Mawu a Yehova Afalikira!
“Motero mawu a Yehova ananka nafalikira ndi kugwira ntchito mwamphamvu.”—MACHITIDWE 19:20, “NW.”
1. Kodi nchiyani chimene chidzakwaniritsidwa m’phunziro ili la Baibulo la bukhu la Machitidwe a Atumwi?
YEHOVA ankatsegulira chitseko ntchito. Makamaka Paulo, “mtumwi wa anthu amitundu,” akakhoza kutsogolera ntchito imeneyo. (Aroma 11:13) Ndithudi, kupitiriza kwathu kuphunzira Machitidwe a Atumwi kumapeza iye woloŵetsedwa mochititsa chidwi m’maulendo aumishonale.—Machitidwe 16:6–19:41.
2. (a) Kodi ndimotani mmene mtumwi Paulo anatumikirira monga mlembi wouziridwa mwaumulungu kuchokera pafupifupi 50 C.E. mpaka 56 C.E.? (b) Kodi chinachitika nchiyani pamene Mulungu anadalitsa utumiki wa Paulo ndi wa ena?
2 Paulo analinso mlembi wouziridwa mwaumulungu. Kuchokera pafupifupi 50 C.E. mpaka 56 C.E., iye analemba 1 ndi 2 Atesalonika ali m’Korinto, Agalatiya ali mumzindawo kapena ali m’Suriya wa Antiokeya, 1 Akorinto ali m’Efeso, 2 Akorinto ali ku Makedoniya, ndi Aroma ali m’Korinto. Ndipo pamene Mulungu anadalitsa utumiki wa Paulo ndi wa ena, “mawu a Yehova ananka nafalikira ndi kugwira ntchito mwamphamvu.”—Machitidwe 19:20, NW.
Kuchokera ku Asiya kunka ku Ulaya
3. Kodi ndimotani mmene Paulo ndi anzake anakhazikitsira chitsanzo chabwino ponena za chitsogozo cha mzimu woyera?
3 Paulo ndi anzake anakhazikitsa chitsanzo chabwino cha kulandira chitsogozo choperekedwa ndi mzimu woyera. (16:6-10) Mwinamwake mwa zivumbulutso zofuula momveka, maloto, kapena masomphenya, mzimuwo unawaletsa kulalikira m’boma la Asiya ndi m’dera la Bitiya, omwe anafikiridwa ndi mbiri yabwino pambuyo pake. (Machitidwe 18:18-21; 1 Petro 1:1, 2) Kodi nchifukwa ninji mzimuwo unaletsa kuloŵedwamoko koyambirira? Antchito anali oŵerengeka, ndipo mzimu unkawatsogoza ku minda yobala zipatso kwenikweni ku Ulaya. Chotero lerolino, ngati njira njotsekedwa m’gawo lina, Mboni za Yehova zimakalalikira kwinakwake, nkukhala zotsimikizira kuti mzimu wa Mulungu udzaŵatsogolera kwa onga nkhosa.
4. Kodi ndiliti lomwe linali yankho la masomphenya a Paulo a munthu wa ku Makedoniya wopempha thandizo?
4 Kenaka Paulo ndi anzake ‘anadutsa’ Musiya, chigawo cha mu Asia Minor, monga munda waumishonale. Komabe, m’masomphenya, Paulo anaona munthu wa ku Makedoniya akupempha thandizo. Chotero amishonalewo mofulumira ananka ku Makedoniya, chigawo cha Chilumba cha Balkan. Mofananamo, Mboni zambiri tsopano zimatsogozedwa ndi mzimu woyera kukatumikira kumene kusoŵa kwa alengezi a Ufumu kuli kwakukulu.
5. (a) Kodi nchifukwa ninji kunganenedwe kuti mawu a Yehova anafalikira mu Filipi? (b) Kodi ndi m’njira yotani mmene Mboni zambiri zamakono zimafananira ndi Lidiya?
