Thandizani Ena Kulabadira Uthenga wa Ufumu
“Agripa anati kwa Paulo, Ndi kundikopa pang’ono ufuna kundiyesera Mkristu.”—MACHITIDWE 26:28.
1, 2. N’chifukwa chiyani mtumwi Paulo anakaonekera kwa Kazembe Festo ndi Mfumu Herode Agripa Wachiŵiri?
MU 58 C.E, Mfumu Herode Agripa Wachiŵiri ndi mlongo wake Bernike anapita ku Kaisareya kwa Kazembe wa Roma, Porkiyo Festo. Ataitanidwa ndi Kazembe Festo, mfumuyi pamodzi ndi mlongo wakeyu anafika ‘ndi chifumu chachikulu, naloŵa momvera milandu, pamodzi ndi akapitawo akulu, ndi amuna omveka a mudziwo.’ Festo analamula kuti awabweretsere mtumwi wachikristu Paulo. Kodi zinatani kuti wotsatira wa Yesu Kristu ameneyu akaime ku mpando wachiweruzo wa Kazembe Festo?—Machitidwe 25:13-23.
2 Zimene Festo anauza alendo ake zikupereka yankho la funso limeneli. Iye anati: ‘Mfumu Agripa, ndi amuna inu nonse muli nafe pano pamodzi, muona uyu, amene unyinji wonse wa Ayuda anandiuza za iye, ku Yerusalemu ndi kunonso, ndi kufuula kuti sayeneranso kukhala ndi moyo. Koma ndinapeza ine kuti sanachita kanthu koyenera imfa iye; ndipo popeza iye yekha anati akatulukire kwa Augusto, ndatsimikiza mtima kum’tumizako. Koma ndilibe ine kanthu koti ndinenetse za iye kakulembera kwa mbuye wanga. Chifukwa chake ndam’tulutsira kwa inu, ndipo makamaka kwa inu, Mfumu Agripa, kuti, ndikatha kum’funsafunsa, ndikhale nako kanthu kakulembera. Pakuti chindionekera chopanda nzeru, potumiza wam’nsinga, wosatchulanso zifukwa zimene akumuneneza.’—Machitidwe 25:24-27.
3. N’chifukwa chiyani atsogoleri achipembedzo anali kumuimba mlandu Paulo?
3 Mawu a Festo akusonyeza kuti Paulo anamusemera mlandu woukira boma—mlandu umene chiweruzo chake chinali kuphedwa. (Machitidwe 25:11) Komabe, Paulo anali wosalakwa. Mlanduwo unayambika chifukwa cha nsanje ya atsogoleri achipembedzo ku Yerusalemu. Anali kutsutsa ntchito ya Paulo monga wolengeza Ufumu ndipo ankadana nazo kwambiri kuti anali kuthandiza anthu ena kukhala otsatira a Yesu Kristu. Ndi chitetezo champhamvu, anachoka naye Paulo ku Yerusalemu kupita naye ku mzinda wa kudoko wa Kaisareya, kumene iye anapempha kuti akaonekere kwa Kaisara. Kuchoka kumeneko akanapita naye ku Roma.
4. Kodi ndi mawu odabwitsa otani amene Mfumu Agripa inanena?
4 Ganizirani Paulo ali kunyumba ya kazembe pamaso pa gulu limene panali wolamulira chigawo chofunika kwambiri mu Ufumu wa Roma. Mfumu Agripa inayang’ana Paulo ndi kunena kuti: “Kwaloleka udzinenere wekha.” Paulo akulankhula, panachitika chinthu chodabwitsa. Zimene Paulo anali kunena zinayamba kuigwira mtima mfumuyo. Ndipotu, Mfumu Agripa inati: “Ndi kundikopa pang’ono ufuna kundiyesera Mkristu.”—Machitidwe 26:1-28.
5. N’chifukwa chiyani mawu a Paulo kwa Agripa anali ogwira mtima kwambiri?
5 Tangoganizani! Chifukwa chakuti Paulo analankhula mwaluso pokana mlanduwo, wolamulira anakhudzidwa mtima ndi mphamvu yaikulu ya Mawu a Mulungu. (Ahebri 4:12) Kodi n’chiyani chinapangitsa zimene Paulo ananenazo kukhala zogwira mtima? Ndipo tingaphunzire chiyani kwa Paulo zimene zingatithandize mu ntchito yathu yopanga ophunzira? Tikaona zimene iye ananena pokana mlanduwo, pali mfundo ziŵiri zimene zili zapadera: (1) Paulo analankhula mfundo zokopa. (2) Anagwiritsa ntchito mwaluso zimene anali kudziŵa m’Mawu a Mulungu, monga momwe mmisiri amagwiritsa ntchito bwino chida.
