“Mbiri Yabwino Iyenera Kulalikidwa Choyamba”
“[Mbiri yabwino, NW] iyenera iyambe kulalikidwa kwa anthu amitundu yonse.”—MARKO 13:10.
1. Nchinthu chimodzi chiti chimene chimapangitsa Mboni za Yehova kukhala zosiyana ndi zipembedzo zonse za Chikristu cha Dziko, ndipo nchifukwa ninji?
MWA ONSE amene amadzinenera kukhala Akristu, kokha Mboni za Yehova zimatenga kulalikira kwa mbiri yabwino mosamalitsa. Iwo amapanga gulu lokha mu limene chiwalo chirichonse chimadzimva kukhala ndi thayo laumwini la kufikira mnansi wake pa maziko okhazikika ndi cholinga chofuna kulankhula kwa iye ponena za zifuno za Mulungu. Nchifukwa ninji ichi chiri tero? Chifukwa chakuti Mboni iriyonse imadzimva kuti, monga Mkristu, iyenera kukhala yotsatira mapazi a Kristu. (1 Petro 2:21) Kodi icho chimasonyeza chiyani?
2. Ndimotani mmene anthu ambiri amawonera Yesu Kristu, koma nchiyani chimene chinali ntchito yake yoyambirira padziko lapansi?
2 M’malingaliro mwa ambiri, Yesu Kristu anali kokha munthu yemwe anachita zinthu zabwino. Iye anachiritsa odwala, kudyetsa anjala, ndi kusonyeza chikondi ndi kukoma mtima kwa awo amene anali osoŵa. Koma Yesu anachita zambiri zoposa. Iye choyambirira anali mlaliki wachangu wa mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu. Miyezi yoŵerengeka pambuyo pa ubatizo wake mu mtsinje wa Yordano, Yesu anayamba kulalikira mwapoyera: “Tembenukani mitima, pakuti ufumu wa kumwamba wayandikira.” (Mateyu 4:17) Mbiri ya Marko imanena kuti: “Yesu anadza ku Galileya, nalalikira [mbiri yabwino, NW] ya Mulungu nanena: ‘Nthaŵi yakwanira, ndipo ufumu wa Mulungu wayandikira. Tembenukani mtima, khulupirirani [mbiri yabwino, NW].’”—Marko 1:14, 15.
3, 4. (a) Ngakhale kuti Yesu anachiritsa mtundu uliwonse wa matenda, nchiyani chimene iye anagogomezera mu utumiki wake? (b) Nchifukwa ninji Yesu anatumizidwa? (c) Kodi Yesu anayerekeza ntchito yake yolalikira ndi chiyani, ndipo nchiyani chimene iye anauza ophunzira ake kuchita?
3 Yesu anaitana Petro, Andreya, Yakobo, ndi Yohane kutsatira iye, ndipo timaŵerenga kuti: “Ndipo anayendayenda m’Galileya monse, analikuphunzitsa m’masunagoge mwawo, nalalikira [mbiri yabwino, NW] ya ufumu, nachiritsa nthenda zonse ndi kudwala konse mwa anthu.” Pamene makamu a m’Galileya anayesa kumchedwetsa iye, iye ananena kuti: “Kundiyenera ine ndilalikire [mbiri yabwino, NW] ya ufumu wa Mulungu ku midzi inanso, chifukwa ndinatumidwa kudzatero.” Kenaka iye anapita kukalalikira m’masunagoge a Yudeya.—Mateyu 4:18-23; Luka 4:43, 44.
4 Akubwereranso ku Galileya, Yesu “anayendayenda ku mizinda ndi ku midzi, kulalikira ndi kuwauza [mbiri yabwino, NW] ya ufumu wa Mulungu.” (Luka 8:1) Iye anayerekeza ntchito yake yolalikira ndi kututa ndipo anati: “Zotuta zichulukadi, koma antchito ali oŵerengeka. Chifukwa chake pemphani Mwini zotuta kuti akokose antchito ku kututa kwake.” (Mateyu 9:35-38) Ngakhale pamene makamu sanampatse iye mpumulo, “iye anawalandira, nalankhula nawo za ufumu wa Mulungu, nachiritsa amene anasowa kuchiritsidwa.”—Luka 9:11.
