Tizikhulupirira Khristu Yemwe Ndi Mtsogoleri Wathu
“Mtsogoleri wanu ndi mmodzi, Khristu.”—MAT. 23:10.
1, 2. Kodi Yoswa anali ndi ntchito yaikulu iti Mose atamwalira?
YEHOVA anauza Yoswa kuti: “Mose mtumiki wanga wamwalira. Tsopano konzeka limodzi ndi anthu onsewa, kuti muwoloke Yorodanoyu ndi kulowa m’dziko limene ndikulipereka kwa ana a Isiraeli.” (Yos. 1:1, 2) Kumeneku kunali kusintha kwakukulu chifukwa Yoswa anali atakhala mtumiki wa Mose kwa zaka pafupifupi 40.
2 Popeza Mose anatsogolera Aisiraeli kwa zaka zambiri, Yoswa ayenera kuti ankadzifunsa ngati anthuwo angamamumvere monga mtsogoleri wawo. (Deut. 34:8, 10-12) Ponena za Yoswa 1:1, 2, buku lina lofotokoza za Baibulo limanena kuti kuyambira kale komanso masiku ano, mtsogoleri akasintha zinthu zimasokonekera pa nkhani ya chitetezo cha dziko.
3, 4. Kodi tikudziwa bwanji kuti Yoswa sanalakwitse pokhulupirira Mulungu, nanga tingadzifunse funso liti?
3 Yoswa anali ndi zifukwa zomveka zomuchititsa kukhala ndi mantha. Koma patangopita masiku ochepa, anachita zinthu molimba mtima. (Yos. 1:9-11) Iye ankakhulupirira kwambiri Mulungu ndipo sanagwiritsidwe mwala. Baibulo limasonyeza kuti Yehova anatsogolera Yoswa ndi mtundu wa Aisiraeli pogwiritsa ntchito mngelo. Pali zifukwa zomveka zokhulupirira kuti mngelo ameneyu anali Mawu, yemwe ndi Mwana wa Mulungu woyamba kubadwa.—Eks. 23:20-23; Yoh. 1:1.
4 Yehova anathandiza Aisiraeli kuti azolowere kutsogoleredwa ndi Yoswa m’malo mwa Mose. Masiku anonso zinthu zambiri zikusintha m’gulu la Yehova ndipo tingamadzifunse kuti, ‘Popeza gululi likupita patsogolo kwambiri, kodi tili ndi zifukwa zokhulupirira kuti Yesu angatitsogolere bwino?’ (Werengani Mateyu 23:10.) Kuti tipeze yankho, tiyeni tikambirane zimene Yehova anachita potsogolera anthu ake m’mbuyomu.
ANATSOGOLERA ANTHU A MULUNGU KULOWA M’DZIKO LA KANANI
5. Kodi Yoswa anakumana ndi ndani atatsala pang’ono kufika ku Yeriko? (Onani chithunzi choyambirira.)
5 Aisiraeli atangowoloka mtsinje wa Yorodano, Yoswa anakumana ndi zinthu zosayembekezereka. Atatsala pang’ono kufika ku Yeriko anakumana ndi munthu atanyamula lupanga. Munthuyo anali wachilendo ndipo Yoswa anamufunsa kuti: “Kodi uli kumbali yathu kapena kumbali ya adani athu?” Yoswa anadabwa pamene msilikaliyu ananena kuti anali ‘kalonga wa gulu lankhondo la Yehova.’ (Werengani Yoswa 5:13-15.) Ngakhale kuti mavesi ena a m’Baibulo amanena kuti Yehova ankalankhula mwachindunji ndi Yoswa, Mulungu ayenera kuti ankalankhula naye pogwiritsa ntchito mngelo ngati mmene ankachitira kale.—Eks. 3:2-4; Yos. 4:1, 15; 5:2, 9; Mac. 7:38; Agal. 3:19.
6-8. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti malangizo ena amene Yehova anapereka akanaoneka ngati osathandiza? (b) N’chiyani chikusonyeza kuti malangizowo anali abwino komanso a pa nthawi yake? (Onaninso mawu am’munsi.)