5 Mawu a Yehova anafalikira mu Makedoniya. (16:11-15) Filipi, dziko lolamulidwa ndi maiko ena lokhalidwa kwakukulukulu ndi nzika Zachiroma, mwachiwonekere anali ndi Ayuda oŵerengeka ndipo analibe sunagoge. Chotero abale ananka ku ‘malo a pemphero’ kumbali kwa mtsinje wokhala kunja kwa mzindawo. Pakati pa opezedwako panali Lidiya, mwinamwake wotembenuka Wachiyuda wochokera ku Tiyatira, mzinda wa mu Asia Minor wotchuka ndi indasitale yake ya zibakuwa. Iye anagulitsa chibakuwa chake chofiira kapena nsalu ndi zovala zopakidwa mitundu yake. Pamene Lidiya ndi am’banja lake anabatizidwa, iye anadzipereka mooloŵa manja kwenikweni kotero kuti Luka analemba kuti: “Anatiumiriza ife.” Tiri oyamikira kwa alongo a mtundu umenewu lerolino.
Mdindo Akhala Mkhulupiriri
6. Kodi ndimotani mmene ntchito ya ziŵanda inatsogolera ku kuponyedwa m’ndende kwa Paulo ndi Sila ku Filipi?
6 Satana ayenera kukhala anakwiya chifukwa cha kupita patsogolo kwauzimu mu Filipi, popeza kuti ntchito zochitidwa ndi ziŵanda kumeneko zinatsogolera kuponyedwa m’ndende kwa Paulo ndi Sila. (16:16-24) Kwa masiku angapo iwo anatsatiridwa ndi namwali yemwe anali ndi “mzimu wambwebwe” (kwenikweni, “mzimu wa nsato”). Chiŵandacho chingakhale chinasanduka munthu wotchedwa Apollo wa ku Pytho, mulungu yemwe ankalingaliridwa kuti ndiye anapha njoka yotchedwa pyʹthon (nsato). Namwaliyo anabweretsera ambuye ake mapindu aakulu mwakuchita ntchito yolosera. Eya, iye angakhale adasimbira alimi nthaŵi yofunikira kufesa mbewu, asungwana nthaŵi yokwatiwa, ndipo anthu a m’migodi kuwauza komwe angapeze golidi! Iye anapitirizabe kutsatira abalewo ndi kufuula kuti: ‘Anthu awa ndi akapolo a Mulungu wa Kumwambamwamba, amene akulalikirani inu njira ya chipulumutso.’ Chiŵandacho chingakhale chidali chimene chinampangitsa iye kunena zimenezi kuti zizindikiridwe kuti kulosera kwakeko kunali kowuziridwa mwaumulungu, koma ziŵanda ziribe kuyenera kwa kupanga kulengeza konena za Yehova ndi makonzedwe ake a chipulumutso. Pamene Paulo anatopa ndi kuvutitsidwako, iye anatulutsa chiŵandacho m’dzina la Yesu. Malonda awo atawonongedwa, ambuye a namwaliyo anakokera Paulo ndi Sila kumalo a msika, kumene anakwapulidwa ndi ndodo. (2 Akorinto 11:25) Pamenepo iwo anaponyedwa m’ndende namangitsa mapazi awo m’zigologolo. Zipangizozi zikakhoza kusinthidwa kotero kuti zikanule miyendo ya munthu, kumpangitsa iye kumva kupweteka kwambiri.
7. Kodi kuponyedwa m’ndende kwa Paulo ndi Sila ku Filipi kunatsogolera ku madalitso a yani ndipo motani?
7 Kuikidwa m’ndendeku kunatsogolera ku madalitso kwa mdindo wa ndendeyo ndi banja lake. (16:25-40) Pakati pausiku Paulo ndi Sila ankapemphera ndi kuyamika Mulungu m’nyimbo, otsimikizira kuti iye anali nawo. (Salmo 42:8) Mwadzidzidzi, chivomezi chinatsegula zitseko ndikumasula maziko onse a ndende pamene maunyolo anamasuka m’mizati kapena makoma. Mdindoyo anagwidwa ndi mantha a kuvutika ndi chilango cha imfa chifukwa chakuti akaidi ake anathaŵa. Iye anali pafupi kudzipha pamene Paulo anafuula kuti: “Usadzipweteka wekha; tonse tiri muno.” Pamene anatulitsira Paulo ndi Sila kunja, mdindoyo anafunsa mmene angapulumutsidwire. “Ukhulupirire Ambuye Yesu,” ndilo linali yankho. Pamene anamva mawu a Yehova, ‘iye ndi apabanja pake anabatizidwa popanda kuchedwa.’ N’chisangalalo chotani nanga chomwe chinabweretsedwa!
