Lengezani Ufumu wa Yehova Molimba Mtima!
“Nalandira onse akufika kwa iye, ndi kulalikira Ufumu wa Mulungu.”—MACHITIDWE 28:30, 31.
1, 2. Kodi ndiumboni uti wa kuchilikizidwa kwaumulungu umene mtumwi Paulo anali nawo, ndipo kodi n’chitsanzo chotani chimene iye anakhazikitsa?
YEHOVA nthaŵi zonse amachilikiza alengezi a Ufumu. Izi zinali zowona chotani nanga kwa mtumwi Paulo! Mwakuchilikizidwa kwaumulungu, iye anawonekera pamaso pa olamulira, anapirira kuwukira kwa makamu, ndipo analengeza molimba mtima Ufumu wa Yehova.
2 Ngakhale monga wandende m’Roma, Paulo ‘analandira onse akufika kwa iye, ndi kulalikira ufumu wa Mulungu.’ (Machitidwe 28:30, 31) N’chitsanzo chabwino kwambiri chotani nanga kwa Mboni za Yehova lerolino! Tingaphunzire zambiri muutumiki wa Paulo monga momwe wasimbidwira ndi Luka m’machaputala omalizira a bukhu la Baibulo la Machitidwe.—20:1—28:31.
Akhulupiriri Anzake Achilikizidwa
3. Kodi chinachitika nchiyani pa Trowa, ndipo kodi nkufanana kuti komwe kungawonedwe m’tsiku lathu?
3 Pambuyo pakutha kwa chipwirikiti m’Efeso, Paulo apitirizabe ndi ulendo wake wachitatu wa umishonale. (20:1-12) Komabe, pamene anali pafupi kuyamba ulendo wapanyanja wonka ku Suriya, iye anadziŵa kuti Ayuda anampangira chiŵembu. Popeza kuti angakhale anakonzekera kukwera ngalawa imodzimodziyo ndi kupha Paulo, iye anadzera ku Makedoniya. Pa Trowa, anathera mlungu umodzi akuchilikiza akhulupiriri anzake monga mmene oyang’anira oyendayenda pakati pa Mboni za Yehova amachitira. Pausiku asanachoke, Paulo anatalikitsa nkhani yake kufikira pakati pa usiku. Utiko, wokhala pazenera, mwachiwonekere anali wotopa ndi ntchito ya tsikulo. Iye anawodzera ndi kugona ndipo anagwa namwalira kuchokera pa nyumba yosanja yachitatu, koma Paulo anamuukitsa. N’chisangalalo chotani nanga chimene ichi chingakhale chinapangitsa! Pamenepa, taganizirani chisangalalo chomwe chidzatulukapo pamene mamiliyoni ambiri aukitsidwa m’dziko latsopano likudzalo.—Yohane 5:28, 29.
4. Ponena za utumiki, kodi nchiyani chimene Paulo anaphunzitsa akulu a ku Efeso?
4 Ali paulendo wonka ku Yerusalemu, pa Mileta, Paulo anakomana ndi akulu a ku Efeso. (20:13-21) Iye anawakumbutsa kuti anawaphutsitsa “m’nyumba m’nyumba” ndikuti iye ‘anachitira umboni mokwanira kwa Ayuda ndi Agiriki wonena za kulapa kubwerera kwa Mulungu ndi kukhala ndi chikhulupiriro mwa Ambuye wathu Yesu.’ Omwe pomalizira pake anakhala akulu anali atalapa, ndipo anakhala ndi chikhulupiriro. Mtumwiyo anakhalanso akuwaphunzitsa kulengeza Ufumu molimba mtima kwa osakhulupirira muutumiki wa kunyumba ndi nyumba mofanana ndi womwe umachitidwa ndi Mboni za Yehova lerolino.
5. (a) Kodi ndimotani mmene Paulo analiri wachitsanzo chabwino ponena za chitsogozo choperekedwa ndi mzimu woyera? (b) Kodi nchifukwa ninji akulu anafunikira uphungu wa ‘kusamalira nkhosa zonse’?