5. Pamene Yesu anatumiza atumwi ake ndi ophunzira ena mu utumiki, ndi malangizo otani amene iye anawapatsa iwo?
5 Zowona, Yesu anachiritsa odwala ndipo pazochitika zina anadyetsa anjala. Koma zoposa izi zonse, iye anali wotanganitsidwa kuwuza anthu ponena za Ufumu wa Mulungu. Iye anafuna kuti otsatira ake achite chofananacho. Pambuyo pa kuphunzitsa atumwi ake, iye anatumiza iwo aŵiri aŵiri kukalalikira, akumanena kuti: “Pamene muli kupita lalikirani kuti, ‘Ufumu wa kumwamba wayandikira.’” (Mateyu 10:7) Luka ananena kuti: “Ndipo anawatuma kukalalikira ufumu wa Mulungu ndi kuchiritsa anthu odwala.” (Luka 9:2) Kwa ophunzira 70, Yesu anaperekanso lamulo la ‘kuchiritsa odwala ndi kuwauza iwo kuti ufumu wa Mulungu wayandikira.’—Luka 10:9.
6. Asanakwere kumwamba, ndi malangizo otani ogwirizana ndi utumiki wawo amene Yesu anapereka kwa atsatiri ake?
6 Asanakwere kumwamba, Yesu anauza atsatiri ake kupitirizabe ntchito yolalikira ndipo ngakhale kuifutukula. Iye anawalamulira iwo kuti: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse . . . ndi kuwaphunzitsa asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” (Mateyu 28:19, 20) M’kuwonjezerapo, iye ananena kuti: “Mudzalandira mphamvu, mzimu woyera utadza pa inu, ndipo mudzakhala mboni zanga m’Yerusalemu, ndi m’Yudeya lonse, ndi m’Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.” (Machitidwe 1:8) Chotero, ponse paŵiri Yesu ndi atumwi ake anapereka chisamaliro choyamba kukulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu.
Ufumu Uyenera Kulalikidwa mu Nthaŵi Yathu
7. Nchiyani chimene Yesu ananena ponena za ntchito yolalikira yodzachitidwa pa “mapeto a dongosolo iri la kachitidwe ka zinthu”?
7 Mu ulosi wake wonena za zochitika zomwe zikafunikira kuchitika pa “mapeto a dongosolo iri la kachitidwe ka zinthu,” Yesu ananena kuti: “Ndipo mbiri yabwino imeneyi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kwa mitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.” (Mateyu 24:3, 14, NW) Kapena, monga mmene chanenedwera pa Marko 13:10, NW: “Mbiri yabwino iyenera iyambe kulalikidwa kwa anthu amitundu yonse.”—Onaninso Chivumbulutso 14:6, 7.
8. (a) Nchiyani chimene mbiri yabwino inaphatikiza m’nthaŵi ya atumwi? (b) Nchiyani chimene uthenga wa mbiri yabwino umaphatikiza lerolino?
8 Mu “masiku otsiriza,” mbiri yabwino ya Ufumu imaphatikizapo zambiri kuposa mmene inachitira m’nthaŵi ya Yesu. Iye analalikira kuti Ufumu wayandikira, kukokera chisamaliro ku nsonga yakuti iye anali pakati pa anthu monga Mesiya ndi Mfumu. (2 Timoteo 3:1; Mateyu 4:17; Luka 17:21) Mbiri yabwino yomwe inalalikidwa ndi Akristu oyambirira inaphatikizapo nkhani ya kuwukitsidwa kwa Yesu ndi kukwera kumwamba, ndipo inalimbikitsa ofatsa kuika chikhulupiriro mu kudza kwa Ufumuwo. (Machitidwe 2:22-24, 32; 3:19-21; 17:2, 3; 26:23; 28:23, 31) Tsopano popeza kuti tafika “kumapeto a dongosolo iri la kachitidwe ka zinthu,” kulalikira kwa mbiri yabwino ya Ufumu kumaphatikizapo uthenga wochititsa chisangalalo wakuti Ufumu unakhazikitsidwa kumwamba.—Chivumbulutso 11:15-18; 12:10.
