‘Yendayenda M’dzikoli’
‘Yendayenda m’dzikoli m’litali mwake ndi m’mimba mwake.’—Genesis 13:17.
1. Kodi Mulungu anauza Abrahamu malangizo ochititsa chidwi otani?
KODI mumasangalala kuona malo osiyanasiyana mukakhala paulendo? Ambirife timasangalala tikamaona madera osiyanasiyana kaya tili m’basi, m’galimoto, panjinga kapenanso tikamayenda pansi. Ena amaona kuti akayenda wapansi m’pamene amatha kuona bwino malo. Nthaŵi zambiri maulendo ameneŵa amakhala anthaŵi yochepa chabe. Komano ganizirani mmene Abrahamu anamvera Mulungu atamuuza kuti: “Tauka, nuyendeyende m’dzikoli m’litali mwake ndi m’mimba mwake; chifukwa kuti ndidzakupatsa iwe limenelo.”—Genesis 13:17.
2. Kodi Abrahamu anapita kuti atachoka ku Igupto?
2 Taganizirani nkhani imene mukupezeka mawu ameneŵa. Abrahamu, pamodzi ndi mkazi wake ndiponso anthu ena, anali atakhala kwa nthaŵi yochepa ku Igupto. Chaputala 13 cha Genesis, chimatiuza kuti iwo anachoka ku Igupto n’kuyenda ndi ziŵeto zawo kupita ku “dziko la kum’mwera,” kapena kuti Negebu. Kenako Abrahamu ‘anamkabe ulendo wake kuchokera ku Negebu kumka ku Beteli.’ Patabuka mkangano pakati pa abusa a ziŵeto zake ndi abusa a mphwake Loti n’kufika poti anthu aŵiriŵa anayenera kupeza malo osiyana odyetserako ziŵeto, Abrahamu chifukwa cha mtima wopatsa anauza Loti kuti ayambe ndi iye kusankha kopita. Loti anasankha ‘chigwa cha Yordano,’ chomwe chinali chachonde kwambiri “monga munda wa Yehova,” ndipo patapita nthaŵi anakakhala ku Sodomu. Mulungu anauza Abrahamu kuti: “Tukulatu maso ako, nuyang’ane kuyambira kumene uliko, kumpoto, ndi kum’mwera, ndi kum’maŵa, ndi kumadzulo.” Zikuoneka kuti, Abrahamu anaima pamalo ena okwera kufupi ndi Beteli ndipo anatha kuona mbali zina za dzikolo. Koma anafunika kuchita zinthu zinanso. Mulungu anamuuza kuti ‘ayendeyende m’dzikolo’ ndi kuona mmene deralo linalili ndi kutinso aone zigawo zake.
3. Kodi n’chifukwa chiyani kungakhale kovuta kuti tipange chithunzithunzi cha maulendo a Abrahamu m’maganizo mwathu?
3 Sitikudziŵa kuti Abrahamu anayenda mtunda wautali motani asanafike ku Hebroni, koma n’zosakayikitsa kuti iye analidziŵa bwino Dziko Lolonjezedwa kusiyana ndi mmene ambirife timalidziŵira. Taganizirani za malo otchulidwa m’nkhaniyi. Amatchulamo za Negebu, Beteli, chigwa cha Yordano, Sodomu, ndi Hebroni. Kodi m’maganizo mwanu mumavutika kupanga chithunzithunzi cha kumene kunali malo ameneŵa? Ambiri mwa anthu a Yehova sangathe kuchita zimenezi chifukwa chakuti ndi ochepa okha amene anakaonapo malo otchulidwa m’Baibulo, ndi kuyendayenda m’chigawo chonsecho. Komabe pali chifukwa chomveka chokhalira ndi chidwi chachikulu chofuna kudziŵa zinthu zokhudza madera otchulidwa m’Baibulo. N’chifukwa chiyani zili choncho?