6 Mngeloyo anapatsa Yoswa malangizo omveka bwino a mmene angagonjetsere mzinda wa Yeriko. Poyamba, malangizo ena akanaoneka ngati osathandiza. Mwachitsanzo, Yehova analamula kuti amuna onse adulidwe ndipo izi zikanachititsa kuti amunawo asathe kuchita chilichonse kwa masiku angapo. Ndiye funso n’kumati, ‘Kodi imeneyi inalidi nthawi yabwino yoti asilikali adulidwe?’—Gen. 34:24, 25; Yos. 5:2, 8.
7 N’kutheka kuti asilikaliwo ankadzifunsa kuti, kodi adani atabwera panopa tingateteze bwanji mabanja athu? Koma kenako anangomva kuti “mzinda wa Yeriko unatsekedwa mwamphamvu chifukwa cha ana a Isiraeli.” (Yos. 6:1) Atangomva zimenezi ayenera kuti anazindikira kuti palibe chifukwa chokayikirira malangizo alionse amene Yehova angawapatse.
8 Aisiraeli analangizidwanso kuti asaukire mzinda wa Yeriko koma azingouzungulira kamodzi pa tsiku kwa masiku 6 ndipo tsiku la 7 auzungulire maulendo 7. Asilikali ena ayenera kuti ankaganiza kuti, ‘Uku ndiye n’kungotaya nthawi chabe komanso kungodzitopetsatu.’ Koma Mtsogoleri wosaoneka wa Aisiraeli ankadziwa zimene akuchita. Kutsatira malangizo a Mulunguwa kunawathandiza kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba komanso kuti asamenyane ndi asilikali amphamvu a ku Yeriko.—Yos. 6:2-5; Aheb. 11:30.a
9. N’chifukwa chiyani tiyenera kutsatira malangizo amene gulu limatipatsa? Perekani chitsanzo.
9 Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani imeneyi? Nthawi zina sitingamvetse chifukwa chimene gulu likuchitira zinthu zinazake. Mwachitsanzo, mwina poyamba tinkadabwa kuti n’chifukwa chiyani gulu likulimbikitsa kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono kumisonkhano, mu utumiki komanso pophunzira patokha. Koma panopa ambirife tazindikira ubwino wake. Tikaona ubwino wa zinthu zimene poyamba sitinkazimvetsa, chikhulupiriro chathu chimalimba ndipo timakhala ogwirizana.
YESU KHRISTU ANKATSOGOLERA AKHRISTU OYAMBIRIRA
10. Kodi ndani anachititsa kuti pakhale msonkhano wa bungwe lolamulira ku Yerusalemu?
10 Patapita zaka 13 kuchokera pamene Koneliyo anakhala Mkhristu, Akhristu ena achiyuda ankalimbikitsabe mdulidwe. (Mac. 15:1, 2) Anthu atasiyana maganizo pa nkhaniyi ku Antiokeya, Paulo anatumidwa kuti akafunse malangizo ku bungwe lolamulira ku Yerusalemu. Koma kodi nzeru yoti apite ku Yerusalemuko inachokera kuti? Paulo ananena kuti “Ndinapita kumeneko chifukwa ndinauzidwa m’masomphenya kuti ndipiteko.” Apa zikuonekeratu kuti Khristu anatsogolera zinthu kuti nkhaniyo ithetsedwe ndi bungwe lolamulira.—Agal. 2:1-3.
11. (a) Kodi Akhristu achiyuda ankaiona bwanji nkhani ya mdulidwe? (b) Kodi Paulo anasonyeza bwanji kuti ankafunitsitsa kuchita zinthu mogwirizana ndi akulu a ku Yerusalemu? (Onaninso mawu am’munsi.)
11 Khristu anatsogolera bungwe lolamulira kuti lipereke malangizo akuti sizinali zofunika kuti Akhristu azidulidwa. (Mac. 15:19, 20) Koma kwa zaka zambiri pambuyo posankha zimenezi, Akhristu achiyuda ankapitiriza kuonetsetsa kuti ana awo akudulidwa. Akulu a ku Yerusalemu atadziwa kuti panali mphekesera yoti Paulo sankatsatira Chilamulo cha Mose, iwo anamupatsa malangizo amene iye sankawayembekezera.b (Mac. 21:20-26) Iwo anamuuza kuti apite ndi anthu 4 kukachisi n’cholinga choti anthu aziona kuti Paulo ‘ankasunga chilamulo.’ Paulo akanatha kuona kuti malangizowo sanali anzeru chifukwa choti vuto linagona pa Akhristu achiyudawo amene sankaona moyenera nkhani ya mdulidwe. Koma iye anachita zimene anamuuzazo. Ankadziwa kuti akuluwo ankafuna kuti Akhristu onse azigwirizana ndipo anadzichepetsa n’kutsatira malangizo awowo. Koma tikhoza kudzifunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani Yesu analola kuti nkhani ya mdulidweyi ipitirirebe kwa zaka zambiri ngakhale kuti imfa yake inathetsa Chilamulo cha Mose?’—Akol. 2:13, 14.