Kodi Ndani Adzalalikira Mbiri Yabwino?
9. (a) Ndimotani mmene ena angatsutsire kuti kulalikira mbiri yabwino sikuli thayo kaamba ka Akristu onse lerolino? (b) Ndi ndani amene Yehova anagwiritsira ntchito m’nthaŵi zapita kulalikira mawu ake, ndipo nchiyani chimene ichi chikutanthauza kwa ife lerolino?
9 Ndani, lerolino, amene ayenera kugawanamo m’ntchito yolalikira? Mwachiwonekere, Chikristu cha Dziko chimadzimva kuti siliri thayo la aliyense, ndipo chiri chowona kuti pamene Yesu ananena kuti mbiri yabwino idzalalikidwa, iye sanasonyeze mwachindunji ndani amene adzachita ntchitoyo. Ndani enanso, ngakhale kuli tero, amene Yehova akagwiritsira ntchito kaamba ka ntchito yoteroyo koma awo amene amaika chikhulupiriro m’Mawu ake ndi kuyamba kugwiritsira ntchito iwo m’miyoyo yawo? Pamene Yehova anagamulapo m’tsiku la Nowa kuchenjeza dziko loipa la mtundu wa anthu za kudza kwa chiwonongeko, iye anagwiritsira ntchito munthu amene “anayenda ndi Mulungu wowona.” (Genesis 6:9, 13, 14; 2 Petro 2:5) Pamene iye anafuna uthenga wa ulosiwu kuperekedwa kwa Israyeli, iye anatumiza ‘atumiki ake, aneneri.’ (Yeremiya 7:25; Amosi 3:7, 8) Mtundu wodzipereka wa Israyeli unali mtundu wa mboni zake. (Eksodo 19:5, 6; Yesaya 43:10-12) Inde, Yehova anagwiritsira ntchito atumiki ake odzipereka monga mboni zake.
10. Ndimotani mmene chingawonedwere kuchokera ku katchulidwe ka Mateyu 28:19, 20 kuti lamulo la kupanga ophunzira limagwira ntchito kwa Akristu onse?
10 Ena anena kuti lamulo la kupanga ophunzira, loperekedwa pa Mateyu 28:19, 20, linaperekedwa kokha kwa atumwi ndipo chotero silimagwira ntchito kwa Akristu mwachisawawa. Koma dziŵani chimene Yesu ananena kuti: “Chifukwa chake mukani phunzitsani anthu amitundu yonse . . . kuwaphunzitsa iwo asunge zinthu zimene ndakulamulirani.” Atsatiri a Yesu anayenera kuphunzitsa ophunzira achatsopano kusunga zinthu zonse zimene Yesu anawalamulira. Ndipo chimodzi cha zinthu zimene iye anawalamulira chinali ‘kumuka ndi kupanga ophunzira.’ Ndithudi, ophunzira onse atsopano anayenera kuphunzitsidwa kusunga lamulo lapadera limenelinso.
11. (a) Ndi thayo lotani limene linakhala pa mpingo Wachikristu m’zana loyamba? (b) Nchiyani chimene chiri choyenera kaamba ka wina kuti apulumutsidwe, ndipo nchiyani chimene ichi chimaphatikizapo?
11 Mpingo Wachikristu wa m’zana loyamba unatchedwa ‘anthu a Mulungu, kotero kuti akalalikire zoposa za iye amene anawaitana atuluke mumdima, kulowa kuwunika kwake kodabwitsa.’ (1 Petro 2:9) Ziwalo zake mokangalika zinachitira umboni ku Ufumu wa Mulungu. (Machitidwe 8:4, 12) Onse “oyera mtima”, Akristu odzozedwa, mu Roma anauzidwa kuti “ndi mkamwa avomereza kutengapo chipulumutso” ndikuti “amene aliyense adzaitana pa dzina la [Yehova, NW] adzapulumuka.” (Aroma 1:7; 10:9, 10, 13) Kulalikira kwapoyera kaamba ka chipulumutso kumeneku, kopangidwa panthaŵi ya ubatizo wa wina, kumaphatikizanso kulalikira poyera kwa mbiri yabwino ya Ufumu wa Yehova.
