“Ndikachita Apilo kwa Kaisara!”
ANTHU achiwawa agwira munthu wopanda chitetezo ndipo ayamba kum’menya. Anthuwo akuganiza kuti munthuyo afunika kuphedwa. Panthaŵi yomwe zikuonekeratu kuti munthuyo aphedwadi, asilikali akutulukira, n’kuyamba kulimbana ndi anthuwo mpaka kulanda munthuyo m’manja mwawo. Munthuyo ndi mtumwi Paulo. Anthu amene amugwirawo ndi Ayuda amene akutsutsa kwambiri zomwe Paulo akulalikira ndipo akumuimba mlandu woipitsa kachisi. Omwe akumulanditsa ndi Aroma motsogozedwa ndi mkulu wa asilikali Klaudiyo Lusiya. Chifukwa cha chipwirikiti chimenecho, Paulo akumuganizira kuti ndi wochita zoipa ndipo amumanga.
Machaputala omalizira asanu ndi aŵiri a buku la Machitidwe akusimba za mlandu wa kumangidwa kumeneku. Kuzindikira zomwe Paulo ankadziŵa kale pankhani ya malamulo, mlandu womwe anamuimba, chitetezo chomwe anali nacho, ndiponso njira zomwe Aroma anali kutsatira poweruza, zimatichititsa kumvetsa bwino machaputala ameneŵa.
M’ndende ya Klaudiyo Lusiya
Udindo wina wa Klaudiyo Lusiya unali kusungitsa mtendere mu Yerusalemu. Kazembe wamkulu wa Roma wa chigawo cha Yudeya anali kukhala ku Kaisareya. Tinganene kuti zomwe Lusiya anachita pa nkhani ya Paulo kunali kuteteza munthu ku chiwawa komanso kumanga munthu wosokoneza mtendere. Lusiya anatengera mkaidi wakeyo ku malo a asilikali omwe anali ku Tower Antonia chifukwa cha mmene Ayuda anali kuchitira pankhaniyi.—Machitidwe 21:27–22:24.
Lusiya anali pantchito yofufuza zomwe Paulo wachita. Panthaŵi ya chipwirikiticho, iye sanadziŵe kalikonse. Mosataya nthaŵi, analamula kuti Paulo ‘amukwapule ndi kum’funsa kuti mwina aulule chifukwa chomwe anthu anali kufuulira motsutsana naye.’ (Machitidwe 22:24) Imeneyi inali njira yopezera umboni kwa anthu aupandu, akapolo, ndiponso anthu wamba. Kukwapula kumeneko (flagrum) kuyenera kuti kunkakwaniritsadi cholinga chake. Komabe, inali njira yopezera umboni yoipa kwambiri. Zina mwa zikoti zomwe ankakwapulira zinali za tcheni lokhala ndi tizitsulo. Zina zinali za chingwe chachikopa chomwe ankachipota pamodzi ndi mafupa akuthwa ndi tizitsulo. Zikoti zimenezi zinali kutema ndi kuchititsa zilonda, ndiponso kunyenya mnofu kukhala ngati sanza.
Zitafika pamenepa, Paulo anaulula kuti iye anali nzika ya Roma. Nzika ya Roma yosalakwa sanali kuikwapula. Choncho, zomwe Paulo anaulula zokhudza ufulu wake zinayamba kugwira ntchito nthaŵi yomweyo. Ngati ofesala atazunza kapena kulanga nzika ya Roma, ntchito yake inkatha nthaŵi yomweyo. N’chifukwa chake kuyambira pamene Paulo anaulula kuti ndi nzika ya Roma, iye ankamuona monga mkaidi wapadera ndipo anali ndi ufulu wolandira alendo odzam’chezera.—Machitidwe 22:25-29; 23:16, 17.