4, 5. (a) Kodi lemba la Miyambo 18:15 limagwirizana motani ndi nkhani ya kudziŵa ndiponso kuzindikira mayiko otchulidwa m’Baibulo? (b) Kodi m’chaputala 2 cha Zefaniya muli chiyani?
4 Mawu a Mulungu amati: “Mtima wa wozindikira umaphunzira; khutu la anzeru lifunitsa kudziŵa.” (Miyambo 18:15) Pali zinthu zambiri zimene munthu angathe kuzidziŵa, koma kudziŵa molondola zinthu zokhudza Yehova Mulungu ndiponso zochita zake ndiko kuli kofunika kwambiri. Kunena zoona, zimene timaŵerenga m’Baibulo ndi zofunika kwambiri kuti tidziŵe zimenezi molondola. (2 Timoteo 3:16) Komabe, onani kuti pamafunikanso kuzindikira. Kuzindikira ndiko kutha kuona nkhani ndi kudziŵa nkhani yonseyo mwa kumvetsa kugwirizana kwa mbali zonse za nkhaniyo ndiponso mutu wake. Timafunikanso kuchita zimenezi tikamaŵerenga za malo otchulidwa m’Baibulo. Mwachitsanzo, ambirife timadziŵa kumene kuli Igupto, koma kodi timamva motani mfundo yakuti Abrahamu anachoka ku Igupto kupita “ku Negebu,” kenako anapita ku Beteli ndipo kenako anamka ku Hebroni? Kodi mumamvetsa kugwirizana kwa malo ameneŵa?
5 Kapena n’kutheka kuti mwatsatirapo ndandanda ya kuŵerenga Baibulo yokhala ndi Zefaniya chaputala 2. M’chaputalachi munapezamo maina a midzi, anthu, ndi mayiko. Chaputala chimodzi chokhachi chimatchula za Gaza, Asikeloni, Asidodi, Ekroni, Sodomu, ndi Nineve komanso Kanani, Moabu, Amoni ndi Asuri. Kodi munakwanitsa bwinobwino kupanga chithunzithunzi m’maganizo mwanu cha malo ameneŵa, amene kunkakhala anthu omwe anakhudzidwa ndi kukwaniritsidwa kwa maulosi a Mulungu?
6. N’chifukwa chiyani oŵerenga Baibulo ena amakonda kugwiritsira ntchito mapu? (Onani bokosi.)
6 Ambiri mwa ophunzira Mawu a Mulungu apindula kwambiri pogwiritsira ntchito mapu a madera otchulidwa m’Baibulo. Iwo amachita izi, osati chifukwa chongokhala ndi chidwi chabe ndi mapu, koma chifukwa chodziŵa kuti pogwiritsa ntchito mapu iwo angadziŵe zinthu zina zambiri za m’Mawu a Mulungu. Mapu angawathandizenso kuzindikira zambiri, poona kugwirizana kumene kulipo pakati pa mfundo zimene akuzidziŵa kale ndi nkhani zina. Pamene tikuona zitsanzo zina za mfundo imeneyi, mosakayikira nanunso muyamba kumukonda kwambiri Yehova ndiponso mumvetsa nkhani za m’Mawu ake.—Onani bokosi patsamba 14.
Mumamvetsa Bwino Nkhani Mukadziŵa Kutalika kwa Mitunda Yake
7, 8. (a) Kodi ndi zinthu zodabwitsa zotani zimene Samsoni anachita zokhudza mudzi wa Gaza? (b) Kodi tingayambe kumvetsa bwino zinthu zogometsa zimene Samsoni anachita tikadziŵa zinthu zina zotani? (c) Kodi kudziŵa ndi kuzindikira nkhani ya Samsoniyi kungatithandize motani?