8. Kodi ndi kachitidwe kotani komwe kanachitidwa ndi oweruza a ku Filipi, ndipo kodi nchiyani chimene chikakwaniritsidwa iwo akanavomereza kuphophonya kwawo poyera?
8 Tsiku lotsatira, oweruza anatumiza akapitao kukamasula Paulo ndi Sila. Koma Paulo anati kwa iwo: ‘Adatikwapula ife pamaso pa anthu, osamva mlandu wathu, ife amene tiri Aroma, natiika m’ndende; ndipo tsopano kodi afuna kutitulutsira ife m’tseri? Iai, ndithu; koma adze okha atitulutse.’ Oweruza akanavomereza poyera kuphophonya kwawo, iwo adakakhala ozengereza kukwapula ndi kuponya m’ndende Akristu ena. Pokhala osakhoza kuthamangitsa nzika Zachiroma, oweruzawo anadza ndikupempha abalewo kupita, koma iwo anatero pambuyo polimbikitsa akhulupiriri anzawo. Chikondwerero choterocho tsopano chimafulumiza ziŵalo za Bungwe Lolamulira ndi oimira ena oyendayenda kuchezera ndi kulimbikitsa anthu a Mulungu padziko lonse lapansi.
Mawu a Yehova Afalikira mu Tesalonika ndi Bereya
9. Kodi ndi mwanjira yotani, yogwiritsiridwabe ntchito ndi Mboni za Yehova, imene Paulo ‘anatanthauzira ndi kutsimikizira’ kuti Mesiya anafunikira kuvutika ndi kuuka kwa akufa?
9 Chotsatira mawu a Mulungu anafalikira mu Tesalonika, mzinda waukulu wa Makedoniya ndi doko lalikulu la nyanja. (17:1-9) Kumeneko Paulo anakambitsirana ndi Ayuda, “natanthauzira, natsimikiza” kuti Mesiya anayenera kuvutika ndi kuuka kwa akufa. (Paulo adatero mwakuyerekezera maulosi ndi zochitika zokwaniritsidwa, monga mmene Mboni za Yehova zimachitira.) Motero, Ayuda ena, otembenuka ambiri, ndi ena anakhala akhulupiriri. Pamene Ayuda ena odukidwa anapanga khamu lowukira koma osatha kumpeza Paulo ndi Sila, iwo anakokera Yasoni ndi abale ena pamaso pa akulu a m’mudzi nawapatsa mlandu wakusanduliza anthu, mlandu wonyenga wounjikidwabe pa anthu a Yehova. Komabe, abalewo anamasulidwa pambuyo popereka ‘chikole.’
10. Kodi ndi m’lingaliro lotani limene Ayuda m’Bereya ‘anasanthulira [Malemba] mosamalitsa’?
10 Chotsatira Paulo ndi Sila ananka ku mzinda wa Bereya. (17:10-15) Kumeneko Ayuda ‘anasanthula [Malemba] mosamalitsa,’ monga momwe Mboni za Yehova zimalimbikitsira anthu kuchita lerolino. Abereyawo sanamkaikire Paulo koma anafufuza kuti atsimikizire kuti Yesu anali Mesiya. Chotulukapo chake? Ayuda ambiri ndi Agiriki ena (mwinamwake otembenuka) anakhala akhulupiriri. Pamene Ayuda ochokera ku Tesalonika anakwiyitsa makamu, abalewo anaperekeza Paulo kugombe, kumene ena a gulu lake angakhale adakwera ngalawa kunka ku Piraeus (yomwe makono iri Piraiévs), doko la mzinda wa Atene.