Gwiritsani Ntchito Luso la Kukopa
6, 7. (a) Monga momwe awagwiritsira ntchito m’Baibulo, kodi mawu oti “kukopa” amatanthauza chiyani? (b) Kodi kukopa kumagwira ntchito yanji pothandiza anthu ena kulabadira zimene Baibulo limaphunzitsa?
6 M’buku la Machitidwe, mawu achigiriki amene anawamasulira kuti kukopa, agwiritsidwa ntchito mobwerezabwereza ponena za Paulo. Kodi akukhudzana bwanji ndi ntchito yathu yopanga ophunzira?
7 M’chinenero choyambirira cha Malemba Achigiriki Achikristu, “kukopa” kumatanthauza “kukhutiritsa” kapena “kumusintha munthu maganizo mwa kukambirana naye kapena pom’patsa mfundo za kakhalidwe kabwino,” linatero buku la Vine lotchedwa Expository Dictionary of New Testament Words. Kupenda tanthauzo lenileni la mawuŵa kumatithandiza kudziŵa zambiri. Limapereka lingaliro la kudalira. Choncho mukakopa munthu kulabadira zimene Baibulo likuphunzitsa, ndiye kuti mwam’pangitsa kuti akudalireni, moti amakhulupirira kuti zimene akuphunzirazo n’zoona. Ndithudi, sikokwanira kungouza munthu zimene Baibulo limanena kuti akhulupirire ndi kuchitapo kanthu. Womvera wanu ayenera kukhutira kuti zimene mukunena n’zoona, kaya munthuyo ndi mwana, woyandikana naye nyumba, mnzanu wakuntchito, kusukulu, kapena wachibale.—2 Timoteo 3:14, 15.
8. Kodi pamafunika chiyani kuti munthu akhutire ndi choonadi cha m’Malemba?
8 Kodi mungatani kuti munthu akhutire kuti zimene mukulalikira kuchokera m’Mawu a Mulungu n’choonadi? Paulo anayesetsa kusintha maganizo a anthu amene analankhula nawo mwa kupereka zifukwa zomveka, kufotokoza zinthu motsatirika, ndiponso kupembedzera anthu moona mtima.a Choncho, m’malo mongolalikira kuti chinachake n’choona, mufunika kupereka umboni wokhutiritsa woikira kumbuyo zimene mukunenazo. Kodi mungachite bwanji zimenezi? Tsimikizirani kuti zonena zanu n’zochokera m’Mawu a Mulungu basi osati m’maganizo mwanu. Ndiponso, gwiritsani ntchito umboni wina poikira kumbuyo zinthu zenizeni za m’Malemba zimene mukunena. (Miyambo 16:23) Mwachitsanzo, ngati mwanena kuti anthu omvera adzasangalala ndi moyo padziko lapansi la paradaiso, tsimikizirani zimenezi popereka umboni wa m’Malemba, monga Luka 23:43 kapena Yesaya 65:21-25. Kodi mungapereke bwanji umboni wina poikira kumbuyo mfundo ya m’Malemba imene mwanena? Mungagwiritse ntchito zitsanzo kuchokera pa zimene womvera wanuyo zamuchitikira pamoyo wake. Mungamukumbutse zinthu zosavuta kuzipeza ndiponso zaulere zimene timasangalala nazo monga kukongola kwa dzuŵa likamaloŵa, kununkhira bwino kwa maluŵa, kukoma kwa chipatso, kapena mmene zimasangalatsira kuona mbalame ikudyetsa ana ake. Muthandizeni kuona kuti zinthu zosangalatsa zimenezi ndi umboni wakuti Mlengi amafuna kuti tisangalale ndi moyo padziko lapansi.—Mlaliki 3:11, 12.