7 Pa Oweruza 16:2 mungaŵerengepo zoti Woweruza Samsoni anali ku Gaza. Dzina loti Gaza limamvekamveka pawailesi, m’manyuzipepala, ndi pa TV masiku ano, motero mungathe kukhala ndi chithunzithunzi cha kumene Samsoni anali, m’dziko la Afilisti kufupi ndi gombe la nyanja ya Mediterranean. [11] Tsopano onani zimene Oweruza 16:3 amanena. Pamenepo pakuti: “Samsoni anagona mpaka pakati pa usiku, nauka pakati pa usiku, nagwira zitseko za pa chipata cha mudzi, ndi mphuthu ziŵirizo, nazichotsa ndi mpiringidzo womwe, naziika pa mapewa ake, nakwera nazo pamwamba pa phiri lili pandunji pa Hebroni.”
8 Mosakayikira, zitseko ndi mphuthu za mudzi wamphamvu monga Gaza zinali zikuluzikulu ndiponso zolemera. Taganizirani kuti mukufuna kuzinyamula. Samsoni anazinyamuladi, koma kodi anapita nazo kuti, ndipo anayenda ulendo wotani? Gaza ali kunyanja, kotsika kwambiri. [15] Koma Hebroni ali chakum’maŵa kwa Gaza pamalo okwera kwambiri. Sitinganene bwinobwino kuti “phiri lili pandunji pa Hebroni” linali pati kwenikweni, koma mudziwu uli pamtunda wa makilomita pafupifupi 60 kuchokera ku Gaza, ndipo uli m’dera lokwera kwabasi. Kodi si zoona kuti kudziŵa mtunda umene Samsoni anayenda kukutichititsa kuyamba kuona mwa njira ina zimene anachita? Ndipo kumbukirani chifukwa chake Samsoni ankatha kuchita zinthu zoterozo. N’chifukwa chakuti, “Unam’gwera iye kolimba mzimu wa Yehova.” (Oweruza 14:6, 19; 15:14) Akristufe masiku ano, sikuti timayembekezera kuti mzimu wa Mulungu utipatsa mphamvu zapadera ngati zimenezo. Komabe, mzimu wamphamvu womwewu ungatithandize kumvetsa bwino zinthu zakuya zauzimu ndi kutipatsa mphamvu zauzimu. (1 Akorinto 2:10-16; 13:8; Aefeso 3:16; Akolose 1:9, 10) Zoonadi, kumvetsa nkhani ya Samsoni kumatithandiza kuti tisakayikire ngakhale pang’ono kuti mzimu wa Mulungu ungathe kutithandiza.
9, 10. (a) Kodi pankhondo yomwe Gideoni anagonjetsa Amidyani panachitika zotani? (b) Kodi kudziŵa mmene dzikolo linalili kukutithandiza motani kuti nkhaniyi tiimve bwino kwambiri?
9 Nkhani inanso yomwe imasonyeza kufunika kodziŵa kutalika kwa mitunda ndi nkhani yokhudza Gideoni pamene anagonjetsa Amidyani. Anthu ambiri oŵerenga Baibulo amadziŵa kuti Woweruza Gideoni ndi gulu lake la anthu 300 anagonjetsa asilikali osiyanasiyana omwe anapanga gulu limodzi okwana 135,000, a mafuko a Amidyani, Aamaleki, ndi ena. Asilikaliwo anamanga misasa m’chigwa cha Yezreeli, kufupi ndi phiri la More. [18] Amuna a Gideoni anawomba malipenga, n’kuswa mbiya kuti aonetse miyuni yawo, ndipo anakuwa kuti: “Lupanga la Yehova ndi la Gideoni.” Izi zinasokoneza ndi kuchititsa mantha adani awowo, moti anayamba kukanthana okhaokha. (Oweruza 6:33; 7:1-22) Kodi zinachitika ndi zokhazi basi, zinthu zongochitika m’kanthaŵi kochepa usiku? Pitirizani kuŵerenga machaputala 7 ndi 8 a buku la Oweruza. Muona kuti Gideoni anapitiriza kulimbana nawo. Mwa malo ambiri amene anatchulidwa, ena masiku ano sadziŵika kuti anali pati, motero n’kutheka kuti sangapezeke m’mapu a malo otchulidwa m’Baibulo. Komabe, pali malo ambiri amene akudziŵika moti tingathe kutsatira zimene Gideoni anachita.