Mawu a Yehova Afalikira mu Atene
11. (a) Kodi ndimotani mmene Paulo anachitira umboni molimba mtima mu Atene, koma kodi ndani yemwe anapikisana naye polankhula naye? (b) Kodi ena anatanthauzanji pamene anatcha Paulo “wobwetuka”?
11 Umboni wolimba mtima unaperekedwa mu Atene. (17:16-21) Chifukwa cha mawu a Paulo onena za Yesu ndi chiukiriro, anthanthi analankhula naye mwampikisano. Ena anali a Epikureya, omwe anagogomezera pa zosangulutsa. Ena anali a Stoiki, omwe anagogomezera pa kudzilanga. ‘Ichi nchiyani afuna kunena wobwetuka uyu?’ anafunsa motero ena. Liwu lakuti “wobwetuka” (kwenikweni, “wotola mbewu”) linatanthauza kuti Paulo anali wofanana ndi mbalame yotola mbewu ndikusonkhanitsa chidziŵitso koma wopanda nzeru. Ena anati: ‘Anga wolalikira ziŵanda zachilendo.’ Ichi chinali chowopsya, popeza kuti Socrates anaphedwa ndi mlandu woterowo. Mwamsanga Paulo anatengedwera ku Areopagi (Phiri la Mars), mwinamwake kumene bwalo lalikulu lamilandu linakumanira pafupi ndi Acropolis.
12. (a) Kodi ndi mbali ziti za kulankhula poyera zomwe zikuwonekera m’kulankhula kwa Paulo pa Areopagi? (b) Kodi ndi mfundo ziti zimene Paulo anapanga ponena za Mulungu, ndipo ndi zotulukapo zotani?
12 Kulankhula kwa Paulo pa Areopagi kunali chitsanzo chabwino kwambiri cha munthu wokhala ndi mawu oyamba otsimikiza, okulitsidwa mwanzeru, ndi zigomeko zokhutiritsa—monga momwe zimaphunzitsidwira mu Sukulu Yautumiki Wateokratiki ya Mboni za Yehova. (17:22-34) Iye anati anthu a ku Atene anali achipembedzo kwenikweni kuposa ena. Eya, iwo adalidi ndi guwa lansembe la ‘Kwa Mulungu Wosadziwika,’ mwinamwake kupeŵa kunyoza mulungu aliyense! Paulo analankhula za Mlengi yemwe ‘analenga mitundu yonse mwa munthu mmodzi’ ndi ‘kupangiratu nyengo zawo, ndi malekezero a pokhala pawo,’ monga ngati nthaŵi yakuwononga Akanani. (Genesis 15:13-21; Danieli 2:21; 7:12) Mulungu ameneyu angapezedwe, ‘pakuti ifenso tiri mbadwa zake,’ anatero Paulo, akumagogomezera kuti munthu analengedwa ndi Yehova ndi kugwira mawu a olemba ndakatulo awo Aratus ndi Cleanthes. Monga mbadwa za Mulungu, sitiyenera kuganiza kuti Mlengi wangwiro ngofanana ndi fano lopangidwa ndi munthu wopanda ungwiro. Mulungu panthaŵi ina analekerera umbuli woterowo koma tsopano ankauza anthu kulapa, popeza kuti anakhazikitsa tsiku lakuweruza anthu ndi Woikidwa wake. Popeza kuti Paulo ‘akalalikira mbiri yabwino ya Yesu,’ khamu lake linadziŵa kuti iye anatanthauza kuti Kristu akakhala Woweruza ameneyo. (Machitidwe 17:18; Yohane 5:22, 30) Nkhani yonena za kulapa inakwiyitsa a Epikureya, ndipo anthanthi Achigiriki akanavomereza ndemanga zonena za kusafa kwa moyo koma osati za imfa ndi chiukiriro. Mwachiwonekere, mofanana ndi ambiri amene tsopano amanyalanyaza mbiri yabwino, ena anati: ‘Tidzakumvanso nthaŵi ina.’ Koma woweruza Dionisiyo ndi ena anakhala akhulupiriri.
