Kodi Makolo Akale Omwe Anamwalira Adzakhalanso ndi Moyo?
ZAKA zapitazo, m’nyuzipepala ina ya ku Korea munali mutu wa nkhani umene unakopa chidwi cha anthu ambiri. Unali wakuti: “Kodi Shim Cheong Anakawotchedwa Kumoto Chifukwa Choti Sankamudziwa Yesu?”
Anthu ambiri anali ndi chidwi chofuna kuwerenga nkhaniyi chifukwa ku Korea kuli nthano yonena za Shim Cheong, yemwe anali mtsikana wabwino kwambiri. Mtsikanayu analolera kufa kuti athandize bambo ake omwe anali osaona. Kwa zaka zambiri, anthu akhala akumutaira kamtengo mtsikana ameneyu. Ndipotu makolo a ku Korea amauza ana awo aakazi kuti atengere chitsanzo cha Shim Cheong.
Anthu ambiri amaona kuti mfundo yoti mtsikanayu anakalangidwa kumoto chifukwa choti sanali Mkhristu wobatizidwa, ndi yosamveka. Iwo amaonanso kuti kuchita zimenezi kungakhale kupanda chilungamo. Komanso nthanoyo imasonyeza kuti nkhaniyi inachitika kalekale, uthenga wokhudza Yesu usanafike n’komwe m’mudzi umene mtsikanayu ankakhala.
Nkhani ya m’nyuzipepala ija inanenanso zimene mtsogoleri wina wa chipembedzo ananena atafunsidwa za nkhaniyi. Anafunsidwa kuti afotokoze ngati zili zoona kuti anthu amene amamwalira asanapeze mwayi wophunzira za Yesu, amakawotchedwa kumoto. Iye anayankha kuti: “Sitikudziwa, koma tikungoganiza kuti mwina pali njira inayake imene Mulungu anakonza [yokhudza anthu amenewa].”
KODI MUNTHU ALIYENSE AMENE SANABATIZIDWE SANGAPULUMUKE?
Buku lina la Akatolika limanena kuti: “Munthu wosabatizidwa sangapulumuke. Monga mmene Yesu ananenera, ngati munthu sanabadwe mwa madzi ndi mzimu woyera, sangathe kulowa mu ufumu wa Mulungu [Yoh. 3:5].” (The New Catholic Encyclopedia) Chifukwa cha zimenezi ena amakhulupirira kuti anthu amene anamwalira asanabatizidwe, anaponyedwa kumoto kapena amazunzika m’njira inayake.
Koma anthu ambiri amaona kuti chiphunzitso chimenechi n’chosamveka. Pali anthu ambiri amene anamwalira asakudziwa za Baibulo. Kodi anthu amenewa ndi oyeneradi kukazunzidwa kumoto? Kodi Baibulo limanena zotani pa nkhani imeneyi?
BAIBULO LIMAPHUNZITSA KUTI CHIYEMBEKEZO CHILIPO
Baibulo limasonyeza kuti Mulungu sadzaimba mlandu anthu chifukwa cha machimo amene anachita pa nthawi imene sankadziwa zofuna zake. Lemba la Machitidwe 17:30 limatsimikizira mfundo imeneyi. Limati: “Mulungu analekerera nthawi ya kusadziwa koteroko.” Ndiye kodi Baibulo limaphunzitsa kuti pali chiyembekezo chotani kwa anthu amene anamwalira asanapeze mwayi wophunzira za Mulungu?
Yankho la funsoli likupezeka pa zimene Yesu anauza chigawenga chomwe chinapachikidwa pafupi naye. Munthuyu anauza Yesu kuti: “Mukandikumbukire mukakalowa mu ufumu wanu.” Kodi Yesu anamuyankha bwanji? Anati: “Ndithu ndikukuuza lero, iwe udzakhala ndi ine m’Paradaiso.”—Luka 23:39-43.
Kodi pamenepa Yesu ankatanthauza kuti munthuyo apita kumwamba? Ayi. Munthuyu sakanapita kumwamba chifukwa ‘sanabadwenso’ mwa madzi ndi mzimu. (Yohane 3:3-6) Choncho pamenepa Yesu ankalonjeza munthuyu kuti adzakhalanso ndi moyo “m’Paradaiso.” Popeza munthuyu anali Myuda, ankadziwa bwino za Paradaiso wotchulidwa m’buku la Genesis, yemwe anali m’munda wa Edeni. (Genesis 2:8) Lonjezo la Yesuli, linasonyeza kuti dzikoli lidzakhalanso Paradaiso ndipo munthuyo adzaukitsidwa n’kumakhala m’Paradaisomo.