9. Kodi tingasonyeze bwanji kulolera mu ntchito yathu yolalikira?
9 Pokopa munthu kulabadira mfundo ina imene Baibulo limaphunzitsa, samalani kuti kulankhula kwanu mogwira mtima kusakupangitseni kuoneka ngati munthu wosalolera, zimene zingapangitse womvera wanu kutseka maganizo ndi mtima wake. Buku la Sukulu ya Utumiki limachenjeza izi: “Mfundo ya choonadi yachindunji yoonetsa kuti chikhulupiriro chimene munthu amachikonda n’chabodza, ngakhale mutapereka Malemba ambiri oikira umboni, kaŵirikaŵiri imakanidwa. Mwachitsanzo, ngati tingotsutsa zikondwerero zofala ndi kunena kuti n’zachikunja, anthuwo sangasinthe maganizo awo pa zikondwerero zimenezo. Koma kukambirana nawo n’kumene kungawathandize.” N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kukhala ololera? Bukuli linati: “Kukambirana nawo bwinobwino kumawalimbikitsa kulankhula. Kumasiyira anthu mfundo yoilingalira inuyo mutachoka, ndipo kumatsegula mpata wodzakambirananso ulendo wina. Komanso kumachititsa munthu kukopeka kwambiri.”—Akolose 4:6.
Luso Lokopa Lomwe Limagwira Mtima
10. Kodi Paulo anayamba bwanji kunena mfundo zake kwa Agripa pokana mlandu umene anali kumuimba?
10 Tsopano tiyeni tione mwachifatse mawu amene Paulo ananena pokana mlandu mu Machitidwe chaputala 26. Onani mmene anayambira kulankhula mfundo zake. Poyamba kulongosola nkhani yake, Paulo anapeza mfundo yoyamikira nayo Agripa, ngakhale kuti mfumuyo inali pachibwenzi ndi mlongo wake Bernike, yomwe inali nkhani yochititsa manyanzi kwambiri. Paulo anati: “Ndidziyesera wamwaŵi, Mfumu Agripa, popeza nditi ndidzikanira lero pamaso panu, za zonse zimene Ayuda andinenera nazo; makamaka popeza mudziŵitsa miyambo yonse ndi mafunso onse a mwa Ayuda; chifukwa chake ndikupemphani mundimvere ine moleza mtima.”—Machitidwe 26:2, 3.
11. Kodi mawu a Paulo kwa Agripa akusonyeza bwanji ulemu, ndipo kodi zinali ndi phindu lanji?
11 Kodi mwaona kuti Paulo anavomereza udindo wapamwamba umene Agripa anali nawo pomutchula dzina lake laulemu lakuti Mfumu? Izi zinasonyeza ulemu, ndipo mwa kusankha mawu abwino, Paulo anam’patsa ulemu Agripa. (1 Petro 2:17) Mtumwiyu anazindikira kuti Agripa anali kudziŵa zambiri za miyambo ndiponso malamulo ovuta a anthu ake achiyuda ndipo anati anali wosangalala kupereka mfundo zake pamaso pa wolamulira wodziŵa zinthu ameneyu. Paulo, yemwe anali Mkristu, sanachite zinthu ngati kuti iye anali wapamwamba kuposa Agripa, amene sanali Mkristu. (Afilipi 2:3) Koma, Paulo anapempha mfumuyo kuti imumvetsere zonena zake moleza mtima. Choncho, Paulo anapangitsa Agripa, komanso anthu ena omvera mlanduwo, kufunitsitsa kumvetsera zimene iye amafuna kunena. Iye anali kuyala maziko, mfundo zimene onse anali kuzidziŵa, oyambira kunena mfundo zake.
12. Mu ntchito yolengeza Ufumu, kodi tingawafike bwanji pamtima omvera athu?
12 Mofanana ndi Paulo pamaso pa Agripa, pamene tikuyamba kunena uthenga wa Ufumu mpaka pamapeto, tiyeni tizimufika pamtima womvera wathu. Tingachite zimenezi mwa kum’patsa ulemu weniweni munthu amene tikumulalikira ndiponso mwa kuchita chidwi chenicheni ndi moyo wake ndiponso maganizo ake.—1 Akorinto 9:20-23.