Lusiya atalephera kupeza chifukwa chenicheni cha mlanduwo, anamutenga Paulo kupita naye ku bwalo lalikulu la Ayuda la Sanihedirini kuti akamve chomwe chinayambitsa mkanganowo. Paulo ananena kuti nkhani ya chiukiriro ndiyo inautsa mapiri pachigwa. Mkanganowo unakula kwambiri moti Lusiya anachita mantha kuti Paulo amupha, motero iye anayenera kumulanditsanso m’manja mwa Ayuda aukaliwo monga mmene anachitira poyamba paja.—Machitidwe 22:30–23:10.
Lusiya sanafune kukhala ndi mlandu wophetsa nzika ya Roma. Atamva kuti Ayuda akonza chiwembu chofuna kupha Paulo, iye anathaŵitsa mwamsanga mkaidi wakeyo kupita ku Kaisareya. Malinga ndi malamulo, mkaidi aliyense ankayenera kukhala ndi lipoti losimba mlandu wake akamapita ku khoti lina lalikulu. Zina zomwe zinkayenera kukhala pa lipotilo zinali kafukufuku yemwe wachitika kale pankhaniyo, chifukwa chomwe apititsira mkaidiyo ku khotilo, ndiponso maganizo a wofufuzayo pa mlanduwo. Lusiya anapereka lipoti lakuti Paulo ‘anamuimba mlandu pankhani ya Chilamulo cha Ayuda osati pankhani iliyonse yoyenera kuti munthu aphedwe kapena kumangidwa.’ Ndiponso anauza amene ankamuimba mlanduwo kuti akapereke madandaulo awo kwa kazembe Felike.—Machitidwe 23:29, 30.
Kazembe Felike Alephera Kuweruza
Felike ndiye anali kulamulira chigawo chonsecho. Iye poweruza milandu anali ndi ufulu wotsatira miyambo ya m’deralo kapena lamulo lomwe linkagwira ntchito kwa anthu otchuka ndi akuluakulu a boma okha. Lamulo limeneli ankalitcha kuti ordo. Nthaŵi zina ankagwiritsanso ntchito njira ina yoweruzira yotchedwa extra ordinem pogamula mlandu wina uliwonse. Kazembeyo sankangofunika ‘kuganizira zomwe zinkachitika ku Roma, koma zomwe ziyenera kuchitika kwa anthu onse.’ Choncho, iye anali ndi ufulu wogamula mmene angafunire.
Sitikudziŵa chilamulo chonse cha Aroma mwatsatanetsatane. Komabe, mlandu wa Paulo unali “chitsanzo cha mlandu umene anatsatira njira yoweruzira yotchedwa extra ordinem.” Kazembeyo pamodzi ndi om’thandiza ake akanayenera kumva madandaulo ochokera kwa anthu ena pankhaniyo. Woimbidwa mlanduyo ankamuitana kuti adzayankhe mlanduwo kuti adziteteze mwa kutsutsa wodandaulayo. Komabe wodandaula ndiye anali ndi udindo wopereka umboni wotsimikiza mlanduwo. Woweruza anali kupereka chilango ngati akuona kuti n’koyenera kutero. Iye anali ndi ufulu wogamula nthaŵi yomweyo, kapena kuimitsa kaye mlanduwo. Ngati mlandu auimitsa ndiye kuti woimbidwa mlanduyo anali kum’tsekera kaye kundende. Katswiri wina wamaphunziro, Henry Cadbury, ananena kuti: “Mosakayikira, chifukwa cha ufulu umenewo wochita zomwe akufuna, kazembeyo anali ndi mpata ‘wosonkhezeredwa kuchita zosayenera’ ndiponso kulandira ziphuphu n’cholinga choti amasule, kapena kumanga wopalamulayo, kapenanso kuimitsa mlanduwo.”
Mkulu wa Ansembe Hananiya, pamodzi ndi amuna akulu a Yuda, ndi Tertulo anauza Felike mlandu umene akumuimba Paulo. Iwo ananena kuti Paulo anali ‘kuyambitsa mapanduko pakati pa Ayuda’ ndiponso kuti anali “m’tsogoleri wa m’panduko wa Anazarene.” Iwo ananenanso kuti Paulo ankafuna kuipitsa kachisi.—Machitidwe 24:1-6.