Ndipotu Baibulo limalonjeza kuti, “kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.” (Machitidwe 24:15) “Osalungama” amene akutchulidwa palembali, ndi anthu amene anamwalira, koma sankachita zofuna za Mulungu chifukwa choti sankadziwa zimene Mulunguyo amafuna. M’Paradaiso, Yesu adzaukitsa chigawenga chija komanso anthu ambirimbiri amene ali m’gulu la anthu osalungama. Ndiyeno anthu amenewa adzaphunzitsidwa zimene Mulungu amafuna kuti apatsidwe mwayi wosankha kumutumikira kapena ayi. Akadzayamba kuchita zimene Mulungu amafuna, adzasonyeza kuti amamukonda ndipo akufuna kumutumikira.
ZIMENE ZIDZACHITIKE ANTHU OSALUNGAMA AKADZAUKITSIDWA
Kodi osalungama akadzaukitsidwa adzaweruzidwa potengera zimene anachita asanamwalire? Ayi. Lemba la Aroma 6:7 limati: “Chifukwa munthu amene wafa wamasuka ku uchimo wake.” Pamene anthu osalungamawa anamwalira, ndiye kuti analipira mtengo wa machimo awo. Choncho adzaweruzidwa potengera zimene adzachite akadzaukitsidwa, osati zimene anachita asanamwalire. Kodi iwo adzapindula bwanji ndi zimenezi?
Anthu amenewa akadzaukitsidwa, adzakhala ndi mwayi wophunzira malamulo a Mulungu, amene adzakhale m’mipukutu yophiphiritsa yomwe idzatsegulidwe. Kenako adzaweruzidwa “mogwirizana ndi ntchito zawo,” potengera zimene adzachite pa nthawiyo. (Chivumbulutso 20:12, 13) Kwa ambiri, umenewu udzakhala mwayi wawo woyamba woti aphunzire zimene Mulungu amafuna. Akadzatsatira zimene Mulungu amafunazo, adzakhala ndi moyo wosatha.
Chiphunzitso cha m’Baibulo chimenechi chathandiza anthu ambiri kuti ayambenso kukhulupirira Mulungu. Mmodzi wa anthu amenewa ndi mtsikana wina, dzina lake Yeong Sug. Iye anakulira m’banja lachikatolika ndipo anthu ena a m’banja lawo anali ansembe. Mtsikanayu ankafuna kudzakhala sisitere, choncho anapita kukakhala pamalo ena a masisitere. Koma kenako anachoka pamalowa chifukwa chokhumudwa ndi zimene zinkachitika. Komanso zinkamuvuta kuvomereza chiphunzitso choti anthu oipa amakawotchedwa kumoto. Iye ankaona kuti Mulungu amene amazunza anthu kumoto, si wachilungamo komanso si wachikondi.
Kenako mayi wina wa Mboni za Yehova anamusonyeza Yeong Sug mawu a m’Baibulo awa: “Amoyo amadziwa kuti adzafa, koma akufa sadziwa chilichonse. Iwo salandiranso malipiro alionse, chifukwa zonse zimene anthu akanawakumbukira nazo zaiwalika.” (Mlaliki 9:5) A Mboni anamuthandiza kuzindikira kuti makolo ake amene anamwalira sakuzunzika kumoto. Koma akuyembekezera kudzaukitsidwa ndipo panopa sakudziwa chilichonse.
Yeong Sug anadziwa kuti pali anthu ambiri omwe sakudziwa mfundo ya m’Baibulo imeneyi. Choncho anamvetsa mawu a Yesu a pa Mateyu 24:14 akuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.” Panopa mtsikanayu amalalikira uthenga wabwino ndipo amauza anthu zokhudza zimene Baibulo limanena, zoti anthu amene anamwalira adzaukitsidwa.
“MULUNGU ALIBE TSANKHO”
Baibulo limanena kuti: “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.” (Machitidwe 10:34, 35) Izi n’zimene tiyenera kuyembekezera kwa Mulungu amene “amakonda chilungamo ndi chiweruzo chosakondera.”—Salimo 33:5.