Mawu a Mulungu Afalikira mu Korinto
13. Kodi ndimotani mmene Paulo anadzichilikizira yekha mu utumiki, ndipo kodi nkufanana kwamakono kotani komwe tikupeza?
13 Paulo anapitirira nanka ku Korinto, mzinda waukulu wa dera la Akaya. (18:1-11) Kumeneko iye anapeza Akula ndi Priskila, amene anapita kumeneko pamene Klaudiyo Kaisara analamulira Ayuda omwe sanali nzika Zachiroma kuchoka m’Roma. Kuti adzichilikize mu utumiki, Paulo anapanga mahema ndi aŵiri okwatirana Achikristu ameneŵa. (1 Akorinto 16:19; 2 Akorinto 11:9) Kucheka ndi kusoka zovala za zikopa zolimba za mbuzi kunali ntchito yolimba. Mofananamo, Mboni za Yehova zimadzipezera zosoŵa zawo za zinthu zakuthupi kupyolera m’ntchito yakuthupi, koma ntchito yawo ndiyo utumiki.
14. (a) Atayang’anizana ndi chitsutso chopitirizabe chochitidwa ndi Ayuda m’Korinto, kodi Paulo anachitanji? (b) Kodi Paulo anatsimikiziridwa motani za kukhalabe m’Korinto, koma ndimotani mmene anthu a Yehova amatsogozedwera lerolino?
14 Ayuda a ku Korinto anapitirizabe kulankhula monyoza pamene Paulo analengeza Umesiya wa Yesu. Chotero iye anakutumula zovala zake kudzichotsera thayo kulinga kwa iwo ndikuyamba kupanga misonkhano m’nyumba ya Tito Yusto, mwachidziŵikire Mroma. Ambiri (kuphatikizapo yemwe kale anali mkulu wa sunagoge Krispo ndi apabanja pake) anakhala akhulupiriri obatizidwa. Ngati chitsutso cha Ayuda chinapangitsa Paulo kukaikira kukhala m’Korinto, kukaikirako kunatha pamene Ambuye anamuuza m’masomphenya kuti: ‘Usaope. koma nena, usakhale chete; chifukwa Ine ndiri pamodzi ndi iwe, ndipo palibe munthu adzautsana ndi iwe kuti akuipse; chifukwa ndiri nao anthu ambiri m’mudzi muno.’ Chotero Paulo anapitirizabe kulalikira mawu a Mulungu kumeneko, kufikira chaka chimodzi ndi miyezi isanu ndi umodzi. Ngakhale kuti tsopano anthu a Yehova samalandira masomphenya, zonse ziŵiri pemphero ndi chitsogozo choperekedwa ndi mzimu woyera zimawathandiza kupanga zosankha zanzeru zofananazo zoyambukira zikondwerero za Ufumu.
15. Kodi chinachitika nchiyani pamene Paulo anaperekedwa pamaso pa Kazembe Galiyo?
15 Ayuda anapereka Paulo kwa Kazembe Junius Galiyo. (18:12-17) Iwo anatanthauza kuti Paulo ankasanduliza anthu mosakhala mwa lamulo—mlandu wonyenga womwe nduna Zachigiriki zikupanga tsopano motsutsana ndi Mboni za Yehova. Galiyo anadziŵa kuti Paulo analibe liŵongo lachinyengolo ndikuti Ayudawo sanasamale nkomwe ponena za makhalidwe abwino a Roma ndi malamulo ake, chotero iye anawathamangitsa. Pamene openyerera anakwapula Sostene, mkulu watsopano wa sunagoge, Galiyo sanaloŵereremo, mwinamwake akumaganiza kuti mtsogoleri watsopanoyo wa kachitidwe ka gulu lowukira motsutsana ndi Paulo ankalandira zomwe zinamuyenerera.