Anthu achiwawa amene anagwira Paulo ankaganiza kuti iye analoŵetsa munthu wakunja wotchedwa Trofimo m’chipinda cha m’kati mwa kachisi chomwe chinali cha Ayuda okha.a (Machitidwe 21:28, 29) Kunena zoona, Trofimo ndiyedi anapalamula mlandu mwa kulowa m’chipinda cha kachisiyo osati Paulo ayi. Koma ngati Ayudawo ankaona kuti zomwe ankati Paulo anali kuchita zinali kuchirikiza tchimolo ndiye kuti umenewunso ukanakhala mlandu womwe chiweruzo chake chinali kuphedwa. Ndipo Aroma akuoneka kuti ankalola chilango choterocho pa mlandu umenewu. Choncho, akanakhala kuti Paulo anagwidwa ndi apolisi apakachisi wachiyuda osati Lusiya, ndiye kuti khoti la Sanihedirini likanatha kum’zenga mlandu ndi kumuweruza mosavuta.
Ayuda ankanena kuti zomwe Paulo ankaphunzitsa sizinali Chiyuda kapena chipembedzo chovomerezeka (religio licita). Choncho ankaziona kukhala zosaloledwa ndiponso zolimbikitsa kuukira boma.
Iwo ankanena kuti Paulo anali ‘kuyambitsa mapanduko kwa Ayuda onse m’dziko lonse lokhalamo anthu.’ (Machitidwe 24:5) Panthaŵiyo n’kuti Mfumu Klaudiyo ataweruza kumene Ayuda a ku Alexandria chifukwa cha “kuyambitsa tsoka lomwe linakhudza aliyense m’dziko lonselo.” Kufanana kwa milandu iŵiriyo n’kochititsa chidwi kwambiri. Wolemba mbiri wina, A. N. Sherwin-White, ananena kuti: “Anali kumuimba mlandu Myuda wina pa nthaŵi imene Klaudiyo anali kulamulira m’boma la Lipabuliki kapena kuchiyambi kwa ulamuliro wa Nero. Ayuda anali kuyesetsa kupangira kazembeyo kuti aone kulalikira kwa Paulo monga kuyambitsa chisokonezo pakati pa Ayuda onse mu Ufumu Waukuluwo. Iwo ankadziŵa kuti akazembe sankafuna kuweruza anthu pazifukwa za chipembedzo. Chotero, anayesa kupotoza mlanduwo kuti ukhale wandale osatinso wachipembedzo.”
Paulo anadziteteza mwa kutchula mfundo imodzi ndi imodzi. Anati: ‘Sindinayambitse chisokonezo ine. N’zoonadi kuti ndili m’gulu lomwe akuti ndi “mpatuko,” koma kukhala m’gulu limeneli kumatanthauza kusunga malamulo achiyuda. Ayuda ena a ku Asiya ndiwo anayambitsa chisokonezo. Ngati iwowo ali ndi dandaulo abwere adzanene.’ Paulo anasonyeza kuti mlanduwo unali wachipembedzo pakati pa Ayuda. Aroma anali kudziŵa zochepa chabe pa milandu yamtunduwu. Pozindikira mkwiyo umene Ayuda aliumawo anali nawo, Felike anaimitsa mlanduwo ndipo sanapereke Paulo kwa Ayuda omwe ankadzinenera kuti anali kudziŵa bwino kuweruza milandu yamtunduwo. Komanso sanamuweruze potsatira lamulo la Aroma kapenanso kum’masula. Palibe amene akanaumiriza Felike kuti aweruze mlanduwo. Kuwonjezera pofuna kukondera Ayudawo, Felike anaimitsa mlanduwo n’cholinga chinanso. Iye ankayembekezera kuti mwina Paulo am’patsa chiphuphu.—Machitidwe 24:10-19, 26.b
Kusintha kwa Zinthu M’nthaŵi ya Porkiyo Festo
Patapita zaka ziŵiri, Ayuda ku Yerusalemu anachita apilo mlandu wawo kutabwera kazembe wina watsopano, Porkiyo Festo. Anapempha kazembe watsopanoyo kuti awatumizire Paulo kuti akam’zenge mlandu. Koma Festo anawayankha motsindika kuti: “Machitidwe a Aroma satero, kupereka munthu asanayambe woneneredwayo kupenyana nawo omunenera ndi kukhala napo podzikanira pa chom’neneracho.” Wolemba mbiri wina, Harry W. Tajra, anati: “Festo anali atadziŵa kale kuti Ayuda anali atakonza chiwembu chofuna kunyonga nzika ya Roma imeneyi.” Choncho, iye anauza Ayudawo kuti akadandaule nkhaniyo ku Kaisareya.—Machitidwe 25:1-6, 16.