10 Gideoni anathamangitsa asilikali omwe anatsala pa asilikali omwe anapanga gulu limodzi lija kudutsa nawo ku Betesita ndipo kenako analoŵera nawo chakum’mwera ku Abelemehola, kufupi ndi Yordano. (Oweruza 7:22-25) Nkhaniyo imati: ‘Gideoni anafika ku Yordano, nawoloka, iye ndi amuna mazana atatu anali naye, ali otopa koma ali chilondolere.’ Atawoloka Yordano, Aisrayeli analondola adaniwo kuloŵera nawo chakum’mwera ku Sukoti ndi ku Penueli, kufupi ndi Yaboki, kenako n’kukwera nawo mapiri kupita ku Yogibeha (kufupi ndi mzinda wamakono wa Amman, m’dziko la Jordan). Uwu unali mtunda wa makilomita pafupifupi 80, akuthamangitsana ndi kumenyana. Gideoni anagwira ndi kupha mafumu aŵiri a Amidyani; kenako n’kubwerera kwawo, ku Ofira, kufupi ndi kumalo omwe kunayambira nkhondo ija. (Oweruza 8:4-12, 21-27) N’zoonekeratu kuti zinthu zogometsa zimene Gideoni anachita sikuti zinali kungowomba malipenga, kunyamula miyuni, ndiponso kufuula, zomwe zinangochitika m’mphindi zochepa basi. Ndipo taganizani mmene izi zikutithandizira kumvetsa bwino mawu aŵa onena za amuna achikhulupiriro, akuti: “Idzandiperewera nthaŵi ndifotokozere za Gideoni [ndi ena amene] analimbikitsidwa pokhala ofoka, anakula mphamvu kunkhondo.” (Ahebri 11:32-34) Nawonso Akristu angathe kutopa, koma kodi sipofunika kupitirizabe kuchita chifuniro cha Mulungu?—2 Akorinto 4:1, 16; Agalatiya 6:9.
Kodi Anthu Amaganiza Motani Ndipo Amachita Bwanji Zinthu?
11. Kodi Aisrayeli anayenda motani asanafike ku Kadesi komanso atachokako?
11 Ena angatsegule mapu a malo otchulidwa m’Baibulo pofuna kuona malo osiyanasiyana, koma kodi mukuganiza kuti mapu angatithandize kudziŵa mmene anthu amaganizira? Mwachitsanzo, taganizirani za Aisrayeli amene anayenda kuchoka ku Phiri la Sinai kuloŵera ku Dziko Lolonjezedwa. Ataima pa malo angapo paulendowo, iwo anafika ku Kadesi (kapena kuti, Kadesi Barinea). [9] Deuteronomo 1:2 amasonyeza kuti uwu unali ulendo wa masiku 11, ndipo unali mtunda wa makilomita pafupifupi 270. Ali kumeneko, Mose anatuma anthu 12 kuti akazonde Dziko Lolonjezedwa. (Numeri 10:12, 33; 11:34, 35; 12:16; 13:1-3, 25, 26) Anthu ozonda dzikowo anapita kumpoto podzera ku Negebu, ndipo zikuoneka kuti anadutsa ku Beereseba, kenako ku Hebroni, n’kukafika kumalire a kumpoto kwa Dziko Lolonjezedwa. (Numeri 13:21-24) Chifukwa chomvera zinthu zoipa zokhudza dzikolo zimene ananena anthu khumi amene anapita kukazonda dziko, Aisrayeliwo anayendayenda m’chipululu zaka 40. (Numeri 14:1-34) Kodi izi zikusonyezanji pankhani ya chikhulupiriro chawo ndiponso mtima wawo wofuna kudalira Yehova?—Deuteronomo 1:19-33; Salmo 78:22, 32-43; Yuda 5.
12. Kodi tinganene chiyani pankhani ya chikhulupiriro cha Aisrayeli, ndipo n’chifukwa chiyani tiyenera kusinkhasinkha za nkhaniyi?