16. Kodi nchifukwa ninji Paulo anavomereza kumeta mutu wake mogwirizana ndi chowinda?
16 Paulo anapita paulendo wapamadzi wochokera ku doko la Aegea la Kenkreya kunka ku Efeso, mzinda wa mu Asia Minor. (18:18-22) Ulendowo usanapangike ‘iye anameta mutu wake pakuti adawinda.’ Nkosanenedwa kaya Paulo adawinda asadakhale mtsatiri wa Yesu kapena ngati ichi chinali kuyambika kapena mapeto a nyengo ya kuwindako. Akristu sali pansi pa Chilamulo, koma kunali kopatsidwa ndi Mulungu ndipo koyera, ndipo panalibe cholakwika m’kuwindako. (Aroma 6:14; 7:6, 12; Agalatiya 5:18) Mu Efeso, Paulo anakambitsirana ndi Ayuda, akumawalonjeza kubwerera ngati Mulungu analola. (Lonjezo limenelo linakwaniritsidwa pambuyo pake.) Kubwerera kwake ku Suriya wa Antiokeya kunamaliza ulendo wake wachiŵiri waumishonale.
Mawu a Yehova Afalikira m’Efeso
17. Ponena za ubatizo, kodi ndi malangizo otani amene Apolo ndi ena anafunikira?
17 Mwamsanga Paulo anayamba ulendo wake waumishonale wachitatu (pafupifupi 52-56 C.E.). (18:23–19:7) Panthaŵiyo m’Efeso, Apolo anaphunzitsa ponena za Yesu koma iye anadziŵa kokha za ubatizo wa Yohane womwe unali chizindikiro cha kulapa machimo olakwira pangano la Chilamulo. Priskila ndi Akula ‘anamfotokozera njira ya Mulungu mosamalitsa,’ mwachidziŵikire akumalongosola kuti kubatizidwa monga mmene anachitira Yesu kunaphatikizapo kumizidwa kwa munthu m’madzi ndi kulandira mzimu woyera wotsanuliridwa. Pambuyo pa kuchitika kwa ubatizo wa mzimu woyera pa Pentekoste wa 33 C.E., aliyense wobatizidwa ndi ubatizo wa Yohane anafunikira kubatizidwanso m’dzina la Yesu. (Mateyu 3:11, 16; Machitidwe 2:38) Pambuyo pake m’Efeso, pafupifupi amuna Achiyuda 12 omwe analowa ubatizo wa Yohane “anabatizidwa m’dzina la Ambuye Yesu” m’kubatizidwanso kokha kolembedwa m’Malemba. Pamene Paulo anaika manja ake pa iwo, awa analandira mzimu woyera ndi zizindikiro ziŵiri zozizwitsa za kuvomerezedwa kwakumwamba—kulankhula m’malirime ndi kunenera.
18. Kodi nkuti kumene Paulo anachitira umboni pamene anali m’Efeso, ndipo ndi zotulukapo zotani?
18 Motsimikizirika Paulo anali wotanganitsidwa m’Efeso, mzinda wa nzika pafupifupi 300,000. (19:8-10) Kachisi wake wa mulungu wachikazi Artemi anali chimodzi cha zinthu zisanu ndi ziŵiri zozizwitsa za dziko lakalekale, ndipo bwalo lake lamaseŵera linkatenga anthu 25,000. M’sunagoge, Paulo ‘anagwiritsira ntchito kukopa’ mwakupereka zigomeko zokhutiritsa koma anachokapo pamene ena analankhula monyoza ponena za Njira, kapena mkhalidwe wamoyo wozikidwa pa chikhulupiriro mwa Kristu. Kwa zaka ziŵiri, Paulo analankhula tsiku ndi tsiku m’nyumba zosonkhanira za Turano, ndipo ‘mawu’ anafalikira kupyola dera la Asiya.
19. Kodi chinachitika nchiyani m’Efeso chomwe chinapangitsa ‘mawu a Yehova kupitirizabe kukula ndi kufalikira’ kumeneko?
19 Mulungu anasonyeza kuvomereza ntchito ya Paulo mwakumtheketsa kuchiritsa ndi kutulutsa ziŵanda. (19:11-20) Koma ana aamuna asanu ndi aŵiri a mkulu wansembe Skeva analephera kutulutsa chiŵanda mwakugwiritsira ntchito dzina la Yesu chifukwa chakuti iwo sanaimire Mulungu ndi Kristu. Iwo anakhoza kuvulazidwa ndi munthu wogwidwa ndi chiŵandayo! Ichi chinapangitsa anthu kukhala amantha, ndipo “dzina la Yesu linakuzika.” Omwe anakhulupirira analeka machitidwe awo akubwebweta ndipo anaotcha poyera mabuku awo amene mwachiwonekere anali ndi zobwebweta ndi zamatsenga. ‘Motero,’ analemba tero Luka, ‘mawu a Yehova ananka nafalikira ndi kugwira ntchito mwamphamvu.’ Lerolinonso, atumiki a Mulungu akuthandizira kuonjola anthu ku ziŵanda.—Deuteronomo 18:10-12.
