndiponso kuti Atate ndi Mwanayo amakondana, kodi si zomveka kunena kuti tingafike kwa Mulungu kudzera mwa Yesu basi? Komabe, pali chifukwa chinanso chimene chikupangitsa kuti Mwana yekhayo akhale woyenera kutitsogolera kwa Atate.
Mwana Yekha Ndi Amene Amawadziwa Bwino Atate
7, 8. N’chifukwa chiyani n’zosadabwitsa kuti Yesu ananena kuti palibe amene amawadziwa bwino Atate “koma Mwana yekha”?
7 Pali zinthu zimene timayenera kuchita kuti tikhale mabwenzi a Yehova. (Salimo 15:1-5) Yesu, yemwe ndi Mwana wa Mulungu, amadziwa bwino kwambiri kuposa munthu aliyense, zimene munthu angachite kuti azitsatira mfundo za Mulungu ndiponso kuti azimusangalatsa. Yesu anati: “Atate wanga wapereka zinthu zonse kwa ine ndipo palibe amene akumudziwa bwino Mwana koma Atate okha. Komanso palibe amene akuwadziwa bwino Atate koma Mwana yekha ndi aliyense amene Mwanayo wafuna kumuululira za Atatewo.” (Mateyu 11:27) Tiyeni tione chifukwa chimene tinganenere kuti Yesu ananena zoona komanso sanakokomeze zinthu pamene ananena kuti palibe amene akuwadziwa bwino Atate “koma Mwana yekha.”
8 Monga “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse,” Mwanayo amakondana kwambiri ndi Yehova. (Akolose 1:15) Taganizirani ubwenzi umene unalipo pakati pa Atate ndi Mwanayo, zaka zosawerengeka pamene anali awiriwiri, ana ena onse auzimu asanalengedwe. (Yohane 1:3; Akolose 1:16, 17) Taganiziraninso za mwayi wapadera umene Mwanayo anali nawo pamene anali ndi Atate ake. Iye anayamba kuona zinthu ngati mmene Atate akewo amaonera, anaphunzira zolinga zawo, mfundo zawo ndiponso mmene amachitira zinthu. N’zoonadi, Yesu sanakokomeze pamene ananena kuti amawadziwa bwino Atate ake kuposa wina aliyense. Chifukwa chakuti ankawadziwa bwino kwambiri, Yesu ankatha kufotokoza zinthu zokhudza Atate ake kuposa mmene munthu wina aliyense akanachitira.
9, 10. (a) Kodi Yesu anasonyeza bwanji makhalidwe a Atate ake? (b) Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti Yehova azitikonda?
9 Zimene Yesu ankaphunzitsa zinasonyeza kuti ankadziwa bwino kwambiri mmene Yehova amaganizira, mmene amaonera zinthu ndiponso zimene amafuna kuti anthu amene amamulambira azichita.b Yesu anasonyeza makhalidwe a Atate ake m’njira inanso yaikulu. Iye anati: “Amene waona ine waonanso Atate.” (Yohane 14:9) Yesu ankatsanzira zochita komanso zolankhula za Atate ake mosaphonyetsa chilichonse. Choncho tikamawerenga za Yesu m’Baibulo, mwachitsanzo mawu ogwira mtima ndiponso anzeru amene ankalankhula pophunzitsa, chifundo chimene chinamuchititsa kuti azichiritsa odwala ndiponso chisoni chimene chinamuchititsa kuti alire, tizizindikira kuti Yehova akanachitanso chimodzimodzi. (Mateyu 7:28, 29; Maliko 1:40-42; Yohane 11:32-36) Zimene Mwanayu ankalankhula ndiponso kuchita, zinkasonyeza bwino kwambiri makhalidwe komanso zimene Atate ake amafuna. (Yohane 5:19; 8:28; 12:49, 50) Choncho kuti Yehova azitikonda, tiyenera kumvera komanso kutsatira zimene Yesu ankaphunzitsa.—Yohane 14:23.
10 Popeza Yesu amamudziwa bwino kwambiri Yehova ndiponso amamutsanzira bwino zedi, n’zosadabwitsa kuti Yehova wasankha Mwanayo kuti akhale njira yokhayo yofikira kwa iye. Popeza tadziwa chifukwa chimene tingafikire kwa Yehova kudzera mwa Yesu yekha basi, tiyeni tsopano tikambirane tanthauzo la mawu amene Yesu ananena akuti: “Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.”—Yohane 14:6.