12 Taonani nkhaniyi mukuganizira za kutalika kwa mitunda ya m’derali. Aisrayeli akanakhulupirira ndi kutsatira malangizo a Yoswa ndi Kalebe, kodi akanafunika kuyenda mtunda wautali kuti afike ku Dziko Lolonjezedwa? Kadesi anali pa mtunda wa makilomita pafupifupi 16 kuchokera ku Beere-lahai-roi, komwe Isake ndi Rebeka ankakhala. [7] Kuchokera ku Kadesi, panali mtunda wosakwana makilomita 95 kukafika ku Beereseba, mudzi womwe ukutchulidwa kuti unali kumalire a kum’mwera kwa Dziko Lolonjezedwa. (Genesis 24:62; 25:11; 2 Samueli 3:10) Atayenda kuchoka ku Igupto kupita ku Phiri la Sinai ndipo kenako n’kuyenda makilomita 270 kukafika ku Kadesi, tingati Aisrayeliwo anali atafika pakhomo pa Dziko Lolonjezedwa. Ifeyo tili m’malire mwa Paradaiso wolonjezedwa wa padziko lapansi. Kodi tikuphunzirapo chiyani? Poganizira nkhani ya Aisrayeliyi mtumwi Paulo anapereka malangizo aŵa: “Chifukwa chake tichite changu cha kuloŵa mpumulowo, kuti wina angagwe m’chitsanzo chomwe cha kusamvera.”—Ahebri 3:16–4:11.
13, 14. (a) Kodi zinthu zinali motani pamene Agibeoni anachita zinthu zoti ziwathandize? (b) Kodi n’chiyani chikusonyeza mtima wa Agibeoni, ndipo kodi tiyenera kuphunzirapo chiyani pamenepa?
13 M’nkhani ya m’Baibulo yonena za Agibeoni timaona mtima wosiyana ndi umenewu, wodalira Mulungu ndi kuchita chifuniro chake. Nthaŵi yothamangitsa Akanani inakwana pamene Yoswa anawolotsa Aisrayeli mtsinje wa Yordano n’kuloŵa nawo m’dziko limene Mulungu analonjeza kuti adzapatsa banja la Abrahamu. (Deuteronomo 7:1-3) Agibeoni anali pamndandanda wa mitundu yofunika kuthamangitsidwayo. Aisrayeli anagonjetsa midzi ya Yeriko ndi Ai ndipo anali atamanga misasa kufupi ndi Agibeoniwo, ku Giligala. Agibeoni sanafune kufa ngati Akanani otembereredwa, motero anatumiza nthumwi kuti zikakumane ndi Yoswa ku Giligala. Pofuna kupanga pangano la mtendere ndi Ahebri, iwo ananamizira kuti achokera kunja kwa dziko la Kanani.
14 Nthumwizo zinati: ‘Akapolo anu afumira dziko la kutalitali, chifukwa cha dzina la Yehova Mulungu wanu.’ (Yoswa 9:3-9) Malingana ndi mmene zovala ndiponso zakudya zawo zinalili, ankaonekadi ngati akuchokera kutali kwambiri, koma mudzi wa Gibeoni unali pamtunda wa makilomita pafupifupi 30 okha kuchokera ku Giligala. [19] Atakhulupirira zimenezi, Yoswa ndi akalonga ake anapanga pangano la mtendere ndi Gibeoni ndiponso midzi yawo yomwe inali kufupi ndi mudzi wa Gibeoni. Kodi chinyengo cha Agibeonichi chinali chongofuna kupeŵa kuwonongedwa? Ayi. Chinasonyeza mtima womwe anali nawo wofuna kuyanjidwa ndi Mulungu wa Israyeli. Yehova anavomereza kuti Agibeoni akhale ‘otema nkhuni, ndi otungira madzi msonkhanowo, ndi guwa la nsembe la Yehova,’ kuti azibweretsa nkhuni zogwiritsa ntchito zofunika popereka nsembe paguwa. (Yoswa 9:11-27) Agibeoni anapitiriza kukhala odzipereka kutumikira Yehova pogwira ntchito zonyozeka. Mwachionekere, ena mwa iwo anali nawo pagulu la Anetini amene anabwerera kuchokera ku Babulo ndi kukatumikira pa kachisi amene anamangidwanso. (Ezara 2:1, 2, 43-54; 8:20) Tingatengere mtima wawo mwa kuyesetsa kupitiriza kukhala pamtendere ndi Mulungu ndi kukhala ofunitsitsa kum’tumikira ngakhale pantchito zonyozeka.