Gwiritsani Ntchito Mawu a Mulungu Mwaluso
13. Kodi inuyo, mofanana ndi Paulo, mungawalimbikitse bwanji omvera anu kuti achitepo kanthu pa zimene amva?
13 Paulo anafuna kulimbikitsa omvera ake kuti achitepo kanthu akamva uthenga wabwino. (1 Atesalonika 1:5-7) Pachifukwa chimenechi, anawafika pamtima wawo wophiphiritsa, umene umalimbikitsa anthu kuchita zinthu. Pamene tikupitiriza kuona zimene Paulo ananena kwa Agripa pokana mlandu uja, onani momwe Paulo ‘analunjikira nawo bwino Mawu a Mulungu’ mwa kutchula zinthu zimene Mose ndi aneneri ananena.—2 Timoteo 2:15.
14. Fotokozani mmene Paulo anagwiritsira ntchito luso la kukopa pamaso pa Agripa.
14 Paulo anadziŵa kuti Agripa anali Myuda dzina lokha. Poona kuti Agripa anali kudziŵa zachiyuda, Paulo ananena kuti ntchito yake yolalikira inali kwenikweni yokhudza ‘osati kanthu kena koma zimene aneneri ndi Mose ananena kuti zidzafika’ zokhudza imfa ndi kuuka kwa Mesiya. (Machitidwe 26:22, 23) Polankhula mwachidunji kwa Agripa, Paulo anafunsa kuti: “Mfumu Agripa, mukhulupirira aneneri kodi?” Agripa anasoŵa choyankha. Akanayankha kuti sakhulupirira aneneri, akanawononga mbiri yake monga Myuda wokhulupirira. Ndipo akanagwirizana ndi maganizo a Paulo, kukanakhala kusonyeza poyera kuti akugwirizana ndi mtumwiyo ndiponso akanatchedwa Mkristu. Paulo anayankha mwanzeru funso lake lomwe, kuti: ‘Ndidziŵa kuti muwakhulupirira.’ Kodi mtima wa Agripa unamulimbikitsa kuyankha zotani? Iye anayankha kuti: “Ndi kundikopa pang’ono ufuna kundiyesera Mkristu.” (Machitidwe 26:27, 28) Ngakhale kuti Agripa sanakhale Mkristu, mwachionekere Paulo anamufika pamtima ndi uthenga wake.—Ahebri 4:12.
15. Kodi Paulo anatha bwanji kuyambitsa mpingo ku Tesalonika?
15 Kodi mwaona kuti Paulo anali kulalikira uthenga wabwino komanso kugwiritsa ntchito mfundo zokopa? Chifukwa chakuti Paulo anagwiritsa ntchito njira imeneyi ‘polunjika nawo bwino mawu a Mulungu,’ ena amene anamumva sanangomvetsera chabe koma anakhulupirira. Ndi zimene zinachitika ku Tesalonika, kumene Paulo anafunafuna Ayuda ndi Akunja oopa Mulungu pa sunagoge. Nkhani ya pa Machitidwe 17:2-4 imati: “Paulo, monga amachita, analoŵa kwa iwo; ndipo masabata atatu ananena ndi iwo za m’malembo, natanthauzira, natsimikiza, kuti kunayenera Kristu kumva zowawa, ndi kuuka kwa akufa . . . Ndipo ena a iwo anakopedwa.” Paulo anali wokopa. Iye anali kukambirana nawo, kuwatanthauzira, ndiponso kuwatsimikizira mwa Malemba kuti Yesu anali Mesiya amene analonjezedwa kalekale. Zotsatira zake zinali zotani? Mpingo wa okhulupirira unakhazikitsidwa.
16. Kodi mungatani kuti musangalale kwambiri polengeza Ufumu?
16 Kodi mungakhale waluso kwambiri pankhani yokopa pofotokoza Mawu a Mulungu? Ngati ndi choncho, mudzasangalala kwambiri mu ntchito yanu yolalikira ndi kuphunzitsa anthu za Ufumu wa Mulungu. Ndi zimene zawachitikira ofalitsa uthenga wabwino amene atsatira mfundo yogwiritsa ntchito Baibulo kwambiri mu ntchito yolalikira.
17. Simbani zimene zinakuchitikirani inuyo kapena mfundo ya zimene zili m’ndimeyi posonyeza phindu logwiritsa ntchito Baibulo mu utumiki wathu.