12. N’chifukwa chiyani mwina Khristu analola kuti nkhani ya mdulidwe isathetsedwe msanga?
12 Anthu ena zimawatengera nthawi kuti azolowere kusintha kwa zinthu. Mwachitsanzo, Akhristu achiyuda ankafunika nthawi yaitali ndithu kuti ayambe kuona zinthu moyenera. (Yoh. 16:12) Ena zinawavuta kuti asiye kuona mdulidwe ngati chizindikiro choti anali pa ubwenzi wapadera ndi Mulungu. (Gen. 17:9-12) Pomwe ena amene ankakhala m’dera lomwe Ayuda ambiri ankakhala ankaopa kuti azizunzidwa ngati atamachita zinthu mosiyana ndi Ayudawo. (Agal. 6:12) Koma patapita nthawi, Khristu anapereka malangizo ena pogwiritsa ntchito Paulo kuti alembe makalata.—Aroma 2:28, 29; Agal. 3:23-25.
KHRISTU AKUTSOGOLERABE MPINGO WAKE
13. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tiziyamikira zimene Khristu amachita potitsogolera masiku ano?
13 Ngati tikuvutika kumvetsa chifukwa chimene zinthu zina zasinthira m’gulu lathu, tingachite bwino kuganizira mmene Khristu ankachitira zinthu m’mbuyomu potsogolera anthu. Munthawi ya Yoswa komanso ya Akhristu oyambirira, Khristu ankapereka malangizo anzeru omwe ankateteza gulu la Mulungu, kulimbitsa chikhulupiriro cha anthu ake komanso kuwathandiza kuti azigwirizana.—Aheb. 13:8.
14-16. Kodi malangizo amene “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amapereka amasonyeza bwanji kuti Khristu amatifunira zabwino potumikira Mulungu?
14 Malangizo a pa nthawi yake amene “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amapereka amasonyeza kuti Yesu amatifunira zabwino potumikira Mulungu. (Mat. 24:45) M’bale wina dzina lake Marc yemwe ali ndi ana 4 anati: “Satana akusokoneza mabanja n’cholinga choti afooketse mipingo. Ndiye masiku ano timalimbikitsidwa kwambiri kuti tizichita kulambira kwa pabanja. Apa zikuonekeratu kuti mitu ya mabanja ikulangizidwa kuti iziteteza mabanja awo.”
15 Tikamaona kuti Khristu akutitsogolera timazindikira kuti amafuna kuti tisabwerere m’mbuyo potumikira Mulungu. M’bale wina yemwe ndi mkulu dzina lake Patrick anati: “Poyamba, anthu ena sankasangalala ndi malangizo oti tizikonzekera utumiki m’timagulu tathu Loweruka ndi Lamlungu. Koma malangizo amenewa anasonyeza bwino khalidwe la Yesu loganizira anthu ofooka kapena amanyazi. Timaguluti tathandiza abale ndi alongo oterewa kuti ayambe kuona kuti ndi ofunika mumpingo ndipo ayamba kuchita zambiri potumikira Yehova.”
16 Kuwonjezera pa kutisamalira mwauzimu, Khristu amatithandiza kugwira mwakhama ntchito yofunika kwambiri padziko lonse. (Werengani Maliko 13:10.) M’bale wina dzina lake André, yemwe waikidwa posachedwapa kukhala mkulu, nthawi zonse amakhala tcheru kuti azindikire malangizo atsopano amene gulu la Mulungu lapereka. Iye anati: “Malangizo oti achepetse anthu amene amagwira ntchito kumaofesi a nthambi amatikumbutsa kuti nthawi imene yatsala ndi yochepa ndipo tiyenera kugwira mwakhama ntchito yolalikira.”