12, 13. (a) Nchiyani chimene “kuvomereza [poyera, NW] chiyembekezo chathu” kotchulidwa pa Ahebri 10:23 kumaphatikiza? (b) Ndimotani mmene Masalmo 96 amasonyezera chifuno cha kulalikira poyera kunja kwa mpingo, ndipo ndimotani mmene Chivumbulutso 7:9, 10 chimachirikizira ichi?
12 Mtumwi Paulo analembera Akristu a ku Ahebri kuti: “Tigwiritse chivomerezo chosagwedera cha chiyembekezo chathu, pakuti wolonjezayo ali wokhulupirika.” (Ahebri 10:23) Chivomerezo cha poyera chimenechi sichiri ndi malire kokha ku misonkhano ya mpingo. (Masalmo 40:9, 10) Pa Masalmo 96:2, 3, 10 timawona mowonekera bwino lamulo la ulosi la kulalikira kunja kwa mpingo, kwa amitundu, m’mawu awa: “Lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku. Fotokozerani ulemerero wake mwa amitundu. Zodabwitsa zake mwa mitundu yonse ya anthu. Nenani mwa amitundu: ‘Yehova achita ufumu.’” Ndithudi, pa Mateyu 28:19, 20 ndi Machitidwe 1:8, Yesu analamulira Akristu kulalikira kwa amitundu.
13 Kulalikira kwapoyera kumeneku kukulozeredwa m’mawu owonjezereka a Paulo kwa Akristu odzozedwa ku Ahebri: “Potero mwa iye tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza [poyera, NW] dzina lake.” (Ahebri 13:15) M’bukhu la Chivumbulutso, “khamu lalikulu,” losonkhanitsidwa kuchokera ku mitundu yonse, likuwonedwanso likuimba ndi mawu a akulu: “Chipulumutso kwa Mulungu wathu wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.” (Chivumbulutso 7:9, 10) Chotero, m’nthaŵi ino yamapeto a dongosolo iri la kachitidwe ka zinthu, kulalikira mbiri yabwino kukuchitidwa ndi Mboni zodzipereka za Yehova, otsalira a abale auzimu a Kristu ndi anzawo onga nkhosa omwe amapanga “khamu lalikulu.” Koma kodi ndimotani kwenikweni mmene iwo ayenera kuchitira ntchitoyi?
“Poyera ndi Kunyumba ndi Nyumba”
14. Ndi kuti kumene Yesu anapangira ulalikira wake, ndipo ndi prinsipulo lotani limene tingaphunzire kuchokera ku ichi?
14 Yesu analalikira mwachindunji kwa anthu. Timaŵerenga, mwachitsanzo, kuti iye analalikira m’masunagoge. Nchifukwa ninji? Chifukwa chakuti anthu anasonkhana kumeneko pa Sabata ndi kumvetsera ku kuŵerengedwa ndi kukambitsirana kwa Malemba. (Mateyu 4:23; Luka 4:15-21) Yesu analalikiranso kwa anthu mphepete mwa msewu, mphepete mwa nyanja, mphepete mwa phiri, pa chitsime kunja kwa mzinda, ndi m’nyumba. Kulikonse kumene kunali anthu, Yesu analalikira kwa iwo.—Mateyu 5:1, 2; Marko 1:29-34; 2:1-4, 13; 3:19; 4:1, 2; Luka 5:1-3; 9:57-60; Yohane 4:4-26.
15. (a) Ndi malangizo otani amene Yesu anapereka kwa ophunzira ake pamene iye anawatumiza kunja kukalalikira? (b) Ndimotani mmene ochitira ndemanga Baibulo ena alongosolera ichi?