Kumeneko Ayuda ananenetsa kuti Paulo “sayeneranso kukhala ndi moyo.” Komabe, analephera kupereka umboni wokwanira ndipo Festo anaona kuti Paulo sanachite kanthu koyenera imfa. Festo anauza wolamulira wina kuti: “Koma anali nawo mafunso ena otsutsana naye a chipembedzero cha iwo okha, ndi mafunso a wina Yesu amene adafa, amene Paulo anati kuti ali ndi moyo.”—Machitidwe 25:7, 18, 19, 24, 25.
Paulo analibe mlandu uliwonse wokhudza ndale. Koma pankhani ya chipembedzo, Ayudawo mwachionekere analimbikira zoti khoti lawo ndilo lingathe kuweruza bwino mlandu umenewu. Kodi Paulo akanapita ku Yerusalemu kuti akamuweruze pa mlandu umenewu? Festo anamufunsa Paulo ngati angafune kupita kumeneko, koma zimenezo zinali zosayenera. Akanabwezeranso mlanduwo ku Yerusalemu ndiye kuti odandaulawo tsopano akanakakhala oweruza ndipo zimenezi zikanatanthauza kuti Paulo akanaperekedwa m’manja mwa Ayuda. Paulo anati: “Ndilikuimirira pa mpando wachiweruziro wa Kaisara, pompano ndiyenera kuweruzidwa ine; Ayuda sindinawachitira kanthu koipa, . . . Palibe mmodzi akhoza kundipereka kwa iwo. Nditulukira kwa Kaisara [“Ndikachita apilo kwa Kaisara!,” NW].—Machitidwe 25:10, 11, 20.
Mlanduwo anauimitsa chifukwa cha mawu ameneŵa omwe nzika ya Roma inalankhula. Ufulu wake wokachita apilo (provocatio) inali nkhani “yomveka ndiponso yogwira mtima.” Choncho atakambirana kuvuta kwa nkhaniyo ndi alangizi ake, Festo anati: “Wati ukachita apilo kwa Kaisara; upita kwa Kaisarako.”—Machitidwe 25:12, NW.
Festo anakondwa kuti wasiyana nawo mlandu wa Paulo. Patapita masiku angapo, iye anavomereza pouza Herode Agripa wachiŵiri kuti mlanduwo unali wovuta kwambiri. Kenako Festo anafunikira kulemba lipoti la mlanduwo kwa mfumu. Koma Festo anaona kuti mlanduwo unali wokhudza zinthu zovuta kuzimvetsa za chilamulo cha Ayuda. Komabe, Agripa anali kudziŵa bwino nkhani zimenezi. Choncho atasonyeza chidwi, anamupempha kuti athandize kulemba lipoti lopita kwa mfumu. Chifukwa chosamvetsa bwino zomwe Paulo ankanena kwa Agripa, Festo anafuula kuti: “Uli wamisala Paulo! Kuŵerengetsa kwako kwakuchititsa misala.” Koma Agripa anamvetsetsa kwambiri ndipo anati: “Ndi kundikopa pang’ono ufuna kundiyesera Mkristu.” Kaya Festo ndi Agripa anaganiza zotani pa zomwe Paulo ananena, mfundo n’njakuti iwo anagwirizana kuti Paulo anali wosalakwa ndipo kuti akanam’masula akanakhala kuti sanachite apilo kwa Kaisara.—Machitidwe 25:13-27; 26:24-32.