5 Paulo anali wachitsanzo chabwino m’kuvomereza chitsogozo choperekedwa ndi mzimu woyera wa Mulungu. (20:22-30) “Womangidwa mumzimu,” kapena kukhala ndi thayo la kutsatira chitsogozo chake, mtumwiyo akapita ku Yerusalemu, ngakhalae kuti nsinga ndi zisautso zinamuyembekezera kumeneko. Iye anauwona moyo kukhala wamtengo wapatali, koma kusunga umphumphu kwa Mulungu kunali chinthu chofunika kwambiri kwa iye, monga momwe ziyenera kukhalira kwa ife. Paulo analimbikitsa akulu ‘kusamalira nkhosa zonse pa zomwe mzimu woyera unawaika iwo kukhala oyang’anira.’ Pambuyo pa ‘kuchoka’ kwake (mwachiwonekere paimfa), “mimbulu yosautsa” ikakhoza ‘kusachitira nkhosazo mokoma mtima.’ Amuna oterowo akabuka pakati pa akulu enieniwo, ndipo ophunzira okhala n’chidziŵitso chochepa akavomereza ziphunzitso zawo zopotozedwa.—2 Atesalonika 2:6.
6. (a) Kodi nchifukwa ninji Paulo mwachidaliro akasiira akulu mwa Mulungu? (b) Kodi ndimotani mmene Paulo anatsatirira malamulo amakhalidwe abwino a pa Machitidwe 20:35?
6 Akulu anafunikira kukhala atcheru mwauzimu kuchinjiriza mpatuko. (20:31-38) Mtumwiyo adawaphunzitsa Malemba Achihebri ndi ziphunzitso za Yesu, zomwe ziri ndi mphamvu ya kuyeretsa yomwe ikawathandiza kulandira Ufumu wakumwamba, ‘cholowa mwa onse oyeretsedwa.’ Mwakugwira ntchito kudzipezera zakudya ndi anzake, Paulo analimbikitsanso akulu kukhala ogwira ntchito amphamvu. (Machitidwe 18:1-3; 1 Atesalonika 2:9) Ngati tilondola njira yofananayo ndi kuthandiza ena kupeza moyo wosatha, tidzayamikira mawu awa a Yesu: ‘Muli chimwemwe chambiri m’kupatsa kuposa m’kulandira.’ Lingaliro la ndemangayi likupezeka m’Mauthenga Abwino koma lagwidwa mawu ndi mtumwi Paulo yekha, yemwe angakhale anaimva ikulankhulidwa kapena mowuziridwa. Tingasangalale ndi chimwemwe chambiri ngati tikhala odzipereka nsembe monga momwe Paulo analiri. Eya, iye anadzikhutula yekha kwambiri kotero kuti kuchokapo kwake kunapangitsa akulu a ku Efeso kuipidwa kwakukulukulu!
Chifuniro cha Yehova Chichitidwe
7. Kodi ndimotani mmene Paulo anakhazikitsira chitsanzo m’kugonjera ku chifuniro cha Mulungu?
7 Pamene ulendo wachitatu waumishonale wa Paulo unayandikira mapeto ake (pafupifupi 56 C.E.), iye anakhazikitsa chitsanzo chabwino m’kugonjera ku chifuniro cha Mulungu. (21:1-14) Mu Kaisareya iye ndi anzake anakhala ndi Filipo, amene anamwali ake anayi “ananenera,” akumaneneratu zochitika mwamzimu woyera. Konko mneneri Wachikristu Agabo anadzimanga yekha manja ndi mapazi ndi lamba la Paulo ndipo anafulumizidwa ndi mzimu kunena kuti Ayuda akamanga nzika yawo m’Yerusalemu ndikumpereka m’manja a Akunja. ‘Ndakonzeka ine si kumangiwa kokha, komatunso kufera ku Yerusalemu chifukwa cha dzina la Ambuye Yesu,’ anatero Paulo. Ophunzirawo anakhala chete, naati: ‘Kufuna kwa Yehova kuchitidwe.’
8. Ngati nthaŵi zina tichipeza kukhala chovuta kuuvomereza uphungu wabwino, kodi tiyenera kukumbukiranji?
8 Paulo anawuza akulu mu Yerusalemu chimene Mulungu anachita pakati pa Akunja kudzera muutumiki wake. (21:15-26) Ngati nthaŵi zonse timachipeza kukhala chovuta kulandira uphungu wabwino, tingakumbukire mmene Paulo anaulandirira. Kuti atsimikizire kuti sankaphunzitsa Ayuda m’maiko Achikunja kuti “apatukane naye Mose,” iye analabadira uphungu wa akulu wa kuchita mwambo wa kudziyeretsa nadzilipirira iyemwini ndi amuna anayi enawo. Ngakhale kuti imfa ya Yesu inachotsapo Chilamulo, Paulo sanachite cholakwa chirichonse mwakuchita mbali zake zokhudza zowinda.—Aroma 7:12-14.