15 Pamene Yesu anatumiza ophunzira ake kukalalikira, iye anawatumizanso mwachindunji kwa anthu. Ichi chikuwonedwa m’malangizo ake olembedwa pa Mateyu 10:1-15, 40-42. Mu versi 11 iye ananena kuti: “Ndipo m’mzinda uli wonse, kapena m’mudzi, mukalowamo, mufunitsitse amene ali woyenera momwemo, ndipo bakhalani komweko kufikira mutulukamo.” The Jerusalem Bible imaika versi iri motere: “Funsani kaamba ka winawake amene ali wokhulupirika,” ngati kuti ophunzirawo anafunikira kufunsa anthu ena otchuka kapena odziŵika m’mudziwo kupeza ndani amene anali ndi kukambidwa kwabwino ndipo chotero anali oyenera uthengawo. (Onaninso Weymouth ndi King James Version.) Ndipo aka ndi kalongosoledwe kamene ochitira ndemanga a Baibulo ena amapereka ku versi 11.
16. Ndi kawonedwe kokhala ndi cholinga kokulirapo kotani ka mawu a Yesu pa Mateyu 10:11 kamene kamasonyeza mmene atumwi anayenera kufunafuna oyenerera?
16 Chiyenera kusungidwa m’maganizo, ngakhale kuli tero, kuti kwa mbali yaikulu, ophunzira maphunziro a zaumulungu a Chikristu cha Dziko samapita kunyumba ndi nyumba, ndipo ochitira ndemanga Baibulo ambiri amayedzamira ku kutembenuza Malemba m’lingaliro la chokumana nacho chawo chenicheni. Kalingaliridwe kokhala ndi cholinga ka malangizo a Yesu kamasonyeza kuti iye anali kulankhula ponena za kufunafuna anthu kwa ophunzira ake mwaumwini, kaya kuchokera kunyumba ndi nyumba kapena mwapoyera, ndipo kupereka kwa iwo uthenga wa Ufumu. (Mateyu 10:7) Chivomerezo chawo chikasonyeza kaya iwo anali oyenera kapena ayi.—Mateyu 10:12-15.
17. Nchiyani chimene chimatsimikizira kuti ophunzira a Yesu sanali kokha kuitanira pa anthu oyenerera kuzikidwa pa kuyamikiridwa kapena kuikidwa?
17 Ichi chikuwoneka m’mawu a Yesu pa Mateyu 10:14: “Ndipo yemwe sadzakulandirani inu, kapena kusamva mawu anu, pamene mulikutuluka m’nyumbayo, kapena m’mudzimo, sansani fumbi m’mapazi anu.” Yesu anali kulankhula ponena za ophunzira ake akupanga maulendo osaitanidwa pa anthu kulalikira kwa iwo. Zowona, iwo akayeneranso kulandira malo ogona ndi mmodzi wa eninyumba yemwe akavomereza ku uthengawo. (Mateyu 10:11) Koma chinthu chachikulu chinali ntchito yolalikira. Pa Luka 9:6 chanenedwa kuti: “Ndipo iwo anatuluka, napita m’midzi m’midzi, ndi kulalikira uthenga wabwino, ndi kuchiritsa ponse.” (Onaninso Luka 10:8, 9.) Oyenerera omwe analandira ophunzirawo m’nyumba zawo monga aneneri, mwinamwake kuwapatsa iwo “chikho cha madzi ozizira” kapena ngakhale malo ogona, sadakataya mphoto yawo. Iwo adakamva uthenga wa Ufumu.—Mateyu 10:40-42.
18, 19. (a) Mogwirizana ndi Machitidwe 5:42, ndimotani mmene Akristu oyambirira anachitira ntchito yawo yolalikira? (b) Ndimotani mmene mawu a Paulo pa Machitidwe 20:20, 21 amasonyezera kuti iye anali kulankhula ponena za utumiki kwa osakhulupirira, osati ntchito ya mkati ya ubusa?