Kutha kwa Mlandu
Paulo atafika ku Roma anaitana amuna akulu achiyuda osati chifukwa chofuna kuwalalikira kokha komanso kufuna kudziŵa zomwe akudziŵa zokhudza iye. Zimenezo zikanavumbula zolinga zomwe anthu omuimba mlanduwo anali nazo. Sizinali zachilendo kuti akuluakulu a boma ku Yerusalemu apemphe thandizo kwa Ayuda achiroma pankhani yoweruza milandu. Koma iwo anauza Paulo kuti palibe chilichonse chomwe awauza chokhudza iye. Paulo akuyembekezera mlandu wake, anamulola kuti apeze nyumba ndiponso kuti azilalikira popanda vuto lililonse. Chifundo cha Aroma chimenechi chiyenera kuti chinatanthauza kuti kwa iwo, Paulo anali wosalakwa.—Machitidwe 28:17-31.
Paulo anakhalabe ali womangidwa kwa zaka zina ziŵiri. Chifukwa chiyani? Baibulo silimanena zifukwa zake. Mlandu wa apilo sanali kuuzenga mpaka pamene odandaula atakaonekeranso ku khoti chifukwa cha mlanduwo. Koma mwina Ayuda a ku Yerusalemu anazindikira kupereŵera kwa mlandu wawowo moti sanapitenso ku khoti. Mwina sanafune kukaonekera ku khotilo monga njira yochititsa kuti Paulo asalalikire kwa nthaŵi yaitali. Kaya anachita zimenezo pa zifukwa zotani, mfundo n’njakuti mwachionekere, Paulo atakaonekera m’khoti la Nero, anamuweruza kuti analibe mlandu ndipo anam’masula kuti akayambenso ntchito yake ya umishonale. Zaka pafupifupi zisanu zinali zitatha kuchokera pamene anamangidwa.—Machitidwe 27:24.
Kwa nthaŵi yaitali otsutsa choonadi akhala ‘akukonza chiwembu mwa lamulo’ pofuna kutsekereza ntchito yolalikira yachikristu. Zimenezi siziyenera kutidabwitsa. Yesu anati: “Ngati anandilondalonda Ine, adzakulondalondani inunso.” (Salmo 94:20, King James Version; Yohane 15:20) Komabe Yesu ananena motsindika kuti tilalikire uthenga wabwino padziko lonse lapansi. (Mateyu 24:14) Choncho, monga momwe mtumwi Paulo anachitira pothana ndi chizunzo ndi chitsutso, Mboni za Yehova lerolinonso ‘zimachirikiza ndi kukhazikitsa mwalamulo uthenga wabwino.’—Afilipi 1:7, NW.
[Mawu a M’munsi]
a Khoma lamiyala lalifupi ndilo linkatchinga pakati pa Chipinda cha anthu Akunja ndi chipinda cha m’kati. Nthaŵi ndi nthaŵi pa khoma limeneli ankaikapo zikwangwani zochenjeza. Zina ankazilemba m’Chigiriki ndipo zina m’Chilatini. Ankalembapo kuti: “Wakunja asadutse chotchinga ichi kuloŵa ku malo opatulika. Aliyense wopezeka atachita zimenezi adzaphedwa.”
b Kuchita zimenezi kunali koletsedwa. Buku lina limanena kuti: “Malinga ndi malamulo pankhani ya katangale, Lex Repetundarum, munthu aliyense waudindo ankaletsedwa kulandira ziphuphu n’cholinga chilichonse kaya kuti am’mange munthu kapena kum’masula, kuweruza kapena kusaweruza, kapena kutulutsa mkaidi m’ndende.”