Lolerani Kuvutikira Ena
15. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi chidwi chofuna kudziŵa mmene madera otchulidwa m’Baibulo analili tikamaŵerenga Malemba Achigiriki Achikristu?
15 Nkhani za m’Malemba Achigiriki Achikristu, monga nkhani zofotokoza maulendo a Yesu ndi mtumwi Paulo komanso utumiki womwe anachita, zimakhudzanso mmene madera otchulidwa m’Baibulo analili. (Marko 1:38; 7:24, 31; 10:1; Luka 8:1; 13:22; 2 Akorinto 11:25, 26) M’nkhani zotsatirazi, tayesani kuona mmene anthuŵa anayendera.
16. Kodi Akristu a ku Bereya anasonyeza motani kuti anali kum’konda Paulo?
16 Paulendo wake wachiŵiri waumishonale (womwe ukusonyezedwa ndi mzera womkera kofiira pamapuwo), Paulo anafika m’mudzi wa Filipi, womwe tsopano uli m’dziko la Girisi. [33] Analalikira kumeneko, anaikidwa m’ndende kenako anamasulidwa n’kupita ku Tesalonika. (Machitidwe 16:6–17:1) Ayuda atayambitsa ziwawa, abale a ku Tesalonika analimbikitsa Paulo kuti apite ku Bereya, mzinda womwe unali pa mtunda wa makilomita pafupifupi 65 kuchokera kumeneko. Ku Bereya, utumiki unamuyendera bwino kwambiri Paulo, koma Ayuda anabwera ndi kudzayambitsa chipwirikiti. Chifukwa cha izi, “abale anatulutsa Paulo amuke kufikira kunyanja,” ndipo “iwo amene anaperekeza Paulo anadza naye kufikira ku Atene.” (Machitidwe 17:5-15) Zikuoneka kuti anthu ena omwe anali atangoloŵa kumene Chikristu anadzipereka kuyenda makilomita 40 kukafika kunyanja ya Aegean, n’kulipira ngalawa, ndi kuyenda ulendo wa makilomita pafupifupi 500. N’kutheka kuti ulendo woterewu unali woopsa, koma abalewo analolera kuika miyoyo yawo pangozi ndipo chifukwa cha izi anakhala nthaŵi yaitali ndi nthumwi yoyendayenda ya Mulunguyi.
17. Kodi ndi zinthu ziti zimene tingazimvetsetse tikadziŵa mtunda wa pakati pa Mileto ndi Efeso?
17 Paulendo wake wachitatu (womwe ukusonyezedwa ndi mzera wobiriŵira pamapuwo), Paulo anafika kudoko la Mileto. Anaitanitsa akulu a mpingo wa ku Efeso, womwe unali pa mtunda wa makilomita 50 kuchokera ku Mileto. Taganizirani kuti akulu ameneŵa anayenera kusiya ntchito zina n’kupita kukakumana ndi Paulo. Mosakayikira, akuluŵa ali m’njira anali kukambirana mosangalala za kukakumana ndi Paulo. Atatha kukumana ndi Paulo ndi kumumva akupemphera, “onseŵa analira kwambiri, nam’kupatira Paulo pakhosi pake, nam’psompsona.” Kenako, “anam’perekeza iye kungalawa” kuti azipita ku Yerusalemu. (Machitidwe 20:14-38) Anthuŵa ayenera kuti anali kukambirana ndi kusinkhasinkha zinthu zambiri pamene amabwerera ku Efeso. Kodi simukugoma poganizira za chikondi chomwe amunaŵa anasonyeza poyenda mtunda wonsewo n’cholinga chokakumana ndi mtumiki woyendayendayu kuti akawapatse malangizo ndi kuwalimbikitsa? Kodi mu nkhaniyi mukuonamo mfundo yomwe mungagwiritse ntchito pa zochita zosiyanasiyana m’moyo wanu ndiponso pa kaganizidwe kanu?