Anawukiridwa Koma Sanagonje
9. Ponena za kuwukira kwachiwawa, kodi nkufanana nako kuti komwe kulipo pakati pa zokumana nazo za Paulo ndi za Mboni za Yehova lerolino?
9 Mboni za Yehova kaŵirikaŵiri zasunga umphumphu kwa Mulungu poyag’anizana ndi kuwukiridwa kwachiwawa. (Mwachitsanzo, onani 1975 Yearbook of Jehovah’s Witnesses, masamba 180-90.) Mofananamo Ayuda ochokera ku Asia Minor anautsa khamu la anthu motsutsana ndi Paulo. (21:27-40) Powona Trofimo wa ku Efeso ali limodzi naye, iwo anazenga mtumwiyo mlandu wonyenga wa kuipitsa kachisi mwa kulowetsamo Agiriki. Paulo anali nenene kuphedwa pamene woweruza Wachiroma Klaudiyo Lusiya ndi amuna ake analetsa chipwirikiticho! Monga momwe kunanenedweratu (koma kochititsidwa ndi Ayuda), Lusiya anapangitsa Paulo kumangidwa maunyolo. (Machitidwe 21:11) Mtumwiyo anali pafupi kuperekedwa kulinga la asilikali loyandikana ndi bwalo la kachisi pamene Lusiya anazindikira kuti Paulo sanali wokopa anthu koma m’Yuda wololedwa kulowa m’bwalo lakachisi. Popempha chilolezo cha kulankhulapo, Paulo analankhula kwa anthuwo m’Chihebri.
10. Kodi ndimotani mmene ndemanga za Paulo zinalandiridwira ndi Ayuda m’Yerusalemu, ndipo kodi nchifukwa ninji sanakwapulidwe?
10 Paulo anapereka umboni wolimba mtima. (22:1-30) Iye anadzizindikiritsa yekha kukhala Myuda wolangizidwa ndi Gamaliyeli wolemekezedwa kwenikweni. Mtumwiyo analongosola kuti paulendo wonka ku Damasiko kukazunza atsatiri a Njira, iye anachititsidwa khungu pamene anawona Yesu Kristu wolemekezedwa, koma Hananiya ndiye anachiritsa khungu lakelo. Pambuyo pake Ambuye adauza Paulo kuti: ‘Pita, chifukwa Ine ndidzakutuma iwe kunka kutali kwa amitundu.’ Mawu omwewo anagwa ngati laŵi la moto mnkhalango. Pamene khamulo linkafuula kuti Paulo sanali woyenerera kukhala ndi moyo, linataya zovala zawo ndikuwaza fumbi mumlengalenga chifukwa chaukali. Chotero Lusiya analola Paulo kutengeredwa ku linga la asilikali nati amfunsefunse ndikumkwapula kuti adziŵe chifukwa chake Ayuda amfulira chomwecho. Kukwapula (ndi chipangizo chokhala ndi chingwe chachikopa chomangidwa mfundo kapena choikidwako zidutswa zazitsulo kapena mafupa) kunaletsedwa pamene Paulo anafunsa kuti: ‘Kodi nkololedwa kukwapula Mroma wopanda mlandu?’ Pozindikira kuti Paulo anali nzika Yachiroma, Lusiya anakhala ndi mantha ndipo anampereka ku Bwalo Lalikulu Lamilandu kukadziŵa chimene iye ankazengedwera mlandu ndi Ayuda.
11. Kodi Paulo anali Mfarisi m’lingaliro lotani?
11 Pamene Paulo anayamba kudzichinjiriza pamaso pa Bwalo Lalikulu Lamilandu mwakunena kuti iye ‘anakhala pamaso pa Mulungu ndi chikumbumtima chokoma chonse,’ Mkulu Wansembe Hananiya analamula kuti apandidwe. (23:1-10) Paulo anati, “Mulungu adzakupanda iwe, khoma loyeretsedwa iwe.” “Ulalatira kodi mkulu wa ansembe?” ena anafunsa tero. Chifukwa cha kusapenya bwino, Paulo angakhale sanamzindikire Hananiya. Koma podziŵa kuti bungwelo linapangidwa ndi Afarisi ndi Asaduki, Paulo anati: ‘Ine ndine Mfarisi woweruzidwa pachiyembekezo cha chiukiriro.’ Ichi chinapangitsa chilekano pakati pa Bwalo Lalikulu Lamilandu, popeza kuti Afarisi anakhulupirira chiukiriro ndipo Asaduki sanatero. Motero mpatuko waukulu unabuka kwakuti Lusiya anafunikira kupulumutsa mtumwiyo.
