-
“Limba Mtima”‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
-
-
10. Kodi Paulo ananamiziridwa milandu yoopsa iti?
10 Ku Kaisareya, Paulo ‘ankamusunga m’nyumba ya Mfumu Herode n’kumamulondera’ podikira kuti anthu amene ankamuimba mlandu afike kuchokera ku Yerusalemu. (Mac. 23:35) Patatha masiku 5, kunafika Mkulu wa Ansembe Hananiya, munthu wina wodziwa kulankhula dzina lake Teritulo komanso akulu ena. Teritulo anayamba n’kuyamikira Felike chifukwa cha zimene ankachitira Ayuda, mwina pofuna kumukopa kuti awakondere pa mlanduwo.b Kenako polankhula za mlandu wa Paulo, Teritulo ananena kuti: “Munthu uyu ndi wovutitsa kwabasi, ndipo akuyambitsa zoukira boma pakati pa Ayuda padziko lonse. Ndiponso ndi mtsogoleri wa gulu lampatuko la anthu a ku Nazareti. Komanso iyeyu ankafuna kudetsa kachisi ndipo tinamugwira.” Ayuda ena “analowerera ndipo ankanena motsimikiza kuti zimenezo n’zoona.” (Mac. 24:5, 6, 9) Kuyambitsa kuukira boma, kutsogolera gulu loopsa lampatuko ndiponso kudetsa kachisi inali milandu yoopsa kwambiri ndipo anthu opalamula milandu imeneyi ankatha kuphedwa.
-
-
“Limba Mtima”‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
-
-
b Teritulo anayamikira Felike kuti anabweretsa “mtendere wambiri” m’dziko lawo. Koma zoona zake zinali zakuti pa nthawi imene Felike anali bwanamkubwa, ku Yudeya kunalibe mtendere poyerekezera ndi nthawi imene abwanamkubwa ena ankalamulira derali. Ndipo mtendere unapitirizabe kusokonekera mpaka pamene Ayuda anagalukira boma la Roma. Komanso iye ananama kwambiri ponena kuti Ayuda ‘ankayamikira kwambiri’ Felike chifukwa anasintha zinthu. Zoona zake zinali zakuti Ayuda ambiri ankadana naye chifukwa chowapondereza komanso chifukwa chopha mwankhanza Ayuda amene anaukira boma.—Mac. 24:2, 3.
-