Dziŵani za Dzikoli Ndiponso Zimene Zili M’tsogolo
18. Kodi tiziyesetsa kuchita chiyani pankhani ya malo otchulidwa m’Baibulo?
18 Zitsanzo zimene taonazi zikusonyeza phindu lodziŵa mmene dziko limene Mulungu anapatsa Aisrayeli linalili ndipotu dzikoli ndi lofunika kwambiri pankhani zambiri za m’Baibulo. (Komanso tingathenso kumvetsetsa kwambiri nkhanizi mwa kuphunzira za mayiko oyandikana ndi dzikoli amene amatchulidwa m’Baibulo.) Tikamamvetsa ndi kuzindikira nkhani zokhudza Dziko Lolonjezedwa, tiyenera kumakumbukira chinthu chomwe chinali chofunika kwambiri kuti Aisrayeli akaloŵe ndi kukhala m’dziko “moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi.” Iwo anafunika kuopa Yehova ndi kusunga malamulo ake.—Deuteronomo 6:1, 2; 27:3.
19. Kodi ndi maparadaiso aŵiri ati amene tikufunika kuikirapo mtima nthaŵi zonse?
19 Nafenso masiku ano tikufunika kuchita mbali yathu. Tiyenera kuopa Yehova ndi kutsatira mosamala njira zake. Potero, tingathandizire nawo kukulitsa ndi kukongoletsa paradaiso wauzimu amene panopo ali mumpingo wachikristu wa padziko lonse. Tingadziŵe bwino kwambiri zinthu zokhudza paradaiso ameneyu komanso madalitso ake. Ndipo tikudziŵa kuti m’tsogolomu muli madalitso enanso ambiri. Yoswa anatsogolera Aisrayeli kuwoloka Yordano n’kuloŵa m’dziko lachonde ndiponso losangalatsa kwambiri. Tsopano tili ndi chifukwa chomveka choyembekezera ndi mtima wonse Paradaiso, dziko lokoma lomwe likubwera.
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi chidwi chofuna kudziŵa bwino za mayiko otchulidwa m’Baibulo ndi kuwamvetsetsa?
• Kodi inuyo mwapindula kwambiri podziŵa za malo ati omwe afotokozedwa m’nkhaniyi?
• Kodi ndi mfundo ziti zomwe mwazimvetsa mutaphunzira zambiri zokhudza mmene madera ena amene munachitikira nkhani inayake analili?
[Bokosi/Chithunzi patsamba 14]
‘Onani Dziko Lokoma’
Pamisonkhano yachigawo mu 2003 ndi 2004, Mboni za Yehova zinasangalala kulandira kabuku kakuti ‘Onani Dziko Lokoma.’ Kabuku katsopanoka, kamene kali m’zilankhulo pafupifupi 80, kali ndi mapu okhala ndi mitundu ndi matchati ambirimbiri osonyeza malo osiyanasiyana otchulidwa m’Baibulo, makamaka Dziko Lolonjezedwa, ndipo mapuwo akusonyeza mmene zinthu zinalili panthaŵi zosiyanasiyana.
Nkhani yomwe muli bokosi lino ikutchula mapu ena ndi ena a m’kabukuka posonyeza nambala za masamba m’zilembo zakuda kwambiri, monga [15]. Ngati muli nako kabuku katsopanoka, pezani nthaŵi yoti mukaphunzire bwinobwino n’kudziŵa zinthu za m’kabukuka zimene zingakuthandizeni kudziŵa bwino ndiponso kuzindikira zinthu zambiri za m’Mawu a Mulungu.