12. Kodi ndimotani mmene Paulo anazembera chiŵembu m’Yerusalemu?
12 Chotsatira Paulo anathawa chiŵembu chopangidwira iye. (23:11-35) Ayuda makumi anayi analumbira kusadya kapena kumwa kufikira atamupha iye. Mphwake wa Paulo anamsimbira izi ndi kwa Lusiya. Mwakuyang’aniridwa ndi msilikali, mtumwiyo anaperekedwa kwa Kazembe Antonio Felike pa Kaisareya, likulu la malamulo Lachiroma la ku Yudeya. Pambuyo polonjeza kumvetsera kwa Paulo, Felike anamsunga iye woyang’aniridwa m’nyumba yachifumu ya ku Praetoria ya Herode Wamkulu, likulu la kazembeyo.
Kulimba Mtima Pamaso pa Olamulira
13. Kodi Paulo anachitira umboni za chiyani kwa Felike, ndipo ndi chotulukapo chotani?
13 Mtumwiyo mofulumira anadzichinjiriza yekha motsutsana ndi kuzengedwa milandu konyenga ndipo anachitira umboni molimba mtima kwa Felike. (24:1-27) Pamaso pa osuliza Achiyuda, Paulo anasonyeza kuti iye sanautse kuwukira kwa khamuko. Iye anati anakhulupirira zinthu zolembedwa m’Chilamulo ndi Aneneri ndipo anayembekezera ‘m’chiukiriro cha olungama ndi osalungama.’ Paulo anapita ku Yerusalemu ndi ‘mphatso zachifundo’ (zopereka za atsatiri a Yesu omwe anasauka chifukwa cha chizunzo) ndipo anayeretsedwa mwamwambo. Ngakhale kuti Felike anasintha tsiku lachiweruzocho, Paulo pambuyo pake analalikira kwa iye ndi mkazi wake Drusila (mwana wamkazi wa Herode Agripa I) ponena za Kristu, chilungamo, kudziletsa, ndi chiweruzo chikudzacho. Atawopsyezedwa ndi nkhaniyo, Felike anamasula Paulo. Komabe, pambuyo pake, iye anatumiza anthu kaŵirikaŵiri kwa mtumwiyo, akumayembekezera chiphuphu koma mosaphula kanthu. Felike anadziŵa kuti Paulo analibe mlandu koma anamsungabe womangidwa, akumayembekezera kupeza phindu kwa Ayuda. Zaka ziŵiri pambuyo pake, Felike analowedwa mmalo ndi Porkiyo Festo.
14. Kodi ndi makonzedwe alamulo otani amene Paulo anazolowerana nawo pamene anawonekera pamaso pa Festo, ndipo kodi nkufanana nako kuti komwe mukupeza mu ichi?
14 Paulo anadzichinjirizanso molimba mtima pamaso pa Festo. (25:1-12) Ngati mtumwiyo anayenerera imfa, iye sakafooka, koma panalibe munthu yemwe akamgwira kumupereka kwa Ayuda pofuna kuyesedwa wachisomo. ‘Ndiri kuimirira pampando wachiweruzo wa Kaisara’ anatero Paulo, akumafotokoza yekha za kuyenera kwa nzika Yachiroma kuyesedwera m’Roma (panthaŵi imeneyo pamaso pa Nero). Apilu imeneyo itavomerezedwa, Paulo akakhoza ‘kuchitira umboni mu Roma,’ monga momwe kunanenedweratu. (Machitidwe 23:11) Mboni za Yehova nazonso zimazolowerana zokha ndi makonzedwe a ‘kuchinjiriza ndi kukhazikitsa mbiri yabwino mwalamulo.’—Afilipi 1:7, NW.
15. (a) Kodi ndi ulosi uti womwe unakwaniritsidwa pamene Paulo anawonekera pamaso pa Mfumu Agripa ndi Kaisara? (b) Kodi ndimotani mmene Saulo ‘anatsalimira pachothwikira’?