18 Pambuyo pa kupangidwa kwa mpingo Wachikristu, timaŵerenga ponena za atumwi kuti: “Ndipo masiku onse m’kachisi ndi [ku nyumba ndi nyumba, NW] sanaleka kuphunzitsa ndi kulalikira [mbiri yabwino, NW] ya Kristu Yesu.” (Machitidwe 5:42; onani Reference Bible, mawu a m’munsi.) Mawu a matembenuzidwe a Chigriki a “kuchokera ku nyumba ndi nyumba” ali kat’ oiʹkon. Pano ka·taʹ liri lingaliro la kugawira. Chotero, chinganenedwe kuti kulalikira kwa ophunzirawo kunagawiridwa kuchokera ku nyumba ndi nyumba. Iwo sanali kupanga kokha maulendo amayanjano okonzekeredweratu. Kugwiritsira ntchito kofananako kwa ka·taʹ kukupezeka pa Luka 8:1 mu kalongosoledwe kakuti “kuchokera ku mzinda ndi mzinda ndi kuchokera ku mudzi ndi mudzi.”
19 Kalongosoledwe kofananako mu pulura, kat’ oiʹkous, kakugwiritsiridwa ntchito ndi mtumwi Paulo pa Machitidwe 20:20. Pamenepo iye ananena kuti: “Sindinakubisirani inu . . . kukuphunzitsani pabwalo ndi m’nyumba m’nyumba.” Kalongosoledwe kakuti “m’nyumba ndi m’nyumba” kakugwiritsiridwa ntchito monga “m’nyumba zanu” m’matembenuzidwe ena. Chotero ochitira ndemanga ena a Baibulo a Chikristu cha Dziko amanena kuti Paulo pano anali kulozera ku maulendo a ubusa m’nyumba za okhulupirira. Koma mawu otsatira a Paulo amasonyeza kuti iye anali kulankhula ponena za utumiki kwa osakhulupirira, popeza iye akunena kuti: “Ndi kuchitira umboni Ayuda ndi Ahelene wa kutembenuza mtima kulinga kwa Mulungu, ndi chikhulupiriro cholinga kwa Ambuye wathu Yesu Kristu.”—Machitidwe 20:21.
20. (a) Ndi kuutali wotani kumene Mboni za Yehova zalalikira mbiri yabwino ya Ufumu m’nthaŵi yathu? (b) Ndimotani mmene ena angawonere nkhani ya kupitiriza kulalikira?
20 Njira iyi ya kufikira anthu iyenera chotero kugwiritsiridwa ntchito m’nthaŵi yathu pamene “mbiri yabwino ya ufumu” iyenera “kulalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kwa mitundu yonse.” (Mateyu 24:14, NW) Kwa zaka zoposa 65, Mboni za Yehova zakhala zikulalikira mwachangu mbiri yabwino ya Ufumu wokhazikitsidwa wa Mulungu mwapoyera ndi kuchokera kunyumba ndi nyumba—tsopano m’maiko 210. Ndi umboni waukulu chotani nanga womwe ukukwaniritsidwa! Ndipo ichi mosasamala kanthu za nsonga yakuti anthu ambiri lerolino amamva uthenga “popanda chivomerezo,” ena ngakhale ndi kuipidwa. (Mateyu 13:15) Nchifukwa ninji Mboni za Yehova zimawumirira kulalikira m’malo kumene anthu amakana kumvetsera kapena ngakhale kuwatsutsa iwo? Funso iri lidzatengedwa m’nkhani yotsatira.
Kodi Mukayankha Motani?
◻ Nchiyani chimene Malemba amasonyeza kuti chinapanga mbali ya utumiki wa Yesu?
◻ Ndi zitsogozo zotani zimene zinaperekedwa kwa atumwi mu utumiki wawo?
◻ Ndi ntchito yotani imene iyenera kuchitidwa m’nthaŵi yathu, ndipo nchifukwa ninji?
◻ Ndi ndani amene Yehova adzagwiritsira ntchito kulalikira mbiri yabwino m’tsiku lathu?
◻ Ndi kuti ndipo ndimotani mmene ntchito yolalikira ifunikira kukwaniritsidwira?