“Ine Ndine Njira”
11. N’chifukwa chiyani tingakhale pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu kudzera mwa Yesu yekha basi?
11 Taphunzira kale kuti sitingathe kufika kwa Mulungu ngati sitingadzere mwa Yesu. Choncho ganizirani mozama mmene mfundo imeneyi ikutikhudzira ifeyo. Mfundo yakuti Yesu ndi “njira” ikutanthauza kuti tingakhale pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu kudzera mwa iyeyo basi. N’chifukwa chiyani zili choncho? N’chifukwa chakuti Yesu anapereka moyo wake nsembe ya dipo ndipo anachita zimenezi pokhalabe wokhulupirika mpaka imfa. (Mateyu 20:28) Zikanakhala zosatheka kuti tifike kwa Mulungu popanda nsembe ya dipo imeneyi. Chifukwa cha uchimo, zinali zosatheka kuti anthu afike kwa Yehova Mulungu popeza iye ndi woyera ndipo amadana ndi uchimowo. (Yesaya 6:3; 59:2) Koma nsembe ya Yesu inachititsa kuti zimenezi zikhale zotheka chifukwa inaphimba machimo athu. (Aheberi 10:12; 1 Yohane 1:7) Tikavomereza komanso kukhulupirira nsembe imene Mulungu anatipatsa kudzera mwa Khristu, tingakhale pa ubwenzi ndi Yehova. Imeneyi ndi njira yokhayo imene ‘tinagwirizanitsidwira ndi Mulungu.’—Aroma 5:6-11.
12. Kodi Yesu ndi “njira” pa nkhani ziti?
12 Yesu ndi “njira” pa nkhani ya pemphero. Kudzera mwa Yesu yekha, mapemphero athu ochokera pansi pa mtima angafike kwa Yehova ndiponso tingakhale ndi chikhulupiro kuti atiyankha. (1 Yohane 5:13, 14) Yesu anachita kunena yekha kuti: “Ngati mungapemphe chilichonse kwa Atate m’dzina langa adzakupatsani. . . . Pemphani ndipo mudzalandira kuti chimwemwe chanu chisefukire.” (Yohane 16:23, 24) Choncho tingagwiritsire ntchito dzina la Yesu popemphera kwa Yehova ndipo tingatchule Mulungu kuti “Atate wathu.” (Mateyu 6:9) Tinganenenso kuti Yesu ndi “njira” chifukwa anapereka chitsanzo chabwino. Monga mmene taonera, Yesu ankatsanzira Atate ake mosaphonyetsa chilichonse. Iye anatipatsa chitsanzo cha zimene tingachite kuti tizisangalatsa Yehova pa moyo wathu. Choncho, kuti tifike kwa Yehova tiyenera kutsatira mapazi a Yesu mosamala kwambiri.—1 Petulo 2:21.
“Ine Ndine . . . Choonadi”
13, 14. (a) Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti Yesu ankalankhula zoona zokhazokha? (b) Kodi Yesu ankayenera kuchita chiyani kuti akhale “choonadi” ndipo n’chifukwa chiyani?
13 Nthawi zonse Yesu ankanena choonadi mogwirizana ndi mawu a ulosi a Atate ake. (Yohane 8:40, 45, 46) Yesu sanalankhulepo mawu achinyengo ngakhale pang’ono. (1 Petulo 2:22) Ngakhale anthu amene ankamutsutsa anavomereza kuti iye ankaphunzitsa “njira ya Mulungu mogwirizana ndi choonadi.” (Maliko 12:13, 14) Komabe, pamene Yesu ananena kuti “ine ndine . . . choonadi,” sanangotanthauza kuti ankalankhula, kulalikira ndiponso kuphunzitsa mfundo za choonadi basi. Mfundo yoti Yesu ndi choonadi imatanthauza zambiri.