15 Mfumu Herode Agripa II wa kumpoto kwa Yudeya ndi mlongo wake Bernike (kwa yemwe anali ndi unansi wochokera ku makolo) anamumva Paulo pamene ankachezera Festo ku Kaisareya. (25:13–26:23) Mwakuchitira umboni kwa Agripa ndi Kaisara, Paulo anakwaniritsa ulosi wakuti akachitira umboni dzina la Ambuye kwa mafumu. (Machitidwe 9:15) Powuza Agripa chomwe chinachitika panjira ponka ku Damasiko, Paulo anafotokoza kuti Yesu anati: ‘Nkukuvuta kutsalima pachothwikira.’ Monga mmene bulu wovuta amadzivulazira mwakulimbana ndi chothwikira, Saulo anadzivulaza yekha mwakulimbana ndi atsatiri a Yesu, omwe anachilikizidwa ndi Mulungu.
16. Kodi ndimotani mmene Festo ndi Agripa anachitira ndi umboni wa Paulo?
16 Kodi Festo ndi Agripa anayankha motani? (26:24-32) Posakhala okhoza kumvetsetsa chiukiriro ndi kudabwitsidwa ndi chigomeko cha Paulo, Festo anati: ‘Kuwerengetsa kwako kwakuchititsa misala.’ Mofananamo, ena amasuliza Mboni za Yehova kukhala zamisala, ngakhale kuti izo ziridi zofanana ndi Paulo mwa ‘kulankhula chowonadi chomvekera.’ “Ndi kundikopa pang’ono ufuna kundiyesera Mkristu,” anatero Agripa, yemwe anathetsa mlanduwo koma anavomereza kuti Paulo akadamasulidwa ngati sanachitire apilu kwa Kaisara.
Moopsya m’Nyanja
17. Kodi mungafotokoze motani ngozi zokumanidwa m’nyanja paulendo wa Paulo wonka ku Roma?
17 Ulendo wonka ku Roma unawunikira Paulo “moopsya m’nyanja.” (2 Akorinto 11:24-27) Nduna yankhondo yotchedwa Yuliyo anayang’anira akaidi onka paulendo wapanyanja kuchokera ku Kaisareya kunka ku Roma. (27:1-26) Pamene ngalawa yawo inafika pa Sidoni, Paulo analoledwa kuchezera akhulupiriri, omwe anamtsitsimula mwauzimu. (Yerekezerani ndi 3 Yohane 14.) Pa Mura mu Asia Minor, Yuliyo anapangitsa akaidi kukwera ngalawa yonyamula zakudya yonka ku Italiya. Mosasamala kanthu za mphepo yaikulu, iwo anakhoza kufika ku doko la Pokocheza Pokoma, pafupi ndi mzinda wa Krete ku Laseya. Atanyamuka kumeneko paulendo wonka ku Foinika, mphepo ya namondwe wa kumpoto kulinga kum’mawa inawopsyeza ngalawayo. Pakuwopa kuti angataike pa Surti (mchenga wofewa) kumpoto kwa Afirika, amalinyerowo “anatsitsa matanga,” mwinamwake zokankhira ndi milongoti yake. Zingwe zinazungulutsidwa chingalawacho kotero kuti milongoti ya ngalawayo isagwe. Chikhalirechobe namondweyo anakunthabe tsiku lotsatira, ngalawayo inapeputsidwa mwa kutulutsamo katundu. Tsiku lachitatu, anataya zipangizo za ngalawa (zokankhira kapena matanga). Pamene chiyembekezo chinacheperachepera, mngero anawonekera kwa Paulo ndikumuwuza kuti asawope, pakuti akaimirira pamaso pa Kaisara. Unali mpumulo wotani nanga pamene mtumwiyo anati apaulendo onse akafikitsidwa kutsidya lina pa chisumbu china!
18. Kodi nchiyani chomwe chinachitika pomalizira pake kwa Paulo ndi apaulendo anzake?
18 Afaulendowo anapulumuka. (27:27-44) Pakati pausiku patsiku la 14, amalinyerowo anawona kuti pamtunda panayandikira. Phokoso linachitsimikizira, ndipo anangula anatsitsidwa kuti apewe ngozi m’matanthwe. Mwakulimbikitsidwa ndi Paulo, amuna onse 276 anadya zakudya. Pamenepo ngalawayo inapeputsidwa mwakutayira kunja tirigu. Potuluka dzuwa, amalinyerowo anadula anangulawo, ndikumasula zingwe zomanga tsigiro nakweza thanga la kulikulu. Chipangizocho chinapepuka pa bondo lamchenga, ndipo kumakaliro kunasweka. Koma aliyense anafika pamtunda.