TIZITSATIRA KHRISTU MOKHULUPIRIKA
17, 18. Kodi kuganizira ubwino wa zinthu zimene zasintha m’gulu kungatithandize bwanji?
17 Tikaganizira zimene Mfumu yathu Yesu Khristu akuchita potitsogolera timadziwiratu kuti iye akuganizira kwambiri zam’tsogolo. Choncho tizisangalala ndi madalitso amene timapeza chifukwa cha zinthu zimene zasintha m’gulu la Yehova. Mukhoza kulimbikitsidwa mukamakambirana pa kulambira kwa pabanja ubwino umene timapeza chifukwa cha zimene zasinthidwa pamisonkhano yathu kapena mu utumiki.
18 Tikazindikira cholinga cha malangizo amene timapatsidwa m’gulu la Yehova komanso ubwino wake, tikhoza kuwatsatira mosavuta. Mwachitsanzo, chiwerengero cha mabuku amene amasindikizidwa chinachepetsedwa chifukwa tikugwiritsa ntchito zipangizo zamakono. Zimenezi zathandiza kuti gulu lisamawononge ndalama zambiri komanso kuti ntchito ya Ufumu iziyenda bwino padziko lonse. Tikamakumbukira zimenezi tikhoza kuyamba kugwiritsa ntchito kwambiri zipangizo zamakono pophunzira kapena mu utumiki ngati n’zotheka. Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti tikuyesetsa kutsatira Khristu pa nkhani yogwiritsa ntchito mwanzeru zinthu za gulu.
19. N’chifukwa chiyani tiyenera kutsatira Khristu mokhulupirika?
19 Tikamatsatira Khristu mokhulupirika timalimbitsa chikhulupiriro cha anzathu ndipo timakhala ogwirizana. Pa nkhani ya kuchepetsa anthu amene amatumikira pa Beteli, André anati: “Mtima wabwino umene anthu omwe anachoka pa Beteli n’kuyamba utumiki wina anasonyeza, umandithandiza kulemekeza ndiponso kukhulupirira kwambiri gululi. Iwo amayenda ndi galeta la Yehova chifukwa amasangalala ndi utumiki uliwonse umene apatsidwa.”
TIZIKHULUPIRIRA MTSOGOLERI WATHU
20, 21. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira Khristu, yemwe ndi Mtsogoleri wathu? (b) Kodi tidzakambirana funso liti munkhani yotsatira?
20 Posachedwapa, Mtsogoleri wathu Yesu Khristu ‘adzapambana pa nkhondo yolimbana’ ndi adani ake ndipo adzachita zinthu zodabwitsa. (Chiv. 6:2; Sal. 45:4) Koma panopa iye akukonzekeretsa anthu a Mulungu kuti adzagwire ntchito yaikulu yophunzitsa ndiponso yomanga imene idzachitike m’tsogolomu anthu akamadzaukitsidwa.
21 Yesu Khristu, yemwe ndi Mfumu yathu, adzatitsogolera kulowa m’dziko latsopano ngati titapitiriza kumukhulupirira ngakhale pamene zinthu zikusintha. (Werengani Salimo 46:1-3.) Nthawi zina timavutika kuvomereza zinthu zikasintha, makamaka ngati zasintha mosayembekezereka pa moyo wathu. Zikatere, kodi tingatani kuti tikhalebe ndi mtendere wamumtima komanso tizikhulupirira kwambiri Yehova? Tidzakambirana funso limeneli munkhani yotsatira.
a Anthu ofufuza zinthu zakale anapeza zokolola zambiri zimene zinakwiririka pamalo amene panali mzinda wa Yeriko ndipo izi zikusonyeza kuti mzindawu sunazunguliridwe ndi Aisiraeli kwa nthawi yaitali moti chakudya sichinathe mumzindawo. Popeza Aisiraeli sanaloledwe kulanda zinthu mumzinda wa Yeriko, nthawi imene anagonjetsa mzindawu inali yabwino chifukwa m’minda munali chakudya chambirimbiri.—Yos. 5:10-12.
b Onani bokosi lakuti “Paulo Anakumana ndi Chiyeso Modzichepetsa” mu Nsanja ya Olonda ya March 15, 2003, tsamba 24.