14 Kumbukirani kuti zaka zambirimbiri Yesu asanabwere padzikoli, Yehova anauzira anthu amene analemba Baibulo kuti alembe maulosi ambiri onena za Mesiya kapena kuti Khristu. Maulosiwa ananeneratu mwatsatanetsatane za moyo wake, utumiki ndiponso imfa yake. Komanso m’Chilamulo cha Mose muli maulosi ambiri onena za Mesiya. (Aheberi 10:1) Kodi Yesu anakhala wokhulupirika mpaka imfa, moti anakwaniritsa maulosi onse onena za iye? Inde, ndipo zimenezi zinasonyeza kuti Yehova ndi Mulungu amene amakwaniritsa zinthu zimene walosera. Yesu anakwaniritsa udindo waukulu kwambiri wochititsa kuti dzina la Yehova lilemekezedwe. Chilichonse chimene Yesu ananena komanso kuchita chinasonyeza kuti maulosi a m’Baibulo ndi olondola. (2 Akorinto 1:20) N’chifukwa chake Yesu akutchedwa “choonadi.” Yesu anakwaniritsa maulosi amenewo ndendende moti zimangokhala ngati maulosiwo analembedwa iye atachita kale zinthuzo.—Yohane 1:17; Akolose 2:16, 17.
“Ine Ndine . . . Moyo”
15. Kodi kukhulupirira Mwana wa Mulungu kumatanthauza chiyani, nanga anthu angadzapeze madalitso otani chifukwa chochita zimenezi?
15 Yesu ndi “moyo” chifukwa choti tingalandire “moyo weniweniwo” kudzera mwa iye yekha basi. (1 Timoteyo 6:19) Baibulo limati: “Amene amakhulupirira Mwanayo adzalandira moyo wosatha. Wosamvera Mwanayo sadzalandira moyowu, koma mkwiyo wa Mulungu udzakhalabe pa iye.” (Yohane 3:36) Kodi mawu akuti kukhulupirira Mwana wa Mulungu akutanthauza chiyani? Akutanthauza kuti timakhulupirira kuti n’zosatheka kudzapeza moyo wosatha popanda Yesu. Komanso amatanthauza kuti timasonyeza kuti tili ndi chikhulupiriro m’njira zosiyanasiyana monga zimene timachita, kupitiriza kuphunzira za Yesu ndiponso kuyesetsa kutsatira zimene ankaphunzitsa komanso chitsanzo chake. (Yakobo 2:26) Choncho, anthu angadzalandire moyo wosatha chifukwa chokhulupirira Mwana wa Mulungu. Akhristu odzozedwa omwe ndi “kagulu kankhosa” adzalandira moyo kumwamba umene sungafe ndipo a “khamu lalikulu” la “nkhosa zina,” adzalandira moyo wangwiro m’paradaiso padziko lapansi.—Luka 12:32; 23:43; Chivumbulutso 7:9-17; Yohane 10:16.
16, 17. (a) Kodi Yesu adzasonyeza bwanji kuti iye ndi “moyo” ngakhale kwa anthu amene anamwalira? (b) Kodi tingakhale ndi chikhulupiriro chotani?
16 Nanga kodi n’chiyani chidzachitikire anthu amene anamwalira? Yesu ndi “moyo” ngakhalenso kwa anthu amenewa. Atatsala pang’ono kuukitsa Lazaro, Yesu anauza Malita, yemwe anali mchemwali wake wa Lazaro kuti: “Ine ndine kuuka ndi moyo. Aliyense wokhulupirira ine, ngakhale atamwalira, adzakhalanso ndi moyo.” (Yohane 11:25) Yehova anapatsa Mwana wake “makiyi a imfa ndi a Manda,” zimene zikutanthauza kuti anamupatsa mphamvu zoti azitha kuukitsa akufa. (Chivumbulutso 1:17, 18) Pogwiritsira ntchito makiyi amenewa, Yesu, yemwe anapatsidwa ulemerero, adzatsegula zitseko za Manda ndipo anthu onse omwe ali m’mandamo adzauka.—Yohane 5:28, 29.
17 Yesu anafotokoza bwino cholinga cha moyo ndi utumiki wake padziko lapansi pano pogwiritsa ntchito mawu osavuta akuti: “Ine ndine njira, choonadi ndi moyo.” Mawu amenewa ndi ofunika kwambiri kwa ife masiku ano. Kumbukirani kuti Yesu anapitiriza kunena mawu a mulembali kuti: “Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.” (Yohane 14:6) Mawu amene Yesu ananenawa ndi ofunikabe kwambiri mpaka lero. Choncho tingakhale ndi chikhulupiriro chonse kuti ngati tikutsatira Yesu, sitidzasochera ngakhale pang’ono. Iye yekha ndi amene angatisonyeze njira ‘yofikira kwa Atate.’
-