17 Mwachitsanzo, woyang’anira woyendayenda wina wa Mboni za Yehova analemba kuti: “Abale ndi alongo ambiri ndithu tsopano akutengera Baibulo m’manja polalikira ku khomo ndi khomo. Izi zathandiza ofalitsa kuŵerenga lemba ndi anthu ambiri amene akumana nawo. Zathandiza eninyumba ndi ofalitsa omwe kuganiza za Baibulo osati magazini ndiponso mabuku okha akaganiza za utumiki wathu.” N’zoona kuti kuika Baibulo poonekera pochita ntchito yolalikira zimadalira zinthu zambiri, kuphatikizapo miyambo ya m’dera lomwe tikukhala. Komabe, tiyenera kufunitsitsa kukhala ndi mbiri yogwiritsa ntchito Mawu a Mulungu mwaluso pokopa ena kulabadira uthenga wa Ufumu.
Uoneni Utumiki Monga Momwe Mulungu Amauonera
18, 19. (a) Kodi Mulungu amauona bwanji utumiki wathu, ndipo n’chifukwa chiyani tiyenera kuuona monga mmene iye amauonera? (b) N’chiyani chingatithandize kupanga maulendo obwereza ogwira mtima? (Onani bokosi lakuti “Mmene Tingapangire Maulendo Obwereza Ogwira Mtima,” patsamba 16.)
18 Njira ina yofikira omvera anthu pamtima imakhudza kuona utumiki monga momwe Mulungu amauonera ndiponso kukhala oleza mtima. Cholinga cha Mulungu n’chakuti anthu onse ‘afike pozindikira choonadi.’ (1 Timoteo 2:3, 4) Kodi zimenezi si zimene timafuna? Yehova ndi wolezanso mtima, ndipo kuleza kwake kwapereka mwayi woti anthu ambiri alape. (2 Petro 3:9) Chotero, tikapeza munthu wofuna kumvetsera uthenga wa Ufumu, kungakhale kofunika kupitako mobwerezabwereza kuti tikakulitse chidwi chake. Zimatenga nthaŵi ndiponso pamafunika kuleza mtima kuti mbewu za choonadi zikule. (1 Akorinto 3:6) Bokosi la m’nkhani ino lakuti “Mmene Tingapangire Maulendo Obwereza Ogwira Mtima” lili ndi mfundo za mmene tingakulitsire chidwi chimene tapeza. Kumbukirani kuti moyo wa anthu—mavuto awo ndiponso mikhalidwe yawo—umasintha nthaŵi zonse. Mwina pangafunike kupita maulendo angapo kuti tiwapeze panyumba, komabe m’pake kuchita zimenezo. Tikufuna kuwapatsa mwayi woti amve uthenga wa Mulungu wa chipulumutso. Choncho, pemphani Yehova Mulungu kuti akupatseni nzeru kuti mukulitse luso lanu lokopa mu ntchito yanu yothandiza ena kulabadira uthenga wa Ufumu.
19 Tikangopeza munthu amene akufuna kumva zambiri za uthenga wa Ufumu, kodi n’chiyaninso tingachite monga antchito achikristu? Nkhani yathu yotsatira itiuza zimene tingachite.
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mudziŵe zambiri pankhani ya kukopa, onani maphunziro 48 ndi 49 m’buku la Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi n’chiyani chinapangitsa zimene Paulo ananena kwa Mfumu Agripa pokana mlandu umene anali kumuimba kukhala zogwira mtima?
• Kodi tingatani kuti uthenga wathu uziwafika anthu pamtima?
• Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizigwiritsa ntchito bwino Mawu a Mulungu powafika anthu pamtima?
• Kodi tingatani kuti tiziona utumiki mmene Mulungu amauonera?
[Bokosi/Zithunzi patsamba 16]
Mmene Tingapangire Maulendo Obwereza Ogwira Mtima
• Chitani chidwi kwambiri ndi anthu.
• Sankhani nkhani ya m’Baibulo yosangalatsa kuti mukambirane.
• Paulendo uliwonse yalani maziko aulendo wotsatira.
• Pitirizani kuganizira munthuyo mukachoka panyumba yake.
• Bwereraniko mofulumira, mwina patatha tsiku limodzi kapena aŵiri, kukakulitsa chidwi cha munthuyo.
• Kumbukirani kuti cholinga chanu ndi kuyambitsa phunziro la Baibulo lapanyumba.
• Pempherani kuti Yehova akulitse chidwi cha munthuyo.
[Chithunzi patsamba 15]
Paulo anagwiritsa ntchito luso la kukopa pamene anakaonekera kwa Kazembe Festo ndi Mfumu Agripa