Kusalekerera kwa Chipembedzo Sikupambana
20. Kodi nchifukwa ninji osula siliva a ku Efeso anayambitsa chipwirikiti, ndipo kodi chinatha motani?
20 Kaŵirikaŵiri Mboni za Yehova zayang’anizana ndi makamu owukira, ndipo anateronso Akristu m’Efeso. (19:21-41) Pamene akhulupiriri anawonjezeka, Demetrio ndi osula siliva ena anatheredwa ndalama chifukwa chakuti anthu oŵerengeka ndiwo ankagula tiakachisi tawo tasiliva ta Artemi mulungu wachikazi wakubala wamaere ambiri. Litasonkhezeredwa ndi Demetrio, gulu lowukira linatengera Gayo ndi Aristarko anzake a Paulo kubwalo lamaseŵera, koma ophunzirawo sanalole Paulo kuloŵamo. Ngakhale ochilikiza zochitika ndi maseŵera ena anachonderera kuti iye asaike moyo wake pachiswe. Pakuti kwa maola aŵiri, gulu lowukiralo linafuula kuti: ‘Wamkulu ndi Artemi wa ku Efeso.’ Pomalizira, mkulu wa mzinda (yemwe anatsogolera boma la mmenemo) ananena kuti amuna osulawo akapereke milandu yawo kwa kazembe, wolamulidwa kupanga zigamulo zachiweruzo, kapena kuti nkhani yawo ikaweruzidwe mu “ziwanga” za nzika. Apo phuluzi, Roma akapatsa mlandu osonkhana popanda lamulowo kukhala odzetsa chipwirikiti. Pomwepo, iye anawapitikitsa.
21. Kodi Mulungu anadalitsa ntchito ya Paulo mwanjira yotani, ndipo kodi ndimotani mmene iye amadalitsira ya Mboni za Yehova lerolino?
21 Mulungu anathandiza Paulo kuyang’anizana ndi ziyeso zosiyanasiyana ndipo anadalitsa zoyesayesa zake za kuthandiza anthu kukana zophophonya zachipembedzo ndi kukupatira chowonadi. (Yerekezerani ndi Yeremiya 1:9, 10.) Tiri oyamikira chotani nanga kuti Atate wathu wakumwamba akudalitsa ntchito yathu mofananamo! Motero, tsopano mofanana ndi m’zaka za zana loyamba, ‘mawu a Yehova akukula ndi kufalikira.’
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi nchitsanzo chotani chimene Paulo anakhazikitsa povomereza chitsogozo cha mzimu woyera?
◻ Kodi ndi mwanjira yotani, yogwiritsiridwabe ndi atumiki a Yehova, imene Paulo ‘anatanthauzira ndi kutsimikizira’ nkhanizo?
◻ Kodi nkufanana kotani komwe kulipo pakati pa kuyankha kwa Paulo pa Areopagi ndi kulalikira kwa Mboni za Yehova?
◻ Kodi ndimotani mmene Paulo anadzichilikizira yekha mu utumiki, ndipo kodi nkufanana kotani kwamakono komwe ichi chili nako?
◻ Monga momwe anachitira ndi ntchito ya Paulo, kodi ndimotani mmene Mulungu wadalitsira ntchito ya Mboni za Yehova lerolino?
[Zithunzi pamasamba 16, 17]
Mawu a Yehova anafalikira mu
1. Filipi
2. ndi 3. Atene
4. ndi 6. Efeso
5. Roma
[Mawu a Chithunzi]
Photo No. 4: Manley Studios