19. Kodi chinachitika nchiyani kwa Paulo pa Melita, ndipo kodi iye anachitanji kwa ena kumeneko?
19 Atanyowa ndi kutopa, minkhole ya ngalawa yoswekayo inafika pa Melita, kumene nzika za pachisumbupo zinawasonyeza ‘zokoma zosachitika pena ponsepo.’ (28:1-16) Komabe, pamene Paulo anaika chisaka cha nkhuni pamoto, kutentha kunatulutsa njoka yaululu imene inakulunga dzanja lake. (Tsopano kulibe njoka zaululu ku Melita, koma iyi inali ‘cholengedwa chaululu kwenikweni.’) Nzika za ku Melita zinaganiza kuti Paulo anali wambanda amene ‘chilungamo’ sichimulola kukhala ndi moyo, koma pamene sanafe kapena kutupa ndi kulumidwako, iwo anati anali mulungu. Pambuyo pake Paulo anachiritsa ambiri, kuphatikizapo tate wa Popliyo, nduna yaikulu ya ku Melita. Miyezi itatu pambuyo pake, Paulo, Luka, ndi Aristarko anachoka pangalawapo ndi dzina lakuti ‘Ana a Zeu’ (Castor ndi Pollux, milungu yamapasa inalingaliridwa kuyanja amalinyero). Pofika pa Potiyoli, Yuliyo anawuka ndi khamu lake. Paulo anayamika Mulungu ndikukhala wolimba mtima pamene Akristu ochokera ku likulu la Roma anakumana naye pa Bwalo la Apiyo ndi Nyumba za Alendo Zitatu Panjira ya Apiyo. Pomalizira, m’Roma, Paulo analoledwa kukhala yekha, ngakhale kuti anayang’aniridwa ndi msilikali.
Pitirizanibe Kulengeza Ufumu wa Yehova!
20. Kodi Paulo anadzitanganitsa ndi ntchito yotani m’bwalo lake m’Roma?
20 M’bwalo lake m’Roma, Paulo analengeza molimba mtima Ufumu wa Yehova. (28:17-31) Iye anauza amuna akuluakulu Achiyuda kuti: ‘Pakuti chifukwa cha chiyembekezo cha Israyeli ndamangidwa ndi unyolo uwu.’ Chiyembekezo chimenecho chinaphatikizapo kuvomereza Mesiya, chinachake chomwe ife tiyeneranso kukhala ofunitsitsa kuchivutikira. (Afilipi 1:29) Ngakhale kuti ambiri a Ayuda amenewo sanakhulupirire, Akunja ambiri ndi Ayuda otsalira anali ndi mtima wolunjika. (Yesaya 6:9, 10) Kwa zaka ziŵiri (pafupifupi 59-61 C.E.) Paulo analandira onse omwe anadza kwa iye, ‘akumalalikira Ufumu wa Mulungu kwa iwo ndi kuphunzitsa zinthu zokhudza Ambuye Yesu Kristu ndi ufulu waukulu wa kulankhula, popanda choletsa.’
21. Kufikira kumapeto amoyo wake padziko lapansi, kodi Paulo anakhazikitsa chitsanzo chotani?
21 Nero mwachiwonekere analengeza Paulo kukhala wopanda mlandu ndi kummasula. Mtumwiyo kenaka anakonzanso ntchito yake mogwirizana ndi Timoteo ndi Tito. Komabe, iye anamangidwanso m’Roma (pafupifupi 65 C.E.) ndipo mwachidziwikire iye anavutika ndi kuphedwera chikhulupiriro m’manja mwa Nero. (2 Timoteo 4:6-8) Koma kufikira kumapeto, Paulo anakhazikitsa chitsanzo chabwino monga mlengezi wa Ufumu wolimba mtima. Ndi mzimu umodzimodziwu m’masiku otsiriza ano, lolani kuti onse odzipereka kwa Mulungu alengeze molimba mtima Ufumu wa Yehova!
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi nkuphunzitsa kwautumiki kotani kumene Paulo anapereka kwa akulu a pa Efeso?
◻ Kodi Paulo anakhazikitsa chitsanzo chotani cha kugonjera ku chifuniro cha Mulungu?
◻ Ponena za kuwukira kwa chiwawa, kodi nkufanana kotani komwe kulipo pakati pa zokumana nazo za Paulo ndi za Mboni za Yehova lerolino?
◻ Kodi Paulo anadzizoloweretsa iyemwini ndi makonzedwe alamulo otani pamene anali pamaso pa Kazembe Festo, ndipo kodi ichi chiri ndi kufanana kwamakono kotani?
◻ Kodi Paulo anadzitanganitsa ndi ntchito yotani m’bwalo lake la m’Roma, akumakhazikitsa chitsanzo chotani?