(1) Muli mapu ambirimbiri okhala ndi mawu ofotokozera kapena bokosi la mndandanda wofotokozera zizindikiro zapadera zimene zili pamapuwo [18]. (2) Ambiri mwa mapuŵa ali ndi mizera yosonyeza mitunda m’mamailo ndi m’makilomita zimene zingakuthandizeni kudziŵa kukula kwa malo kapena kutalika kwa mitunda [26]. (3) Mapu ambiri m’kabukuka ali ndi chizindikiro cholozera kumpoto, ndipo chizindikirochi chingakuthandizeni kudziŵa kuti kumpoto, kum’mwera, kum’maŵa, kapena kumadzulo n’kuti [19]. (4) Ambiri mwa mapuŵa ali ndi mitundu yosiyanasiyana pofuna kusonyeza kuti malowo ndi okwera motani [12]. (5) M’mphepete mwa mapu ena muli zilembo ndi manambala kuti muthe kudziŵa mzera wa pamapupo umene midzi kapena maina akupezekamo [23]. (6) Pa mlozeramalo wa masamba aŵiri [34-5], mungapezepo nambala zamasamba, zimene zili m’zilembo zakuda kwambiri, ndipo nthaŵi zambiri patsogolo pa nambalazo pali zilembo ndi nambala zosonyeza mizera yomwe mukupezeka malowo, monga E2. Mukagwiritsa ntchito zinthu zimenezi maulendo angapo, mudabwa kuona mmene zikukuthandizirani kudziŵa zinthu zochuluka za m’Baibulo ndiponso kulimvetsa bwino kwambiri.
[Tchati/Mapu pamasamba 16, 17]
TCHATI CHA ZINTHU ZACHILENGEDWE
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
A. Gombe la Nyanja Yaikulu
B. Zidikha Kumadzulo kwa Yordano
1. Chidikha cha Aseri
2. Mkwasa wa Gombe la Doro
3. Mabusa a Saroni
4. Chidikha cha Filistiya
5. Chigwa Chapakati Chochokera Kum’maŵa Kupita Kumadzulo
a. Chidikha cha Megido
b. Chigwa cha Yezreeli
C. Mapiri Kumadzulo kwa Yordano
1. Mapiri a Galileya
2. Mapiri a Karimeli
3. Mapiri a Samariya
4. Shefela (zitunda)
5. Dera la Mapiri la Yuda
6. Chipululu cha Yuda
7. Negebu
8. Chipululu cha Parana
D. Araba (Chigwa cha Mng’alu)
1. Chidikha cha Hula
2. Dera la Nyanja ya Galileya
3. Chigwa cha Yordano
4. Nyanja ya Mchere (Nyanja Yakufa)
5. Araba (kum’mwera kwa Nyanja ya Mchere)
E. Mapiri/Malo Okwera Kum’maŵa kwa Yordano
1. Basana
2. Gileadi
3. Amoni ndi Moabu
4. Dera la M’mapiri la Edomu
F. Mapiri a Lebano
[Mapu]
Phiri la Hermoni
More
Abelemehola
Sukoti
Yogebeha
Beteli
Giligala
Gibeoni
Yerusalemu
Hebroni
Gaza
Beereseba
Sodomu?
Kadesi
[Mapu/Chithunzi patsamba 15]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
KANANI
Megido
GILEADI
Dotana
Sekemu
Beteli (Luzi)
Ai
Yerusalemu (Salemu)
Betelehemu (Efrati)
Mamre
Hebroni (Makipela)
Gerari
Beereseba
Sodomu?
NEGEBU
Rehoboti?
[Mapiri]
Moriya
[Nyanja]
Nyanja ya Mchere
[Matsinje]
Yordano
[Chithunzi]
Abrahamu anayendayenda m’dziko lonseli
[Mapu patsamba 18]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Trowa
SAMATRAKE
Neapoli
Filipi
Amfipoli
Tesalonika
Bereya
Atene
Korinto
Efeso
Mileto
RODE